NSANJA YA MLONDA—YOPHUNZILA June 2018

Magazini ino ili na nkhani zophunzila wiki ya August 6-September 2, 2018.

“Ufumu Wanga Suli Mbali ya Dziko Lino”

Kodi kuganizila mmene Yesu anacitila na mikangano ya zandale m’nthawi yake, kuyenela kukhudza bwanji mmene timaonela mikangano yandale ndi ya cikhalidwe masiku ano?

Tikhale Amodzi, Monga Mmene Yehova na Yesu Alili Amodzi

Mungacite ciani kuti mulimbitse mgwilizano pakati pa anthu a Mulungu?

Akanayanjidwa na Mulungu

Citsanzo ca Rehobowamu, mfumu ya Yuda, cingatithandize kudziŵa kuti Mulungu amafuna kuti tikhale anthu otani.

Lolani Malamulo a Mulungu na Mfundo Zake Kuphunzitsa Cikumbumtima Canu

Mulungu anatipatsa cikumbumtima. Koma tifunika kuciphunzitsa kuti cizititsogolela bwino.

“Onetsani Kuwala Kwanu” Kuti Yehova Alemekezeke

Kuwonjezela pa kulalikila, palinso zina zimene tifunika kucita

MBILI YANGA

N’natonthozedwa pa Mavuto Anga Onse

M’bale Edward Bazely anakumana na mavuto a m’banja, citsutso, zolefula, na nkhawa.

Mphamvu ya Moni

Ngakhale moni wacidule umathandiza m’njila zambili.

Kodi Mukumbukila?

Kodi mungakwanitse kuyankha mafunso awa ocokela m’magazini a posacedwa a Nsanja ya Mlonda?