Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

“Ufumu Wanga Suli Mbali ya Dziko Lino”

“Ufumu Wanga Suli Mbali ya Dziko Lino”

“Cimene ndinabwelela m’dziko, ndico kudzacitila umboni coonadi.”—YOH. 18:37.

NYIMBO: 15, 74

1, 2. (a) N’ciani cionetsa kuti vuto la kusagwilizana m’dziko likukulila-kulila? (b) Kodi tidzakambilana mafunso ati m’nkhani ino?

POKAMBA za kale lake, mlongo wina wa kum’mwela kwa Europe anati: “Kucokela nili mwana, n’nali kuona zinthu zopanda cilungamo zokha-zokha.” Iye anapitiliza kuti: “Conco, n’naleka kugwilizana na boma n’kuyamba kucilikiza magulu a anthu ofuna kuti zinthu zisinthe. Ndipo kwa zaka zambili, n’nali pa cisumbali na cigaŵenga cinacake.” M’bale wina wa kum’mwela kwa Africa, nayenso poyamba anali kuona kuti kucita zaciwawa kulibe vuto. Iye anati: “N’nali kuona kuti mtundu wanga ni wabwino kwambili kuposa ina yonse, komanso n’nangena m’cipani candale. M’cipanico, anatiphunzitsa kupha adani athu na mikondo, kuphatikizapo anthu a mtundu wathu amene anali kucilikiza zipani zina zandale.” Mlongo winanso wa ku Central Europe anati: “N’nali watsankho, n’nali kuzonda munthu aliyense amene sanali wa m’dziko lathu kapena amene sanali wacipembedzo canga.”

2 Masiku ano, anthu ambili ali na makhalidwe ngati amene Akhristu atatu amenewa anali nawo poyamba. Magulu aciwawa omenyela ufulu wodzilamulila aculuka, mikangano ya zandale ikukulila-kulila, komanso m’maiko ambili, anthu amazonda kwambili alendo ocokela ku maiko ena. Monga mmene Baibo inakambila, anthu ambili masiku otsiliza ano ‘safuna kugwilizana ndi anzawo.’ (2 Tim. 3:1, 3) Popeza kuti anthu ambili m’dzikoli ni osagwilizana, kodi Akhristu angateteze bwanji mgwilizano wawo? Tingaphunzile zambili pa nkhaniyi mwa kuona mmene Yesu anacitila zinthu m’nthawi yake pamene kunali mavuto a zandale. Tiyeni tikambilane mafunso atatu ofunika aya: N’cifukwa ciani Yesu anakana kucilikiza magulu a zandale? Kodi anaonetsa bwanji kuti atumiki a Mulungu safunika kutengamo mbali m’zandale? Nanga anatiphunzitsa bwanji kuti kucitila anthu ena zaciwawa n’kulakwa?

MMENE YESU ANALI KUONELA ANTHU OMENYELA UFULU WODZILAMULILA

3, 4. (a) Kodi Ayuda a m’nthawi ya Yesu anali kuyembekezela ciani? (b) Nanga zimenezo zinawakhudza bwanji ophunzila a Yesu?

3 Ayuda ambili amene Yesu anali kuwalalikila anali kufuna kuti azidzilamulila okha osati kulamulidwa na Aroma. Kagulu ka Ayuda omenyela ufulu wa dziko lawo, kochedwa Azeloti, kanali kulimbikitsa anthu kukhala na maganizo amenewa. Ambili mwa Ayuda amenewo anali kutengela nzelu za Yudasi Mgalileya. Iye anali Mesiya wa bodza wa m’nthawi imeneyo amene anasoceletsa anthu ambili. Katswili wolemba mbili ya Ayuda, Josephus, anafotokoza kuti Yudasi “anali kusonkhezela anthu kuukila boma, mwa kuwanena kuti ni amantha cifukwa cololela kupeleka msonkho kwa Aroma.” Mwa ici, Aroma anamupha Yudasi. (Mac. 5:37) Ndipo Azeloti ena anali kucita zaciwawa pofuna kukhala na ufulu wodzilamulila.

4 Kuwonjezela pa Ayuda aciwawa amenewo, Ayuda ena ambili anali kuyembekezela mwacidwi kubwela kwa Mesiya. Iwo anali kuyembekezela kuti Mesiya akadzabwela, adzabweletsa ulemelelo m’dziko lawo na kulimasula ku ulamulilo wa Aroma. (Luka 2:38; 3:15) Ambili anali kukhulupilila kuti Mesiya adzakhazikitsa ufumu wake mu Isiraeli. Ndipo zikadzakala conco, Ayuda mamiliyoni ambili amene anabalalikila m’maiko ena adzabwelelanso m’dziko lawo. Kumbukilani kuti nthawi ina, Yohane Mbatizi anafunsa Yesu kuti: “Kodi Mesiya amene tikumuyembekezela uja ndinu kapena tiyembekezele wina?” (Mat. 11:2, 3) Mwina Yohane anafuna kudziŵa ngati kudzabwela munthu wina amene adzakwanilitsa zonse zimene Ayuda anali kuyembekezela. Nawonso ophunzila aŵili amene anakumana ndi Yesu panjila yopita ku Emau, pambuyo pakuti waukitsidwa, anaona kuti zinthu zina zokhudza Mesiya zimene anali kuyembekezela sizinakwanilitsike. (Ŵelengani Luka 24:21.) Patapita nthawi yocepa, atumwi a Yesu anam’funsa kuti: “Ambuye, kodi mubwezeletsa ufumu kwa Isiraeli pa nthawi ino?”—Mac. 1:6.

5. (a) N’cifukwa ciani anthu a ku Galileya anafuna kumulonga ufumu Yesu? (b) Nanga Yesu anawathandiza bwanji kuwongolela maganizo awo?

5 Mosakayikila, ziyembekezo zimene anthu anali nazo zokhudza Mesiya n’zimene zinacititsa kuti anthu a ku Galileya aganize zolonga Yesu ufumu. Mwacionekele, iwo anaona kuti Yesu angakhale mtsogoleli wabwino ngako. Iye anali wodziŵa kulankhula, anali kucilitsa odwala, komanso anakwanitsa ngakhale kupatsa cakudya anthu amene anali na njala. Pambuyo podyetsa amuna pafupi-fupi 5,000, Yesu anazindikila zimene anthuwo anafuna kucita. Baibo imati: “Yesu atadziŵa kuti iwo akufuna kumugwila kuti amuveke ufumu, anacoka ndi kupitanso kuphili yekhayekha.” (Yoh. 6:10-15) Tsiku lotsatila pamene anali ku tsidya lina la nyanja ya Galileya, Yesu anaona kuti maganizo ofuna kumulonga ufumu amene anthuwo anali nawo, acepako. Conco, anawafotokozela colinga ceni-ceni ca utumiki wake. Anawauza kuti sanabwele kudzawapatsa zinthu zakuthupi, koma kudzawaphunzitsa za Ufumu wa Mulungu. Anati: “Musamagwile nchito kuti mungopeza cakudya cimene cimawonongeka, koma kuti mupeze cakudya cokhalitsa, copeleka moyo wosatha.”—Yoh. 6:25-27.

6. Kodi Yesu anaonetsa bwanji kuti sanali kufuna kukhala mfumu pa dziko lapansi? (Onani pikica kuciyambi.)

6 Atatsala pang’ono kuphedwa, Yesu anazindikila kuti ena mwa otsatila ake anali kuyembekezela kuti iye adzakhazikitsa ufumu wake pa dziko lapansi ku Yerusalemu. Iye anawathandiza kuwongolela maganizo olakwikawo mwa kuwafotokozela fanizo la ndalama za mina. Fanizolo linaonetsa kuti “munthu wina wa m’banja lacifumu,” kutanthauza Yesu, adzafunika kupita kutali kukakhala kumeneko kwa nthawi yaitali asanalandile ufumu. (Luka 19:11-13, 15) Yesu anafotokozelanso atsogoleli aciroma kuti iye sali mbali ya dziko. Pontiyo Pilato anafunsa Yesu kuti: “Kodi ndiwe mfumu ya Ayuda?” (Yoh. 18:33) N’kutheka kuti Pilato anali kudela nkhawa kuti mwina Yesu angayambitse msokonezo pa zandale. Iyi ndiyo inali nkhawa yaikulu ya Pilato mu ulamulilo wake wonse. Yesu anamuyankha kuti: “Ufumu wanga suli mbali ya dziko lino.” (Yoh. 18:36) Yesu sanafune kutenga mbali m’zandale cifukwa Ufumu wake ni wakumwamba. Iye anauza Pilato kuti cimene anabwelela pa dziko lapansi ni “kudzacitila umboni coonadi.”—Ŵelengani Yohane 18:37.

Kodi mumaika kwambili maganizo anu pa mavuto a m’dzikoli kapena pa Ufumu wa Mulungu? (Onani palagilafu 7)

7. N’cifukwa ciani n’cosavuta munthu kuyamba kucilikiza mwakacetecete anthu andale omenyela ufulu wodzilamulila?

7 Na ise ngati timaidziŵa bwino nchito yathu mofanana ndi Yesu, tidzapewa kucilikiza ngakhale mwakacetecete magulu andale omenyela ufulu wodzilamulila. Nthawi zina, kucita izi kungakhale kovuta. Woyang’anila dela wina anati: “Masiku ano, anthu ambili m’dela lathu amafunitsitsa kuti zinthu zisinthe pa zandale. Mzimu wokonda dziko lako ukukulila-kulila, ndipo ambili amakhulupilila kuti kukhala na ufulu wodzilamulila kungawathandize kukhala na umoyo wabwino. Koma cokondweletsa n’cakuti abale amaika mtima wawo wonse pa nchito yolalikila uthenga wabwino wa Ufumu. Izi zathandiza kuti akhalebe ogwilizana. Iwo amadalila Mulungu kuti ndiye adzathetsa zinthu zopanda cilungamo na mavuto ena amene timakumana nawo.”

KODI YESU ANAPEWA BWANJI KUTENGA MBALI M’MIKANGANO YA NDALE?

8. Pelekani citsanzo cimodzi ca zinthu zopanda cilungamo zimene Ayuda anali kucitilidwa m’nthawi ya atumwi.

8 Anthu ambili amatenga mbali m’zandale cifukwa coona zinthu zopanda cilungamo zimene zicitika. M’nthawi ya Yesu, nkhani ya kupeleka msonkho inali yovuta ngako. Ndipo cimene cinacititsa kuti Yudasi Mgalileya, amene tamuchula poyamba paja, aukile ulamulilo wa Roma ni kukhazikitsidwa kwa lamulo lakuti Ayuda azipeleka msonkho kwa Aroma. Anthu olamulidwa ndi Aroma, kuphatikizapo anthu amene Yesu anali kuwalalikila, anali kupeleka misonkho yambili, monga wa katundu, malo, ndi wa nyumba. Ndipo cimene cinawonjezela vuto n’cakuti anthu okhometsa msonkho anali acinyengo. Nthawi zina, iwo anali kucita kugula udindo wokhometsa msonkho kwa akulu-akulu a boma na kuuseŵenzetsa kuti apeze ndalama zambili. Zakeyu, mkulu wa okhometsa msonkho ku Yeriko, analemela kwambili cifukwa colanda anthu ndalama. (Luka 19:2, 8) Mwina, izi n’zimene okhometsa msonkho ambili anali kucita.

9, 10. (a) Kodi adani a Yesu anamuyesa bwanji kuti atengeko mbali m’mikangano ya ndale? (b) Nanga tiphunzilapo ciani pa zimene Yesu anayankha? (Onani pikica kuciyambi.)

9 Adani a Yesu anafuna kum’kola kuti atengeko mbali m’mikangano yokhudzana ndi za misonkho. Iwo anamuyesa pa nkhani ya kupeleka msonkho wa dinari imodzi, umene munthu aliyense wolamulidwa na Ufumu wa Roma anali kufunika kupeleka. (Ŵelengani Mateyu 22:16-18.) Ayuda ambili anali kuuzonda ngako msonkho umenewu, cifukwa unali kuonetsa kuti iwo ali pansi pa ulamulilo wa Aroma. “Acipani ca Herode” anayambitsa nkhaniyi poganiza kuti ngati Yesu angakambe kuti Ayuda asamapeleke msonkhowo, Aroma adzamuimba mlandu woukila boma. Komanso, Yesu akanakamba kuti Ayuda afunika kupeleka msonkhowo, ndiye kuti ophunzila ake sembe anayamba kumuzonda.

10 Yesu anacita zinthu mosamala kuti asatengeko mbali pa mikangano imeneyi ya misonkho. Iye anati: “Pelekani . . . za Kaisara kwa Kaisara, koma za Mulungu, kwa Mulungu.” (Mat. 22:21) Yesu anali kudziŵa kuti okhometsa msonkho ambili anali acinyengo. Koma iye sanafune kuti zimenezo zimusokoneze na kumulepheletsa kuika maganizo ake pa nkhani yofunika maningi ya Ufumu wa Mulungu, umene udzathetsa mavuto onse. Mwa ici, iye anapeleka citsanzo cabwino kwa otsatila ake onse. Iwo ayenela kupewa kutengako mbali m’mikangano ya ndale, olo anthu ena andale aoneke kuti akucita zabwino kapena zacilungamo kusiyana ndi ena. Akhristu amafuna-funa Ufumu wa Mulungu na cilungamo cake. Ndiye cifukwa cake amapewa kukhala na maganizo amphamvu ofuna kutsutsa zinthu zina zopanda cilungamo zimene boma lingacite.—Mat. 6:33.

11. Kodi njila yabwino kwambili yothetsela zinthu zopanda cilungamo ni iti?

11 A Mboni za Yehova ambili anakwanitsa kuthetsa maganizo olakwika amene anali nawo pa zandale. Mlongo wina wa ku Britain anati: “Pambuyo pocita maphunzilo a za cikhalidwe ku yunivesite, n’nayamba kufunitsitsa kuti zinthu zisinthe. N’nali kufuna kuti anthu akuda akhale na ufulu woculuka, cifukwa pa nthawiyo tinali kucitilidwa zinthu zambili zopanda cilungamo. N’nali na luso lokamba mfundo zomveka pomenyela ufulu anthu akuda, koma sizinaphule kanthu. Sin’nali kudziŵa kuti cingathetse vuto la kusankhana mitundu ni kuthandiza anthu kusintha mitima yawo. Koma n’tayamba kuphunzila Baibo, n’nazindikila kuti nifunika kuyamba ndine kusintha mtima wanga. Ndipo mlongo waciyela na amene ananithandiza moleza mtima kupanga masinthidwe amenewo. Lomba nikutumikila monga mpainiya wanthawi zonse mumpingo wa citundu camanja, ndipo naphunzila kulalikila anthu a mitundu yonse.”

“BWEZELA LUPANGA LAKO M’CIMAKE”

12. Kodi “cofufumitsa” cimene Yesu anauza ophunzila ake kuti afunika kupewa cinali ciani?

12 M’nthawi ya Yesu, cipembedzo nthawi zambili cinali kutenga mbali m’zandale. Buku lina lokamba za umoyo wa anthu a m’nthawi ya Yesu limati, “magulu a cipembedzo aciyuda anali kucita zinthu mofanana ndi zipani zandale” (Daily Life in Palestine at the Time of Christ). N’cifukwa cake Yesu anacenjeza ophunzila ake kuti: “Khalani maso! Cenjelani ndi cofufumitsa ca Afarisi ndi ca Herode.” (Maliko 8:15) Pamene Yesu anakamba kuti cofufumitsa ca Herode, zionetsa kuti anali kukamba za a cipani ca Herode. Pa zandale, Afarisi anali kufuna kuti Ayuda akhale na ufulu wodzilamulila okha. Malinga n’zimene Mateyu analemba, Yesu anachulakonso za Asaduki. Asaduki anali kufuna kuti anthu apitilize kuwaona kukhala apamwamba. Ambili mwa iwo anali na maudindo apamwamba mu ulamulilo wa Roma. Mpake kuti Yesu anacenjeza ophunzila ake mwamphamvu kuti akhale maso na cofufumitsa, kapena kuti ziphunzitso zimene magulu atatu amenewa anali kulimbikitsa. (Mat. 16:6, 12) N’zocititsa cidwi kuti Yesu anauza ophunzila ake zimenezi pasanapite nthawi itali kucokela pamene anthu anafuna kumulonga ufumu.

13, 14. (a) Kodi nkhani zandale ndi zacipembedzo zinayambitsa bwanji ciwawa na kupanda cilungamo? (b) N’cifukwa ciani sitifunika kucita zaciwawa olo pamene ena akuticitila zinthu zopanda cilungamo? (Onani pikica kuciyambi.)

13 Ngati cipembedzo citenga mbali m’zandale, kaŵili-kaŵili zotulukapo zake zimakhala ciwawa. Yesu anauza ophunzila ake kuti safunika kutengako mbali m’zandale. Ici n’cimodzi mwa zifukwa zimene ansembe aakulu na Afarisi anapangila ciwembu copha Yesu. Anali kuyopa kuti anthu adzayamba kulemekeza kwambili iye m’malo mwa iwo. Ndipo pamapeto pake iwo sadzakhalanso na mphamvu pa zandale ndi pa za cipembedzo. Iwo anati: “Ngati timulekelela, onse adzakhulupilila mwa iye, ndipo Aroma adzabwela kudzatenga malo athu ndi mtundu wathu.” (Yoh. 11:48) N’cifukwa cake Mkulu wa Ansembe, Kayafa, anali patsogolo popanga ciwembu ca kupha Yesu.—Yoh. 11:49-53; 18:14

14 Kayafa anatuma asilikali kuti akagwile Yesu usiku. Yesu anali kudziŵa za ciwembu cimeneci. Conco, pamene Yesu anali kudya cakudya pamodzi na atumwi ake pa tsiku lakuti iye adzaphedwa maŵa, anawauza kuti atenge malupanga aŵili. Iye anali kufuna kuwaphunzitsa mfundo inayake yofunika kwambili. (Luka 22:36-38) Usiku wa tsiku limenelo, Petulo anatenga lupanga na kutema nalo mmodzi wa anthu amene anabwela kudzagwila Yesu. Mwacionekele, iye anakwiya poona kupanda cilungamo kumene anthuwo anaonetsa pobwela kudzagwila Yesu usiku. (Yoh. 18:10) Koma Yesu anauza Petulo kuti: “Bwezela lupanga lako m’cimake, pakuti onse ogwila lupanga adzafa ndi lupanga.” (Mat. 26:52, 53) Mfundo yamphamvu imeneyi ni yogwilizana ndi pemphelo limene iye anapeleka madzulo a tsikulo, lakuti ophunzila ake sayenela kukhala mbali ya dziko. (Ŵelengani Yohane 17:16.) Iwo anafunika kuyembekezela Mulungu kuti ndiye adzathetsa zinthu zopanda cilungamo.

15, 16. (a) Kodi Mau a Mulungu athandiza bwanji Akhristu kupewa mikangano? (b) Ni kusiyana kwanji pakati pa anthu kumene Yehova amaona akayang’ana pa dzikoli?

15 Mlongo wa kum’mwela kwa Europe amene tam’tomola kuciyambi kwa nkhani ino, anaphunzila mfundo imeneyi. Iye anati: “N’nazindikila kuti kucita ciwawa sikungathetse zinthu zopanda cilungamo. N’naona kuti nthawi zambili anthu amene amakonda kucita ciwawa amaphedwa. Ndipo ambili amakhumudwa cifukwa cogwilitsidwa mwala. N’nakondwela ngako pamene n’naphunzila m’Baibo kuti Mulungu yekha na amene angabweletse mtendele padziko lapansi. Uwu ni uthenga umene nakhala nikulalikila kwa zaka 25.” Nayenso m’bale wa kum’mwela kwa Africa amene tam’chula poyamba paja, analeka kuseŵenzetsa mikondo. Iye anayamba kugwilitsila nchito “lupanga la mzimu,” limene ni Mau a Mulungu, polalikila uthenga wamtendele kwa anthu a mtundu uliwonse. (Aef. 6:17) Komanso pambuyo pokhala Mboni ya Yehova, mlongo uja wa ku Central Europe, anakwatiwa na m’bale wa mtundu umene anali kudana nawo poyamba. Akhristu onse atatu amenewa anasintha makhalidwe awo cifukwa cofunitsitsa kutengela Khristu.

16 Ndithudi! Kusintha kumeneku n’kofunika ngako. Baibo imayelekezela mtundu wa anthu na nyanja imene ikuwinduka, imene ikulephela kukhala bata. (Yes. 17:12; 57:20, 21; Chiv. 13:1) Pamene mavuto a zandale akucititsa anthu kukhala osagwilizana komanso aciwawa, ise Akhristu takhalabe ogwilizana ndi amtendele. Ndipo pamene Yehova aona kusagwilizana kwa anthu padzikoli, amanyadila kuona mgwilizano umene uli pakati pa anthu ake.—Ŵelengani Zefaniya 3:17.

17. (a) Kodi tingalimbitse mgwilizano wathu m’njila zitatu ziti? (b) Tidzakambilana ciani m’nkhani yokonkhapo?

17 M’nkhani ino, takambilana kuti tingalimbitse mgwilizano pakati pathu m’njila zitatu izi: (1) Mwa kudalila Ufumu wa Mulungu wakumwamba kuti ni umene udzathetsa kupanda cilungamo, (2) kupewa kutenga mbali m’zandale, ndi (3) kupewa kucita zaciwawa. Komabe, nthawi zina mgwilizano wathu ungasokonezeke cifukwa ca khalidwe la tsankho. Akhristu a m’nthawi ya atumwi sanalole tsankho kusokoneza mgwilizano wawo. M’nkhani yokonkhapo, tidzakambilana zimene ifenso tingacite kuti tsankho lisasokoneze mgwilizano wathu.