Anadzipeleka na Mtima Wonse—ku Myanmar
“ZOKOLOLA n’zoculukadi, koma anchito ndi ocepa. Conco pemphani Mwini zokololazo kuti atumize anchito okam’kololela.” (Luka 10:2) Mau a Yesu amenewa, amene anakambidwa zaka pafu-pifupi 2,000 zapitazo akufotokoza bwino mmene zinthu zilili ku Myanmar masiku ano. N’cifukwa ciani takamba conco? Cifukwa ku Myanmar kuli ofalitsa uthenga wabwino 4,200 cabe, koma m’dzikolo muli anthu 55 miliyoni.
Komabe, “Mwini zokololazo,” Yehova, wasonkhezela abale na alongo ambili ocokela m’maiko ena kupita ku Myanmar kukathandiza pa nchito yokolola mwauzimu imeneyi. Dziko la Myanmar lili kum’mwela cakum’maŵa kwa Asia. N’ciani cinapangitsa ofalitsawo kukhala na colinga cokukila ku dzikolo? N’ciani cinawathandiza kuti akwanitse kukuka? Nanga apeza madalitso anji? Tiyeni tione.
“BWELANI, TIFUNA APAINIYA AMBILI KUNO!”
Zaka zapitazo, mpainiya wina wa ku Japan, dzina lake Kazuhiro, anakomoka ndipo anapita naye ku cipatala. A dokota anamuuza kuti, kwa zaka ziŵili, safunika kuyendetsa motoka. Kazuhiro anakhala na nkhawa. Iye anadzifunsa kuti, ‘Nidzapitiliza bwanji kucita utumiki wa upainiya, umene nimaukonda kwambili?’ Kazuhiro anapemphela na mtima wonse kwa Yehova. Anamupempha kuti amutsegulile njila kuti apitilize kutumikila monga mpainiya.
Kazuhiro anafotokoza kuti: “Patapita mwezi umodzi, mnzanga wina amene anali kutumikila ku Myanmar anamvela za vuto langa. Iye ananitumila foni na kuniuza kuti: ‘Kuno ku Myanmar, nthawi zambili timayenda pa basi. Ngati mungabwele kuno, mungapitilize kucita upainiya popanda kukhala na motoka yoyendela.’ Conco n’nafunsa a dokota kuti, ‘Kodi ningapite kukakhala ku Myanmar mosasamala kanthu za vuto langali?’ N’nakondwela pamene iwo ananiyankha kuti: ‘Dokota wa ku Myanmar wodziŵa bwino za matenda a ubongo adzabwela kuno ku Japan posacedwapa. Nidzamuuza za vuto lako. Ngati vutoli lidzayambilanso, adzakuthandiza.’ N’naona kuti zimene dokotayo anakamba ni yankho yocokela kwa Yehova.”
Posakhalitsa, Kazuhiro analembela imelo ofesi ya nthambi ya ku Myanmar na kufotokoza kuti iye na mkazi wake akulakalaka kukatumikila m’dzikolo monga apainiya. Patapita cabe masiku 5, ofesiyo inawayankha kuti, “Bwelani, tifuna apainiya ambili kuno!” Kazuhiro na mkazi wake, Mari, anagulitsa mamotoka awo, anapeza mapasipoti, na kugula matiketi a ndeke. Pali pano, iwo akutumikila mwacimwemwe m’kagulu ka citundu ca manja mu mzinda wa Mandalay. Kazuhiro anati: Salimo 37:5, pamene pamati: ‘Lola kuti Yehova akutsogolele panjila yako, umudalile ndipo iye adzacitapo kanthu.’”
“Zimene zinacitikazi zatithandiza kukhulupilila kwambili lonjezo la Mulungu la paYEHOVA ANATSEGULA NJILA
Mu 2014, Mboni za Yehova ku Myanmar zinali na msonkhano wacigawo wapadela. Mboni zina zocokela m’maiko ena zinapezekapo. Mmodzi wa iwo anali Monique, mlongo wa zaka za m’ma 30 wocokela ku United States. Iye anati: “Nitabwelako ku msonkhanowo, n’napempha Yehova kuti anithandize kudziŵa zimene nifunika kucita mu umoyo wanga. Cinanso, n’nakambilana na makolo anga pa nkhani ya zolinga zanga zauzimu. Tonse tinaona kuti nifunika kukatumikila ku Myanmar. Koma panatenga nthawi komanso n’napeleka mapemphelo ambili kuti nifike popanga cosankha cimeneci.” Monique anafotokoza cifukwa cake.
Iye anati: “Yesu analangiza otsatila ake kuti afunika ‘kuwelengela zimene angawononge’ kuti akwanilitse zolinga zawo. Conco, n’nadzifunsa kuti: ‘Kodi nidzakwanitsa kukuka? Nikapita kumeneko, kodi nidzakwanitsa kupeza zofunikila mu umoyo wanga? Kapena nizikangothela nthawi yanga pa nchito yakuthupi?’” Monique anapitiliza kuti: “Nthawi yomweyo n’nazindikila kuti n’nalibe ndalama zokwanila, ndipo n’nali wosakonzekela kukukila ku dziko lina.” Nanga anakwanitsa bwanji kukuka?—Luka 14:28.
Monique anati: “Tsiku lina abwana anga ananiitana. N’nacita mantha, poganiza kuti afuna kunicotsa nchito. Koma iwo ananiyamikila cifukwa cogwila bwino nchito. Ndiyeno ananiuza kuti anikonzela mphatso. Mphatso yake inali ndalama yokwanila kulipilila zonse zofunikila.”
Monique wakhala akutumikila ku Myanmar kucokela mu December 2014. Kodi amamvela bwanji tsopano pamene akutumikila kosowa? Iye anati: “Nimakondwela ngako kutumikila kuno. Nili na maphunzilo a Baibo atatu. Mmodzi wa iwo ndi mzimayi wa zaka 67. Ponipatsa moni, nthawi zonse amamwetulila na kunikumbatila. Ataphunzila kuti dzina la Mulungu ni Yehova, anagwetsa misozi yacimwemwe. Anati: ‘N’kuyamba mu umoyo wanga kumvela kuti Mulungu dzina lake ni Yehova. Iwe ndiwe mwana kwambili poyelekezela na ine, koma waniphunzitsa cinthu cofunika kwambili mu umoyo wanga.’ Inenso n’nagwetsa misozi yacimwemwe. Zocitika monga zimenezi zapangitsa kuti nizikhala wokondwela kwambili na utumiki wanga kuno.” Posacedwa, Monique anakhala na mwayi woloŵa Sukulu ya Alengezi a Ufumu.
Abale na alongo ena analimbikitsidwa kupita ku Myanmar ataŵelenga nkhani yokamba za dzikolo, imene inatuluka mu Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2013. Panthawiyo, Li mlongo wa zaka za m’ma 30, anali kukhala m’dziko linalake ku Southeast Asia komweko. Iye anali pa nchito yolembedwa. Koma ataŵelenga nkhani ya m’bukulo, anayamba kuganizila zokatumikila ku Myanmar. Iye anati: “Mu 2014, n’napezeka pa msonkhano wacigawo wapadela mu mzinda wa Yangon. Kumeneko n’nakumana na banja linalake limene linali kutumikila m’gawo losoŵa la Cichainizi mu Myanmar. Popeza nimakamba Cichainizi, n’naganiza zokukila ku Myanmar kuti nikacilikize kagulu ka Cichainizi kumeneko. N’nagwilizana ndi Monique, ndipo tinakukila ku mzinda wa Mandalay. Yehova anatidalitsa mwa kutithandiza kupeza nchito yophunzitsa ya maola ocepa pa sukulu ina yake. Tinapezanso nyumba yokhalamo, kufupi na sukuluyo. Olo kuti nyengo ya kuno ni yotentha, ndipo timakumana na mavuto ena, nimakondwela na utumiki wanga. Anthu kuno ku Myanmar ali na umoyo wosalila zambili, koma ni aulemu ndipo amamvetsela mwacidwi uthenga wabwino. N’zokondweletsa ngako kuona mmene Yehova akuthamangitsila nchito yake. Sinikayikila kuti ni cifunilo ca Yehova kuti nizitumikila kuno ku Mandalay.”
YEHOVA AMAMVELA MAPEMPHELO
Abale na alongo ena otumikila ku malo osoŵa anadzionela okha mphamvu ya pemphelo. Mwacitsanzo, ganizilani za Jumpei na mkazi wake, Nao, amene ali na zaka
za m’ma 30. Iwo anali kutumikila mu mpingo wa citundu ca manja ku Japan. Nanga n’cifukwa ciani anakukila ku Myanmar? Jumpei anati: “Kuyambila kale-kale, ine na mkazi wanga tinali na colinga cokatumikila m’gawo losoŵa ku dziko lina. M’bale wina wocokela mu mpingo wathu wa ku Japan anakukila ku Myanmar. Mu May 2010, na ise tinakukila kumeneko olo kuti tinali na ndalama zocepa. Abale na alongo ku Myanmar anatilandila na manja aŵili!” Kodi Jumpei amamvela bwanji pamene akutumikila m’gawo la citundu ca manja ku Myanmar? Iye anati: “Anthu kuno ali na cidwi ngako. Tikaonetsa munthu wogontha vidiyo ya citundu ca manja, amacita cidwi kwambili. Ndise okondwa kuti tinapanga cosankha cobwela kuno kudzatumikila Yehova.”Kodi Jumpei ndi Nao amapeza bwanji zofunikila mu umoyo wawo? Jumpei anakamba kuti: “Patapita zaka zitatu, ndalama zimene tinasunga zinatsala pang’ono kutha. Ndipo tinalibe ndalama zokwanila zolipilila lendi caka cotsatila. Ine na mkazi wanga tinapeleka mapemphelo ambili mocokela pansi pa mtima. Mosayembekezela, tinalandila kalata yocokela ku ofesi ya nthambi yotipempha kuti tiyambe kutumikila monga apainiya apadela akanthawi. Tinadalila Yehova, ndipo iye sanatisiye. Koma wakhala akutipatsa zilizonse zofunikila mu umoyo wathu.” Posacedwapa, Jumpei na Nao nawonso analoŵa Sukulu ya Alengezi a Ufumu.
YEHOVA ANASONKHEZELA AMBILI
Simone, m’bale wa zaka za m’ma 40 amene anakulila ku Italy, na mkazi wake wa zaka za m’ma 30 dzina lake Anna, amene anakulila ku New Zealand, onse anasamukila ku Myanmar. Kodi n’ciani cinawasonkhezela kusamukila kumeneko? Anna anati: “Cinanisonkhezela ni nkhani yokhudza dziko la Myanmar ya mu Buku Lapachaka la 2013.” Ndipo Simone anati: “Ni mwayi waukulu ngako kutumikila kuno ku Myanmar. Umoyo wa kuno ni wopepukilapo cakuti timakhala na nthawi yoculuka yotumikila Yehova. N’zolimbikitsa kwambili kuona mmene Yehova akutisamalila pamene tikutumikila m’gawo losoŵa.” (Sal. 121:5) Anna anati: “Panopa nili na cimwemwe coculuka kuposa kale lonse. Tili na umoyo wosalila zambili. Nili na nthawi yoculuka yokhala na mwamuna wanga, ndipo izi zalimbitsa kwambili mgwilizano wathu. Komanso tapeza mabwenzi atsopano apamtima. Anthu a kuno sazonda Mboni, ndipo ali na cidwi ngako na uthenga wabwino.” Kodi amaonetsa bwanji kuti ali na cidwi?
Anna anati: “Tsiku lina, n’nalalikila mtsikana wina wa pa univesiti ku maketi na kupangana naye kuti tidzakumanenso. Nitapitako, n’napeza kuti waitana mnzake. Ulendo wotsatila, n’napeza kuti waitana anzake ena angapo. Patapita nthawi, anabwela na anzake ena owonjezeleka. Lomba nikuphunzila na atsikana 5 mwa atsikana amenewo.” Simone anati: “Anthu m’gawo lathu ni aubwenzi komanso ambili ni acidwi. Timapeza anthu ambili acidwi. Timacita kusoŵa nthawi yowaphunzitsa.”
Koma kodi abale na alongo amenewa anacita ciani kuti akwanitse kukukila ku Myanmar? Mizuho, amene anacokela ku Japan anati: “Ine na mwamuna wanga, Sachio, takhala tikulakalaka kukatumikila m’dziko limene
kuli ofalitsa ocepa. Koma sitinali kudziŵa kuti tingapite kuti. Titaŵelenga nkhani yokhudza dziko la Myanmar ya mu Buku Lapachaka la 2013, tinakhudzidwa mtima na zocitika zolimbikitsa zimene tinamva cakuti tinayamba kuganizila zokatumikila m’dzikolo.” Sachio anawonjezela kuti: “Tinaganiza zopita ku Yangon, mzinda waukulu ku Myanmar n’kukakhalako kwa wiki imodzi. Tinapita kukayendela malo, titelo kukamba kwake. Zimene tinaona pa ulendo wacidule umenewo, zinaticititsa kutsimikizila kuti tiyenela kukukila kumeneko.”KODI IMWE MUDZALABADILA CIITANO?
Rodney na mkazi wake Jane, amene anacokela ku Australia, ndipo ni a zaka za m’ma 50, akhala akutumikila ku Myanmar kuyambila mu 2010 pamodzi ndi ana awo Jordan na Danica. Rodney anati: “Tinakhudzidwa kwambili titaona njala yauzimu imene anthu kuno ali nayo. Nikulimbikitsa mabanja ena kuti nawonso ayeseko kukatumikila ku gawo losoŵa monga kuno ku Myanmar.” Cifukwa ciani? M’baleyo anati: “Ndithudi! N’zocititsa cidwi kuona mmene utumiki wathu kuno watithandizila kulimbitsa ubwenzi wathu na Yehova. Acicepele ambili amatangwanika na mafoni awo, mamotoka, nchito, na zinthu zina. Koma ana athu amatangwanika na kuphunzila mau atsopano oseŵenzetsa mu ulaliki. Amaphunzila mmene angalalikilile kwa anthu amene sadziŵa Baibo na mmene angayankhile pa misonkhano ya mpingo. Amakhalanso otangwanika na zocita zina zambili zotsitsimula mwauzimu.”
Oliver, ni m’bale wocokela ku United States wa zaka pafupi-fupi 40. Iye anafotokoza cifukwa cake amayamikila utumiki umenewu, anati: “Kutumikila Yehova m’dela limene sin’nazoloŵele kwanipindulitsa m’njila zambili. Kwanithandiza kudalila kwambili Yehova mosasamala kanthu za mmene zinthu zilili mu umoyo wanga. Kutumikila pamodzi na anthu amene kale sin’nali kuwadziŵa, koma amene ali na cikhulupililo cofanana ndi canga, kwanithandiza kuona kuti palibe ciliconse m’dzikoli cimene n’cofunika mofanana ndi Ufumu wa Mulungu.” Pali pano, Oliver na mkazi wake, Anna, akutumikilabe mwakhama m’gawo la Chichainizi.
Mlongo wina wocokela ku Australia, dzina lake Trazel, amene ali na zaka za m’ma 50, wakhala akutumikila ku Myanmar kuyambila mu 2004. Iye anati: “Kwa inu nonse amene mungakwanitse kutumikila kosoŵa, nikukulimbikitsani kuti mucite zimenezo. Ine naona kuti ngati munthu ali na mtima wofuna kutumikila, Yehova amam’dalitsa. Poyamba sin’nali kudziŵa kuti ningakhale na umoyo monga umene nili nawo kuno. Nili na umoyo waphindu ndi wokhutilitsa kwambili.”
Pempho lathu n’lakuti mau ocokela pansi pa mtima okambidwa ndi abale na alongo otumikila ku Myanmar amenewa, akulimbikitseni kuyesetsa kuthandiza anthu oona mtima m’magawo osalalikilidwa. Inde, abale na alongo otumikila ku gawo losoŵa akutiitana kuti, “Conde, bwelani kuno ku Myanmar mudzatithandize!”