MBILI YANGA
N’natonthozedwa pa Mavuto Anga Onse
N’nabadwa pa November 9, 1929 mu mzinda wa Sukkur, m’dziko limene lomba limachedwa Pakistan. Mzindawu uli kumadzulo kwa mtsinje wa Indus. Ca pa nthawiyi, makolo anga analandila mabuku kwa mmishonale wina wocokela ku England. Mabuku ofotokoza Baibo amenewo ananithandiza ngako kuti nisinthe na kukhala Mboni ya Yehova.
MABUKUWO anali kuchedwa mpukutu wa utawaleza. N’tayamba kuwaŵelenga, n’nacita cidwi kwambili na zithunzi zake zokongola. Conco, kuyambila nili wamng’ono, n’nayamba kulakalaka kuphunzila mfundo zambili za m’Baibo, monga zimene n’naŵelenga m’mabuku ocititsa cidwi amenewo.
Pamene Nkhondo Yaciŵili ya Padziko Lonse inali kufalikila m’madela ambili ku India, n’nayamba kukumana na mavuto ambili mu umoyo wanga. Makolo anga anapatukana, ndipo kenako anasudzulana. Sin’namvetsetse kuti n’cifukwa ciani anthu amene n’nali kuwakonda analekana. N’nayamba kuona kuti palibe amanikonda. N’nali kudziona monga mwana wosiyidwa. Popeza mwana m’banjali n’nali nekha, n’nali kusoŵa munthu wonitonthoza na kunilimbikitsa.
Panthawiyo, ine na amayi tinali kukhala m’tauni yaikulu ya Karachi. Tsiku lina, dokota wina wacikulile amene anali wa Mboni za Yehova, dzina lake Fred Hardaker, anabwela ku nyumba kwathu. Cikhulupililo cake cinali colingana ndi ca mmishonale uja amene anapatsa banja lathu mabuku. Iye anapempha amayi kuti aziwaphunzitsa Baibo. Amayi anakana, koma anawauza kuti mwina ine ningakonde kuphunzila. Wiki yotsatila, n’nayambadi kuphunzila na M’bale Hardaker.
Patapita mawiki angapo, n’nayamba kupezeka pa misonkhano, imene inali kucitikila ku cipatala ca M’bale Hardaker. Kumeneko kunali kusonkhana Mboni zacikulile 12. Iwo anali kunitonthoza na kunisamalila monga mwana wawo. Sinidzaiŵala mmene anali kukhalila nane pamisonkhano. Komanso anali kuwelama kufika pa msinkhu wanga, na kukamba nane monga mabwenzi anga eni-eni. Izi n’zimene n’nali kufunikila kwambili pa nthawiyo.
Posapita nthawi, M’bale Hardaker ananipempha kuti niyambe kuyenda naye mu ulaliki. Ananiphunzitsa kuseŵenzetsa galamafoni kuti tizilizila anthu nkhani zazifupi za m’Baibo zojambulidwa. Zina mwa nkhanizo zinali kukamba mfundo mosapita m’mbali, ndipo eninyumba ena anali kukhumudwa nazo. Koma n’nali kukondwela ngako na nchito yolalikila. Coonadi ca m’Baibo n’nali kucikonda kwambili, komanso n’nali kukonda kuciphunzitsako kwa ena.
Asilikali a Japan atatsala pang’ono kuukila dziko la India, akulu-akulu a dziko la Britain amene anali kulamulila dzikolo, anayamba kuvutitsa kwambili Mboni za Yehova. Mu July 1943, inenso n’nakhudzidwa. A hedi a pa sukulu pathu, amene anali m’busa wa Anglican, ananicotsa sukulu. Anakamba kuti n’nali “mwana wosayenelela” kukhala pa sukulupo. Anauza amayi kuti cifukwa cakuti n’nali kugwilizana ndi a Mboni, sin’nali kupeleka citsanzo cabwino kwa ana a sukulu anzanga. Amayi anakhumudwa ndipo ananiletsa kugwilizana ndi a Mboni. Pambuyo pake, ananitumiza kwa atate ku Peshawar, tauni imene inali pa msenga wa makilomita 1,370, kumpoto kwa India. Cifukwa cosoŵa cakudya cauzimu na mayanjano olimbikitsa, n’nakhala wozilala.
N’NAKHALANSO WOLIMBA MWAUZIMU
Mu 1947, n’nabwelela ku Karachi kuti nikasakile nchito. Nili kumeneko, n’napita kukaonana ndi a Hardaker kucipatala cawo. Iwo ananilandila na manja aŵili.
Poganiza kuti nabwela kudzalandila thandizo lakuthupi, ananifunsa kuti, “N’ciani cavuta?”
N’nawayankha kuti: “A dokota, ndine wodwala mwauzimu osati mwakuthupi. Nifuna muyambe kuphunzila nane Baibo.”
Iwo anati: “Ungakonde kuyamba liti kuphunzila?”
N’nawayankha kuti: “Ngati n’kotheka, olo lelo tingayambe”
N’nakondwela kuphunzila Baibo madzulo a tsiku limenelo. N’nalimbikitsidwa cifukwa cokhalanso pamodzi na anthu a Yehova. Amayi anayesetsa kuniletsa kuyanjana ndi a Mboni, koma panthawiyi n’nali wotsimikiza mtima kupanga coonadi kukhala canga. Pa August 31, 1947, n’nadzipatulila kwa Yehova na kubatizika. Posapita nthawi, nili na zaka 17, n’nayamba kutumikila monga mpainiya.
UTUMIKI WOKONDWELETSA WA UPAINIYA
Utumiki wanga wa upainiya n’nauyambila ku Quetta, kumene kunali kukhala gulu lina la asilikali a Britain. Mu 1947, dziko la India linagaŵidwa paŵili. Mbali ina inakhala India ndipo ina Pakistan. * Izi zinacititsa kuti anthu ambili ayambe kucita zaciwawa cifukwa cosiyana kwa zipembedzo. Zotulukapo zake zinali zakuti anthu ambili kuposa kale lonse anathaŵa kwawo. Anthu pafupi-fupi 14 miliyoni anacoka m’maiko awo. Asilamu a ku India anathaŵila ku Pakistan, ndipo Ahindu na Asikhi a ku Pakistan anakakhala ku India. M’nthawi yovutayi, n’nakwela sitima ku Karachi yopita ku Quetta. Munali anthu oculuka kwambili cakuti nthawi yaitali pamene sitimayo inali kuyenda, n’nangokhala kunja n’kugwila ku cinsimbi.
Ku Quetta, n’nakumana na m’bale George Singh, amene anali mpainiya wapadela wa zaka za m’ma 20. M’baleyu ananipatsa njinga yakale yoti niziyendelapo polalikila m’gawo langa, limene kunali mapili ambili. Kambili n’nali kulalikila nekha. Patapita cabe miyezi 6, n’nakhazikitsa maphunzilo a Baibo 17, ndipo ena anakhala Mboni. M’modzi wa iwo anali msilikali, dzina lake Sadiq Masih. Iye anali kuthandiza ine na m’bale George kumasulila mabuku ofotokoza Baibo m’citundu cacikulu ca ku Pakistan, cochedwa Ciudu. M’kupita kwa nthawi, Sadiq anakhala mlaliki wacangu wa uthenga wabwino.
Patapita nthawi, n’nabwelela ku Karachi. Kumeneko, n’nayamba kutumikila na m’bale Henry Finch na Harry Forrest, amishonale amene anali atangofika kumene kucokela ku Sukulu ya Giliyadi. Iwo ananiphunzitsa zambili. Nthawi ina, n’napelekeza M’bale Finch pa ulendo wake wokalalikila kumpoto kwa dziko la Pakistan. M’madela a mapili a kumeneko, tinapeza anthu ambili odzicepetsa okamba Ciudu, amene anali na njala ya coonadi. Patapita zaka ziŵili, na ine n’naloŵa Sukulu ya
Giliyadi. N’tatsiliza maphunzilo, n’nabwelela ku Pakistan, kumene nthawi zina n’nali kutumikila monga woyang’anila dela. N’nali kukhala pa nyumba ya amishonale ya ku Lahore, pamodzi na abale ena atatu, amene anali amishonale.KUTUMIKILANSO MWACIMWEMWE PAMBUYO POPATSIDWA UPHUNGU WAMPHAMVU
Mu 1954, amishonale amene anali kukhala ku Lahore anakangana kwambili cifukwa cosiyana zibadwa. Izi zinacititsa kuti ofesi ya nthambi iwasinthile m’mautumiki ena. Popeza kuti n’natengako mbali pa mkanganowo, n’napatsiwa uphungu wamphamvu. Cinaniŵaŵa ngako cakuti n’nayamba kudziona monga munthu wolephela pa zinthu zauzimu. N’nabwelela ku Karachi, ndipo kenako n’napita ku London, m’dziko la England, nili na maganizo okalimbitsanso umoyo wanga wauzimu.
Mu mpingo wathu wa ku London, munali atumiki ambili a pa Beteli. Mtumiki wa nthambi ya m’dzikolo, dzina lake Pryce Hughes, anali munthu wokoma mtima, ndipo mwacikondi ananiphunzitsa zinthu zambili. Tsiku lina, iye ananiuza kuti anapatsidwapo uphungu wamphamvu na M’bale Joseph F. Rutherford, amene anali kuyang’anila nchito yolalikila pa dziko lonse. Pamene M’bale Hughes anayamba kupeleka zifukwa zodzikhululukila, M’bale Rutherford anamudzudzula mwamphamvu. N’nadabwa kuti M’bale Hughes anali kumwetulila pamene anali kuniuza zimenezi. Iye anakamba kuti poyamba zimene zinacitikazo zinamukhumudwitsa. Koma pambuyo pake, anazindikila kuti anali kufunikiladi uphungu wamphamvu, ndiponso kuti uphunguwo unali umboni wa cikondi ca Yehova. (Aheb. 12:6) Zimene anakambazo zinanikhudza mtima na kunithandiza kuyambanso kutumikila Yehova mwacimwemwe.
Pa nthawiyi, amayi anabwela kudzakhala ku London. Ndipo anavomela kuyamba kuphunzila Baibo na M’bale John E. Barr, amene pambuyo pake anatumikila m’Bungwe Lolamulila. Iwo anapita patsogolo mwamsanga ndipo anabatizika mu 1957. Patapita zaka, n’namvela kuti atate asanamwalile, nawonso anali kuphunzila Baibo na Mboni za Yehova.
Mu 1958, n’nakwatila Lene, mlongo wa ku Denmark amene anali kukhala mu London. M’caka cotsatila, tinakhala na mwana wathu woyamba wamkazi, dzina lake Jane. Pambuyo pake, tinabeleka ana ena 4. N’napatsidwanso mwayi wotumikila monga mkulu mu mpingo wa Fulham. Koma m’kupita kwa nthawi, cifukwa ca kufooka kwa thanzi la Lene, tinaganiza zokukila ku dziko lotentha. Conco, mu 1967, tinakukila ku Adelaide m’dziko la Australia.
ZOCITIKA ZOPWETEKA MTIMA
Mumpingo wathu wa ku Adelaide munali Akhristu odzodzedwa acikulile okwana 12. Iwo anali acangu pa nchito yolalikila. Titafika kumeneko, mwamsanga tinapitiliza kucita zinthu zauzimu.
Mu 1979, tinakhala na mwana wa namba 5, dzina * ndipo tinali kuganiza kuti posapita nthawi adzamwalila. Ngakhale lomba, siningakwanitse kufotokoza kukula kwa cisoni cimene tinali naco. Tinayesetsa kumusamalila bwino mmene tikanathela, kwinaku tikusamalilanso ana athu ena 4. Nthawi zina, khungu la Daniel linali kuoneka buluu cifukwa cosoŵa oxygen m’thupi. Oxygen yambili inali kucoka m’thupi lake cifukwa ca mibowo iŵili imene inali mkati mwa mtima wake. Zikakhala conco, tinali kuthamangila naye kucipatala. Olo kuti anali na matenda, anali wanzelu kwambili komanso anali na mtima wacikondi. Analinso wokonda kwambili zinthu zauzimu. Mwacitsanzo, pamene tipemphela monga banja tisanayambe kudya, anali kupinda tumanja twake, kuŵelama, na kuyankha na mtima wonse kuti “Ame!” Tikapemphela m’pamene anali kukhala womasuka kudya.
lake Daniel. Iye anabadwa na matenda a Down syndrome,Pamene Daniel anali na zaka 4, anadwala matenda oopsa a khansa ya m’magazi. Ine na mkazi wanga tinali kukhala olema komanso opanikizika maganizo. N’nayamba kuona monga kuti natsala pang’ono kudwala matenda ovutika maganizo. Tsiku lina, pamene zinthu zinafika poipa kwambili, woyang’anila dela wathu, M’bale Neville Bromwich, anabwela kunyumba kwathu madzulo. Misozi ikulengeza m’maso mwake, anatikumbatila. Tonse tinalila. Iye anatilimbikitsa ngako na mau ake acikondi na okoma mtima. Anacoka ca ku ma 01:00hrs. Patapita nthawi yocepa, Daniel anamwalila. Zinali zopweteka mtima kwambili. Olo zinali conco, tinapilila podziŵa kuti ciliconse, ngakhale imfa, sicingalekanitse Daniel na cikondi ca Yehova. (Aroma 8:38, 39) Tiyembekezela mwacidwi kudzaonana naye m’dziko latsopano la Mulungu akadzaukitsidwa.—Yoh. 5:28, 29.
KUPEZA CIMWEMWE POTHANDIZA ENA
Masiku ano, nikutumikilabe monga mkulu mumpingo, olo kuti n’nadwalapo sitroko kaŵili konse. Zimene zinanicitikila mu umoyo wanga, zanithandiza kukhala woganizila ena ndi wacifundo, maka-maka kwa anthu amene akukumana na mavuto. Nimapewa kuwaweluza. M’malomwake, nimadzifunsa kuti: ‘Kodi zokumana nazo mu umoyo wawo zakhudza bwanji maganizo awo na mmene amamvelela? Nanga ningawathandize bwanji? Ningawalimbikitse bwanji kuti azicita zinthu mogwilizana na malangizo a Yehova?’ Nchito yaubusa nimaikonda kwambili! Nikalimbikitsa na kutsitsimula ena mwauzimu, inenso nimalimbikitsidwa na kutsitsimulidwa.
Nimamvela monga mmene wamasalimo anamvelela pamene anati: “Malingalilo osautsa atandiculukila mumtima mwanga, mau . . . otonthoza [a Yehova] anayamba kusangalatsa moyo wanga.” (Sal. 94:19) Yehova wakhala akunithandiza pa mavuto a m’banja, citsutso, zolefula, na nkhawa. Ndithudi! Iye ni Tate wanga weni-weni.