Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

N’cikondi Cotani Cimene Cimabweletsa Cimwemwe Ceni-ceni?

N’cikondi Cotani Cimene Cimabweletsa Cimwemwe Ceni-ceni?

“Odala ndi anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.”—SAL. 144:15.

NYIMBO: 111, 109

1. N’cifukwa ciani nthawi imene tikukhala ni yapadela?

TIKUKHALA m’nthawi yapadela kwambili. Monga mmene Baibo inakambila, Yehova akusonkhanitsa “khamu lalikulu la anthu . . . locokela m’dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu uliwonse, ndi cinenelo ciliconse.” Osonkhanitsidwawo tsopano ni “mtundu wamphamvu” wa anthu acimwemwe oposa 8 miliyoni, amene “akucitila [Mulungu] utumiki wopatulika usana ndi usiku.” (Chiv. 7:9, 15; Yes. 60:22) Kuposa kale lonse, masiku ano pali anthu ambili amene amakonda Mulungu na anthu anzawo.

2. Kodi anthu otalikilana na Mulungu amaonetsa cikondi cotani? (Onani pikica pamwambapa.)

2 Komabe, Malemba ouzilidwa anakambilatu kuti masiku otsiliza ano, anthu otalikilana ndi Mulungu adzakhala na cikondi cadyela. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Masiku otsiliza . . . , anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, . . . okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu.” (2 Tim. 3:1-4) Cikondi cadyela cimeneci n’cosagwilizana na cikondi cacikhristu. Anthu amene ali na zolinga zadyela sapeza cimwemwe cimene amafuna. Popeza kuti anthu ambili ali na cikondi cadyela, dzikoli lakhala ‘lovuta.’

3. Kodi m’nkhani ino tidzakambilana ciani? Ndipo n’cifukwa ciani kukambilana zimenezo n’kofunika?

3 Paulo anazindikila kuti cifukwa cakuti anthu ambili m’masiku otsiliza adzakhala na cikondi cadyela, Akhristu adzakhala pa ciopsezo mwauzimu. Conco, iye anapeleka cenjezo lakuti tiyenela ‘kupewa’ anthu amene ali na cikondi cadyela. (2 Tim. 3:5) Komabe, n’zosatheka kuwapewelatu anthu aconco. Nanga tingapewe bwanji kutengela makhalidwe oipa a anthu a m’dzikoli kuti tipitilize kucita zinthu zokondweletsa Yehova, Mulungu wathu wa cikondi? Tiyeni tikambilane kusiyana pakati pa cikondi cogwilizana ndi mfundo za m’Baibo na cikondi cimene lemba la 2 Timoteyo 3:2-4 limakamba. Kukambilana zimenezi kudzatithandiza kudzipenda na kuona mmene tingaonetsele cikondi cimene cimabweletsa cimwemwe ceni-ceni.

KUKONDA MULUNGU KAPENA KUDZIKONDA?

4. N’cifukwa ciani kudzikonda pa mlingo woyenelela si kulakwa?

4 Mtumwi Paulo anauzilidwa kulemba kuti: “Anthu adzakhala odzikonda.” Kudzikonda pa mlingo woyenelela kuli cabe bwino, ndipo n’kofunika. Umu ni mmene Yehova anatilengela. Yesu anati: “Uzikonda mnzako mmene umadzikondela wekha.” (Maliko 12:31) Ngati timadzizonda ise eni, n’zosatheka kukonda anzathu. Malemba amakambanso kuti: “Amuna akonde akazi awo monga matupi awo. Amene amakonda mkazi wake amadzikonda yekha, pakuti palibe munthu anadapo thupi lake, koma amalidyetsa ndi kulikonda.” (Aef. 5:28, 29) Conco, kudzikonda pa mlingo woyenelela n’kwabwino.

5. Kodi anthu odzikonda amacita zinthu motani?

5 Komabe, kudzikonda kochulidwa pa 2 Timoteyo 3:2 si kwabwino; n’kwadyela. Anthu odzikonda amadziganizila kwambili kuposa mmene ayenela kudziganizilila. (Ŵelengani Aroma 12:3.) Amangofuna kuti zawo ziziwayendela. Saganizila zofuna za ena. Ndipo zinthu zikalakwika, amakonda kuimba mlandu ena, m’malo movomeleza kulakwa kwawo. Buku lina lofotokoza Baibo linakamba kuti munthu wodzikonda ali ngati “kanyama kochedwa kanungu [kapena kuti kansoni], kamene . . . kamadzipinda n’kukhala ngati bola. Kamamva kuthuma bwino pobisa mutu na miyendo yake, . . . koma. . . kwa ena kamaonetsa minga zokha-zokha.” Anthu odzikonda otelo sakhala na cimwemwe ceni-ceni.

6. Kodi pamakhala zotulukapo zanji ngati munthu amakonda Mulungu?

6 Onani kuti Paulo pochula makhalidwe oipa amene adzakhala ofala m’masiku otsiliza, anayambila kuchula khalidwe la kudzikonda. Akatswili ena a Baibo amakamba kuti iye anatelo cifukwa makhalidwe enawo amayamba cifukwa ca kudzikonda. Mosiyana na zimenezi, anthu amene amakonda Mulungu, amakhala na makhalidwe abwino. Baibo imaonetsa kuti anthu okonda Mulungu amakhala ‘acimwemwe, amtendele, oleza mtima, okoma mtima, abwino, a cikhulupililo, ofatsa ndi odziletsa.’ (Agal. 5:22, 23) Wamasalimo analemba kuti: “Odala ndi anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.” (Sal. 144:15) Yehova ni Mulungu wacimwemwe, ndipo anthu ake amakhalanso acimwemwe. Kuwonjezela apo, mosiyana na anthu odzikonda amene amangofuna kulandila zinthu kwa ena, atumiki a Yehova amapeza cimwemwe mwa kukhala opatsa.—Mac. 20:35.

Tingapewe bwanji kukhala odzikonda? (Onani palagilafu 7)

7. Ni mafunso ati amene angatithandize kudziŵa ngati timam’kondadi Mulungu?

7 Kodi tingadziŵe bwanji ngati tayamba kudzikonda kwambili kuposa mmene timakondela Mulungu? Ganizilani malangizo a pa Afilipi 2:3, 4, akuti: “Musacite ciliconse ndi mtima wokonda mikangano kapena wodzikuza, koma modzicepetsa, ndi kuona ena kukhala okuposani. Musamaganizile zofuna zanu zokha, koma muziganizilanso zofuna za ena.” Ndiyeno, dzifunseni kuti: ‘Kodi nimatsatila malangizo amenewa mu umoyo wanga? Kodi nimayesetsa kucita cifunilo ca Mulungu na mtima wonse? Kodi nimayesetsa kuthandiza ena, kaya a mu mpingo kapena amene nimapeza mu ulaliki?’ Kudzipeleka kuti tithandize ena, nthawi zina kumakhala kovuta. Kumafuna khama na kudzimana. Koma ngati tiyesetsa kuthandiza ena, tidzapeza cimwemwe coculuka podziŵa kuti Mfumu ya cilengedwe conse ikukondwela nase.

8. N’ciani cimene ena acita cifukwa cokonda Mulungu?

8 Cifukwa cokonda Mulungu, ena asiya nchito zapamwamba n’colinga cakuti atumikile Yehova mokwanila. Mwacitsanzo, Ericka, amene amakhala ku United States, ni dokota. M’malo moika mtima wake wonse pa nchitoyi, iye anayamba upainiya wa nthawi zonse. Ndipo wakhala akutumikila m’maiko osiyana-siyana pamodzi na mwamuna wake. Ericka anati: “Tapeza madalitso ambili potumikila mumpingo wa citundu cina, kuphatikizapo mabwenzi. Izi zatithandiza kukhala na umoyo waphindu. Sin’nalekeletu kugwila nchito ya udokota. Koma nimaseŵenzetsa nthawi na mphamvu zanga zoculuka pothandiza kucilitsa anthu mwauzimu, ndi kuthandiza abale na alongo mu mpingo. Izi zimanipatsa cimwemwe mumtima ndi kunithandiza kukhala okhutila.”

KUUNJIKA CUMA KUMWAMBA KAPENA PA DZIKO?

9. N’cifukwa ciani anthu okonda ndalama sapeza cimwemwe?

9 Paulo analemba kuti anthu adzakhala “okonda ndalama.” Zaka zapitazo, mpainiya wina ku Ireland anakamba na munthu wina za Mulungu. Munthuyo anatenga kacikwama kake, na kutulutsamo ndalama. Kenako anamuonetsa ndalamazo, na kukamba monyadila kuti: “Uyu ndiye mulungu wanga!” Si ambili amene angacite kukamba kuti amaona ndalama monga mulungu wawo. Ngakhale n’conco, anthu ambili m’dzikoli amakonda kwambili ndalama na zinthu zakuthupi. Komabe, Baibo imakamba kuti: “Munthu wokonda siliva sakhutila ndi siliva, ndipo wokonda cuma sakhutila ndi phindu limene amapeza.” (Mlal. 5:10) Anthu aconco sakhutila na ndalama zimene amapeza, ndipo pofuna kudziunjikila ndalama zambili, amadzibweletsela “zopweteka zambili.”—1 Tim. 6:9, 10.

10. Kodi Aguri analemba ciani ponena za cuma na umphawi?

10 Tonse timafunikila ndalama. Zimatitetezela pa zinthu zina. (Mlal. 7:12) Koma kodi munthu angakhaledi wacimwemwe ngati ali cabe na ndalama zocepa zomuthandiza kugula zinthu zofunikila mu umoyo? Inde! (Ŵelengani Mlaliki 5:12.) Aguri mwana wa Yake analemba kuti: “Musandipatse umphawi kapena cuma. Ndidye cakudya cimene ndikufunika kudya.” N’zosavuta kudziŵa cifukwa cake sanafune kukhala wosauka kwambili. Iye anafotokoza kuti sanafune kuti akabe, cifukwa kuba kukananyozetsa Mulungu. Nanga n’cifukwa ciani anapempha Mulungu kuti asam’patse cuma? Iye anafotokoza kuti: “Kuti ndisakhute kwambili n’kukukanani kuti: ‘Kodi Yehova ndani?’” (Miy. 30:8, 9) Mwacionekele, mudziŵako anthu ena amene amadalila cuma cawo m’malo mokhulupilila Mulungu.

11. Kodi Yesu anapeleka malangizo anji ponena za ndalama?

11 Anthu okonda ndalama sangakondweletse Mulungu. Yesu anati: “Kapolo sangatumikile ambuye awili, pakuti adzadana ndi mmodzi ndi kukonda winayo, kapena adzakhulupilika kwa mmodzi ndi kunyoza winayo. Simungathe kutumikila Mulungu ndi Cuma nthawi imodzi.” Asanakambe izi, iye anati: “Lekani kudziunjikila cuma padziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbili zimawononga, ndiponso pamene mbala zimathyola ndi kuba. Koma unjikani cuma canu kumwamba, kumene njenjete kapena dzimbili sizingawononge, ndiponso kumene mbala sizingathyole n’kuba.”—Mat. 6:19, 20, 24.

12. Kodi kukhala na umoyo wosalila zambili kumatithandiza bwanji kutumikila Mulungu momasuka? Fotokozani citsanzo.

12 Ambili aona kuti kukhala na umoyo wosalila zambili kumawathandiza kukhala acimwemwe, komanso kumawapatsa nthawi yokwanila yotumikila Yehova. Mwacitsanzo, Jack, amene amakhala ku United States, anagulitsa nyumba yake yaikulu na bizinesi n’colinga cakuti akhale na nthawi yocita upainiya pamodzi na mkazi wake. Iye anati: “Cinali covuta kusiya nyumba yathu yokongola na malo athu m’dela labwino. Koma, kwa zaka zambili, n’nali kubwela ku nyumba nili osasangalala cifukwa ca mavuto a ku nchito. Mkazi wanga, amene ni mpainiya, nthawi zonse anali kukhala wosangalala. Anali kukonda kukamba kuti: ‘Ine nimaseŵenzela bwana wabwino ngako!’ Koma popeza tonse lomba ndise apainiya, timaseŵenzela Bwana mmodzi, Yehova.”

Tingapewe bwanji kukhala okonda ndalama? (Onani palagilafu 13)

13. Tingadzipende bwanji kuti tidziŵe ngati timaona ndalama moyenela?

13 Pofuna kudzipenda ngati timaona ndalama moyenela, tingacite bwino kuyankha mafunso awa moona mtima: ‘Kodi nimakhulupililadi malangizo a m’Baibo pa nkhani ya ndalama? Nanga kodi nimawaseŵenzetsa? Kodi nimaona kuti kufuna-funa ndalama ndiye cinthu cofunika kwambili? Kodi nimaona zinthu zakuthupi kukhala zofunika ngako kuposa ubwenzi wanga na Yehova ndiponso na anthu? Kodi nimakhulupililadi kuti Yehova adzanipatsa zosowa zanga?’ Dziŵani kuti Mulungu sangawagwilitse mwala anthu amene amayembekezela pa iye.—Mat. 6:33.

KUFUNA-FUNA YEHOVA KAPENA KUFUNA-FUNA ZOSANGALATSA?

14. Kodi zosangalatsa tiyenela kuziona bwanji?

14 Mogwilizana ndi ulosi wa m’Baibo, anthu ambili masiku ano ni “okonda zosangalatsa.” Monga taonela, kudzikonda pa mlingo woyenelela kulibe vuto, komanso ndalama pazokha zilibe vuto. N’cimodzi-modzi na zosangalatsa. Kucita zosangalatsa zabwino pa mlingo woyenela kulibenso vuto. Yehova safuna kuti tizikhala na umoyo wodzimana mopambanitsa, kapena kuti tizipewelatu zosangalatsa zonse, ni zabwino zomwe. Pokamba za atumiki okhulupilika a Mulungu, Baibo imati: “Pita ukadye cakudya cako mokondwela ndi kumwa vinyo wako ndi mtima wosangalala.”—Mlal. 9:7.

15. Kodi kukhala “okonda zosangalatsa” kumatanthauza ciani?

15 Komabe, lemba la 2 Timoteyo 3:4 limakamba za kukonda zosangalatsa koiŵala nako Mulungu. Onani kuti lembali silikamba kuti anthu adzakhala okonda zosangalatsa kuposa Mulungu, ngati kuti Mulunguyo amam’kondako pang’ono. Koma limati adzakhala okonda zosangalatsa ‘m’malo mokonda Mulungu.’ Katswili wina anati: “[Vesi] imeneyi sitanthauza kuti anthuwo amakondako Mulungu pa mlingo winawake. Koma imatanthauza kuti sam’konda ngakhale pang’ono.” Ili ni cenjezo lamphamvu kwa anthu amene amakonda zosangalatsa mopambanitsa. Mau akuti “okonda zosangalatsa” amakamba za anthu ‘otengeka ndi . . . zosangalatsa za moyo uno.’—Luka 8:14.

16, 17. N’citsanzo canji cimene Yesu anapeleka pa nkhani ya zosangalatsa?

16 Yesu anapeleka citsanzo cabwino kwambili pa nkhani yoona zosangalatsa moyenela. Nthawi ina, iye anapezeka pa “phwando la ukwati” komanso pa phwando lina lalikulu. (Yoh. 2:1-10; Luka 5:29) Pamene vinyo anatha pa phwando la cikwatilo, iye anasandutsa madzi kukhala vinyo. Ndipo pa nthawi ina, iye anatsutsa zokamba za anthu odzilungamitsa, amene anali kumunena cifukwa cakuti anali kudya na kumwa.—Luka 7:33-36.

17 Komabe, Yesu sanali kukonda kwambili zosangalatsa. Anali kukonda kwambili Yehova, ndipo anadzipeleka ngako pothandiza ena. Iye analolela kufa mozunzika pa mtengo wozunzikilapo pofuna kuti anthu ambili akapeze moyo. Yesu pokamba na anthu amene anali kufuna kukhala otsatila ake, anati: “Ndinu odala pamene anthu akukunyozani ndi kukuzunzani, komanso kukunamizilani zoipa zilizonse cifukwa ca ine. Kondwelani, dumphani ndi cimwemwe, cifukwa mphoto yanu ndi yaikulu kumwamba, pakuti umu ndi mmenenso anazunzila aneneli amene analipo inu musanakhaleko.”—Mat. 5:11, 12.

Tingapewe bwanji kukhala okonda zosangalatsa? (Onani palagilafu 18)

18. Ni mafunso ati amene angatithandize kudziŵa ngati timakonda zosangalatsa moyenela?

18 Tingadziŵe bwanji kuti sitikonda zosangalatsa mopambanitsa? Tingadzifunse mafunso monga awa: ‘Kodi nimaona zosangalatsa kukhala zofunika ngako kuposa misonkhano na ulaliki? Kodi nimalolela kudzimana zosangalatsa zina pofuna kutumikila Mulungu? Posankha zosangalatsa, kodi nimaganizila mmene Yehova adzaonela zosankhazo?’ Ngati timam’kondadi Mulungu, tidzayesetsa kupewa zosangalatsa zimene timadziŵilatu kuti iye amadana nazo, komanso ngakhale zimene tikuona kuti mwina iye angadane nazo.—Ŵelengani Mateyu 22:37, 38.

ZIMENE ZINGATIBWELETSELE CIMWEMWE

19. Ni anthu ati amene sakhala na cimwemwe ceni-ceni?

19 Dziko la Satanali lacititsa kuti anthu avutike kwa zaka zoposa 6,000, koma posacedwapa lidzawonongedwa. Tsopano m’dzikoli muli anthu ambili odzikonda, okonda ndalama, na zosangalatsa. Anthu amenewa ni adyela, ndipo amangofuna kukhutilitsa zokhumba zawo. Anthu aconco sakhala na cimwemwe ceni-ceni. Mosiyana na zimenezi, wamasalimo anati: “Wodala [wosangalala] ndi munthu amene thandizo lake limacokela kwa Mulungu wa Yakobo, amene ciyembekezo cake cili mwa Yehova Mulungu wake.”—Sal. 146:5.

20. Kodi kukonda Mulungu kwakuthandizani bwanji kukhala acimwemwe?

20 Cikondi pa Mulungu cikukulila-kulila pakati pa anthu ake. Ndipo caka ciliconse, anthu ambili amabwela m’gulu lathu. Umenewu ni umboni wakuti Ufumu wa Mulungu ukulamulila, ndipo posacedwa udzabweletsa madalitso osaneneka pa dzikoli. Munthu amapeza cimwemwe ceni-ceni komanso cokhalitsa ngati acita cifunilo ca Mulungu, na kudziŵa kuti akukondweletsa Yehova. Ndipo anthu amene amakonda Yehova adzakhala osangalala kwamuyaya. M’nkhani yotsatila, tidzakambilana makhalidwe ena amene munthu amakhala nawo ngati ali na cikondi cadyela. Tidzaonanso mmene makhalidwewo alili osiyana ndi makhalidwe a atumiki a Yehova.