Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Makolo, Kodi Mukuthandiza Ana Anu Kupita Patsogolo kuti Akabatizike?

Makolo, Kodi Mukuthandiza Ana Anu Kupita Patsogolo kuti Akabatizike?

“Ukucedwelanji? Nyamuka, ubatizidwe.” —MAC. 22:16.

NYIMBO: 51, 135

1. Kodi makolo acikhristu amafuna kutsimikizila ciani ana awo asanabatizike?

POFOTOKOZA zimene zinacitika atapanga cosankha cobatizika, mlongo Blossom Brandt anati: “Kwa miyezi ingapo n’nali kuuza atate na amayi kuti nifuna kubatizika, ndipo iwo nthawi zambili anali kukamba nane za nkhaniyi. Iwo anali kufuna kutsimikizila ngati n’nali kudziŵadi kuti kubatizika ni nkhani yaikulu. Tsiku la cocitika capadela cimeneci mu umoyo wanga, linafika pa December 31, 1934.” Masiku anonso, makolo acikhristu amayesetsa kuthandiza ana awo kupanga zosankha mwanzelu. Ndipo kuzengeleza kubatizika kungaononge ubwenzi wa munthu na Yehova. (Yak. 4:17) Komabe, ana asanabatizike, makolo amafuna kutsimikizila kuti anawo ni okonzeka kukwanilitsa udindo wokhala wophunzila wa Khristu.

2. (a) N’ciani cacititsa oyang’anila dela ena kukhala na nkhawa? (b) Tikambilana ciani m’nkhani ino?

2 Oyang’anila dela ena ali na nkhawa cifukwa nthawi zambili amapeza acicepele a zaka pafupi-fupi 20 kapena kuposelapo, amene sanabatizikebe olo kuti anakulila m’banja la Mboni. Ambili mwa acicepelewo amasonkhana ndi kulalikila. Ndipo amadziona kuti ni a Mboni za Yehova. Koma pa cifukwa cina, safuna kudzipeleka kwa Yehova na kubatizika. Kodi cifukwa cake n’citi? Nthawi zambili, makolo awo na amene amawauza kuti asabatizike mwamsanga. M’nkhani ino, tidzakambilana mafunso anayi okhudza zinthu zimene makolo ena acikhristu amada nazo nkhawa. Zinthu zimenezo n’zimene zimawalepheletsa kuthandiza ana awo kupita patsogolo mpaka kubatizika.

KODI MWANA WANGA WAFIKA PA MSINKHU WAKUTI N’KUBATIZIKA?

3. Kodi makolo a Blossom anali kufuna kutsimikizila ciani?

3 M’pomveka kuti makolo a Blossom, amene tam’chula m’ndime yoyamba, anali kufuna kutsimikizila ngati mwana wawo anali wokhwima mokwanila cakuti n’kumvetsetsa kuti kubatizika n’kofunika ndiponso ni nkhani yaikulu. Kodi makolo angadziŵe bwanji kuti mwana wawo angathe kudzipeleka moyenela?

4. Kodi lamulo la Yesu la pa Mateyu 28:19, 20 lingawathandize bwanji makolo pamene akuphunzitsa ana awo?

4 Ŵelengani Mateyu 28:19, 20. Monga tinakambila m’nkhani yapita, Baibo siichula msinkhu umene munthu afunika kufikapo kuti ayenelele kubatizika. Komabe, makolo angapindule mwa kuganizila zimene kupanga ophunzila kumatanthauza. Liu la Cigiriki lomasulidwa kuti ‘kuphunzitsa anthu’ pa Mateyu 28:19, limatanthauza kuphunzitsa na colinga copanga ophunzila. Wophunzila ni munthu amene waphunzila na kumvetsetsa ziphunzitso za Yesu, ndipo ni wokonzeka kucita zimene waphunzilazo. Conco, pamene makolo acikhristu akuphunzitsa ana awo kuyambila ali aang’ono, afunika kukhala na colinga cowathandiza kukhala ophunzila a Khristu obatizika. N’zoona kuti makanda sangayenelele kubatizika. Komabe, Baibo imaonetsa kuti ngakhale acicepele angamvetse coonadi ca m’Baibo na kuyamba kucikonda.

5, 6. (a) Kodi zimene Baibo imakamba zokhudza Timoteyo zitiphunzitsa ciani pa nkhani ya ubatizo? (b) Kodi makolo ozindikila angathandize bwanji ana awo?

5 Timoteyo anali wophunzila wa Khristu amene anayamba kukonda coonadi ali wacicepele. Mtumwi Paulo anakamba kuti Timoteyo anaphunzila coonadi kuyambila ali wakhanda. Olo kuti Timoteyo anabadwila m’banja la makolo osiyana zikhulupililo, amayi ake aciyuda ndi ambuye ake aakazi anam’thandiza kumvetsetsa Malemba, mogwilizana ndi cidziŵitso cimene Ayuda anali naco pa nthawiyo. Zotulukapo zake zinali zakuti iye anakhala na cikhulupililo colimba. (2 Tim. 1:5; 3:14, 15) Pamene anali na zaka pafupi-fupi 20 kapena kuposelapo, Timoteyo anali atakhala Mkhristu wofikapo, woti n’kupatsidwa maudindo apadela mumpingo.—Mac. 16:1-3.

6 Tifunika kukumbukila kuti mwana aliyense ali na cibadwa cake, ndipo ana amakula mosiyana-siyana. Ena amayamba kuganiza na kucita zinthu mwaucikulile ali aang’ono, ndipo angakhale na colinga cobatizika. Enanso angafunike kusinkhukilapo kuti ayenelele ubatizo. Conco, makolo ozindikila sakakamiza ana awo kuti abatizike. M’malomwake, amathandiza mwana aliyense kuti apite patsogolo mwauzimu mogwilizana ndi cibadwa cake komanso nzelu zake. Makolo amakondwela ngati mwana wawo wacita zinthu mwanzelu. (Ŵelengani Miyambo 27:11.) Komabe, sayenela kuiŵala colinga cawo, cimene ni kuthandiza ana awo kukhala ophunzila a Khristu. Pokhala na mfundo imeneyi m’maganizo, makolo angacite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi mwana wanga ali na cidziŵitso cokwanila moti angathe kudzipeleka kwa Mulungu ndi kubatizika?’

KODI MWANA WANGA ALI NA CIDZIŴITSO COFIKAPO?

7. Kuti munthu ayenelele ubatizo, kodi ayenela kudziŵa zonse? Fotokozani.

7 Monga aphunzitsi m’banja, mpake kuti makolo amafuna kuti ana awo akhale na cidziŵitso cokwanila cimene cingasonkhezele anawo kudzipeleka. Ngakhale n’conco, munthu safunika kucita kudziŵa zonse kuti adzipeleke kwa Mulungu na kubatizika. Pambuyo pa ubatizo, ophunzila onse afunika kupitiliza kukula m’cidziŵitso colongosoka. (Ŵelengani Akolose 1:9, 10.) Kodi cidziŵitsoco cifunika kukhala coculuka bwanji?

8, 9. Tingaphunzile zotani pa nkhani yokhudza Paulo na woyang’anila ndende?

8 Zimene zinacitikila banja lina m’nthawi ya atumwi zingathandize makolo kudziŵa kuculuka kwa cidziŵitso cimene munthu amafunikila kuti abatizike. (Mac. 16:25-33) Pa ulendo wake waciŵili waumishonale, ca mu 50 C.E., Paulo anafikanso ku mzinda wa Filipi. Ali kumeneko, iye na mnzake Sila anamangiwa pa mlandu wabodza, ndipo anaponyedwa m’ndende. Usiku, civomezi camphamvu cinagwedeza maziko a ndendeyo cakuti zitseko zonse zinatsekuka. Poganiza kuti akaidi aja athawa, woyang’anila ndende anacita mantha cakuti anatenga lupanga kuti adziphe. Koma Paulo anafuula pomuletsa. Ndiyeno iye na Sila analalikila mogwila mtima kwa woyang’anila ndendeyo na banja lake. Kodi mwamunayo na banja lake anatenga sitepi yanji ataphunzila coonadi cokhudza Yesu? Mosataya nthawi, anabatizika. Kodi tingaphunzilepo ciani pa cocitika ici?

9 Woyang’anila ndendeyo ayenela kuti anali msilikali wopuma pa nchito. Ndipo anali wosadziŵa Malemba. Conco, kuti ayale maziko olimba a cidziŵitso ca Malemba, anafunikila kuphunzila mfundo zoyambilila za coonadi ca m’Baibo, kumvetsa bwino tanthauzo la kukhala mtumiki wa Mulungu, ndi kukhala wokonzeka kutsatila ziphunzitso za Yesu. M’nthawi yocepa, mfundo zoyambilila za m’Malemba zimene anaphunzila ndi kuziyamikila, zinam’sonkhezela kuti abatizike. Mosakayikila, pambuyo pobatizika, anapitiliza kuwonjezela cidziŵitso cake. Poganizila citsanzo cimeneci, mungacite ciani ngati muona kuti mwana wanu amamvetsetsa ziphunzitso zoyambilila za m’Malemba, kuphatikizapo tanthauzo ndi kufunika kodzipeleka na kubatizika? Monga makolo acikhristu, mungamulimbikitse kuti akaonane na akulu kuti akam’pende ngati ali woyenelela kubatizika. * Mofanana ndi Akhristu ena obatizika, iye adzapitiliza kuwonjezela cidziŵitso cake pa colinga ca Yehova. Adzacita zimenezi mu umoyo wake wonse, ngakhale kwamuyaya.—Aroma 11:33, 34.

KODI MAPHUNZILO ABWINO KWAMBILI KWA MWANA WANGA NI ATI?

10, 11. (a) Kodi makolo ena amakhala na maganizo otani? (b) N’ciani cimene kholo liyenela kuona kuti ndiye cofunika kwambili kwa mwana wake?

10 Makolo ena amaona kuti ni bwino kuti mwana wawo acedweko kubatizika n’colinga cakuti aciteko maphunzilo apamwamba coyamba na kupeza nchito yabwino. Pocita izi, iwo angakhale na colinga cabwino ndithu. Koma kodi kucita zimenezi kungathandize mwana wawo kukhaladi na umoyo wopambana? Komanso cofunika kwambili makolo afunika kudzifunsa kuti, kodi kucita zimenezi n’kogwilizana na Malemba? Nanga Mau a Yehova amatilimbikitsa kucita ciani?—Ŵelengani Mlaliki 12:1.

11 Tifunika kukumbukila kuti dziko loipali na zonse za m’dziko n’zosagwilizana ndi cifunilo ca Yehova kapena maganizo ake. (Yak. 4:7, 8; 1 Yoh. 2:15-17; 5:19) Kukhala pa ubwenzi wolimba na Yehova ndiye citetezo camphamvu kwa mwana kuti asasoceletsedwe na Satana, dziko lake, kapena maganizo a anthu a m’dzikoli. Kulimbikitsa mwana kukhala na zolinga zakuthupi kungamusokoneze na kumuononga mwauzimu. Kodi makolo acikondi acikhristu angafune kuti mwana wawo aziyendela maganizo a dzikoli pa nkhani ya kukhala na umoyo wabwino? Mfundo ni yakuti, timakhala na cimwemwe ceni-ceni komanso umoyo wopambana, kokha ngati tiika Yehova patsogolo mu umoyo wathu.—Ŵelengani Salimo 1:2, 3.

NANGA BWANJI MWANA WANGA AKADZACIMWA?

12. N’cifukwa ciani makolo ena amafuna kuti ana awo asabatizike mwamsanga?

12 Mlongo wina pofotokoza zifukwa zimene anali kuletsela mwana wake kubatizika, anati, “N’zocititsa manyazi kufotokoza, koma cifukwa cacikulu n’cakuti n’nali kudela nkhawa kuti angadzacotsedwe.” Mofanana ndi mlongo ameneyu, makolo ena amaona kuti ni bwino kuti mwana wawo asabatizike mwamsanga mpaka atakhwima n’kuleka kucita zinthu mwacibwana. (Gen. 8:21; Miy. 22:15) Iwo angakambe kuti, ‘Popeza mwana wanga akali wosabatizika, sangacotsedwe.’ Kuganiza mwanjila imeneyi n’kudzinamiza. Cifukwa ciani takamba conco?—Yak. 1:22.

13. Kodi kucedwa kubatizika kumacititsa munthu kusakhala na mlandu pa maso pa Yehova akacimwa? Fotokozani.

13 M’pomveka kuti makolo acikhristu safuna kuti mwana wawo abatizike asanafike poti n’kudzipeleka moyenela kwa Mulungu. Komabe, n’kulakwa kuganiza kuti ngati mwana sanabatizike, ndiye kuti Yehova sangamuŵelengele mlandu akacimwa. Takamba conco cifukwa cakuti kuŵelengeledwa mlandu na Yehova sikudalila pa kubatizika. Mwana akacimwa, amakhala na mlandu pamaso pa Mulungu ngati amadziŵa coyenela ndi cosayenela pamaso pa Yehova. (Ŵelengani Yakobo 4:17.) Conco, m’malo mocedwetsa mwana kubatizika, makolo anzelu amayesetsa kupeleka citsanzo cabwino kwa mwanayo. Amam’thandiza kuyambila ali wakhanda, kuti azikonda kutsatila mfundo zapamwamba za Yehova za makhalidwe abwino. (Luka 6:40) Kukhala na mtima wokonda kutsatila mfundo za Mulungu ndiye citetezo camphamvu kwa mwana, cifukwa kudzam’thandiza kusagonja potsatila njila zolungama za Yehova.—Yes. 35:8.

ENA ANGATHANDIZEKO

14. Kodi akulu angathandize bwanji makolo amene akuthandiza ana awo kupita patsogolo kuti akabatizike?

14 Monga abusa auzimu, akulu mu mpingo angathandize makolo pa nchito yophunzitsa ana awo mwa kukamba ndi anawo za ubwino wokhala na zolinga zauzimu. Mlongo wina anafotokoza mmene mau a M’bale Charles T. Russell anam’khudzila. Pa nthawiyo, mlongoyo anali na zaka 6 cabe zakubadwa. Iye anati: “M’baleyo anakambilana nane kwa mamineti 15 pa nkhani ya zolinga zanga zauzimu.” Pambuyo pake, mlongoyo anatumikila monga mpainiya kwa zaka zoposa 70. Ndithudi, kukamba mau olimbikitsa kungakhale na zotulukapo zabwino na zokhalitsa. (Miy. 25:11) Akulu angapemphenso makolo pamodzi ndi ana awo kuti agwile nchito za pa Nyumba ya Ufumu, ndipo angapatse anawo nchito mogwilizana ndi msinkhu komanso luso lawo.

15. Kodi ni njila zina ziti zimene abale na alongo mu mpingo angalimbikitsile acicepele?

15 Abale na alongo mu mpingo angalimbikitse acicepele mwa kucita zinthu zoonetsa kuti amawaona kukhala ofunika. Izi zingaphatikizepo kukhala chelu akaona zizindikilo zakuti wacicepele akupita patsogolo mwauzimu. Kodi iye caposacedwa anapeleka ndemanga yabwino komanso yocokela pansi pa mtima? Kodi anali na mbali pa msonkhano wa mkati mwa wiki? Kodi anapilila ciyeso ca cikhulupililo cake kapena analalikila ku sukulu? Wacicepele akacita zinthu ngati zimenezi, musalephele kumuyamikila mocokela pansi pa mtima. Bwanji osakhala na colinga cakuti nthawi zonse, misonkhano isanayambe kapena ikatha, muzikambako na wacicepele mmodzi, pofuna kuonetsa kuti mumamuganizila? Ngati mucita zinthu monga zimenezi, acicepele adzayamba kudzimva kuti ali mbali ya “mpingo waukulu.”—Sal. 35:18.

THANDIZANI ANA ANU KUPITA PATSOGOLO KUTI AKABATIZIKE

16, 17. (a) Kodi kubatizika kumakhudza bwanji ciyembekezo cathu ca moyo wosatha? (b) Kodi kholo lililonse lacikhristu limafuna kupeza cimwemwe cotani? (Onani pikica kuciyambi.)

16 Kulela ana “m’malangizo a Yehova ndi kuwaphunzitsa kaganizidwe kake” ni udindo umodzi waukulu umene kholo lililonse lacikhristu lili nawo. (Aef. 6:4; Sal. 127:3) Mosiyana ndi ana a mu Isiraeli wakale, ana a Mboni akabadwa sakhala mbali ya anthu odzipeleka a Yehova. Komanso, kukonda Mulungu na coonadi sikuli monga coloŵa cimene munthu amalandila kwa makolo ake. Conco, mwana akangobadwa, makolo afunika kukhala na colinga com’thandiza kuti adzakhale wophunzila wa Khristu kapena kuti mtumiki wa Yehova, wodzipeleka na wobatizika. Palibe cina cofunika kwambili kuposa kukhala mtumiki wa Mulungu. Ndipo munthu afunika kudzipeleka, kubatizika, na kupitiliza kutumikila Mulungu mokhulupilika kuti akakhale na mwayi woikiwa cizindikilo ca cipulumutso pa cisautso cacikulu cimene cikubwela.—Mat. 24:13.

Makolo afunika kukhala na colinga cothandiza mwana wawo kuti adzakhale wophunzila wa Khristu (Onani palagilafu 16, 17)

17 Pamene Blossom Brandt anapanga cosankha cakuti abatizike, makolo ake acikhristu anafuna kutsimikizila kuti anali wokonzekadi kutenga sitepi yofunika kwambili imeneyi. Ataona kuti ni wokonzeka, anamulimbikitsa kucita zimenezo. Madzulo a tsiku lakuti maŵa Blossom adzabatizika, atate ake anacita cinthu cinacake cocititsa cidwi. Blossom anati: “Tonse anatiuza kuti tigwade. Kenako anapeleka pemphelo. Iwo anauza Yehova kuti akondwela ngako kuti ine mwana wawo wamng’ono nasankha kupeleka moyo wanga kwa iye.” Patapita zaka zoposa 60, Blossom anati: “Kukamba zoona, sinidzaiŵala zimene zinacitika nthawi imeneyo!” Inu makolo, yesetsani kuthandiza ana anu mwauzimu kuti mupeze cimwemwe cimene cimabwela pamene ana asankha kukhala atumiki a Yehova odzipeleka na obatizika.

^ par. 9 Makolo pamodzi ndi mwana wawo angaŵelenge buku lakuti Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa—Buku Lachiwiri, peji 304 mpaka 310. Onaninso “Bokosi la Mafunso” mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa April 2011, peji 2.