Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Mudziŵa?

Kodi Mudziŵa?

Kodi mfundo za m’Cilamulo ca Mose analidi kuzigwilitsila nchito pothetsa milandu m’nthawi ya Aisiraeli?

INDE, nthawi zina. Onani citsanzo cimodzi. Lemba la Deuteronomo 24:14, 15 limati: “Usacitile cinyengo waganyu wovutika ndiponso wosauka n’kumubela, kaya akhale mmodzi wa abale ako kapena mmodzi mwa alendo okhala m’dziko lanu . . . Angafuule kwa Yehova cifukwa ca zimene iweyo wam’citila, iwe n’kupezeka kuti wacimwa.”

Phale limene panalembewa dandaulo la munthu wina woseŵenza m’munda

Pali mau olembedwa pa phale, amene ni dandaulo la munthu winawake pa mlandu wokhudzana ndi lamulo limeneli. Mauwa analembedwa m’zaka za m’ma 600 B.C.E. Phale lokhala na mau amenewa linapezeka m’dela la kufupi na ku Asidodi. Cioneka kuti mauwa amakamba za munthu wogwila nchito ya m’munda amene anali kum’ganizila kuti analephela kusonkhanitsa mbewu zonse zimene anauzidwa kuti asonkhanitse. Mau ake ni akuti: “Ine mtumiki wanu [wodandaula] nitatsiliza kusonkhanitsa mbeu masiku angapo apitawo, Hoshayahu mwana wa Shobayi anabwela n’kutenga covala canga. . . . Anzanga onse amene n’nali kugwila nawo nchito yokolola pa dzuŵa angacitile umboni . . . kuti zimene nakamba n’zoona. Ine sin’nalakwe ciliconse. . . . Ngati inu a bwanamkubwa simuona kuti ni udindo wanu kumuuza kuti abweze covala ca mtumiki wanu, mucite zimenezi cifukwa conimvela cifundo. Musakhale cete pamene ine mtumiki wanu nikukhala wopanda covala.”

Katswili wina wa mbili yakale, dzina lake Simon Schama, anakamba kuti dandaulo limeneli “likutiphunzitsa zambili osati cabe zakuti munthu woseŵenza m’munda anali kucondelela kuti amubwezele [covala cake]. Lionetsanso kuti wopemphayu anali kudziŵa malamulo a m’Baibo, maka-maka a mu Levitiko na mu Deuteronomo, oletsa kucitila nkhanza anthu osauka.”