Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Muziona Kusiyana Pakati pa Anthu

Muziona Kusiyana Pakati pa Anthu

‘Mudzaona kusiyana pakati pa munthu wolungama ndi woipa.’—MAL. 3:18.

NYIMBO: 127, 101

1, 2. N’cifukwa ciani umoyo ungakhale wovuta kwa anthu a Mulungu masiku ano? (Onani pikica pamwambapa.)

ANTHU ambili ogwila nchito zacipatala amaseŵenza pakati pa anthu odwala matenda oyambukila. Iwo amayesetsa kusamalila odwalawo cifukwa amafuna kuwathandiza. Komabe, pocita zimenezi, amafunika kudziteteza kuti asatengele matendawo. Molingana na zimenezi, ambili a ise timakhala ndi kuseŵenza pamodzi na anthu a makhalidwe osagwilizana ndi a Mulungu. Izi zingapangitse umoyo kukhala wovuta kwa ise.

2 Masiku otsiliza ano, makhalidwe a anthu afika poipa kwambili. M’kalata yaciŵili yopita kwa Timoteyo, mtumwi Paulo anachula makhalidwe oipa amene anthu otalikilana ndi Mulungu ali nawo. Makhalidwe amenewa adzafika poipilatu m’tsogolomu. (Ŵelengani 2 Timoteyo 3:1-5, 13.) N’zoona kuti timaipidwa na makhalidwe amenewa. Komabe, tingathe kutengela makhalidwe na maganizo oipa a anthu amene timakhala nawo. (Miy. 13:20) M’nkhani ino, tidzakambilana mmene makhalidwe a anthu m’masiku otsiliza ano amasiyanilana ndi makhalidwe a anthu a Mulungu. Tidzakambilanso mmene tingapewele kutengela makhalidwe oipa, pamene tikuthandiza anthu mwauzimu.

3. Ni anthu ati amene ali na makhalidwe ochulidwa pa 2 Timoteyo 3:2-5?

3 M’kalata yake yopita kwa Timoteyo, mtumwi Paulo analemba kuti “masiku otsiliza” adzakhala “nthawi yapadela komanso yovuta.” Kenako, anachula makhalidwe 19 oipa amene anthu ali nawo masiku otsiliza ano. Makhalidwe amene anachula ni ofanana ndi amene ali pa Aroma 1:29-31. Koma pochula makhalidwewa m’kalata yopita kwa Timoteyo, iye anaseŵenzetsa mau ena amene sapezeka kwina kulikonse m’Malemba Acigiriki Acikhristu. Paulo anayamba kuchula makhalidwewa ni mau akuti “pakuti anthu adzakhala . . . ” Komabe, si anthu onse amene ali na makhalidwe oipa amenewa. Akhristu ali na makhalidwe abwino.—Ŵelengani Malaki 3:18.

MMENE TIMADZIONELA ISE ENI

4. Kodi anthu odzitukumula na onyada amadziona bwanji?

4 Paulo analemba kuti anthu adzakhala odzikonda ndi okonda ndalama. Kenako, analemba kuti anthu adzakhala odzimva, odzikweza, odzitukumula ndiponso onyada. Nthawi zambili, munthu amakhala na makhalidwe amenewa cifukwa codziona ngati wapamwamba kwambili kaamba ka maluso amene ali nawo, maonekedwe, cuma, kapena udindo wake. Anthu a makhalidwe amenewa amafuna kuti ena aziwatamanda. Katswili wina anafotokoza mmene munthu wonyada kwambili amadzionela. Analemba kuti: “Mu mtima mwake amakhala ngati ali na kaguwa, kamene amapitapo kukagwada n’kumadzilambila.” Ena amakamba kuti khalidwe lonyada n’loipa kwambili cakuti olo anthu onyadawo amaipidwanso na anthu anzawo onyada.

5. Kodi atumiki ena okhulupilika a Mulungu anakhala bwanji na mtima wodzikuza?

5 Yehova amadana kwambili na khalidwe la kunyada na kudzikweza. Iye amazonda anthu a “maso odzikweza.” (Miy. 6:16, 17) Kunyada na kudzikweza kumalepheletsa munthu kukhala pa ubwenzi na Mulungu. (Sal. 10:4) Amenewa ni makhalidwe a Mdyelekezi. (1 Tim. 3:6) Koma n’zomvetsa cisoni kuti ngakhale atumiki ena a Yehova anagwela mu msampha wa kudzikweza. Mwacitsanzo, mfumu ya Yuda, Uziya, anali wokhulupilika kwa zaka zambili. Koma Baibo imati: “Atangokhala wamphamvu, mtima wake unadzikuza mpaka kufika pom’pweteketsa. Conco anacita zosakhulupilika kwa Yehova Mulungu wake ndipo anapita m’kacisi wa Yehova kukafukiza paguwa lansembe zofukiza.” Patapita zaka, nayenso Mfumu Hezekiya anakhala na mtima wodzikuza, koma anasintha mwamsanga.—2 Mbiri 26:16; 32:25, 26.

6. N’zinthu ziti zimene zikanacititsa Davide kukhala wonyada kapena wodzikweza? Nanga n’ciani cinam’thandiza kukhalabe wodzicepetsa?

6 Anthu ena amayamba kunyada na kudzikweza cifukwa ca kukongola, kuchuka, maluso a kuimba, mphamvu, kapena udindo umene ali nawo. Davide anali na zonse zimenezi. Koma anakhalabe na mtima wodzicepetsa mu umoyo wake wonse. Davide atapha Goliyati na kupatsidwa mwana wamkazi wa Mfumu Sauli kukhala mkazi wake, anakamba kuti: “Ndine yani ine, ndipo abale anga, anthu a m’banja la bambo anga ndani mu Isiraeli monse muno kuti ndikhale mkamwini wa mfumu?” (1 Sam. 18:18) N’ciani cinathandiza Davide kukhalabe wodzicepetsa? Iye anadziŵa kuti anakhala na maluso, mphamvu, na maudindo cifukwa cakuti Mulungu ‘anatsika m’munsi,’ kapena kuti anadzicepetsa, kuti amuthandize. (Sal. 113:5-8) Davide anadziŵanso kuti zabwino zonse zimene anali nazo anapatsiwa na Yehova.—Yelekezelani na 1 Akorinto 4:7.

7. N’ciani cingatithandize kukhala odzicepetsa?

7 Mofanana na Davide, anthu a Yehova lelolino amayesetsa kukhala odzicepetsa. Timacita cidwi podziŵa kuti Yehova, amene ni wamkulu koposa m’cilengedwe conse, ali na khalidwe labwino la kudzicepetsa. (Sal. 18:35) Conco, timatsatila malangizo ouzilidwa akuti: “Valani cifundo cacikulu, kukoma mtima, kudzicepetsa, kufatsa, ndi kuleza mtima.” (Akol. 3:12) Komanso, timadziŵa kuti cikondi “sicidzitama, sicidzikuza.” (1 Akor. 13:4) Tikakhala odzicepetsa, anthu ena adzakopeka na kufuna kuphunzila za Yehova. Malemba amakamba kuti mwamuna amakopeka na khalidwe labwino la mkazi wake popanda mau. Mofananamo, anthu ena amayandikila Mulungu cifukwa ca kudzicepetsa kwa anthu ake.—1 Pet. 3:1.

MMENE TIMACITILA ZINTHU NA ENA

8. (a) Kodi kusamvela makolo, anthu ena amakuona bwanji masiku ano? (b) Kodi Malemba amalangiza ana kucita ciani?

8 Paulo anafotokoza mmene anthu adzayamba kucitila zinthu na anthu anzawo m’masiku otsiliza. Iye analemba kuti m’masiku otsiliza, ana adzakhala osamvela makolo. Masiku ano, mabuku ambili, mafilimu, na mapulogilamu a pa TV, amalimbikitsa ana kukhala osamvela makolo kapena kuona ngati khalidweli lilibe vuto. Koma zoona zake n’zakuti kusamvela makolo kumasokoneza mtendele wa banja, lomwe ndilo maziko ofunika a cikhalidwe ca anthu. Kuyambila kale-kale, anthu akhala akuidziŵa bwino mfundo imeneyi. Mwacitsanzo, ku Girisi, ngati munthu wamenya makolo ake, anali kulandidwa ufulu uliwonse umene anali nawo monga nzika. Ndipo m’malamulo a Aroma, kumenya tate unali mlandu waukulu kulingana na mlandu wa kupha munthu. Komanso, Malemba Aciheberi na Malemba Acigiriki Acikhristu, onse amalangiza ana kuti azilemekeza makolo awo.—Eks. 20:12; Aef. 6:1-3.

9. N’ciani cingathandize ana kuti azimvela makolo awo?

9 Ana angapewe kutengela khalidwe losamvela makolo mwa kuganizila zabwino zimene makolo awo amawacitila. Cina cimene cingawalimbikitse kucita izi, ni kukumbukila kuti kumvela ni lamulo locokela kwa Mulungu, Atate wa ife tonse. Ndipo ngati ana amakamba zabwino ponena za makolo awo, angathandize ana anzawo kuti azilemekezanso makolo awo. Ngati makolo saonetsa cikondi cacibadwa kwa ana awo, cingakhale covuta kuti anawo aziwamvela na mtima wonse. Koma ngati ana amaona kuti makolo awo amawakondadi, amalimbikitsidwa kuwamvela ngakhale pamene aona kuti n’zovuta kutelo. Mnyamata wina, dzina lake Austin anati: “N’nali na mtima wosafuna kumvela. Koma makolo anga anali kunipatsa malamulo amene ningakwanitse kuwatsatila, anali kunifotokozela cifukwa cake anipatsa malamulowo, na kumakamba nane momasuka. Izi zinanithandiza kukhala womvela. N’nali kuona kuti amanikonda, ndipo zimenezo zinanilimbikitsa kuti nizicita zinthu zowakondweletsa.”

10, 11. (a) Ni makhalidwe oipa ati amene amaonetsa kuti anthu sakonda anzawo? (b) Kodi cikondi cimene Akhristu oona ali naco pa anthu anzawo n’cacikulu motani?

10 Paulo anachulanso makhalidwe ena oipa amene amaonetsa kuti anthu alibe cikondi pa wina na mnzake. Iye atachula za “kusamvela makolo,” anachula za kusayamika. Anthu osayamika amasuliza zabwino zimene ena amawacitila. Anakambanso kuti anthu adzakhala osakhulupilika. Adzakhala osafuna kugwilizana ndi anzawo, kapena kuti osafuna kukambilana kuti agwilizanenso na anthu amene anakangana nawo. Adzakhalanso onyoza ndi aciwembu, kapena kuti okamba mau opweteka ndi acipongwe kwa anthu anzawo, ngakhale kwa Mulungu. Komanso, anakamba kuti anthu adzakhala onenela anzawo zoipa pofuna kuwaipitsila mbili. *

11 Mosiyana ndi anthu ambili m’dzikoli, amene alibe cikondi, anthu a Yehova amaonetsa cikondi ceni-ceni kwa anthu anzawo. Ndipo akhala akucita izi kucokela kale-kale. Yesu anakamba kuti kukonda anzathu, komwe ni mbali ya cikondi ca a·ga’pe, ndi lamulo laciŵili lalikulu kwambili m’Cilamulo ca Mose, ndipo loyamba ni kukonda Mulungu. (Mat. 22:38, 39) Yesu anakambanso kuti kukondana cidzakhala cizindikilo ca Akhristu oona. (Ŵelengani Yohane 13:34, 35.) Akhristu oona amakondanso ngakhale adani awo.—Mat. 5:43, 44.

12. Kodi Yesu anaonetsa bwanji kuti anali kukonda anthu?

12 Yesu anali kukonda kwambili anthu. Anali kuyenda mu mzinda na mzinda kukalalikila uthenga wabwino wokamba za Ufumu wa Mulungu. Anali kucilitsa akhungu, olumala, akhate, na ogontha. Analinso kuukitsa akufa. (Luka 7:22) Yesu anafika ngakhale popeleka moyo wake pofuna kuwombola mtundu wa anthu. Anacita izi olo kuti ambili anali kumuzonda. Yesu anaonetsa bwino kwambili cikondi cimene Atate wake ali naco. Masiku ano, Mboni za Yehova pa dziko lonse zimatengela Yesu mwa kuonetsa cikondi kwa anthu anzawo.

13. Kodi cikondi cimene timaonetsa kwa ena cingawathandize bwanji kuphunzila za Yehova?

13 Cikondi cimene timaonetsa kwa anthu cimawalimbikitsa kufuna kuphunzila za Atate wathu wakumwamba. Mwacitsanzo, mwamuna wina ku Thailand atapezeka pa msonkhano wa cigawo, anacita cidwi kwambili na cikondi ca pakati pa abale na alongo. Atabwelela ku nyumba, anapempha kuti ayambe kuphunzila Baibo kaŵili pa wiki. Iye anayamba kulalikila kwa acibululu ake onse. Patapita cabe miyezi 6 kucokela pamene anapezeka pa msonkhano wa cigawo, iye anakamba nkhani yake yoyamba yoŵelenga Baibo ku Nyumba ya Ufumu. Pofuna kudzipenda kuti tione ngati timakonda anthu ena na mtima wonse, tingadzifunse kuti: ‘Kodi nimayesetsa kuthandiza ena pa banja pathu, mu mpingo, kapena mu ulaliki? Kodi nimayesetsa kuona ena mmene Yehova amawaonela?’

NKHOSA NA MIMBULU

14, 15. Ni makhalidwe ati olingana ndi a nyama amene anthu ambili ali nawo? Nanga n’ciani cinathandiza ena kusintha?

14 M’masiku otsiliza ano, anthu alinso na makhalidwe ena oipa amene tiyenela kuwapewa. Baibo inakamba kuti anthu osaopa Mulungu adzakhala osakonda zabwino. Ma Baibo ena amamasulila mau amenewa kuti, “odana ndi zabwino” kapena kuti “oipidwa na ciliconse cabwino.” Inakambanso kuti anthu adzakhala osadziletsa, na oopsa. Komanso adzakhala osamva za ena, kapena kuti opupuluma ndi ocita zinthu mosasamala.

15 Anthu ambili amene poyamba anali na makhalidwe monga a nyama, anasintha na kukhala a khalidwe labwino. Kusintha kumeneku kunanenedwelatu mu ulosi wa m’Baibo. (Ŵelengani Yesaya 11:6, 7.) Lembali limakamba za nyama za m’sanga, monga mimbulu na mikango, zimene zidzakhala pamodzi mwamtendele na nyama zoŵeta, monga ana a nkhosa ndi a ng’ombe. Onani kuti lembali lionetsa kuti mtendele umenewu udzakhalapo “cifukwa dziko lapansi lidzadzaza ndi anthu odziŵa Yehova.” (Yes. 11:9) Popeza kuti nyama sizingaphunzile za Yehova, mwauzimu ulosiwu ukukwanilitsika pakati pa anthu.

Kutsatila mfundo za m’Baibo kumathandiza munthu kusintha khalidwe lake (Onani palagilafu 16)

16. Kodi Baibo yathandiza bwanji anthu kusintha umunthu wawo?

16 Pali anthu ambili amene poyamba anali oopsa monga mimbulu, koma lomba amakhala mwamtendele ndi anzawo. Mungaŵelenge za ena mwa anthu amenewa, m’nkhani za pa jw.org, za mutu wakuti “Baibo Imasintha Anthu.” Anthu amene adziŵa Yehova na kuyamba kum’tumikila sacita zinthu ngati anthu a m’dzikoli, amene amaoneka ngati odzipeleka kwa Mulungu, koma amakana kuti mphamvu ya kudzipelekako iwasinthe. Anthu a m’dzikoli amadzionetsa monga olambila Mulungu, koma zocita zawo sizionetsa kuti amam’lambiladi. Mosiyana na anthu amenewa, pakati pa anthu a Yehova, pali ambili amene kale anali oopsa, koma ‘avala umunthu watsopano umene unalengedwa mogwilizana ndi cifunilo ca Mulungu ndipo umatsatila zofunika pa cilungamo ceniceni ndi pa kukhulupilika.’ (Aef. 4:23, 24) Anthu akayamba kuphunzila za Mulungu, amaona kufunika kotsatila mfundo zake pa umoyo wawo. Izi zimawalimbikitsa kusintha zikhulupililo zawo, maganizo, na khalidwe lawo. Kusintha mwanjila imeneyi si kopepuka. Koma n’kotheka cifukwa mzimu wa Mulungu umathandiza anthu amene amafunitsitsa kucita cifunilo cake.

“ANTHU AMENEWA UWAPEWE”

17. Tingapewe bwanji kutengela anthu a makhalidwe oipa?

17 Kusiyana pakati pa anthu amene amatumikila Mulungu na amene sam’tumikila kukuonekela ngako tsopano. Ise atumiki a Mulungu tifunika kusamala kuti tisayambe kutengela makhalidwe oipa a anthu ena. Timaonetsa nzelu mwa kupewa anthu amene ali na makhalidwe ochulidwa pa 2 Timoteyo 3:2-5. N’zoona kuti sitingawapeweletu anthu a makhalidwe oipa. Ena mwa anthu aconco timaseŵenza nawo, kuphunzila nawo ku sukulu, kapena kukhala nawo. Koma tingakwanitse kupewa kutengela maganizo na makhalidwe awo. Tingacite bwanji zimenezi? Tiyenela kulimbitsa ubwenzi wathu na Yehova mwa kuŵelenga Baibo na kugwilizana kwambili na anthu odzipeleka potumikila Yehova.

18. Kodi zokamba zathu na makhalidwe athu zingapindulitse bwanji anthu ena mwauzimu?

18 Tiyenelanso kuyesetsa kuthandiza ena mwauzimu. Muzisakila mipata yolalikila kwa ena, ndipo muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kudziŵa zoyenela kukamba pa nthawi yoyenela. Sitiyenela kudzibisa kuti ndise a Mboni za Yehova. Tikatelo, anthu adzalemekeza Mulungu cifukwa ca makhalidwe athu abwino m’malo molemekeza ise. Yehova watiphunzitsa “kukana moyo wosaopa Mulungu ndi zilakolako za dziko, koma kukhala amaganizo abwino, acilungamo ndi odzipeleka kwa Mulungu m’nthawi ino.” (Tito 2:11-14) Tikakhala na makhalidwe abwino, anthu adzaona, ndipo ena angafike pokamba kuti: “Anthu inu tipita nanu limodzi, cifukwa tamva kuti Mulungu ali ndi inu.”—Zek. 8:23.

^ par. 10 Liu la Cigiriki limene linamasulidwa kuti “onenela anzawo zoipa,” kapena kuti “woneneza” ni di·aʹbo·los. M’Baibo, liu limeneli limagwilitsidwa nchito monga dzina la Satana, amene amanenela Mulungu zoipa.