Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kucelezana ni Khalidwe Lofunika Kwambili!

Kucelezana ni Khalidwe Lofunika Kwambili!

“Muzicelezana popanda kudandaula.” —1 PET. 4:9.

NYIMBO: 100, 87

1. Ni mavuto anji amene Akhristu a m’nthawi ya Atumwi anakumana nawo?

CAPAKATI pa 62 na 64 C.E., mtumwi Petulo analembela kalata ‘alendo osakhalitsa, amene anali atamwazikana ku Ponto, Galatiya, Kapadokiya, Asia, ndi ku Bituniya.’ (1 Pet. 1:1) Abale na alongo a m’mipingo ya m’madela amenewa anali a zikhalidwe zosiyana-siyana. Akhristuwo anali kufunikila cilimbikitso na citsogozo cifukwa anthu anali kuwatsutsa na kuwanyoza. Iwo anakumana na ziyeso zoopsa ngati “moto.” Komanso anali kukhala m’nthawi yapadela. Petulo anawauza kuti “mapeto a zinthu zonse ayandikila”. Inde, panali patangotsala zaka zocepa cabe kuti mzinda wa Yerusalemu uwonongedwe momvetsa cisoni. Kodi n’ciani cikanathandiza Akhristuwo kupilila m’nthawi zovuta zimenezo?—1 Pet. 4:4, 7, 12.

2, 3. N’cifukwa ciani Petulo analimbikitsa Akhristu anzake kuti azicelezana? (Onani pikica pamwambapa.)

2 Cimodzi mwa zinthu zimene zikanawathandiza ni kukhala oceleza. Petulo anawauza kuti “muzicelezana popanda kudandaula.” (1 Pet. 4:9) Liu la Cigiriki lomasulidwa kuti “kuceleza” limatanthauza “kukonda alendo kapena kuwakomela mtima.” Komabe, onani kuti Petulo anauza Akhristu anzake kuti “muzicelezana.” Apa, iye anali kuwalimbikitsa kuti aziceleza Akhristu anzawo. Kodi kukhala oceleza kukanawathandiza bwanji?

3 Kukanawathandiza kuti akhale ogwilizana ngako. Kodi munakhalapo na mwayi woitanidwa ku nyumba kwa munthu wina kuti mukaceze? Kodi imeneyo siinali nthawi yosangalatsa kwa inu? Nanga bwanji pamene munaceleza abale na alongo ena a mu mpingo mwanu, kodi ubwenzi wanu na iwo sunalimbe? Tikamaceleza abale na alongo athu, timawadziŵa bwino kuposa mmene tingawadziŵile m’zocitika zina. Akhristu a m’nthawi ya Petulo anafunika kukhala ogwilizana pamene zinthu zinali kuipilaipila. N’cimodzimodzinso kwa ise Akhristu “masiku otsiliza” ano.—2 Tim. 3:1.

4. Kodi tidzakambilana mafunso ati m’nkhani ino?

4 Kodi tili na mipata iti ‘yoceleza’ ena? Tingagonjetse bwanji zopinga zimene zingatilepheletse kukhala oceleza? Nanga n’ciani cingatithandize kukhala alendo abwino?

MIPATA YOCELEZA ENA IMENE TILI NAYO

5. Pa misonkhano yathu, tingaonetse bwanji kuti ndise oceleza?

5 Pa misonkhano: Anthu onse amene amabwela ku misonkhano yathu, timawalandila monga alendo anzathu amene abwela kudzadya nase cakudya cauzimu. Yehova na gulu lake ndiwo amatiitana ku phwando lauzimu limeneli. (Aroma 15:7) Koma ku misonkhano kukabwela acatsopano, na ise timakhala m’gulu la olandila alendo. Conco kukabwela alendo, tiyenela kuwalandila, mosasamala kanthu za maonekedwe kapena kavalidwe kawo. (Yak. 2:1-4) Ngati mlendo alibe wina amene akumusamalila, bwanji osamupempha kuti akhale namwe pafupi? Iye angayamikile kwambili ngati mum’thandiza kutsatila bwino pulogilamu na kupeza malemba amene akuŵelengedwa. Kucita izi ni njila yabwino yoonetsela kuti ndise “oceleza.”—Aroma 12:13.

6. Kodi n’ndani amene tifunika kuwaonetsa kwambili mzimu woceleza?

6 Kuitanila ena ku cakudya: M’nthawi zakale, kaŵili-kaŵili anthu anali kuceleza anzawo mwa kuwaitanila ku nyumba kwawo kuti akadye nawo cakudya. (Gen. 18:1-8; Ower. 13:15; Luka 24:28-30) Kuitanila munthu ku cakudya kunali ngati kumupempha kuti ukhale naye pa ubwenzi ndiponso pamtendele. Kodi n’ndani amene tifunika kuwaonetsa kwambili mzimu woceleza? Ni abale na alongo athu mu mpingo. Abale na alongo athu amenewa ni amene adzatithandiza pa nthawi ya mavuto. Conco, tifunika kukhala pa mtendele na Akhristu onse ndiponso kukhala nawo pa ubwenzi wolimba. N’zocititsa cidwi kuti mu 2011, Bungwe Lolamulila linasintha nthawi imene atumiki a pa Beteli ku United States anali kuyamba kucita Phunzilo la Nsanja ya Mlonda, kucoka pa 18:45hrs kubwela pa 18:15hrs. N’cifukwa ciani anasintha? Cilengezo cimene cinapelekedwa pa nthawiyo cinakamba kuti kusinthako kudzathandiza atumiki a pa Beteli kuti azikhala na mpata wocelezana pambuyo pa phunzilolo. Maofesi a nthambi m’maiko ena anacitanso cimodzi-modzi. Kusintha kumeneku kwathandiza mabanja a Beteli kukhala ogwilizana kwambili.

7, 8. Tingaonetse bwanji mzimu woceleza kwa alendo odzakamba nkhani mu mpingo mwathu na alendo ena oimilako gulu la Yehova?

7 Ngati tikucezeledwa na oyang’anila dela, abale ocokela ku mipingo ina kudzakamba nkhani, kapena oimila ofesi ya nthambi, timakhala na mwayi wowaceleza. (Ŵelengani 3 Yohane 5-8.) Njila imodzi imene tingawacelezele ndi mwa kuwaitanila ku cakudya. Bwanji osacitako zimenezi?

8 Mlongo wina wa ku United States anati: “Kwa zaka zambili, ine na mwamuna wanga takhala tikuceleza abale obwela kudzakamba nkhani mu mpingo mwathu pamodzi na akazi awo. Nthawi zonse tikacita zimenezi, timakhala osangalala ngako, ndipo koposa zonse, timalimbikitsidwa mwauzimu. Sitiona ngati kuti timangotaya nthawi yathu.”

9, 10. (a) N’ndani angafunike kucelezedwa kwa nthawi yaitali? (b) Kodi Akhristu amene ali na nyumba zosaukila angapeleke malo awo kwa alendo? Fotokozani.

9 Alendo okhalitsa: M’nthawi zakale, kuceleza kunali kuphatikizapo kukonzela alendo malo ogona. (Yobu 31:32; Filim. 22) Masiku anonso, kucita zimenezi kungakhale kofunika. Mwacitsanzo, nthawi zambili, oyang’anila dela amafunikila malo okhala pamene akucezela mpingo. Oloŵa masukulu ophunzitsa Baibo komanso atumiki odzipeleka amene amagwila nchito yomanga malo olambilila, nawonso angafunike malo okhala. Nthawi zinanso, ena nyumba zawo zingawonongeke cifukwa ca tsoka la zacilengedwe, ndipo angafunikile malo okhala mpaka nyumba zawozo zitakonzedwanso. Sitifunika kuganiza kuti okhawo amene ali na nyumba zapamwamba ndiwo ayenela kuthandiza, cifukwa iwo angakhale kuti anacitapo kale zimenezi nthawi zambili. Na imwe mungathandizeko olo kuti nyumba yanu ni yosaukila.

10 M’bale wina wa ku South Korea amasangalala akakumbukila nthawi imene anali kulandila abale na alongo oloŵa masukulu ophunzitsa Baibo. Iye analemba kuti: “Poyamba n’nali kuyopa kulandila alendo cifukwa tinali titangokwatilana kumene, ndipo tinali kukhala m’nyumba yaing’ono. Koma tinakondwela ngako kukhala na abale na alongo amenewo. Monga okwatilana kumene, tinaona cimwemwe cimene anthu amakhala naco ngati akutumikila Yehova mogwilizana na kuyesetsa kukwanilitsa zolinga zawo zauzimu pamodzi.”

11. N’cifukwa ciani tifunika kuceleza ofalitsa amene akukila mu mpingo mwathu?

11 Amene akukila mu mpingo mwanu: Akhristu ena angakukile m’dela lanu. Ena angabwele monga otumikila kosoŵa. Komanso, ena angakhale apainiya amene atumizidwa kuti adzacilikize mpingo wanu. Onse amenewa, poyamba sakhala omasuka, amacita cilendo. Amakhala kuti sanajaile kukhala m’dela latsopano ndi mu mpingo watsopano. Angakhalenso kuti sadziŵa citundu kapena cikhalidwe ca kwanuko. Conco, mungawaitanileko ku nyumba kwanu kuti mudzadye nawo cakudya, kapena mungawapemphe kuti mukayende nawo kwina kwake. Kucita izi kudzawathandiza kupeza mabwenzi atsopano na kujaila umoyo wa m’delalo.

12. Fotokozani citsanzo cimene cionetsa kuti kuceleza sikulila kukhala na zinthu zambili.

12 Kuceleza sikulila kukhala na zinthu zambili. (Ŵelengani Luka 10:41, 42.) Pofotokoza mmene zinthu zinalili pamene anayamba utumiki wa umishonale, m’bale wina anati: “Tinali acicepele osadziŵa zambili, ndipo tinali kuyewa ku nyumba. Tsiku lina, mkazi wanga anayewa kwambili ku nyumba. N’nayesetsa kumulimbikitsa, koma sizinathandize. Ndiyeno, ca m’ma 19:30hrs tinamva kugogoda pakhomo. Titatsegula, tinaona kuti amene anali kugogoda ni wophunzila Baibo, ndipo anatibweletsela maolenji atatu. Iye anabwela kudzationa. Tinamuuza kuti aloŵe, ndipo tinamupatsa madzi akumwa. Kenako, tinamupangila tiyi na cokoleti. Pa nthawiyo tinali tikalibe kudziŵa Ciswahili, ndipo nayenso sanali kudziŵa Cizungu. Koma cocitika cimeneci n’cimene cinatsegula mwayi wakuti tiyambe kupeza mabwenzi pakati pa abale a m’delalo.”

MMENE TINGAGONJETSELE ZOPINGA ZIMENE ZINGATILEPHELETSE KUKHALA OCELEZA

13. Ni mapindu anji amene timapeza tikakhala oceleza?

13 Kodi munalephelapo kuceleza anthu ena cifukwa codela nkhawa zinthu zina? Ngati n’conco, ndiye kuti munataya mwayi wa maceza okondweletsa ndi wopeza mabwenzi okhalitsa. Kukhala woceleza ni mankhwala amphamvu othetsela vuto la kusungulumwa. Koma mwina mungafunse kuti, ‘N’cifukwa ciani ena amaopa kuceleza anzawo?’ Pali zifukwa zingapo.

14. N’ciani cimene tingacite ngati kulema na kutangwanika kumatilepheletsa kuceleza ena kapena kukaceza kwa Akhristu anzathu?

14 Kutangwanika na kulema: Atumiki a Yehova amakhala otangwanika nthawi zambili. Akhristu ena amaona kuti sangakwanitse kuceleza alendo cifukwa kaŵilikaŵili amakhala otangwanika na olema. Ngati umu ni mmene zinthu zilili mu umoyo wanu, mungafunike kupendanso bwino ndandanda ya zimene mumacita. Kodi mungasintheko zinthu zina n’colinga cakuti mukhale na nthawi yoceleza ena kapena yokaceza kwa Akhristu amene akuitanilani ku nyumba kwawo? Malemba amatilimbikitsa kuti tifunika kukhala oceleza. (Aheb. 13:2) Kupatula nthawi yoceleza ena si kutaya nthawi, ndipo n’kofunika ngako. Kuti mucite zimenezi, mwina mungafunike kucepetsa zinthu zina zosafunika kweni-kweni zimene mumacita.

15. Kodi ena amaopa kuceleza alendo pa zifukwa ziti?

15 Kudzikayikila: Kodi mumafuna kukhala oceleza, koma mumadzikayikila? Ena ni amanyazi ndipo amaopa kuti akaitana munthu ku nyumba kwawo adzasoŵa nkhani zoceza naye. Akhristu ena ni osauka, ndipo amaona kuti sangakwanitse kupatsa alendo zakudya zabwino monga zimene ena amapatsa alendo. Koma kumbukilani kuti cofunika ngako si kukhala na zinthu zapamwamba pa nyumba. Kumbukilani kuti cofunika kwambili si cakuti nyumba ikhale yapamwamba, koma pa nyumba pafunika kukhala padongosolo, paukhondo, ndi pooneka bwino.

16, 17. N’ciani cingakulimbikitseni ngati mumaopa kuceleza alendo?

16 Ngati mumaopa kuceleza alendo, dziŵani kuti si ndinu nokha. Mkulu wina wa ku Britain anati: “Nthawi zina, munthu angakhale na nkhawa pamene akukonzekela kulandila alendo. Koma molingana na zinthu zina zimene timacita potumikila Yehova, kuceleza ena kumatibweletsela mapindu na cimwemwe coculuka. Ine nthawi zina nimamwa cabe khofi na alendo, kwinaku tikuceza.” Kumbukilani kuti kuonetsa cidwi kwa alendo n’kothandiza nthawi zonse. (Afil. 2:4) Pafupi-fupi aliyense amakondwela kuuzako anzake zokhudza umoyo wake. Kambili, pa maceza aconco m’pamene ena amakhala omasuka kutifunsa zokhudza umoyo wathu. Mkulu winanso analemba kuti: “Kuceza na abale a mu mpingo mwathu ku nyumba kwanga kumanipatsa mwayi wowadziŵa bwino, maka-maka kudziŵa mmene anaphunzilila coonadi.” Ndithudi, kuonetsa cidwi kwa alendo kumathandiza kuti maceza akhale okondweletsa.

17 Mlongo wina amene ni mpainiya anacelezapo abale na alongo oloŵa masukulu ophunzitsa Baibo. Iye anati: “Poyamba n’nali kuyopa kulandila alendo cifukwa nyumba yanga ni yosaukila ndipo muli mipando yakale imene ena ananipatsa. Koma mkazi wa mmodzi wa alangizi a sukuluzi ananilimbikitsa ngako. Anakamba kuti pamene iye na mwamuna wake akutumikila m’dela, amakondwela kwambili akapita kukaceza kwa munthu wauzimu, olo wosauka, amene ali na umoyo wosalila zambili, ndipo amaika mtima wake wonse pa kutumikila Yehova. Izi zinanikumbutsa zimene amayi anali kutiuza pamene tinali ana. Anali kukamba kuti ‘Ni bwino kudya zamasamba pamene pali cikondi.’” (Miy. 15:17) Conco, musamaope kuceleza ena cifukwa cofunika ngako ni kuwaonetsa cikondi.

18, 19. Kodi kukhala oceleza kungatithandize bwanji kuthetsa maganizo oipa amene tingakhale nawo okhudza anthu ena?

18 Mmene mumaonela ena: Kodi mu mpingo mwanu muli wina amene zocita zake sizikukondweletsani? Ngati simungacitepo kanthu, ndiye kuti maganizo olakwika amene muli nawo okhudza munthuyo siyangasile. Nthawi zina, kusiyana kwa zibadwa kungacititse kuti tisakhale omasuka kuceleza anthu ena. Komanso n’kutheka kuti munthu wina anatikhumudwitsa m’mbuyomo, koma tikulephela kuiŵalako colakwaco.

19 Kuti tikhale pa unansi wabwino ndi ena, ngakhale adani athu, Baibo imatilimbikitsa kukhala oceleza. (Ŵelengani Miyambo 25:21, 22.) Kuceleza munthu kungacepetse vuto la kukwesana ndi kuthetsa maganizo oipa amene mungakhale nawo okhudza munthuyo. Kungakupatseni mwayi woona makhalidwe ake abwino, amenenso Yehova anaona pamene anamukokela m’coonadi. (Yoh. 6:44) Ngati muceleza munthu cifukwa comukonda, ubwenzi wanu na iye umalimba. Mungacite ciani kuti cikondi cizikusonkhezelani kuceleza ena? Cimodzi cimene mungacite ni kulabadila malangizo a pa Afilipi 2:3, pamene pamatilimbikitsa kukhala ‘odzicepetsa, ndi kuona ena kukhala otiposa.’ Conco, tifunika kumaganizila zinthu zimene abale na alongo athu amacita bwino kuposa ise. N’kutheka kuti ali na cikhulupililo colimba, ni opilila, opanda mantha, kapena ali na makhalidwe enanso abwino. Kuganizila zimenezi kudzacititsa kuti tiziwakonda kwambili, ndipo kudzatilimbikitsa kuwaceleza na mtima wonse.

KUKHALA MLENDO WABWINO

Nthawi zambili, anthu amene aitana alendo amakonzekela bwino (Onani palagilafu 20)

20. N’cifukwa ciani tifunika kuonetsa ulemu ngati tavomela kukaceza ku nyumba kwa wina wake? Nanga tingacite bwanji zimenezi?

20 Wamasalimo Davide anafunsa kuti: “Inu Yehova, ndani amene angakhale mlendo m’cihema canu?” (Sal. 15:1) Davide anayankha funsoli mwa kuchula makhalidwe abwino amene Mulungu amafuna kuti alendo ake akhale nawo. Limodzi mwa makhalidwe amene anachula ni kusunga malonjezo. Iye anati: “Akalumbila kucita zinthu zimene kenako zakhala zoipa kwa iye, sasintha malingalilo ake.” (Sal. 15:4) Ngati tavomela kukaceza ku nyumba kwa wina wake, sitifunika kusintha maganizo popanda zifukwa zomveka. Munthu amene anatiitana angakhale kuti wakonzekela kale zambili, ndipo tingamuonongetse zinthu zambili ngati tasintha maganizo. (Mat. 5:37) Ena akavomela ciitano kwa wina, amasintha maganizo akalandila ciitano cina cocokela kwa munthu amene aona kuti ali na zinthu zapamwamba. Kucita izi n’kupanda cikondi komanso n’kusowa ulemu. Conco, tifunika kuvomela ciitano na mtima wonse na kuyamikila zilizonse zimene otiitanawo atikonzela. (Luka 10:7) Koma ngati taona kuti sitidzapita pa zifukwa zina zomveka, tingaonetse kuti timawakonda na kuwaganizila amene anatiitanawo mwa kuwadziŵitsa mwamsanga za kusinthako.

21. Kodi kulemekeza cikhalidwe ca kumene tikhala kungathandize bwanji kuti tikhale alendo abwino?

21 Cinanso, ni bwino kulemekeza cikhalidwe ca kwanuko. M’zikhalidwe zina, alendo amene sanaitanidwe amalandilidwa. Koma m’zikhalidwe zina, anthu amayamikila ngati alendo akambilatu kuti adzabwela kudzawacezela. M’madela ena, eni nyumba amalemekeza alendo mwa kuwapatsa zakudya zabwino kwambili kuposa zimene iwo amadya. Koma m’madela ena, alendo komanso eni ake nyumba, onse amadya zakudya zolingana. M’zikhalidwe zinanso, alendo amatengako mphatso popita kukaceza. Koma m’zikhalidwe zina olandila alendo amaona kuti ni bwino kuti alendowo asabwele na mphatso iliyonse. Komanso, m’zikhalidwe zina, munthu amayembekezeledwa kukana mwaulemu akaitanidwa koyamba, ngakhale kaciŵili. Koma m’zikhalidwe zina, kukana ciitano kumaoneka monga n’kusayamikila. Conco, tiyenela kucita zilizonse zimene tingathe kuti tikondweletse amene atiitana.

22. N’cifukwa ciani ‘kucelezana’ n’kofunika ngako?

22 Koposa kale lonse, “mapeto a zinthu zonse ayandikila” kwambili. (1 Pet. 4:7) Tatsala pang’ono kukumana na cisautso cacikulu cimene sicinacitikepo pa dzikoli. Pamene mavuto akuculukila-culukila, tifunika kulimbitsa kwambili cikondi cathu pa abale na alongo athu. Kuposa kale lonse, ino ndiyo nthawi yofunika kumvela malangizo a Petulo akuti: “Muzicelezana popanda kudandaula.” Limeneli ni khalidwe lokondweletsa komanso lofunika limene silidzatha.—1 Pet. 4:9.