Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Mukumbukila?

Kodi Mukumbukila?

Kodi munaŵelenga mosamala magazini aposacedwa a Nsanja ya Mlonda? Yesani kuyankha mafunso otsatilawa:

Kodi abale, monga amadela ndi akulu mumpingo, ayenela kucitanji akalandila malangizo a gulu la Mulungu?

Afunika kulabadila mwamsanga. Conco, angacite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ine nimalimbikitsa abale na alongo kukhalabe okhulupilika? Kodi nimalabadila mofulumila malangizo ocokela kwa otiyang’anila ndi kuwacilikiza?’—w16.11, peji 11.

Kodi Akhristu oona analoŵa liti ukapolo kwa Babulo wamkulu?

Izi zinacitika pamene atumwi onse anafa. Nthawi imeneyo, kagulu ka akulu-akulu a chechi kanayamba kuonekela. Chechi na Boma zinalimbikitsa Cikhristu campatuko ndi kupondeleza Akhristu amene anali monga tiligu. Koma m’zaka zambili zokatifikitsa ku 1914, odzozedwa anali kumasuka mu ukapolowo.—w16.11, mapeji 23-25.

N’cifukwa ciani nchito ya Lefèvre d’Étaples inali yofunika kwambili?

M’zaka za m’ma 1520, Lefèvre anamasulila Baibo m’Cifulenci kuti athandize anthu wamba kulimvetsetsa. Zimene analemba zinakhudza kwambili Martin Luther, William Tyndale, ndi John Calvin.—wp16.6, mapeji 10-12.

Kodi “kuika maganizo pa zinthu za thupi” kusiyana bwanji na “kuika maganizo pa zinthu za mzimu”? (Aroma 8:6)

Munthu woika maganizo ake pa zinthu za thupi amasumika maganizo na mtima wake pa zolakalaka ndi zofuna za thupi lake lopanda ungwilo. Amangokhalila kukamba mokokomeza zinthu za thupi. Koma munthu woika maganizo pa zinthu za mzimu ni amene moyo wake wonse umakhala pa kucita zinthu zokhudzana ndi kulambila Mulungu, ndipo amayesetsa kugwilizanitsa maganizo ake ndi a Mulungu. Mkhristu waconco amalola maganizo ake kutsogoleledwa na mzimu woyela. Kuika maganizo pa zinthu za thupi kumabweletsa imfa, koma kuika maganizo pa zinthu za mzimu kumabweletsa moyo ndi mtendele.—w16.12, mapeji 15-17.

Mungacite ciani kuti mucepetseko nkhawa?

Muziika zinthu zofunika kwambili patsogolo, muziona zinthu zotheka, muzipatula nthawi yopumula tsiku lililonse, muzisangalala na cilengedwe ca Yehova, muzikhala wansangala, muzicita masewela olimbitsa thupi kawili-kawili, ndi kugona mokwanila.—w16.12, mapeji 22-23.

“Inoki anasamutsidwa kuti asafe mozunzika.” (Aheb. 11:5) Kodi zimenezi zinacitika bwanji?

Yehova ayenela kuti anacotsa moyo wa Inoki pang’no-pang’ono popanda iye kudziŵa kuti ali kufa.—wp17.1, mapeji 12-13.

N’cifukwa ciani kudzicepetsa n’kofunikabe?

Kudzicepetsa kumaphatikizapo kusadziika pamene suli, komanso kudziŵa bwino zimene sungakwanitse. Tifunika kudziŵa mmene khalidwe lathu lingakhudzile ena ndiponso kupewa kucita zinthu mopambanitsa.—w17.01, peji 18.

Ni umboni uti umene uonetsa kuti Mulungu anali kutsogolela Bungwe Lolamulila m’zaka 100 zoyambila mofanana ndi mmene akutsogolela a m’Bungwe Lolamulila masiku ano?

Mzimu woyela unawathandiza kumvetsa bwino coonadi ca m’Malemba cimene sanali kucimvetsa poyamba. Mothandizidwa ndi angelo, anali kuyang’anila nchito yolalikila, ndipo anali kudalila Mau a Mulungu popeleka malangizo. Ni mmene zililinso masiku ano.—w17.02, mapeji 26-28.

Ni zinthu ziti zimene zimapangitsa dipo kukhala mphatso yamtengo wapatali?

Ni zinthu zinayi izi: Amene anatipatsa, cifukwa cimene anatipatsila, zimene anatailapo kuti atipatse, ndiponso zosoŵa zimene inakwanilitsa. Tifunika kusinkhasinkha mmene zinthu zimenezi zimaonetsela kuti dipo ni mphatso yamtengo wapatali.—wp17.2, mapeji 4-5.

Kodi n’koyenela Mkhristu kusintha maganizo ake pambuyo popanga cosankha?

Tifunika kucita zimene tasankha. Komabe, nthawi zina timafunika kuganizilaponso pa cosankha cathu. Yehova anasintha maganizo ataona kuti Anineve alapa ndi kusiya njila zawo zoipa. Nthawi zina, ifenso tingafunike kusintha cosankha cathu ngati zinthu zasintha kapena ngati tadziŵa mfundo zina zimene poyamba sitinali kuzidziŵa.—w17.03, mapeji 16-17.

N’cifukwa ciani misece ni yoopsa?

Misece ingapangitse kuti vuto likule kwambili. Conco, kaya munthuyo anatilakwiladi kapena ayi, tiyenela kukumbukila kuti kukamba zinthu zimene zingaipitse mbili yake sikungathetse vutolo.—w17.04, peji 21.