Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi N’kumupatsilanji Amene Zonse N’zake?

Kodi N’kumupatsilanji Amene Zonse N’zake?

“Inu Mulungu wathu, tikukuyamikani ndi kutamanda dzina lanu lokongola.”—1 MBIRI 29:13.

NYIMBO: 80, 50

1, 2. Kodi Yehova amaseŵenzetsa bwanji zinthu zake mooloŵa manja?

YEHOVA ni Mulungu wooloŵa manja. Zonse zimene tili nazo n’zocokela kwa iye. Yehova ndiye mwini golide na siliva yense, kuphatikizapo zinthu zina zonse zacilengedwe. Zinthu zimenezi amaziseŵenzetsa pocilikiza zamoyo. (Sal. 104:13-15; Hag. 2:8) M’Baibo muli nkhani zambili zoonetsa mmene Yehova anasamalila anthu ake mozizwitsa.

2 Mwacitsanzo, kwa zaka 40, Yehova anapatsa mtundu wa Isiraeli mana na madzi pamene anali m’cipululu. (Eks. 16:35) Conco, iwo “sanasowe kanthu.” (Neh. 9:20, 21) Kupitila mwa mneneli Elisa, Yehova mozizwitsa anaculukitsa mafuta ocepa amene mayi wina wamasiye wokhulupilika anali nawo. Izi zinathandiza kuti mayiyo akwanitse kubweza nkhongole yake, na kutsala na ndalama zina zokwanila kusamalila banja lake. (2 Maf. 4:1-7) Komanso, ndi thandizo la Yehova, Yesu mozizwitsa anapeleka cakudya, ngakhale ndalama pamene kunakhala kofunikila.—Mat. 15:35-38; 17:27.

3. Kodi tidzakambilana ciani m’nkhani ino?

3 Yehova ali na zinthu zoculuka kwambili zimene amaseŵenzetsa posamalila zolengedwa zake za padziko. Ngakhale n’conco, iye wapatsa atumiki ake mwayi wogwilitsila nchito cuma cawo pocilikiza nchito ya gulu lake. (Eks. 36:3-7; ŵelengani Miyambo 3:9.) N’cifukwa ciani Yehova amafuna kuti tizim’patsako cuma cathu olo kuti zonse ni zake? Kodi atumiki okhulupilika a Yehova akale anali kucilikiza bwanji nchito yake? Kodi gulu la Mulungu limaseŵenzetsa bwanji zopeleka masiku ano? Tidzakambilana mafunso amenewa m’nkhani ino.

N’CIFUKWA CIANI TIMAPELEKA CUMA CATHU KWA YEHOVA?

4. N’ciani cimene timaonetsa Yehova pamene ticilikiza nchito yake ndi cuma cathu?

4 Timapeleka cuma cathu kwa Yehova cifukwa timam’konda ndiponso timamuyamikila. Timakhudziŵa kwambili tikaganizila zonse zimene Yehova waticitila. Pamene Mfumu Davide anali kufotokoza zinthu zofunika pomanga kacisi, iye anavomeleza kuti zonse zimene tili nazo zimacokela kwa Yehova, ndi kuti zonse zimene tingapeleke kwa Yehova n’zocokela kwa iye.—Ŵelengani 1 Mbiri 29:11-14.

5. Kodi Malemba amaonetsa bwanji kuti kupeleka zopeleka ni mbali yofunika kwambili ya kulambila koona?

5 Cinanso, kupatsa ni mbali ya kulambila Yehova. M’masomphenya, mtumwi Yohane anamvela atumiki a Yehova a kumwamba akunena kuti: “Ndinu woyenela, inu Yehova Mulungu wathu wamphamvu, kulandila ulemelelo ndi ulemu, cifukwa munalenga zinthu zonse, ndipo mwa kufuna kwanu, zinakhalapo ndipo zinalengedwa.” (Chiv. 4:11) Ndithudi, Yehova tiyenela kum’patsa ulemelelo na ulemu waukulu. Ndipo tingacite izi mwa kupeleka kwa iye zinthu zathu zabwino kwambili. Kupitila mwa Mose, Yehova analamula Aisiraeli kuti azikaonekela pamaso pake, pa zikondwelelo zitatu za pa caka. Monga mbali ya kulambila kwawo, pa zikondwelelozo Aisiraeli sanafunikile ‘kukaonekela kwa Yehova cimanjamanja.’ (Deut. 16:16) Masiku anonso, kupeleka zopeleka zathu mowoloŵa manja poyamikila na kucilikiza nchito ya gulu la Yehova, ni mbali yofunika kwambili ya kulambila kwathu.

6. Kodi kupatsa kuli na ubwino wanji kwa ife? (Onani pikica kuciyambi.)

6 Komanso, kupatsa kuli na ubwino wake kwa ise, kusiyana n’kumangolandila zinthu kwa ena. (Ŵelengani Miyambo 29:21.) Tiyelekezele kuti makolo apatsa mwana wawo wamng’ono ndalama. Ndipo pambuyo pake, mwanayo wapatulako ndalamayo n’kupatsa makolowo monga mphatso. Kodi iwo sangayamikile? Tiyelekezelenso kuti mpainiya wacicepele amene akukhala pakhomo pa makolo ake wapatsa makolowo ndalama zocepa kuti agulile zinthu zina zofunikila pa nyumba. N’kutheka kuti makolowo sanali kuyembekezela zimenezi, koma angalandilebe mphatsoyo cifukwa ni njila imene mwanayo angaonetsele kuti amayamikila zimene makolowo amam’citila. N’cimodzi-modzi na Yehova. Iye amadziŵa kuti kum’patsa zina mwa zinthu zathu zamtengo wapatali kuli na ubwino wake kwa ise.

KUCITA ZOPELEKA M’NTHAWI ZAKALE

7, 8. Kodi anthu a Yehova a m’nthawi yakale anapeleka bwanji citsanzo cabwino pa nkhani yocita zopeleka zothandizila (a) pa nchito zapadela? (b) pa nchito za masiku onse?

7 Baibo imaonetsa kuti, kuyambila kale, anthu a Mulungu akhala akucita zopeleka. Nthawi zina, anthu a Yehova anali kucita zopeleka zothandizila pa nchito zapadela. Mwacitsanzo, Mose anauza Aisiraeli kuti apeleke zopeleka zothandizila pa nchito yomanga cihema. Pa nthawi inanso, Mfumu Davide anapempha anthu a Mulungu kuti acite zopeleka zothandizila pa nchito yomanga kacisi. (Eks. 35:5; 1 Mbiri 29:5-9) M’nthawi ya Mfumu Yehoasi, ansembe anakonza zinthu zowonongeka pa nyumba ya Yehova poseŵenzetsa ndalama zimene anthu anapeleka. (2 Maf. 12:4, 5) Komanso, m’nthawi ya atumwi, abale atamva kuti anzawo akuvutika cifukwa ca njala, “anatsimikiza mtima kutumiza thandizo lililonse limene akanatha kwa abale okhala ku Yudeya.”—Mac. 11:27-30.

8 Nthawi zina, anthu a Yehova anali kucita zopeleka zothandizila anthu amene anali kutsogolela pa nchito yake. Mwacitsanzo, malinga ndi Cilamulo ca Mose, Alevi sanali kulandila coloŵa mofanana ndi Aisiraeli ena onse. Koma Aisiraeli anali kupatsa Aleviwo cakhumi, cimene cinali kuwathandiza kuti aziika mtima wawo pa nchito yawo ya pa cihema. (Num. 18:21) Mofananamo, Yesu na atumwi ake analandila thandizo kwa azimayi ‘amene anali kutumikila iwo pogwilitsa nchito cuma cawo.’—Luka 8:1-3.

9. Kodi anthu a Mulungu ena akale anali kupeza bwanji ndalama na zinthu zina zimene anali kupeleka?

9 Zopeleka zimene atumiki a Mulungu anali kupeleka anali kuzipeza m’njila zosiyana-siyana. Mwacitsanzo, pamene Aisiraeli anali kucita zopeleka zomangila cihema m’cipululu, ayenela kuti anapeleka zinthu zimene anatenga pocoka ku Iguputo. (Eks. 3:21, 22; 35:22-24) M’nthawi ya atumwi, Akhristu ena anali kugulitsa zinthu zawo, monga minda na nyumba, ndipo ndalamazo anali kuzipeleka kwa atumwi. Ndiyeno, atumwiwo anali kugaŵila osowa ndalamazo. (Mac. 4:34, 35) Akhristu ena anali kuika ndalama pa mbali kuti nthawi zonse azicita copeleka pocilikiza nchito ya Mulungu. (1 Akor. 16:2) Conco, munthu aliyense, kaya wolemela kwambili kapena wosauka kwambili, anali na mwayi wocita zopeleka.—Luka 21:1-4.

KUCITA ZOPELEKA MASIKU ANO

10, 11. (a) Tingatengele bwanji citsanzo ca atumiki a Yehova akale amene anali owoloŵa manja? (b) Mumamvela bwanji mukaganizila mwayi umene muli nawo wocilikiza pa nchito ya Ufumu?

10 Masiku ano, na ise nthawi zina tingafunikile kupeleka ndalama zothandizila pa nchito inayake yapadela. Mwacitsanzo, kodi pali makonzedwe omanga Nyumba ya Ufumu yatsopano imene muzisonkhanamo? Kapena kodi nyumba yanu ya Ufumu ikukonzedwanso? Nthawi zina, tingafunikile kupeleka ndalama zothandizila pa nchito yokonzanso ofesi yathu ya nthambi, zocilikizila msonkhano wacigawo, kapena zothandizila abale athu amene akhudzidwa na tsoka la zacilengedwe. Zopeleka zathu zimathandizanso pa nchito yosamalila abale na alongo amene akutumikila ku likulu lathu na m’maofesi a nthambi osiyana-siyana pa dziko lonse. Zimathandizanso kusamalila amishonale, apainiya apadela, na oyang’anila madela. Komanso, n’zodziŵikilatu kuti mpingo wanu unacita coŵinda ca ndalama zothandizila pa nchito yomanga Mabwalo a Misonkhano na Nyumba za Ufumu pa dziko lonse, kuti abale athu azisonkhanamo.

11 Tonse tili na mwayi wothandiza pa nchito imene Yehova akucita masiku ano otsiliza. Nthawi zambili, zopeleka zimapelekedwa mwamseli. Timaponya zopeleka zathu mosadzionetsela m’bokosi ya m’Nyumba ya Ufumu, kapena tingapeleke kupitila pa jw.org. Nthawi zina, tingaone ngati zopeleka zathu zocepa sizingathandize kweni-kweni. Komabe, dziŵani kuti gawo lalikulu la zopeleka limacokela kwa anthu amene amapeleka zocepa. Abale athu, ngakhale osauka kwambili, ali ngati Akhristu a ku Makedoniya. Akhristu amenewo anali “pa umphawi wadzaoneni,” koma anapempha mocondelela kuti awapatse mwayi wopelekako mphatso zacifundo, ndipo anapelekadi mowolowa manja.—2 Akor. 8:1-4.

12. Kodi gulu lathu limacita bwanji kuti zopeleka zizigwilitsidwa nchito moyenela?

12 Bungwe Lolamulila limacita zinthu mokhulupilika ndi mwanzelu pogwilitsila nchito zopeleka. (Mat. 24:45) Abale a m’bungweli amapemphela kuti apange zosankha zoyenela. Ndiyeno, zopelekazo amazipangila bajeti, na kuzigwilitsila nchito mogwilizana na colinga cake. (Luka 14:28) M’nthawi yakale, anthu osamalila zopeleka anali kucita zinthu mosamala pofuna kuonetsetsa kuti zopelekazo zikugwilitsidwa nchito mogwilizana na colinga cake. Mwacitsanzo, pamene Ezara anabwelela ku Yerusalemu, anatenga zinthu zimene mfumu ya Peresiya inapeleka monga copeleka. Katunduyo anaphatikizapo golide, siliva, na zinthu zina zimene mtengo wake masiku ano ungapose madola 100 miliyoni a ku America. Ezara anaona kuti zinthu zimenezi zinali zopeleka zaufulu zopita kwa Yehova. Conco, anayesetsa kucita zinthu mosamala pofuna kuteteza katunduyo pa ulendo wawo wodutsa m’dela loopsa. (Ezara 8:24-34) M’nthawi ya atumwi, Paulo analandila ndalama zimene Akhristu anapeleka kuti zikathandizile abale a ku Yudeya. Iye anaonetsetsa kuti anthu amene anapita kukapeleka ndalamazo ‘akusamalila zinthu zonse moona mtima, osati pamaso pa Yehova pokha ayi, komanso pamaso pa anthu.’ (Ŵelengani 2 Akorinto 8:18-21.) Gulu lathu limatengela citsanzo ca Ezara na Paulo. Limacita zinthu mosamala kwambili pofuna kuonetsetsa kuti zopeleka zikugwilitsidwa nchito moyenela.

13. N’cifukwa ciani gulu la Mulungu linasintha zinthu zina m’zaka zapitazi?

13 Banja lingasinthe zinthu zina n’colinga cakuti lisamaononge ndalama zambili kuposa zimene limapeza. Kapena angayambe kukhala na umoyo wosalila zambili n’colinga cakuti acite zambili potumikila Yehova. N’cimodzi-modzi na gulu la Yehova. M’zaka zaposacedwa, m’gululi mwakhala mukucitika nchito zambili zocititsa cidwi. Izi zinacititsa kuti nthawi zina ndalama zowonongedwa zizikhala zambili kuposa zimene zimabwela. Conco, gulu la Mulungu limayesetsa kupeza njila zocepetselako ndalama zowonongedwa, komanso limapepukitsako nchito zina, n’colinga cakuti likwanitse kucita zambili poseŵenzetsa zopeleka zanu zimene mumapeleka mowolowa manja.

MAPINDU AMENE AKHALAPO CIFUKWA CA ZOPELEKA ZANU

Zopeleka zanu zimathandiza pa nchito ya padziko lonse (Onani palagilafu 14-16)

14-16. (a) N’zinthu zina ziti zimene gulu lakhala likucita poseŵenzetsa zopeleka zanu? (b) Kodi imwe pacanu mwapindula bwanji na zinthu zimenezi?

14 Abale na alongo ambili amene atumikila Yehova kwa nthawi yaitali, amakonda kukamba kuti masiku ano kuli cakudya cauzimu ca mwana alilenji kuposa kale lonse. Ganizilani cabe! M’zaka zapitazi, tinayamba kuseŵenzetsa webusaite ya jw.org na JW Broadcasting. Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lafalitsidwa m’zitundu zambili. Mu 2014 ndi mu 2015, tinaseŵenzetsa masitediyamu akulu-akulu m’mizinda 14 padzikoli, pocita msonkhano wa maiko wa mutu wakuti, “Pitilizani Kufunafuna Ufumu wa Mulungu Coyamba.” Onse amene anapezekapo anasangalala kwambili.

15 Ambili amayamikila zinthu zabwino zimene gulu la Yehova likuticitila. Mwacitsanzo, pokamba za JW Broadcasting, m’bale wina na mkazi wake, amene akutumikila m’dziko lina ku Asia, analemba kuti: “Timatumikila m’tauni inayake yaing’ono. Mwa ici, nthawi zina timadziona monga tili kwa tekha, ndipo timaiwala zinthu zambili zimene Yehova akucita m’gulu lake. Koma tikaonelela mapulogilamu a JW Broadcasting, timakumbukila kuti tili m’gulu la abale a pa dziko lonse. Abale na alongo athu okondedwa amakondwela ngako na JW Broadcasting. Nthawi zambili amakamba kuti akaonelela mapulogilamu apamwezi, amamvela kuti ali pafupi na abale a m’Bungwe Lolamulila. Tsopano amanyadila kwambili kukhala m’gulu la Mulungu.”

16 Tikamba pano, padziko lonse pali Nyumba za Ufumu pafupi-fupi 2,500 zimene zikumangiwa kapena kukonzewanso. Abale a mu mpingo wina ku Honduras atayamba kusonkhana m’Nyumba ya Ufumu yatsopano, analemba kuti: “Ndise okondwela maningi kukhala m’banja la Yehova la m’cilengedwe conse na kukhala m’gulu labwino la abale a pa dziko lonse. Onse amenewa atithandiza kuti tikhale na Nyumba ya Ufumu m’dela lathu.” Enanso ambili amayamikila akalandila Baibo na zofalitsa za m’citundu cawo, akalandila thandizo pa nthawi ya tsoka la zacilengedwe, kapena akaona zotulukapo zabwino za ulaliki wa pa tumasitandi ndi wapoyela m’dela lawo.

17. N’ciani cimaonetsa kuti Yehova akucilikiza gulu lake masiku ano?

17 Anthu otiona samvetsetsa kuti timakwanitsa bwanji kugwila nchito yonseyi mwa kuseŵenzetsa cabe zopeleka zaufulu. Mwacitsanzo, bwana wa pa kampani ina yaikulu atapita kukaona makina athu opulintila, anadabwa kudziŵa kuti nchito yonse imagwilidwa na anchito ongodzipeleka. Anadabwanso kudziŵa kuti siticita malonda, koma timaseŵenzetsa cabe ndalama zimene anthu amapeleka mwa kufuna kwawo. Iye anakamba kuti izi sizingatheke mwa nzelu zathu cabe. Ndipo izi n’zoona. Tidziŵa kuti nchitoyi imatheka kokha cifukwa ca thandizo la Yehova.—Yobu 42:2.

MAPINDU AMENE TINGAPEZE POPELEKA CUMA CATHU KWA YEHOVA

18. (a) Ni madalitso anji amene timapeza ngati ticita zopeleka zocilikiza Ufumu wa Mulungu? (b) Tingawaphunzitse bwanji ana athu ndi acatsopano kucita zopeleka kuti nawonso alandile madalitso?

18 Yehova watilemekeza kwambili mwa kutipatsa mwayi wothandiza pa nchito yaikulu imene ikucitika masiku ano. Iye amatitsimikizila kuti tidzalandila madalitso ngati tipeleka cuma cathu pocilikiza Ufumu wake. (Mal. 3:10) Yehova analonjeza kuti munthu wopatsa mowoloŵa manja adzalandila mphoto. (Ŵelengani Miyambo 11:24, 25.) Kuwonjezela apo, ngati ndise opatsa, timakhala acimwemwe cifukwa “kupatsa kumabweletsa cimwemwe coculuka kuposa kulandila.” (Mac. 20:35) Mwa mau na zocita zathu, tingathandize ana athu ndi acatsopano kuona mmene angacilikizile pa nchitoyi, kuti nawonso alandile madalitso.

19. Kodi nkhani ino yakulimbikitsani bwanji?

19 Zonse zimene tili nazo n’zocokela kwa Yehova. Kupeleka cuma cathu kwa iye ni umboni wakuti timam’konda na kuti timayamikila zonse zimene waticitila. (1 Mbiri 29:17) Pocita zopeleka zocilikizila nchito yomanga kacisi, “anthu anasangalala cifukwa ca nsembe zaufulu zimene anapeleka, pakuti anapeleka nsembezo kwa Yehova ndi mtima wathunthu.” (1 Mbiri 29:9) Tiyeni na ise tipitilize kupeza cimwemwe mwa kupatsa Yehova zinthu zocokela m’dzanja lake.