Kodi Mukumbukila?
Kodi munaŵelenga mosamala magazini aposacedwa a Nsanja ya Mlonda? Yesani kuyankha mafunso otsatilawa:
N’zinthu 4 ziti zimene zingatithandize kuwongolela kaimbidwe kathu?
Tifunika kuimilila mowongoka na kukwezako m’mwamba buku lathu la nyimbo. Tifunika kukoka mpweya wokwanila. Ngati titsegula pakamwa mokwanila, tingathe kuimba mokweza.—w17.11, peji 5.
N’ciani cocititsa cidwi tikaganizila madela amene kunali mizinda yothaŵilako mu Isiraeli na miseu yopita kumeneko?
Mu Isiraeli munali mizinda 6 yothaŵilako. Mizindayo inali m’madela osiyana-siyana, ndipo kunali miseu yokonzedwa bwino yopita ku mzinda uliwonse. Conco, munthu akanatha kuthaŵilako mwamsanga ndi mosavuta.—w17.11, peji 14.
N’cifukwa ciani mphatso ya Mulungu ya dipo la Yesu ndiyo yoposa zonse zimene tingalandile?
Imakhutilitsa colaka-laka cathu copitiliza kukhala na moyo. Inatipatsa mwayi womasuka ku ucimo na imfa. Pamene tinali ocimwa, Mulungu anapeleka Yesu kuti adzatifele cifukwa cotikonda ise mbadwa za Adamu.—wp17.6, mape. 6-7.
Tidziŵa bwanji kuti lemba la Salimo 118:22 linalosela za kuuka kwa Yesu?
Tidziŵa cifukwa cakuti Yesu anakaniwa kuti si Mesiya ndipo anaphedwa. Kuti iye akhale “mwala wofunika kwambili wapakona,” anaukitsidwa.—w17.12, mape. 9-10.
Kodi kukhala pa mzela wa makolo a Mesiya kunadalila kukhala oyamba kubadwa?
Nthawi zina mzela wobadwila wa Yesu unali kupitila mwa mwana woyamba kubadwa, koma osati nthawi zonse. Mwacitsanzo, olo kuti Davide sanali mwana woyamba wa Jese, Mesiya anabadwa kupitila mu mzela wa Davide.—w17.12, mape. 14-15.
Kodi m’Baibo muli malangizo anji pankhani ya zaumoyo?
Malinga na Cilamulo ca Mose, anthu odwala matenda ena anali kufunika kukhala kwaokha. Anthu anafunika kusamba pambuyo pogwila mtembo. Cilamulo cinakamba kuti zonyansa za munthu ziyenela kufoceledwa kutali. Mdulidwe unali kucitidwa pa tsiku la namba 8 kucokela pamene mwana wabadwa. Ndipo iyi inali nthawi yabwino cifukwa m’pamene magazi amayamba kuundana mosavuta.—wp18.1, peji 7.
N’cifukwa ciani kudzikonda pa mlingo woyenelela kuli cabe bwino kwa Mkhristu?
Timafunika kukonda anzathu mmene timadzikondela. (Maliko 12:31) Amuna amalamulidwa kuti ‘azikonda akazi awo monga matupi awo.’ (Aef. 5:28) Komabe, munthu akhoza kuyamba kudzikonda mosayenela.—w18.01, peji 23.
Kodi zinthu zina zimene tingacite kuti tipite patsogolo mwauzimu n’ziti?
Tifunika kuŵelenga Mau a Mulungu, kuwasinkha-sinkha, na kuseŵenzetsa zimene taphunzila. Tifunikanso kulola mzimu woyela kutsogolela maganizo na mtima wathu. Cinanso, tifunika kulandila moyamikila thandizo locokela kwa ena.—w18.02, peji 26.
N’cifukwa ciani kukhulupilila nyenyezi na kulosela zam’tsogolo sikungathandize munthu kudziŵa zam’tsogolo?
Pali zifukwa zambili, koma cifukwa cacikulu n’cakuti Baibo imaletsa kukhulupilila nyenyezi na kulosela zam’tsogolo.—wp18.2, mape. 4-5.
Kodi munthu akatiitanila ku cakudya tifunika kucita ciani?
Tikalonjeza kuti tidzapita, tiyenela kukwanilitsa lonjezo lathu. (Sal. 15:4) Sitiyenela kusintha maganizo popanda zifukwa zomveka. Munthu amene anatiitana amakhala kuti wagwila nchito yaikulu kuti atikonzele cakudya.—w18.03, peji 18.
Kodi amuna apaudindo angaphunzile ciani kwa Timoteyo?
Timoteyo anali kukonda anthu na mtima wonse komanso anali kuika zinthu zauzimu patsogolo. Anali kucita utumiki wopatulika modzipeleka na kuseŵenzetsa zimene anaphunzila kwa ena. Anapitiliza kudziphunzitsa na kudalila mzimu wa Yehova. Akulu kuphatikizapo ise tonse tiyenela kutengela citsanzo cake.—w18.04, mape. 13-14.