NSANJA YA MLONDA—YOPHUNZILA March 2018

Magazini ino ili na nkhani zophunzila wiki ya April 30-June 3, 2018.

Ubatizo Ni Wofunika kwa Mkhristu Aliyense

Kodi Baibo imaphunzitsa ciani pa nkhani ya ubatizo? N’zinthu ziti zimene munthu afunika kucita kuti ayenelele ubatizo? Nanga n’cifukwa ciani mphunzitsi wa Baibo ayenela kumakumbukila kufunika kwa ubatizo pamene aphunzitsa mwana wake kapena wophunzila Baibo?

Makolo, Kodi Mukuthandiza Ana Anu Kupita Patsogolo kuti Akabatizike?

Kodi makolo acikhristu ayenela kutsimikila za ciani mwana wawo asanabatizike?

STUDY GUIDES

Cinyanja
Released
Cinyanja
Pending
(ID#939552)

ZOTHANDIZILA KUPHUNZILA

Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga

N’cifukwa ciani Mboni za Yehova zimajambula mtumwi Paulo ali na dazi kapena ali na tsitsi locepa?

Kucelezana ni Khalidwe Lofunika Kwambili!

N’cifukwa ciani Malemba amalimbikitsa Akhristu kuceleza anzawo? Ni mipata iti imene tili nayo yoceleza ena? Tingagonjetse bwanji zopinga zimene zingatilepheletse kukhala oceleza?

MBILI YANGA

Yehova Sananigwilitse Mwala

Erika Nöhrer Bright watumikilapo monga mpainiya wa nthawi zonse, mpainiya wapadela, na mmishonale. Iye akufotokoza mmene Mulungu anam’thandizila, kumulimbikitsa, na kumugwilitsitsa pa zaka zonse zimene wakhala akutumikila Mulungu mokhulupilika.

Cilango Ni Umboni Wakuti Mulungu Amatikonda

Kodi tingaphunzile ciani kwa atumiki a Mulungu amene iye anawapatsapo cilango m’nthawi yakale? Nanga tingatengele bwanji Yehova pamene tipatsa munthu cilango?

“Mvelani Malangizo Kuti Mukhale Anzelu”

Kodi Yehova amatiphunzitsa bwanji kuti tizitha kudzilanga tekha? Nanga tingapindule bwanji na cilango cimene tingalandile mu mpingo?