Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mgwilizano Wokondweletsa pa Cikumbutso

Mgwilizano Wokondweletsa pa Cikumbutso

‘Taonani! Ndi zabwino komanso zosangalatsa kwambili . . . kukhala pamodzi mogwilizana!’—SAL. 133:1.

NYIMBO: 18, 14

1, 2. N’cocitika citi cimene cidzagwilizanitsa anthu oculuka mu 2018? Takamba conco cifukwa ciani? (Onani pikica pamwambapa.)

PA March 31, 2018, pamene dzuŵa lizikaloŵa, anthu a Mulungu na okondwelela ambili adzasonkhana pa Mgonelo wa Ambuye, umene umacitika kamodzi pa caka. Pa tsikulo, anthu mamiliyoni akakumbukila imfa ya Khristu. Cocitika cimeneci cimagwilizanitsa anthu ambili-mbili pa dziko lonse lapansi caka ciliconse.

2 Tangoganizilani mmene Yehova na Yesu adzakondwelela popenyelela anthu mamiliyoni pa dziko lapansi, akusonkhana pa cocitika cimeneci, ola ndi ola mpaka kutha kwa tsikulo. Baibo inakambilatu kuti “khamu lalikulu la anthu, limene palibe munthu aliyense amene anatha kuliŵelenga, locokela m’dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu uliwonse, ndi cinenelo ciliconse” lidzafuula kuti: “Cipulumutso cathu cacokela kwa Mulungu wathu, amene wakhala pampando wacifumu, ndi kwa Mwanawankhosa.” (Chiv. 7:9, 10) N’kosangalatsa cotani nanga! kuona kuti citamando cimeneci cimakwela kwa Yehova na Yesu caka ndi caka pa mwambo wa Cikumbutso.

3. Kodi nkhani ino idzayankha mafunso ati?

3 Conco, pali mafunso amene nkhani ino idzayankha. (1) Kodi aliyense wa ise angakonzekele bwanji kuti akapindule pa Cikumbutso? (2) Kodi Cikumbutso cimagwilizanitsa bwanji anthu a Mulungu? (3) Kodi aliyense payekha angalimbikitse bwanji mgwilizano? (4) Kodi kudzakhala Cikumbutso cothela? Ngati n’conco, ni liti?

MMENE TINGAKONZEKELELE CIKUMBUTSO KUTI TIKAPINDULE

4. N’cifukwa ciani tifunika kucita zonse zotheka kuti tikapezeke pa Cikumbutso?

4 Ganizilani za kufunika kopezeka pa Cikumbutso. Kumbukilani kuti misonkhano yonse ya mpingo ni mbali ya kulambila kwathu. Mwacidziŵikile, Yehova na Yesu amaona anthu amene amayesetsa kuti akapezeke pa msonkhano wofunika kwambili umenewu wa pa caka. Conco, timafuna kuti iwo aone kuti sitifuna kuphonya msonkhano umenewu, kupatulapo ngati pali vuto lalikulu kwambili. Tiyenela kuonetsa mwa zocita zathu kuti timaona misonkhano kukhala yofunika kwambili. Tikatelo, timapatsa Yehova cifukwa cina cosungila dzina lathu ‘m’buku la cikumbutso,’ kapena kuti “buku la moyo,” limene mumalembedwa maina a anthu amene akuyembekezela kukalandila moyo wosatha.—Mal. 3:16; Chiv. 20:15.

5. Pamene Cikumbutso cikuyandikila, kodi tingadziyese bwanji ‘kuti tione ngati tikali olimba m’cikhulupililo’?

5 Pamene Cikumbutso cikuyandikila, tingacite bwino kupatula nthawi yopemphela na kupenda mosamala ubwenzi wathu na Yehova. (Ŵelengani 2 Akorinto 13:5.) Tingacite bwanji zimenezi? Tifunika ‘kudziyesa kuti tione ngati tikali olimba m’cikhulupililo.’ Tingadziyese mwa kudzifunsa kuti: ‘Kodi nimakhulupililadi kuti nili m’gulu limene Yehova akuseŵenzetsa pokwanilitsa cifunilo cake? Kodi nimacita zonse zimene ningathe pa nchito yolalikila na kuphunzitsa anthu uthenga wabwino wa Ufumu? Kodi zocita zanga zimaonetsa kuti nimakhulupililadi kuti ano ni masiku otsiliza, ndi kuti mapeto a ulamulilo wa Satana ali pafupi? Kodi nimadalila Yehova na Yesu monga mmene n’nali kucitila pamene n’nadzipeleka kwa Yehova Mulungu?’ (Mat. 24:14; 2 Tim. 3:1; Aheb. 3:14) Kuganizila mayankho a mafunso amenewa kudzatithandiza kupitiliza kudziyesa kuti tidziŵe kuti ndise anthu otani.

6. (a) Kodi cofunika kwambili n’ciani kuti tikapeze moyo wosatha? (b) Kodi mkulu wina amakonzekela bwanji Cikumbutso caka ciliconse? Nanga imwe mungatengele bwanji citsanzo cake?

6 Ŵelengani na kusinkha-sinkha Malemba okamba za kufunika kwa Cikumbutso. (Ŵelengani Yohane 3:16; 17:3.) Cofunika kwambili kuti tikapeze moyo wosatha ni “kudziŵa” Yehova na “kukhulupilila” Yesu, Mwana wake wobadwa yekha. Pokonzekela Cikumbutso, mungacite bwino kupanga pulogilamu yapadela yoŵelenga imene ingakuthandizeni kuyandikila kwambili Yehova na Yesu. Ganizilani zimene mkulu wina, amene watumikila kwa zaka zambili, wakhala akucita. Kwa zaka, iye wakhala akusonkhanitsa nkhani za mu Nsanja ya Mlonda, zimene zimakamba za Cikumbutso ndi za cikondi cimene Yehova na Yesu anationetsa. Kukatsala mawiki ocepa kuti ticite Cikumbutso, iye amaŵelenganso nkhani zimenezo ndi kusinkha-sinkha kufunika kwa mwambo umenewu. Nthawi na nthawi, iye amaonjezela nkhani imodzi kapena ziŵili pa nkhani zimene anasonkhanitsazo. Mkuluyu amaona kuti ngati aŵelenga nkhani zimenezo, kuwonjela pa kuŵelenga na kusinkha-sinkha Malemba a pa nyengo ya Cikumbutso, amaphunzila mfundo zatsopano caka ciliconse. Koposa zonse, iye amaona kuti cikondi cake pa Yehova na Yesu cimakulila-kulila caka na caka. Conco, kukhala na pulogilamu ngati imeneyi, kungakuthandizeni kukulitsa cikondi na ciyamikilo canu pa Yehova na Yesu. Izi zidzakuthandizani kuti mukapindule mokwanila pa Cikumbutso.

MMENE CIKUMBUTSO CIMALIMBITSILA MGWILIZANO WATHU

7. (a) Kodi Yesu anapemphelela ciani pa tsiku limene anayambitsa Mgonelo wa Ambuye? (b) N’ciani cimaonetsa kuti Yehova anayankha pemphelo la Yesu?

7 Pa tsiku limene Yesu anayambitsa Mgonelo wa Ambuye, iye anapemphelela ophunzila ake kuti akhale ogwilizana ngati mmene iye alili wogwilizana ndi Atate wake. (Ŵelengani Yohane 17:20, 21.) Yehova anayankha pemphelo limenelo la Mwana wake wokondedwa, ndipo tsopano anthu mamiliyoni ambili amakhulupilila kuti Yehova anatumiza Mwana wake. Kupambana misonkhano ina yonse ya anthu a Mulungu, Cikumbutso cimapeleka umboni wamphamvu kwambili wakuti Mboni za Yehova n’zogwilizana. Anthu a Mulungu m’maiko osiyana-siyana, komanso a mitundu yosiyana-siyana amasonkhana pa malo olambilila padziko lonse lapansi. M’madela ena, cimaoneka cacilendo anthu a mitundu yosiyana-siyana kusonkhana pamodzi kuti alambile Mulungu. Ndipo anthu ena amaipidwa nazo. Koma Yehova na Yesu amakondwela kwambili na mgwilizano umenewu.

8. Pa nkhani ya mgwilizano, kodi Yehova anamuuza ciani Ezekieli?

8 N’zosadabwitsa kuti ise anthu a Yehova ndise ogwilizana. Yehova anakambilatu za mgwilizano umenewu. Ganizilani zimene iye anauza mneneli Ezekieli zokhudza kugwilizanitsa ndodo “ya Yuda” ndi “ya Yosefe” kuti zikhale ndodo imodzi. (Ŵelengani Ezekieli 37:15-17.) Nkhani ya “Mafunso Ocokela Kwa Aŵelengi,” imene inafalitsidwa mu Nsanja ya Mlonda ya July 2016, inakamba kuti: “Kupitila mwa mneneli wake Ezekieli, Yehova analosela kuti anthu [ake] adzabwelela ku Dziko Lolonjezedwa ndi kugwilizananso kuti akhale mtundu umodzi. Ulosiwo unakambanso kuti anthu amene amalambila Mulungu m’masiku ano otsiliza adzagwilizana ndi kukhala mtundu umodzi.”

9. Kodi kukwanilitsika kwa ulosi wa Ezekieli kumaonekela bwanji pa Cikumbutso caka ciliconse?

9 Kucokela mu 1919, Yehova anayambanso kusonkhanitsa odzozedwa. Amenewa ndiwo akuimilidwa na ndodo “ya Yuda.” M’kupita kwa nthawi, anthu ambili okhala na ciyembekezo ca padziko lapansi anayamba kugwilizana ndi odzozedwa. Anthu okhala na ciyembekezo ca padziko amenewa ndi amene akuimilidwa na ndodo “ya Yosefe.” Yehova analonjezelatu kuti adzaika pamodzi ndodo ziŵilizi kuti zikhale ndodo imodzi m’dzanja lake. (Ezek. 37:19) Iye anapanga magulu aŵiliwa kukhala “gulu limodzi” la nkhosa. (Yoh. 10:16; Zek. 8:23) Pa nthawi ino, magulu aŵiliwa akutumikila mogwilizana motsogoleledwa na Mfumu imodzi yaulemelelo, Yesu Khristu, amene mu ulosi wa Ezekieli akuchedwa “mtumiki [wa Mulungu] Davide.” (Ezek. 37:24, 25) Mgwilizano wocititsa cidwi umene unaloseledwa m’buku la Ezekieli, umaonekela kwambili pamene otsalila odzozedwa ndi a “nkhosa zina” asonkhana kuti akumbukile imfa ya Khristu caka ciliconse. Koma kodi n’ciani cimene aliyense wa ise angacite kuti alimbitse mgwilizano umenewu?

NJILA ZIMENE ALIYENSE WA ISE ANGALIMBITSILE MGWILIZANO

10. Kodi tingalimbitse bwanji mgwilizano pakati pa anthu a Mulungu?

10 Njila yoyamba imene tingalimbitsile mgwilizano wa anthu a Mulungu ni kukhala odzicepetsa. Pamene Yesu anali padziko lapansi, analangiza ophunzila ake kuti ayenela kukhala odzicepetsa. (Mat. 23:12) Ngati tili na mtima wodzicepetsa, ndiye kuti tidzapewa kutengela mzimu wodzikweza wa anthu a m’dzikoli. Kudzicepetsa kudzatithandiza kukhala ogonjela kwa anthu amene akutitsogolela. Ndipo kukhala ogonjela n’kofunika kwambili kuti mu mpingo mukhale mgwilizano. Koposa zonse, ngati ndise odzicepetsa, Mulungu amakondwela cifukwa iye “amatsutsa odzikweza, koma odzicepetsa amawasonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu.”—1 Pet. 5:5.

11. Kodi kuganizila tanthauzo la zizindikilo za pa Cikumbutso kungatithandize bwanji kulimbitsa mgwilizano?

11 Njila yaciŵili imene tingalimbitsile mgwilizano ni kuganizila tanthauzo la zizindikilo za pa Cikumbutso. Cikumbutso citatsala pang’ono kucitika, komanso maka-maka pa nthawi ya cikumbutso yeni-yeniyo, yesetsani kuganizila mozama za tanthauzo la mkate wopanda cofufumitsa ndi vinyo wofiila. (1 Akor. 11:23-25) Mkate umaimila thupi la Yesu langwilo limene linapelekedwa monga nsembe, ndipo vinyo amaimila magazi ake amene anakhetsedwa. Koma kudziŵa cabe tanthauzo la zizindikilo zimenezi, pakokha si kokwanila. Tifunikanso kukumbukila kuti nsembe ya dipo la Khristu, imationetsa cikondi cacikulu cimene Yehova na Yesu anatisonyeza. Yehova anatikonda popeleka Mwana wake monga nsembe yotiombola, ndipo Yesu nayenso anatikonda polola kutifela. Kuganizila cikondi cawo kuyenela kutilimbikitsa kuti tiziwakonda. Ndipo cikondi cimene ise na Akhristu anzathu tili naco pa Yehova cili ngati comangila cotigwilizanitsa pamodzi kwambili.

Ngati timakhululukila ena, timalimbitsa mgwilizano (Onani palagilafu 12, 13)

12. M’fanizo la Yesu la mfumu imene inakongoletsa anthu ndalama, kodi iye anaonetsa bwanji kuti Yehova amafuna kuti tizikhululukila ena?

12 Njila yacitatu imene tingalimbitsile mgwilizano ni kukhululukila ena na mtima wonse. Pamene tikhululukila ena, timaonetsa kuti timayamikila Yehova cifukwa cotikhululukila macimo athu kupitila mu nsembe ya dipo la Khristu. Ganizilani fanizo limene Yesu anakamba pa Mateyu 18:23-34. Ndiyeno, dzifunseni kuti, ‘Kodi nimacita zimene Yesu anaphunzitsa? Kodi nimawalezela mtima abale anga na kuwamvetsetsa? Kodi ndine wokonzeka kukhululukila amene anilakwila?’ N’zoona kuti zolakwa zimasiyana kukula kwake, ndipo kwa ise anthu opanda ungwilo zolakwa zina n’zovuta kwambili kukhululukila. Komabe, fanizo la Yesu limatiphunzitsa kuti Yehova amafuna kuti tizikhululuka. (Ŵelengani Mateyu 18:35.) Yesu anagogomeza momveka bwino kuti Yehova sangatikhululukile ngati tilephela kukhululukila abale athu, pamene pali maziko abwino ocitila zimenezo. Imeneyi ni nkhani yaikulu. Zili conco cifukwa ngati timakhululukila ena monga mmene Yesu anatiphunzitsila, timateteza na kulimbitsa mgwilizano wathu wamtengo wapatali.

13. Kodi kukhala anthu okhazikitsa mtendele kumalimbitsa bwanji mgwilizano?

13 Ngati timakhululukila ena, timaonetsa kuti ndise anthu okhazikitsa mtendele. Kumbukilani kuti mtumwi Paulo anapeleka malangizo akuti tiyenela ‘kuyesetsa ndi mtima wonse kusunga umodzi wathu mwa mzimuwo, ndi mwamtendele monga comangila cotigwilizanitsa.’ (Aef. 4:3) M’nyengo ino ya Cikumbutso, komanso maka-maka pa tsiku la Cikumbutso, tiyenela kuganizila mmene timacitila zinthu na ena. Tingadzifunse kuti: ‘Kodi nimaonetsa kuti ndine munthu amene sasungila ena zifukwa? Kodi nimadziŵika monga munthu amene amalimbikitsa mtendele na mgwilizano?’ Aya ni mafunso ofunika kwambili amene tiyenela kuwaganizila m’nyengo ino ya Cikumbutso.

14. Tingaonetse bwanji kuti ‘timalolelana m’cikondi’?

14 Njila yacinayi imene tingalimbitsile mgwilizano ni kukonda anthu ena potengela Yehova, amene ni Mulungu wacikondi. (1 Yoh. 4:8) Tifunika kupewa kukhala na maganizo akuti, “Ningafunike kuwakonda abale anga cifukwa ni lamulo ngakhale sinikondwela nawo.” Kaganizidwe kameneka n’kosiyana na malangizo a Paulo akuti tiyenela ‘kulolelana m’cikondi.’ (Aef. 4:2) Onani kuti pamenepa, Paulo sanakambe cabe kuti ‘tizilolelana.’ Koma anakamba kuti tifunika kulolelana “m’cikondi.” Kulolelana m’cikondi kumaphatikizapo zambili. Kumbukilani kuti mu mpingo mumapezeka anthu a mitundu yosiyana-siyana amene Yehova wawakokela kwa iye. (Yoh. 6:44) Popeza kuti Yehova wawakokela kwa iye, ndiye kuti amawaona kuti ni ofunika, ndipo amawakonda. Ngati iye amawakonda, nanga ise n’kulekelanji kuwakonda? Conco, tiyeni tiziwakonda abale athu monga mmene Yehova watilamulila.—1 Yoh. 4:20, 21.

KODI CIKUMBUTSO COTHELA CIKACITIKA LITI?

15. Tidziŵa bwanji kuti kudzakhala Cikumbutso cothela?

15 Tsiku lina, tidzacita Cikumbutso cothela. Tidziŵa bwanji zimenezi? M’kalata yoyamba youzilidwa imene Paulo analembela Akhristu odzozedwa a ku Akorinto, iye anakamba kuti mwa kucita Cikumbutso ca imfa ya Yesu caka ciliconse, iwo ‘amalengezabe imfa ya Ambuye mpaka iye adzafike.’ (1 Akor. 11:26) Pa lembali, mau akuti “adzafike” akamba za nthawi ya ‘kubwela’ kwa Yesu, kumene iye anakamba mu ulosi wake wonena za mapeto a nthawi ino. Ponena za cisautso cacikulu, cimene tsopano cayandikila, Yesu anati: “Cizindikilo ca Mwana wa munthu cidzaonekela kumwamba. Ndiyeno mafuko onse a padziko lapansi adzadziguguda pa cifuwa cifukwa ca cisoni, ndipo adzaona Mwana wa munthu akubwela pa mitambo ya kumwamba ndi mphamvu ndi ulemelelo waukulu. Iye [Yesu] adzatumiza angelo ake ndi kulila kwamphamvu kwa lipenga, ndipo adzasonkhanitsa osankhidwa ake kucokela ku mphepo zinayi, kucokela kumalekezelo a m’mlengalenga mpaka kumalekezelo ena.” (Mat. 24:29-31) ‘Kusonkhanitsa osankhidwa’ kochulidwa pa lembali, kudzacitika pa nthawi imene Akhristu odzozedwa onse amene adzakhala akali pa dziko lapansi adzalandila mphoto yawo ya kumwamba. Izi zidzacitika ikadzatha mbali yoyamba ya cisautso cacikulu, koma nkhondo ya Aramagedo isanayambe. Kenako, onse a 144,000 pamodzi na Yesu adzamenya nkhondo yogonjetsa mafumu onse a padziko lapansi. (Chiv. 17:12-14) Cikumbutso cimene cidzacitika odzozedwa atangotsala pang’ono kusonkhanitsidwa kupita kumwamba, n’cimene cidzakhala cothela. Zili conco cifukwa pa nthawiyo, Yesu adzakhala ‘atafika.’

16. Kodi ndinu wofunitsitsa kukapezekapo pa Cikumbutso ca caka cino? Cifukwa ciani?

16 Tiyeni ticite zilizonse zotheka kuti tikapindule mwa kupezekepo pa Cikumbutso ca pa March 31, 2018. Ndipo tiyeni tizimupempha Yehova kuti atithandize kupitilizabe kucita mbali yathu polimbitsa mgwilizano wa anthu ake. (Ŵelengani Salimo 133:1.) Kumbukilani kuti tsiku lina, tidzacita Cikumbutso cothela. Conco, pali pano tiyeni tiziyesetsa kupezeka pa Cikumbutso ciliconse. Komanso, tiziona mgwilizano umene timakhala nawo pa Cikumbutso kukhala wamtengo wapatali.