Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

“Onetsani Kuwala Kwanu” Kuti Yehova Alemekezeke

“Onetsani Kuwala Kwanu” Kuti Yehova Alemekezeke

“Onetsani kuwala kwanu pamaso pa anthu, kuti . . . alemekeze Atate wanu wakumwamba.”—MAT. 5:16.

NYIMBO: 77, 59

1. Kodi tili na cifukwa capadela citi cokhalila okondwela?

N’ZOKONDWELETSA cotani nanga kuona mmene gulu la Yehova likupitila patsogolo! Caka catha, tinatsogoza maphunzilo a Baibo oposa 10,000,000. Ndithudi! Atumiki a Mulungu akuonetsa kuwala kwawo. Komanso ganizilani za anthu acidwi mamiliyoni ambili amene anapezeka pa Cikumbutso. Iwo anali na mwayi wophunzila za cikondi cimene Mulungu anationetsa mwa kupeleka dipo.—1 Yoh. 4:9.

2, 3. (a) Ni copinga citi cimene sicinatilepheletse kuwala “monga zounikila”? (b) Malinga ni mau a Yesu pa Mateyu 5:14-16, kodi tidzakambilana ciani?

2 Padziko lonse, anthu a Yehova amakamba zitundu zosiyana-siyana. Ngakhale n’conco, izi sizitilepheletsa kutamanda Atate wathu Yehova mogwilizana. (Chiv. 7:9) Mosasamala kanthu za citundu cathu, kapena kumene tikhala, tingaonetse kuwala kwathu “monga zounikila m’dzikoli.”—Afil. 2:15.

3 Utumiki wathu, mgwilizano wathu wacikhristu, na kukhala kwathu maso mwauzimu, zonse zimapeleka ulemelelo kwa Yehova. Koma kodi tingaonetse bwanji kuwala kwathu m’mbali zitatu zimenezi?—Ŵelengani Mateyu 5:14-16.

THANDIZANI ENA KUTI AYAMBE KULAMBILA YEHOVA

4, 5. (a) Kuwonjezela pa kulalikila, kodi tingaonetse bwanji kuwala kwathu? (b) Kodi kuonetsa mzimu wa ubwenzi kuli na ubwino wanji? (Onani pikica kuciyambi.)

4 Nkhani imene inafalitsidwa mu Nsanja ya Mlonda ya June 1, 1925, ya mutu wakuti “Kuwala mu Mdima,” inati: “Palibe Mkhristu amene angakhale wokhulupilika kwa Ambuye m’masiku otsiliza ano . . . ngati saonetsa kuwala kwake.” Kenako, nkhaniyo inati: “Mkhristu afunika kucita zimenezi mwa kulalikila uthenga wabwino kwa anthu, ndiponso mwa kutsatila miyezo yolungama ya Yehova mu umoyo wake.” Zoonadi, njila imodzi imene timaonetsela kuunika kwathu, ndi mwa kulalikila uthenga wabwino na kupanga ophunzila. (Mat. 28:19, 20) Kuwonjezela apo, timapeleka ulemelelo kwa Yehova mwa khalidwe lathu labwino. Anthu amene timawalalikila komanso amene timakumana nawo, amaona khalidwe lathu. Ngati timwetulila na kuwapatsa moni mwaubwenzi, angacite cidwi na khalidwe lathu komanso ndi Mulungu amene timalambila.

5 Yesu anauza ophunzila ake kuti: “Pamene mukuloŵa m’nyumba, pelekani moni kwa a m’banja limenelo.” (Mat. 10:12) M’dela limene Yesu na ophunzila ake anali kulalikilamo kaŵili-kaŵili, anthu anali na cizoloŵezi coitanila alendo m’nyumba zawo. Masiku ano, cizoloŵezi cimeneci m’madela ambili mulibe. Komabe, kukhala aubwenzi pamene mukufotokoza cifukwa cimene mwafikila pa khomo la munthu, nthawi zambili kumathandiza kucepetsa nkhawa kapena ukali umene mwininyumba angakhale nawo. Kaŵili-kaŵili, kumwetulila mwaubwenzi kumakhala ciyambi cabwino ca makambilano. Kucita izi kumakhalanso kothandiza kwa abale na alongo amene amacita ulaliki wa pa kasitandi. Pamene mucita ulaliki umenewu, nthawi zambili anthu amakhala omasuka kudzatenga mabuku athu ngati mumwetulila na kuwapatsa moni mwaubwenzi. Kuonetsa mzimu waubwenzi kungakuthandizeninso kuyambitsa makambilano mosavuta.

6. Kodi banja lina lacikulile linawonjezela bwanji zocita mu ulaliki wawo?

6 M’bale wina wa ku England na mkazi wake, amene ni acikulile sakwanitsa kulalikila ku nyumba na nyumba cifukwa ca kufooka kwa thanzi. Conco, anayamba kuonetsa kuwala kwawo mwa kulalikila panja pa nyumba yawo. Iwo amaika zofalitsa pa thebulo, nthawi imene makolo amapita kukatenga ana awo pa sukulu imene ili pafupi na nyumba yawo. Makolo ambili amacita cidwi ndipo amatengako mabuku akuti Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, buku loyamba na laciŵili, kuphatikizapo tumabuku twina. Mlongo wina wa mumpingo mwawo, amene ni mpainiya anayamba kucita nawo ulaliki umenewu. Cifukwa coona khalidwe laubwenzi la mlongoyo komanso khama la Akhristu acikulilewo, kholo lina linavomela kuphunzila Baibo.

7. Kodi mungawathandize bwanji anthu othaŵa kwawo amene akukhala m’dela lanu?

7 M’zaka zaposacedwa, m’maiko ambili mwakhala mukubwela anthu oculuka othaŵa kwawo. Ngati m’dela lanu muli anthu othaŵa kwawo, kodi mungawathandize bwanji kudziŵa Yehova na colinga cake? Bwanji osaphunzilako moni m’citundu cawo? Pulogalamu ya JW Language ingakuthandizeni kucita zimenezi. Cinanso, mungaphunzileko mau ocepa a m’citundu cawo amene angawakope cidwi. Ndiyeno, mungaŵalongoze webusaiti ya jw.org na kuwaonetsa mavidiyo na zofalitsa zimene zilipo m’citundu cawo.—Deut. 10:19.

8, 9. (a) Kodi pa msonkhano wa mkati mwa wiki timalandila malangizo ati othandiza? (b) Kodi makolo angathandize bwanji ana awo kuti azitengako mbali pa misonkhano?

8 Mwacikondi, Yehova anatikonzela Msonkhano wa Umoyo na Utumiki Wathu n’colinga cakuti tikhale aluso kwambili mu ulaliki. Malangizo amene timalandila pa msonkhanowu amatithandiza kudziŵa bwino mocitila maulendo obwelelako ndi mocititsila maphunzilo a Baibo.

9 Anthu acidwi akabwela ku misonkhano, amaona kuti ana athu amatengako mbali pa misonkhano. Conco, makolo muzithandiza ana anu kuonetsa kuwala kwawo mwa kuwaphunzitsa kupeleka ndemanga m’mau awo-awo. Mayankho aafupi na ocokela pansi pa mtima opelekedwa ndi ana, acititsa anthu ena acidwi kuzindikila kuti timaphunzila coonadi.—1 Akor. 14:25.

MUZILIMBIKITSA MGWILIZANO

10. Kodi kulambila kwa pabanja kumalimbikitsa bwanji mgwilizano?

10 Njila ina imene mungaonetsele kuwala kwanu ni mwa kulimbikitsa mgwilizano m’banja lanu na mumpingo. Njila imodzi imene makolo angacitile zimenezi ni mwa kukhala na pulogalamu yokhazikika ya Kulambila kwa Pabanja. Ambili amakonza zakuti tsiku lina pa kulambila kwawo kwa pabanja, azitambako JW Broadcasting. Pambuyo potamba pulogalamuyo, bwanji osapatula nthawi yokambilana na banja lanu mmene mungaseŵenzetsele mfundo zimene mwamvetsela? Pocititsa kulambila kwa pabanja, kholo lifunika kumbukilani kuti malangizo amene mwana angafunikile amasiyana na amene wacinyamata amafunikila. Motelo, muzifotokoza bwino mmene aliyense angaseŵenzetsele mfundo zimene mwaphunzila pa kulambila kwa pabanja, kuti nonse mupindule.—Sal. 148:12, 13.

Kupatula nthawi yoceza na okalamba n’kolimbikitsa ngako (Onani palagilafu 11)

11-13. Kodi tonse tingalimbikitse bwanji mgwilizano mumpingo na kuthandiza ena kuonetsa kuwala kwawo?

11 Kodi acicepele angalimbikitse bwanji mgwilizano mumpingo na kuthandiza ena kuonetsa kuwala kwawo? Ngati ndimwe Mkhristu wacicepele, bwanji osakhala na colinga codziŵana bwino na acikulile mumpingo mwanu? Mungawafunse mwaulemu kuti akufotokozelenkoni zocitika za mu utumiki wawo. Mukacita zimenezi, mudzaphunzila zambili. Ndipo imwe na iwo mudzalimbikitsidwa kupitiliza kuonetsa kuwala kwa coonadi. Cinanso, ise tonse tiyenela kukhala na colinga colandila aliyense amene wabwela pa misonkhano. Kucita izi kungalimbitse mgwilizano mu mpingo, ndipo kungasonkhezele mabwenzi athu amene timasonkhana nawo kuyamba kutumikila Mulungu. Mungawalandile mwa kuwapatsa moni mwaubwenzi, kapenanso kuwathandiza kupeza malo okhala. Adziŵikitseni kwa ena kuti akhale omasuka.

12 Ngati mwapatsidwa mwayi wotsogoza pa kukumana kokonzekela ulaliki, mungacite zambili pothandiza okalamba kutengamo mbali mu nchito yolalikila. Okalamba ayenela kupatsiwa gawo lowayenelela. Nthawi zina, mungawagaŵe na wacicepele kuti aziwathandizako pamene ayenda m’gawo. Muyenelanso kuwaganizila ofalitsa amene amalephela kucita zambili cifukwa ca kufooka kwa thanzi kapena pa zifukwa zina. Inde, kukhala ozindikila na oganizila ena kungathandize onse kuti azilalikila uthenga wabwino modzipeleka, kaya ni acicepele kapena acikulile, aciyambakale kapena acatsopano.—Lev. 19:32.

13 Wamasalimo anakamba kuti: “Ndi zabwino komanso zosangalatsa kwambili abale akakhala pamodzi mogwilizana!” (Ŵelengani Salimo 133:1, 2.) Aisiraeli akasonkhana pamodzi na olambila anzawo, anali kupindula kwambili na mayanjano olimbikitsa. Anali kukhala na mayanjano abwino ndi otsitsimula monga mafuta odzozela munthu. Na ise tingatsitsimule ena mwa kukhala aubwenzi na okoma mtima. Mwa ici, tidzalimbikitsa mgwilizano pakati pa abale na alongo mumpingo. Ngati munayamba kale kucita zimenezi, ndiye kuti mukucita bwino. Koma kodi ‘mungafutukule mtima wanu’ mwa kuwonjezela zimene mumacita polimbikitsa abale na alongo?—2 Akor. 6:11-13.

14. N’ciani cimene mungacite kuti muzionetsa kuwala kwanu kwa anthu okhala nawo pafupi?

14 Mungacite ciani kuti muwonjezele kuwala kwa coonadi ca m’Baibo m’dela lanu? Muyenela kukhala okoma mtima m’zokamba na zocita zanu. Mukatelo, anansi anu angakopeke na coonadi. Dzifunseni kuti: ‘Kodi anthu a m’dela langa amaniona bwanji? Kodi panyumba panga na katundu wanga zimakhala zaukhondo nthawi zonse? Kodi nimayesetsa kuthandiza ena?’ Cinanso, pamene muceza na abale na alongo, bwanji osawafunsako mmene kukoma mtima na khalidwe lawo labwino zakhudzila abululu awo, maneba, anzawo a kunchito, kapena a kusukulu? Mwacionekele, iwo adzakufotokozelani zocitika zolimbikitsa.—Aef. 5:9.

KHALANI MASO

15. N’cifukwa ciani kukhala maso n’kofunika ngako?

15 Kukhala maso n’kofunika kwambili pamene tikuyesetsa kuonetsa kuwala kwathu. Yesu analangiza ophunzila ake mobweleza-bweleza kuti: “Khalani maso.” (Mat. 24:42; 25:13; 26:41) Izi zionetsa kuti ngati timaona kuti “cisautso cacikulu” cikali kutali, kapena kuti cidzabwela ise titafa kale, tingayambe kugwila nchito yathu yolalikila mwamphwayi. (Mat. 24:21) Ndipo m’malo moonetsa kuwala kwambili kwa anthu a m’dela lathu, kuwala kwathu kudzayamba kuzimililika kapena kudzazimilatu.

16, 17. Mungacite ciani kuti mukhalebe maso mwauzimu?

16 Pamene zinthu zikuipila-ipila masiku ano otsiliza, tonse tifunika kukhalabe maso. Tiyenela kukumbukila kuti Yehova adzacitapo kanthu panthawi yake yoyenelela. Sitifunika kukayikila zimenezi. (Mat. 24:42-44) Koma tiyenela kukhala oleza mtima ndi achelu nthawi zonse. Muziŵelenga Baibo tsiku lililonse, ndipo musamanyalanyaze kupemphela. (1 Pet. 4:7) Muziganizila zitsanzo zabwino za abale na alongo amene ali na umoyo wacimwemwe cifukwa cokhalabe maso mwauzimu na kuonetsa kuwala kwawo. Citsanzo cimodzi ni cimene cinafotokozedwa m’nkhani yakuti: “Ndagwira Chovala cha Myuda kwa Zaka Zoposa 70,” imene ili mu Nsanja ya Olonda ya April 15, 2012 peji 18-21.

17 Muzikhala na zocita zambili potumikila Yehova. Ndiponso muzikhala na mayanjano olimbikitsana ndi abale na alongo anu. Kucita izi kudzakubweletselani cimwemwe coculuka, ndipo mudzayamba kuona kuti nthawi ikuthamanga. (Aef. 5:16) Zaka 100 zapitazo, abale athu anali okangalika ndipo anacita zambili potumikila Yehova. Koma motsogoleledwa na Yehova, masiku ano tikucita zambili kuposa kale lonse. Tikuonetsa kuwala kwathu pa mlingo waukulu kwambili kuposa mmene tinali kuyembekezela.

Maulendo aubusa amene akulu amacita amatipatsa mwayi wopeza nzelu zocokela m’Mau a Mulungu (Onani palagilafu 18, 19)

18, 19. Kodi akulu angatithandize bwanji kukhala acangu ndi ogalamuka mwauzimu? Fotokozani citsanzo.

18 N’zolimbitsa cikhulupililo kudziŵa kuti ngakhale ndise opanda ungwilo, tingathe kutumikila Yehova movomelezeka. Mwa ici, muziyamikila “mphatso za amuna,” kapena kuti akulu, amene Yehova wapeleka m’mipingo. (Ŵelengani Aefeso 4:8, 11, 12) Conco, pamene mkulu wakuyendelani, muziona kuti ni mwayi wophunzilapo kanthu pa nzelu zake na malangizo ake.

19 Mwacitsanzo, banja lina ku England linapempha akulu aŵili kuti akalithandize pa mavuto a m’banja lawo. Mkazi anali kuona kuti mwamuna wake sanali kutsogolela banjalo pa zinthu zauzimu. Mwamuna anavomeleza kuti sanali mphunzitsi wabwino komanso sanali kucititsa kulambila kwa pabanja mokhazikika. Akulu anathandiza banjali mwa kuwafotokozela citsanzo ca Yesu. Iye anali kusamalila ophunzila ake na kuganizila zosoŵa zawo. Akuluwo analimbikitsa mwamuna kuti ayenela kutengela citsanzo ca Yesu. Analimbikitsanso mkazi kuti ayenela kukhala woleza mtima. Akuluwo anafotokozelanso banjalo mfundo zimene zikanawathandiza kuti capamodzi apange makonzedwe ocita kulambila kwa pabanja ndi ana awo aŵili. (Aef. 5:21-29) Patapita nthawi, akuluwo anayamikila mwamunayo cifukwa ca kuyesa-yesa kwake. Iwo anamuuza kuti alimbikile komanso kuti azidalila mzimu woyela kuti umuthandize kukhala mutu wa banja wabwino. Cifukwa ca thandizo la akuluwo na cikondi cawo, tsopano banjalo likuonetsa kuwala mwauzimu.

20. Kodi pamakhala zotulukapo zanji ngati tionetsa kuwala kwathu?

20 Wamasalimo anati: “Wodala ndi aliyense woopa Yehova, amene amayenda m’njila za Mulungu.” (Sal. 128:1) Pamene muonetsa kuwala kwanu mwa kuthandiza ena kuyamba kutumukila Mulungu, kucita zinthu zolimbikitsa mtendele, na kukhalabe maso mwauzimu, mudzapeza cimwemwe coculuka. Anthu ena adzaona makhalidwe anu abwino, ndipo ambili adzalemekeza Atate wathu wakumwamba.—Mat. 5:16.