Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Anadzipeleka na Mtima Wonse—Ku Madagascar

Anadzipeleka na Mtima Wonse—Ku Madagascar

“ANZANGA atanifotokozela zocitika zosangalatsa zimene anakumana nazo potumikila ku madela amene kunali apainiya ocepa, n’nayamba kulaka-laka kuti nikalaŵeko utumikiwo,” anatelo Sylviana, mpainiya wa zaka za m’ma 20. Kenako anakamba kuti: “Koma n’nali kuona monga siningakwanitse kukatumikila kosoŵa.”

Kodi na imwe mumamvela monga mmene Sylviana anamvelela? Kodi mumalaka-laka kukatumikila ku gawo limene kuli olengeza Ufumu ocepa, koma mumakayikila ngati mungakwanitse? Ngati n’conco, musataye mtima. Na thandizo la Yehova, abale na alongo ambili-mbili akwanitsa kuthetsa zopinga zimene zinali kuwalepheletsa kuwonjezela zocita mu utumiki wawo. Kuti mudziŵe mmene Yehova anathandizila ena a iwo, tiyeni tikambilane za abale na alongo amene akutumikila ku Madagascar, cisumbu cacinayi pa zisumbu zikulu-zikulu pa dziko lapansi.

M’zaka zoposa 10 zapitazi, ofalitsa na apainiya opitilila 70 ocokela m’maiko 11 * akhala akubwela kudzatumikila m’dziko la mu Africa limeneli, limene muli anthu acidwi, ndipo ambili amalemekeza Baibo. Komanso, ofalitsa ambili a kumeneko adzipeleka kukukila ku madela ena kuti akalalikile uthenga wa Ufumu m’gawo lonse la cisumbu cacikulu cimeneci. Lomba tiyeni tikambeko za ena mwa abale na alongo amene akutumikila m’dzikoli.

KUTHETSA MANTHA NA ZOFOOKETSA

Perrine na Louis

Louis na mkazi wake Perrine, amene ali na zaka za m’ma 30, anacoka ku France kupita ku Madagascar. Kwa zaka zambili, iwo anali kuganizila zowonjezela utumiki wawo mwa kukatumikila ku dziko lina, koma Perrine anali kuopa. Iye anati: “N’nali kuopa kukakhala ku malo acilendo. N’nali kuopa kucoka kwathu n’kusiya umoyo umene n’nazoloŵela, komanso kusiya acibululu, mpingo, na nyumba yathu. Kukamba zoona, nkhawa ndiyo inali copinga cacikulu cimene n’nafunika kulimbana naco.” Mu 2012, Perrine analimba mtima, ndipo iye na mwamuna wake Louis anakukila ku Madagascar. Kodi amamvela bwanji akaganizila zimene anasankha? Iye anati: “Zakhala zolimbitsa cikhulupililo kwambili kuona mmene Yehova akutithandizila pa umoyo wathu.” Nayenso Louis anati: “Tangoganizilani! Pa Cikumbutso cimene tinacita nawo koyamba m’dziko la Madagascar, maphunzilo athu a Baibo 10 anapezekapo.”

N’ciani cinalimbikitsa banjali kupitiliza kutumikila m’dzikolo pamene anakumana na mavuto? Anali kupemphela kwa Yehova mocondelela kuti awapatse mphamvu zowathandiza kupilila. (Afil. 4:13) Louis anafotokoza kuti: “Tinaona kuti Yehova anayankha mapemphelo athu potipatsa ‘mtendele wa Mulungu.’ Izi zinatithandiza kuika maganizo athu pa cimwemwe cimene tinali kupeza mu utumiki wathu. Cinanso, anzathu a m’dziko limene tinacokela anali kutitumila mameseji pa kompyuta na makalata otilimbikitsa kuti tipitilize utumiki wathu.”—Afil. 4:6, 7; 2 Akor. 4:7.

Yehova anadalitsa kwambili Louis na Perrine cifukwa ca kupilila kwawo. Louis anati: “Mu October 2014, tinakaloŵa Sukulu Yophunzitsa Baibo ya Akhristu Ali Pabanja * ku France. Sukuluyi inakhala mphatso yosaiwalika yocokela kwa Yehova.” Atatsiliza maphunzilo, iwo anatumizidwa kuti akapitilize kutumikila ku Madagascar, ndipo anakondwela maningi.

“MUKAPITA . . . TIDZAKUNYADILANI”

Nadine na Didier

Didier na mkazi wake Nadine anacoka ku France kupita ku Madagascar mu 2010. Pa nthawiyo, iwo anali na zaka za m’ma 50. Didier anati: “Tinacitapo upainiya tili acinyamata. Pambuyo pake, tinakhala ndi ana atatu, ndipo tinaleka upainiya kuti tilele anawo. Pamene anakula, tinayamba kuganizila zokatumikila ku dziko lina.” Nadine anakamba kuti: “Kuganizila zosiya ana athu kunali kunidetsa nkhawa. Koma iwo anatiuza kuti: ‘Mukapita kukatumikila kosoŵa ku dziko lina, tidzakunyadilani.’ Mau awo anatilimbikitsa kuti tipite. Olo kuti lomba timakhala kutali ndi ana athu, ndise okondwa kuti nthawi zambili timakwanitsa kukamba nawo.”

Cinali covuta kuti Didier na Nadine aphunzile citundu ca Cimalagase. “Sitilinso acicepele amene savutika kuphunzila citundu,” anatelo Nadine, kwinaku akumwetulila. Nanga anakwanitsa bwanji kuphunzila Cimalagase? Coyamba, anayamba kusonkhana mu mpingo wa Cifulenchi. Pambuyo pake, pamene anaona kuti angakwanitse kuphunzila Cimalagase, anakukila mu mpingo wa citundu cimeneci. Nadine anati: “Anthu ambili amene timakumana nawo mu ulaliki, amakondwela tikamaphunzila nawo Baibo. Nthawi zambili amayamikila tikapita kukaphunzila nawo. Poyamba, n’nali kuona ngati nikulota cabe. Nimakondwela kwambili kucita upainiya kuno. Nikauka m’maŵa, mu mtima nimati, ‘Kwaca lomba, niyende mu ulaliki!’”

Didier amaseka akakumbukila nthawi imene anayamba kuphunzila Cimalagase. Iye anati: “Tsiku lina, n’nali kucititsa msonkhano wa mpingo, koma sin’nali kumvetsetsa zimene abale na alongo anali kuyankha. N’nali kungoyamikila yankho iliyonse. N’tayamikila mlongo wina amene anapeleka yankho, abale na alongo amene anakhala kumbuyo kwake anayamba kunipatsa zizindikilo zoonetsa kuti yankho limene mlongoyo anapeleka silinali lolondola. Conco, mwamsanga n’nalata m’bale wina kuti ayankhenso. Kaya iye anayankha molondola kaya. Nikhulupilila kuti anatelo.”

ANAVOMELA NA MTIMA WONSE ATAITANIWA

Pa msonkhano wa cigawo wa mu 2005, Thierry na mkazi wake Nadia anaonelela seŵelo la mutu wakuti, “Yesetsani Kukwanilitsa Zolinga Zimene Zimalemekeza Mulungu.” Seŵelo la m’Baibo limeneli linali kukamba za Timoteyo. Seŵeloli linawagwila mtima kwambili cakuti anakhala ofunitsitsa kukatumikila kumene kunali olengeza Ufumu ocepa. Thierry anati: “Seŵelo litatha, tinayamba kuomba m’manja, ndipo ine n’nayang’ana mkazi wanga na kumufunsa kuti, ‘Kodi ise tingayende kuti kukatumikila?’ Mkazi wanga anakamba kuti nayenso anali kuganizila za kumene tingakatumikile.” Posakhalitsa, iwo anayamba kusintha zina na zina kuti akwanilitse colinga cawo. Nadia anakamba kuti: “Pang’ono m’pang’ono tinacepetsa katundu wathu cakuti tinangotsala na katundu wokwana m’masutukesi anayi.”

Kumanzele: Nadia na Marie-Madeleine. Kulamanja : Thierry

Iwo anapita ku Madagascar mu 2006. Atangoyamba kutumikila m’dzikolo, anaukonda kwambili utumiki wawo. Nadia anati: “Timakondwela na ŵanthu amene timakumana nawo mu ulaliki.”

Koma patapita zaka 6, banjali linakumana na vuto. Amayi ake a Nadia, a Marie-Madeleine, amene anali kukhala ku France, anagwa ndipo anathyoka dzanja na kuvulala ku mutu. Pambuyo pofunsila kwa dokota amene anali kuwathandiza, Thierry ndi Nadia anapempha amayiwo kuti abwele kudzakhala nawo ku Madagascar. Olo kuti pa nthawiyo anali na zaka 80, iwo anavomela na mtima wonse ataitaniwa. Kodi mlongo wacikulileyo anamvela bwanji atakukila ku dziko lina? Iye anakamba kuti: “Zinthu zina zimanivuta kujaila, koma ngakhale kuti sinikwanitsa kucita zambili, nimaona kuti ndine wofunika mu mpingo. Cimene cimanikondweletsa ngako n’cakuti kubwela kuno kwathandiza kuti ana anga apitilize kucita utumiki wopindulitsa kuno.”

“N’NAONA KUTI YEHOVA ANANITHANDIZA”

Riana akamba nkhani m’citundu ca Citandiroyi

Riana ni m’bale wa zaka za m’ma 20. Anakulila ku dela laconde lochedwa Alaotra Mangoro, kum’maŵa kwa dziko la Madagascar. Iye anaphasa bwino ku sukulu, ndipo anali na colinga cocita maphunzilo apamwamba. Komabe, pambuyo pophunzila Baibo, anasintha maganizo. Iye anati: “N’nayesetsa kuti nitsilize maphunzilo anga a ku sekondale mofulumilapo ndipo n’nalonjeza Yehova kuti, ‘Ngati nidzaphasa mayeso, nidzayamba upainiya.’” Atatsiliza maphunzilo, Riana anacitadi zimene analonjeza. Anayamba kukhala na m’bale wina amene ni mpainiya, anapeza nchito ya maola ocepa, ndipo anayamba upainiya. Riana anati: “Nimaona kuti n’napanga cosankha cabwino ngako.”

Komabe, acibululu ake sanamvetsetse cifukwa cimene iye anakanila kucita maphunzilo apamwamba kuti akapeze nchito yabwino. Riana anati: “Atate anga, amalume, na ambuya aakazi, onse anali kunilimbikitsa kuti nikacite maphunzilo apamwamba. Koma sin’nalole ciliconse kunicititsa kuleka upainiya.” Pasanapite nthawi, Riana anakhala na colinga cokatumikila kosoŵa. N’ciani cinacititsa kuti akhale na colinga cimeneci? Iye anakamba kuti: “Akawalala anathyola nyumba yathu na kuba katundu wanga wambili. Mwa ici, n’nayamba kuganizila mau a Yesu, akuti tiyenela ‘kuunjika cuma kumwamba.’ Conco, n’naganiza zoyamba kutumikila mwakhama kuti nipeze cuma cauzimu.” (Mat. 6:19, 20) Riana anakukila ku dela la kum’mwela kweni-kweni kwa dzikolo, kumene kumacitika cilala kaŵili-kaŵili. Delali lili pa mtunda wa makilomita 1,300 kucokela kumene iye anali kukhala poyamba. Kumeneko ndiye kwawo kwa anthu a mtundu wa Antandiroyi. Kodi n’cifukwa ciani iye anapita kumeneko?

Mwezi umodzi m’mbuyomo, akawalala asanamubele, Riana anali atayamba kuphunzila Baibo na amuna aŵili a mtundu wa Antandiroyi. Iye anaphunzilako kukamba citundu cawo, ndipo anayamba kuganizila za anthu ambili a mtundu wa Antandiroyi amene anali asanamveleko uthenga wa Ufumu. Iye anati: “N’napemphela kwa Yehova kuti anithandize kukwanilitsa colinga canga cokukila ku dela la anthu okamba Citandiroyi.”

Riana anakukadi, koma atangofika ku delalo anakumana na vuto. Sanapeze nchito. Munthu wina anamufunsa kuti: “N’cifukwa ciani unabwela kuno? Sudziŵa kuti anthu amacoka kuno kupita kumene wacokelako kukafuna nchito?” Patapita mawiki aŵili, Riana ananyamuka ku delalo kupita ku msonkhano wa cigawo. Pa nthawiyo, anali na ndalama zocepa kwambili, ndipo sanali kudziŵa kuti adzacita ciani. Pa tsiku lothela la msonkhanowo, m’bale wina anaika ndalama m’thumba la jekete ya Riana. Zinali ndalama zokwanila kuyendela ulendo wobwelela ku dela la anthu a mtundu wa Antandiroyi na kukayamba kabizinesi kogulitsa yogati. Riana anakamba kuti: “N’naona kuti Yehova ananithandiza pa nthawi imene n’nali kufunikadi thandizo. Izi zinanipatsa mwayi wopitiliza kuthandiza anthu amene analibe mwayi wophunzila za Yehova.” Panalinso zambili zimene anali kufunika kucita mu mpingo. Riana anati: “N’nali kukamba nkhani ya anthu onse pakangopita wiki imodzi. Yehova anali kuniphunzitsa kupitila m’gulu lake.” Masiku ano, Riana akupitiliza kulalikila uthenga wa Ufumu kwa anthu ambili okamba Citandiroyi, amene afuna kuphunzila za Yehova.

“ADZADALITSIDWA NDI MULUNGU WOKHULUPILIKA”

Yehova amatitsimikizila kuti “aliyense wofuna kudalitsidwa padziko lapansi adzadalitsidwa ndi Mulungu wokhulupilika.” (Yes. 65:16) Ngati ticita khama kulimbana na zopinga n’colinga cakuti tiwonjezele utumiki wathu, tidzalandila madalitso ocokela kwa Yehova. Ganizilani za Sylviana, amene tam’chula kuciyambi kwa nkhani ino. Iye anakamba kuti anali kuopa kukatumikila ku malo osoŵa cifukwa coganiza kuti sangakwanitse. N’cifukwa ciani anali kuganiza conco? Iye anati: “Mwendo wanga wa kumanzele ni waufupi na masentimita 9 kuyelekezela na unzake. Conco, nimayenda motsimphina moti nimalema mwamsanga.”

Sylviana (kumanzele) na Sylvie Ann (kulamanja) ali na Doratine pa tsiku la ubatizo wake

Ngakhale n’conco, mu 2014, Sylviana anagwilizana na Sylvie Ann, mpainiya wacitsikana wa mu mpingo mwawo, ndipo anakukila ku mudzi wina waung’ono umene uli pa mtunda wa makilomita 85 kucokela m’tauni yawo. Mosasamala kanthu za vuto limene Sylviana ali nalo, zimene anali kulaka-laka zinatheka. Ndipo anadalitsidwa kwambili. Iye anakamba kuti: “N’tatumikila ku malo osoŵa caka cimodzi cabe, Doratine, mayi wacitsikana amene n’nali kuphunzila naye Baibo, anabatizika pa msonkhano wa dela.”

“NDIKUTHANDIZA”

Mau oonetsa cikhulupililo amene abale na alongo athu amenewa anakamba, asonyeza kuti ngati tiyesetsa kulimbana na zopinga n’colinga cakuti tiwonjezele utumiki wathu, timadzionela tekha kukwanilitsika kwa lonjezo la Yehova kwa atumiki ake, lakuti: “Ndikulimbitsa. Ndithu ndikuthandiza.” (Yes. 41:10) Tikatelo, ubwenzi wathu na Yehova umalimba. Cinanso, kudzipeleka na mtima wonse kutumikila m’dela lathu kapena kukatumikila ku dziko lina, kumatithandiza kukonzekela mautumiki osiyana-siyana a m’dziko latsopano. Didier, amene tam’chulapo kale m’nkhaniyi, anakamba kuti: “Kutumikila ku malo osoŵa ni maphunzilo abwino amene amatithandiza kukonzekela umoyo wa m’tsogolo.” Tikulimbikitsa abale na alongo ambili odzipeleka kuti ayambe utumiki umenewu kuti aphunzitsidwe na Mulungu.

^ par. 4 Abale na alongo amene akutumikila m’dzikoli anacokela ku Canada, Czech Republic, France, Germany, Guadeloupe, Luxembourg, New Caledonia, Sweden, Switzerland, United Kingdom, na United States.

^ par. 8 Sukuluyi manje inaloŵedwa m’malo na Sukulu ya Alengezi a Ufumu. Atumiki a nthawi zonse amene akutumikila ku dziko lina, ndipo ni oyenelela kuloŵa sukuluyi malinga na ziyenelezo, angafunsile kuti akaloŵe sukuluyi m’dziko lawo kapena ku dziko lina, kumene imacitikila m’citundu cawo.