Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Cilango Ni Umboni Wakuti Mulungu Amatikonda

Cilango Ni Umboni Wakuti Mulungu Amatikonda

“Yehova amalanga aliyense amene iye amamukonda.”—AHEB. 12:6.

NYIMBO: 123, 86

1. Kodi Baibo imaonetsa kuti cilango n’cinthu cotani?

MUKAMVA liu lakuti “cilango,” mumaganizila za ciani? Mwina maganizo anu amathamangila ku cibalo kapena mkwapulo. Koma “cilango” cimaphatikizapo mbali zingapo. Baibo imachula cilango monga cinthu cabwino, mofanana ndi cidziŵitso, nzelu, cikondi, na moyo. (Miy. 1:2-7; 4:11-13) Cilango ca Mulungu n’cabwino cifukwa cimaonetsa kuti iye amatikonda ndipo amafuna kuti tikapeze moyo wosatha. (Aheb. 12:6) Cilango cimene Mulungu amapeleka sicikhala ca nkhanza. Conco, “cilango” cimene Baibo imakamba, mbali yaikulu cimatanthauza kuphunzitsa, monga mmene makolo amaphunzitsila mwana wawo wokondedwa.

2, 3. Kodi cilango cingaphatikizepo bwanji kuphunzitsa na cibalo? (Onani pikica pamwambapa.)

2 Tiyelekezele conco: Mwana dzina lake Johnny akuseŵeletsa bola m’nyumba. Ndiyeno, amayi ake amuuza kuti: “Iwe Johnny, leka kuseŵeletsa bola m’nyumba! Ungaphwanye zinthu.” Koma iye sakuwamvela. Apitiliza kuseŵela na bolayo, ndipo akuphwanya mphika wa maluŵa. Kodi amayi ake angam’lange bwanji? Angacite izi mwa kum’phunzitsa na kum’patsa cibalo. Pomuphunzitsa, angamuuze cifukwa cake zimene wacita si zabwino. Iwo angacite izi pofuna kuthandiza mwanayo kuona kufunika kowamvela, na kumufotokozela kuti malamulo awo ni oyenelela ndiponso ofunika kuwatsatila. Ndiyeno, pofuna kum’thandiza kuti aphunzilepo kanthu, angam’patse cilango casaizi. Mwacitsanzo, angamulande bolayo na kum’bisila kwa masiku angapo. Kucita izi kungam’thandize kuona kuti kusamvela kumabweletsa mavuto.

3 Ise Akhristu, ndise a m’nyumba ya Mulungu. (1 Tim. 3:15) Mwa ici, timadziŵa kuti Yehova ali na ufulu wotiikila malamulo na kutipatsa cilango mwacikondi ngati taphwanya malamulowo. Komanso, tikakumana na mavuto cifukwa ca chimo limene tacita, timaona kuti kumvela Atate wathu wakumwamba n’kofunika kwambili. Iyinso ni mbali ya cilango ca Yehova. (Agal. 6:7) Mulungu amatikonda ngako ndipo samafuna kuti tikumane na mavuto.—1 Pet. 5:6, 7.

4. (a) Kodi Yehova amafuna kuti tiziwaphunzitsa bwanji ena? (b) N’ciani cimene tidzakambilana m’nkhani ino?

4 Mwa kupatsa mwana wathu kapena wophunzila Baibo cilango ca m’Malemba, tingamuthandize kukwanilitsa colinga cokhala wotsatila wa Khristu. Mau a Mulungu, amene ni cida cathu cofunika kwambili pophunzitsa, angatithandize polangiza ena m’cilungamo. Ngati tiseŵenzetsa Mau a Mulungu pophunzitsa, tingathandize mwana wathu kapena wophunzila Baibo kumvetsetsa na ‘kusunga zinthu zonse zimene Yesu anatilamulila.’ (2 Tim. 3:16; Mat. 28:19, 20) Kuphunzitsa mwanjila imeneyi n’kumene Yehova amafuna, cifukwa kumakonzekeletsa ophunzila kuti nawonso akathe kupanga ophunzila a Khristu. (Ŵelengani Tito 2:11-14.) Lomba tiyeni tikambilane mayankho pa mafunso atatu ofunika aya: (1) Kodi cilango ca Mulungu cimaonetsa bwanji kuti amatikonda? (2) Kodi tingaphunzile ciani kwa atumiki a Mulungu amene iye anawapatsapo cilango m’nthawi yakale? (3) Kodi tingatengele bwanji Yehova na Mwana wake pamene tipatsa ena cilango ca uphungu?

MULUNGU AMAPELEKA CILANGO MWACIKONDI

5. Kodi cilango ca Yehova cimaonetsa bwanji kuti amatikonda?

5 Cifukwa ca cikondi cake, Yehova amatiwongolela na kutiphunzitsa n’colinga cakuti tikhalebe mabwenzi ake, na kuti tisapatuke pa njila ya ku moyo. (1 Yoh. 4:16) Iye satinyazitsa kapena kuticititsa kudziona monga osafunika. (Miy. 12:18) Koma amationa kuti ndise ofunika, ndipo amayang’ana kwambili pa zabwino zimene timacita. Komanso, amalemekeza ufulu wathu wodzisankhila zocita. Kodi imwe mumaona kuti cilango cimene Mulungu amatipatsa kupitila m’Mau ake, zofalitsa, makolo acikhristu, kapena akulu mu mpingo, ni umboni wakuti iye amatikonda? Ndithudi, akulu akatiwongolela mwacikondi ndi mokoma mtima pamene tayamba kuloŵela “njila yolakwika” mwina mosazindikila, zimaonetsa cikondi ca Yehova pa ise.—Agal. 6:1.

6. Ngati cilango ciphatikizapo kucotsedwa pa udindo, kodi cimaonetsa bwanji cikondi ca Mulungu?

6 Koma nthawi zina, cilango ca Mulungu cingapose pa uphungu kapena kuwongolela cabe. Ngati Mkhristu wacita chimo lalikulu, amalandiwa udindo kapena mwayi wa mautumiki ena mu mpingo. Olo zikhale conco, cilango cotelo cimaonetsa kuti Mulungu amam’konda munthuyo. Mwacitsanzo, kulandiwa udindo kungam’thandize kuona kufunika kocita phunzilo la Baibo laumwini, kusinkha-sinkha, na kupemphela. Kucita izi kungamuthandize kuti akhalenso wolimba mwauzimu. (Sal. 19:7) M’kupita kwa nthawi, angapatsiwenso maudindo. Ngakhale kucotsa munthu mu mpingo kumaonetsa cikondi ca Yehova, cifukwa kumateteza mpingo ku makhalidwe oipa. (1 Akor. 5:6, 7, 11) Ndipo popeza Mulungu amapeleka cilango coyenelela, kucotsa munthu mu mpingo kungam’thandize kuzindikila kukula kwa chimo lake na kum’sonkhezela kulapa.—Mac. 3:19.

ANAPINDULA NA CILANGO CA YEHOVA

7. Kodi Sebina anali ndani? Nanga ni khalidwe liti loipa limene iye anayamba kukhala nalo?

7 Kuti timvetsetse phindu la cilango, tiyeni tikambilane za anthu aŵili amene anapatsidwako cilango na Yehova. Anthu ake ni Sebina, amene anakhalako m’nthawi ya Mfumu Hezekiya, ndi Graham, m’bale wa m’nthawi yathu ino. Sebina anali kapitawo “woyang’anila nyumba ya mfumu.” Mwina mfumuyo inali Hezekiya. Conco, Sebina anali na udindo waukulu. (Yes. 22:15) Koma comvetsa cisoni n’cakuti iye anakhala wodzikuza, ndipo anayamba kudzifunila ulemelelo. Anafika mpaka podzigobela manda olemekezeka, ndiponso anali kukwela pa ‘magaleta ankhondo aulemelelo.’—Yes. 22:16-18.

Mulungu amatidalitsa ngati tidzicepetsa na kusintha khalidwe lathu (Onani palagilafu 8-10)

8. Kodi Yehova anam’patsa cilango canji Sebina? Nanga zotulukapo zake zinali zotani?

8 Cifukwa cakuti Sebina anayamba kudzifunila ulemelelo, Mulungu ‘anamucotsa pa udindo wake” na kuikapo Eliyakimu. (Yes. 22:19-21) Izi zinacitika pa nthawi imene Mfumu Senakeribu ya Asuri anali kufuna kuwononga Yerusalemu. Patapita nthawi, mfumuyo inatumiza nthumwi zake ku Yerusalemu, pamodzi na gulu la asilikali kuti akalefule Ayuda na kuopseza Hezekiya kuti angodzipeleka m’manja mwawo. (2 Maf. 18:17-25) Eliyakimu anatumiwa kuti akakambilane na nthumwizo, koma sanapite yekha. Anapita ndi anthu ena aŵili. Mmodzi wa iwo anali Sebina, ndipo pa nthawiyo anali kutumikila monga kalembela. Cioneka kuti Sebina atapatsiwa cilango na Yehova sanakhumudwe, koma anaonetsa kudzicepetsa mwa kulandila udindo wotsikilapo wa ukalembela. Ngati zinalidi conco, kodi tingaphunzilepo ciani pa nkhaniyi? Tiyeni tikambilane mfundo zitatu zimene tingaphunzilepo.

9-11. (a) Fotokozani zimene tingaphunzilepo pa citsanzo ca Sebina. (b) Kodi imwe mwalimbikitsidwa bwanji na mmene Yehova anacitila zinthu na Sebina?

9 Coyamba, kumbukilani kuti Sebina anacotsewa pa udindo. Izi zitsimikizila mfundo yakuti “kunyada kumafikitsa munthu ku ciwonongeko, ndipo mtima wodzikuza umacititsa munthu kupunthwa.” (Miy. 16:18) Ngati muli na udindo mu mpingo, umene ungacititse kuti ena azikulemekezani, muyenela kukhalabe wodzicepetsa. Ndipo ngati muli na luso linalake, kapena ngati mwacita cina cake cotamandika, muyenela kukumbukila kuti zonse n’zocokela kwa Yehova. (1 Akor. 4:7) Mtumwi Paulo analemba kuti: “Ndikuuza aliyense wa inu kumeneko kuti musamadziganizile kuposa mmene muyenela kudziganizila. Koma aliyense aziganiza m’njila yakuti akhale munthu woganiza bwino.”—Aroma 12:3.

10 Caciŵili, popatsa Sebina uphungu wamphamvu, zionetsa kuti Yehova sanaone Sebina kukhala wothimbilila kapena wosawongoleka. (Miy. 3:11, 12) Apa pali phunzilo lofunika ngako kwa Akhristu amene anacotsedwa pa udindo mu mpingo, kapena amene alandiwa mwayi wa utumiki wina wake. M’malo mokhumudwa, iwo ayenela kupitiliza kutumikila Mulungu mokhulupilika pa malo awo atsopano. Kucita conco kudzaonetsa kuti amaona cilango ca Yehova kukhala umboni wa cikondi cake. Kumbukilani kuti ngati tadzicepetsa pamaso pa Mulungu, iye amaona kuti tili na mtima wofuna kusintha. (Ŵelengani 1 Petulo 5:6, 7.) Mulungu amatipatsa cilango n’colinga cakuti atiumbe. Conco, tiyeni tipitilize kukhala monga dongo lofewa m’manja mwake.

11 Cacitatu, mmene Yehova anapelekela cilango kwa Sebina zili na phunzilo lofunika kwa Akhristu amene ali na udindo wopeleka cilango, monga makolo na akulu mu mpingo. Phunzilo lanji? N’zoona kuti cilango ca Yehova cimaonetsa kuti iye amazonda chimo. Koma cimaonetsanso kuti amadela nkhawa munthu amene wacimwa. Ngati ndimwe kholo kapena mkulu, ndipo mufuna kupeleka cilango kwa mwana kapena kwa Mkhristu mnzanu, muyenela kutengela citsanzo ca Yehova. Muyenela kuzonda coipa cimene munthuyo anacita kwinaku mukuyesetsa kuyang’ana zabwino mwa iye.—Yuda 22, 23.

12-14. (a) N’ciani cimene ena amacita akapatsiwa cilango na Mulungu? (b) Kodi Mau a Mulungu anathandiza bwanji m’bale wina kusintha khalidwe lake? Nanga panakhala zotulukapo zanji?

12 Comvetsa cisoni n’cakuti ena akalandila cilango, amakhumudwa. Amasiya Mulungu na kuleka kugwilizana ndi anthu ake. (Aheb. 3:12, 13) Koma kodi zimenezi zitanthauza kuti anthu otelo basi anathimbilila sangasinthe? Iyai. Ganizilani za Graham. Iye anacotsewa mu mpingo, ndipo pambuyo pobwezeletsedwa, anakhala wozilala. Patapita zaka, anapempha mkulu amene anali kugwilizana naye kuti aziphunzila naye Baibo.

13 Mkuluyo anati: “Graham anali na khalidwe lonyada. Anali kupeza zifukwa akulu amene anasamalila mlandu wake umene unam’cotsetsa mu mpingo. Conco, pa maulendo angapo otsatila, tinakambilana malemba ofotokoza za kunyada na zotulukapo za khalidweli. Pamene tinali kukambilana, zinali monga kuti Graham akudziyang’ana pa gilasi ya Mau a Mulungu, ndipo sanakondwele na mmene anali kuonekela. Izi zinacititsa kuti asinthe modabwitsa. Graham anavomeleza kuti anacititsidwa khungu na mzimu wonyada, umene unali ngati “mtanda wa denga” m’diso lake. Anazindikila kuti iye ndiye anali na vuto. Anali kukonda kupeza zifukwa akulu. Conco, mwamsanga anayamba kusintha. Iye anayamba kupezeka pa misonkhano ya mpingo nthawi zonse, kuphunzila Mau a Mulungu mwakhama, na kupemphela tsiku lililonse. Cinanso, anayamba kusamalila udindo wake monga mutu wa banja. Izi zinakondweletsa mkazi wake ndi ana.”—Luka 6:41, 42; Yak. 1:23-25.

14 Mkuluyo anakambanso kuti: “Tsiku lina, Graham ananiuza mau ocititsa cidwi. Anati, ‘Nakhala m’coonadi kwa zaka zambili, ndipo natumikilapo monga mpainiya. Koma lomba m’pamene ningakambe kuti nimam’kondadi Yehova.’ Posapita nthawi, Graham anapatsidwa utumiki wopelekela maikolofoni pa misonkhano. Iye anayamikila ngako udindowu. Citsanzo cake cinaniphunzitsa kuti ngati munthu wadzicepetsa pa maso pa Mulungu mwa kulandila cilango cake, amalandila madalitso oculuka.”

POPELEKA CILANGO CA UPHUNGU, TENGELANI CITSANZO CA MULUNGU NA KHRISTU

15. Kuti cilango cathu ciwafike pa mtima anthu, n’ciani cimene tifunika kucita?

15 Kuti tikhale aphunzitsi abwino, tifunika kumacita zimene timaphunzitsa. (1 Tim. 4:15, 16) Conco, Akhristu amene ali na udindo wa m’malemba wopeleka cilango cauphungu kwa ena, ayenela kupitiliza kumvela malamulo a Yehova na mtima wonse. Kucita izi kumapangitsa kuti ena aziwalemekeza ndipo kumawapatsa ufulu wa kulankhula pophunzitsa na kulangiza ena. Ganizilani citsanzo ca Yesu.

16. Tingaphunzile ciani kwa Yesu pa nkhani ya kupeleka cilango moyenelela na kuphunzitsa mogwila mtima?

16 Nthawi zonse, Yesu anali kumvela Atate wake na mtima wonse, olo pamene kucita izi kunali kovuta. (Mat. 26:39) Cinanso, pofuna kuti ulemelelo upite kwa Mulungu, Yesu anauza anthu kuti nzelu na ziphunzitso zake zinali zocokela kwa Atate ake. (Yoh. 5:19, 30) Popeza kuti Yesu anali wodzicepetsa na womvela, anthu a mitima yabwino anali kumasuka naye. Kudzicepetsa na kumvela kunam’thandizanso kuti akhale mphunzitsi wacifundo ndi wokoma mtima. (Ŵelengani Luka 4:22.) Mau ake abwino analimbikitsa anthu amene mophiphilitsa anali ngati bango lophwanyika kapena monga nyale yofuka imene yatsala pang’ono kuzima. (Mat. 12:20) Ngakhale pamene anakumana na zinthu zokhumudwitsa, Yesu anali kucita zinthu mokoma mtima ndi mwacikondi. Izi zinaonekela bwino kwambili pamene anapatsa uphungu atumwi ake cifukwa coonetsa khalidwe lodzikonda na mzimu wofunitsitsa ulamulilo.—Maliko 9:33-37; Luka 22:24-27.

17. Ni makhalidwe abwino ati amene angathandize akulu kukhala abusa abwino a nkhosa za Mulungu?

17 Akhristu onse amene ali na udindo wopeleka cilango ca m’Malemba, afunika kutengela citsanzo ca Khristu. Kucita izi kumaonetsa kuti afuna kutsogoleledwa na Mulungu komanso na Mwana wake. Mtumwi Petulo anati: “Wetani gulu la nkhosa za Mulungu lomwe analisiya m’manja mwanu, osati mokakamizika, koma mofunitsitsa. Osatinso cifukwa cofuna kupindulapo kenakake, koma ndi mtima wonse. Osati mocita ufumu pa anthu amene ali coloŵa cocokela kwa Mulungu, koma mukhale zitsanzo kwa gulu la nkhosa.” (1 Pet. 5:2-4) Kukamba zoona, akulu amene amagonjela Mulungu na Khristu, mutu wa mpingo, amapindula komanso amapindulitsa nkhosa zimene akuziyang’anila.—Yes. 32:1, 2, 17, 18.

18. N’ciani cimene Yehova amafuna kuti makolo azicita? (b) Kodi Mulungu amawathandiza bwanji makolo kukwanilitsa udindo wawo?

18 Mfundo zimenezi zimagwilanso nchito m’banja. M’Baibo, mitu ya mabanja imalangizidwa kuti: “Musamapsetse mtima ana anu, koma muwalele m’malangizo a Yehova ndi kuwaphunzitsa kaganizidwe kake.” (Aef. 6:4) Kodi nkhani imeneyi ni yaikulu bwanji? Lemba la Miyambo 19:18 limaonetsa kuti imeneyi ni nkhani ya moyo kapena imfa. Ndithudi, Yehova amaona kuti makolo acikhristu ali na mlandu ngati amanyalanyaza udindo wawo wolanga ana moyenelela. (1 Sam. 3:12-14) Komabe, ngati makolo amacondelela Yehova na kufuna-funa citsogozo ca Mau ake na mzimu wake, iye amawapatsa nzelu na kuwathandiza kukwanilitsa udindowu.—Ŵelengani Yakobo 1:5.

KUKONZEKELA UMOYO WOSATHA KOMANSO WAMTENDELE

19, 20. (a) Ni madalitso anji amene timapeza tikalandila cilango ca Mulungu? (b) Tidzakambilana ciani m’nkhani yotsatila?

19 N’zosatheka kufotokoza madalitso onse amene timapeza ngati talandila cilango ca Mulungu, ndiponso ngati titengela citsanzo ca Yehova na Yesu polanga ena. Kungochulako ocepa cabe, m’banja na mu mpingo mumakhala mtendele. Komanso, aliyense amadzimva kukhala wofunika, wokondedwa, na wotetezeka. Izi ni dyonkho cabe ya madalitso am’tsogolo. (Sal. 72:7) Ndithudi, cilango ca Yehova cimatikonzekeletsa kudzakhala na moyo wosatha mwamtendele ndi mogwilizana, monga banja lake losamalidwa mwacikondi. (Ŵelengani Yesaya 11:9.) Ngati tikumbukila mfundo imeneyi, tidzaona cilango ca Mulungu kukhaladi umboni wa cikondi cake cacikulu pa ise.

20 M’nkhani yotsatila, tidzakambilana mbali zina za cilango cimene cimapelekedwa m’banja na mu mpingo. Tidzakambilananso za kudzilanga tekha ndi za cinacake cimene cimakhala coŵaŵa kwambili kuposa ululu uliwonse umene tingamve tikapatsidwa cilango.