Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

“Mvelani Malangizo Kuti Mukhale Anzelu”

“Mvelani Malangizo Kuti Mukhale Anzelu”

“Ananu, . . . mvelani malangizo kuti mukhale anzelu.” —MIY. 8:32, 33.

NYIMBO: 56, 89

1. Kodi nzelu zocokela kwa Mulungu timazipeza bwanji? Nanga zimatipindulitsa bwanji?

YEHOVA ndiye Gwelo la nzelu, ndipo amagaŵilako ena nzelu zake mowoloŵa manja. Yakobo 1:5 imati: “Ngati wina akusoŵa nzelu, azipempha kwa Mulungu, ndipo adzamupatsa, popeza iye amapeleka mowoloŵa manja kwa onse ndiponso amapeleka mosatonza.” Njila imodzi imene timapezela nzelu zocokela kwa Mulungu ni mwa kulandila cilango cake. Ndipo nzelu zimenezi zimatiteteza ku makhalidwe oipa komanso ku zinthu zina zimene zingatiwononge mwauzimu. (Miy. 2:10-12) Mwa ici, timakhalabe m’cikondi ca Mulungu, tili na ciyembekezo ‘cokalandila moyo wosatha.’—Yuda 21.

2. Tingacite ciani kuti tione phindu la cilango cocokela kwa Mulungu?

2 Komabe, cifukwa ca kupanda ungwilo, mmene tinaleledwela, na zifukwa zina, nthawi zina cimativuta kulandila cilango kapena kuciona moyenela. Timayamba kuyamikila cilango ngati taona mapindu ake. Ndipo mapindu amene timapeza amaonetsa kuti Mulungu amatikonda. Miyambo 3:11, 12 imati: “Mwana wanga, usakane malangizo a Yehova, . . . cifukwa Yehova amadzudzula munthu amene amam’konda.” Inde, tisaiŵale kuti Yehova amatifunila zabwino. (Ŵelengani Aheberi 12:5-11.) Popeza Mulungu amatidziŵa bwino kwambili, cilango cake nthawi zonse cimakhala coyenelela ndiponso cofunikila. Lomba tiyeni tikambilane mbali zinayi izi zokhudza cilango: (1) kudzilanga wekha, (2) cilango ca makolo, (3) cilango ca mu mpingo, ndi (4) cinacake coŵaŵa kuposa ululu wa cilango.

KUDZILANGA WEKHA KUMAONETSA KUTI ULI NA NZELU

3. Kodi mwana angaphunzile bwanji kudzilanga yekha? Fotokozani fanizo.

3 Kudzilanga wekha kumaphatikizapo kudziletsa ku zinthu zina pofuna kuwongolela khalidwe lathu na maganizo athu. Mwacibadwa, ise anthu sitifuna kudzilanga tekha. Timacita kuphunzila khalidwe limeneli. Tiyelekezele motele: Mwana akayamba kuphunzila kuyendetsa njinga, kholo lake limagwilila njingayo kuti asagwe. Koma mwanayo akayamba kudziŵa, kholo mosamala limayamba kumutailila pang’ono-pang’ono. Limalekelatu kugwilila njingayo ngati mwanayo wadziŵa kuyendetsa. Mofananamo, ngati moleza mtima na mosalekeza makolo aphunzitsa ana awo ‘malangizo a Yehova ndi kaganizidwe kake,’ amawathandiza kukhala odzilanga okha ndi anzelu.—Aef. 6:4.

4, 5. (a) N’cifukwa ciani kudzilanga wekha ni mbali yofunika kwambili ya “umunthu watsopano”? (b) N’cifukwa ciani sitiyenela kutaya mtima ngati tacita colakwa mobweleza-bweleza?

4 Umu ni mmenenso zimakhalila na anthu amene aphunzila za Yehova ali aakulu kale. N’zoona kuti pa mlingo wina wake, iwo amakhala ataphunzila kale kudzilanga okha. Komabe, wophunzila watsopano aliyense wa Khristu amakhala wosakhwima mwauzimu. Koma pang’ono-m’pang’ono, iye amakula mwauzimu pamene akuphunzila kuvala “umunthu watsopano” wofanana ndi wa Khristu. (Aef. 4:23, 24) Kudzilanga wekha ni mbali yofunika kwambili ya umunthu watsopano. Kumatithandiza “kukana moyo wosaopa Mulungu ndi zilakolako za dziko, koma kukhala amaganizo abwino, acilungamo ndi odzipeleka kwa Mulungu m’nthawi ino.”—Tito 2:12.

5 Komabe, tonse timalakwa kaŵili-kaŵili. (Mlal. 7:20) Olo n’conco, tikalakwa sitiyenela kudziona monga olephelelatu kapena osatha kudzilanga tekha ngakhale pang’ono. Miyambo 24:16 imati: “Wolungama akhoza kugwa ngakhale nthawi 7 ndipo ndithu adzadzukanso.” Kodi n’ciani cingatithandize ngati tagwa? Osati mphamvu zathu cabe, koma mzimu wa Mulungu. (Ŵelengani Afilipi 4:13.) Cipatso ca mzimu umenewu cimaphatikizapo khalidwe la kudziletsa, limene n’logwilizana kwambili na kudzilanga tekha.

6. Tingacite ciani kuti tizikonda kuŵelenga Mau a Mulungu? (Onani pikica kuciyambi.)

6 Zinthu zina zimene zingatithandize kukhala odzilanga tekha ni kupemphela mocokela pansi pa mtima, kuŵelenga Baibo, na kusinkha-sinkha. Koma bwanji ngati mumaona kuti kuŵelenga Mau a Mulungu n’kovuta? Mwina zoŵelenga simuzikonda kweni-kweni. Ngati n’conco, dziŵani kuti Yehova angakuthandizeni ngati mumulola kutelo. Angakuthandizeni kukhala na ‘cilakolako’ cophunzila Mau ake. (1 Pet. 2:2) Coyamba, pemphani Yehova kuti akuthandizeni kukhala odzilanga nokha n’colinga cakuti muzipeza nthawi yophunzila Mau ake. Ndiyeno, yesetsani kucita zinthu mogwilizana na mapemphelo anu, mwina mwa kucepetsako utali wa nthawi yophunzila. M’kupita kwa nthawi, mudzaona kuŵelenga Baibo kukhala kosavuta na kokondweletsa. Ndithudi, ngati musinkha-sinkha mozama zimene mumaŵelenga m’Mau a Yehova amtengo wapatali, mudzayamba kukondwela pophunzila.—1 Tim. 4:15.

7. Kodi kudzilanga tekha kungatithandize bwanji kukwanilitsa colinga cauzimu?

7 Kudzilanga tekha kumatithandiza kukwanilitsa zolinga zauzimu. Mwacitsanzo, ganizilani za m’bale wina wa pabanja amene anaona kuti cangu cake pa nchito yolalikila cayamba kucepa. Atazindikila vutoli, anadziikila colinga cokhala mpainiya wa nthawi zonse, ndipo anayamba kuŵelenga nkhani za m’magazini athu zokhudza utumikiwu. Kucita izi komanso kupemphela, kunamuthandiza kukhala wolimba mwauzimu. Anakonzanso zakuti nthawi zina azicitako upainiya wothandiza. Kodi panakhala zotulukapo zotani? Ngakhale kuti panali zopinga zina, iye sanalole zimenezo kumulepheletsa kukwanilitsa colinga cake cokhala mpainiya wa nthawi zonse, ndipo m’kupita kwa nthawi anacikwanilitsadi.

MUZILELA ANA ANU M’MALANGIZO A YEHOVA

Ana sabadwa na nzelu zosiyanitsa cabwino na coipa. Amafunika kuphunzitsidwa (Onani palagilafu 8)

8-10. N’ciani cingathandize makolo acikhristu kuti akwanitse kuphunzitsa ana awo kukhala atumiki a Yehova? Fotokozani citsanzo.

8 Makolo acikhristu ali na udindo waukulu wolela ana awo “m’malangizo a Yehova ndi kuwaphunzitsa kaganizidwe kake.” (Aef. 6:4) Umenewu ni udindo wovuta, maka-maka masiku ano. (2 Tim. 3:1-5) Ana sabadwa na nzelu zosiyanitsa cabwino na coipa. N’zoona kuti amabadwa na cikumbumtima, koma cimafunika kuphunzitsidwa. (Aroma 2:14, 15) Buku lina lofotokoza Baibo limati liu la Cigiriki lomasulidwa kuti “malangizo” lingatanthauzenso “kulela bwino mwana.”

9 Ana amene amalangiwa mwacikondi, nthawi zambili amadzimva kukhala otetezeka. Amaphunzila kuti ufulu uli na malile, na kuti khalidwe lathu na zosankha zathu zimakhala na zotulukapo, kaya zoipa kapena zabwino. Conco, imwe makolo mufunika kumadalila malangizo a Yehova pophunzitsa ana anu. Musaiŵale kuti nzelu za anthu na njila zawo zolelela ana zimasiyana-siyana malinga ndi cikhalidwe ndiponso zimasintha m’kupita kwa nthawi. Koma ngati mudalila malangizo a Mulungu, m’malo modalila cidziŵitso canu kapena nzelu zanu, mudzakwanitsa kulela bwino ana.

10 Ganizilani citsanzo ca Nowa. Pamene Yehova anam’lamula kuti amange cingalawa, Nowa sanadalile luso lake. Iye anali asanamangepo cingalawa. Conco, anadalila Yehova. Baibo imati iye “anacitadi momwemo,” kutanthauza kuti anatsatila malangizo a Yehova. (Gen. 6:22) Kodi zotulukapo zake zinali zotani? Anakwanitsa kumanga bwino cingalawa olo kuti kunali kuyamba. Komanso, Nowa anakwanitsa kusamalila udindo wake monga mutu wa banja cifukwa codalilanso nzelu za Mulungu. Iye anakwanitsa kuphunzitsa bwino ana ake na kuwapatsa citsanzo cabwino, olo kuti kucita zimenezo kunali kovuta ngako m’masiku oipa amenewo Cigumula cisanacitike.—Gen. 6:5.

11. N’cifukwa ciani citsanzo ca makolo n’cofunika ngako pophunzitsa mwana?

11 Makolo, mungatengele bwanji citsanzo ca Nowa? Muzimvela Yehova. Muloleni kuti akuphunzitseni kulela bwino ana anu. Muziseŵenzetsa malangizo amene iye amapeleka kupitila m’Mau ake na gulu lake. M’kupita kwa nthawi, ana anu adzayamikila kwambili zimene mumawaphunzitsa. M’bale wina anati, “Nimayamikila ngako kuti makolo anga ananilela bwino. Iwo anali kuyesetsa kuniphunzitsa monifika pamtima. Niona kuti cinthu cikulu cimene cacititsa kuti nipite patsogolo mwauzimu ni mmene n’naleledwela.” Komabe, olo kuti makolo amayesetsa kuphunzitsa ana awo, ana ena amam’siya Yehova. Ngakhale n’conco, ngati makolo ayesetsa kukhomeleza coonadi mu mtima mwa mwana wawo, safunika kudziimba mlandu ngati mwanayo wapanduka. Ndipo ayenela kukhala na ciyembekezo cakuti tsiku lina mwana wosocelayo “adzabwelela” kwa Yehova.

12, 13. (a) Ngati mwana wacotsedwa, kodi makolo acikhristu angaonetse bwanji kuti amamvela Mulungu? (b) Kodi banja lina linapindula bwanji pamene makolo a m’banjalo anamvela Yehova?

12 Ciyeso cimodzi covuta kwambili cimene makolo ena akumana naco n’cokhudza kuyanjana na mwana wocotsedwa. Ganizilani za mlongo wina amene mwana wake wamkazi anacotsedwa na kucoka pa nyumba. Mlongoyo anati: “N’nali kusakila mfundo zina m’zofalitsa zathu zimene n’nali kuona monga zinganipatse ufulu woceza na mwana wanga komanso mdzukulu wathu.” Kenako anati: “Koma amuna anga mokoma mtima ananithandiza kuona kuti mwana wathu salinso m’manja mwathu, ndi kuti sitifunika kulepheletsa cilango ca Mulungu kugwila bwino nchito.”

13 Patapita zaka, mwanayo anabwezeletsedwa. Amayi ake anati: “Lomba amanitumila foni kapena kunilembela meseji pafupi-fupi tsiku lililonse. Ndipo ise makolo ake amatilemekeza cifukwa amadziŵa kuti tinamvela Mulungu. Timagwilizana ngako tsopano.” Ngati muli na mwana wocotsedwa, kodi mudzakhulupilila Yehova na mtima wanu wonse, na kupewa kudalila luso lanu lomvetsa zinthu? (Miy. 3:5, 6) Musaiŵale kuti cilango ca Yehova cimaonetsa cikondi cake na nzelu zake zopanda malile. Musaiŵalenso kuti iye anapeleka Mwana wake kaamba ka anthu onse, kuphatikizapo mwana wanu. Mulungu safuna kuti wina aliyense akaonongeke. (Ŵelengani 2 Petulo 3:9.) Conco, inu makolo muzikhulupilila kuti cilango ca Yehova na malangizo ake n’zoyenela olo cikhale covuta kwa inu kucita zimene iye walamula. Inde, muzicilikiza cilango ca Mulungu osati kucita zinthu motsutsana naco.

MU MPINGO

14. Timapindula bwanji na malangizo amene Yehova amapeleka kupitila mwa “mtumiki woyang’anila nyumba wokhulupilika”?

14 Yehova amasamalila, kuteteza, na kulangiza mpingo wacikhristu. Amacita izi m’njila zingapo. Mwacitsanzo, wapatsa Mwana wake udindo woyang’anila mpingo, ndipo Mwanayo anasankha “mtumiki woyang’anila nyumba wokhulupilika” kuti azipeleka cakudya cauzimu pa nthawi yoyenela. (Luka 12:42) Amatipatsa cakudya cimeneci kupitila m’zofalitsa zosiyanasiyana zokhala na malangizo othandiza kapena cilango. Motelo mungadzifunse kuti, ‘N’kangati pamene nkhani zokambiwa pa msonkhano kapena zolembewa m’magazini athu zinanilimbikitsa kusintha maganizo kapena khalidwe langa?’ Ngati munalabadila malangizowo na kusintha, muyenela kukondwela. Ndiye kuti mukulola Yehova kukuumbani na kukulangani kuti mupindule.—Miy. 2:1-5.

15, 16. (a) Tingacite ciani kuti tipindule na “mphatso za amuna” mu mpingo? (b) N’ciani cimene tiyenela kucita kuti akulu azikondwela na utumiki wawo?

15 Cinanso, Khristu anapeleka “mphatso za amuna” ku mipingo, kutanthauza akulu kuti aziŵeta nkhosa za Mulungu. (Aef.4:8, 11-13) Tingacite ciani kuti tipindule na mphatso zimenezi? Coyamba, tifunika kutengela cikhulupililo ca akulu na citsanzo cawo cabwino. Cina, tiyenela kumvela malangizo awo ocokela m’Malemba. (Ŵelengani Aheberi 13:7, 17.) Kumbukilani kuti akulu amatikonda ndipo amafuna kuti tikule mwauzimu. Mwacitsanzo, akaona kuti timaphonya misonkhano kapena cangu cathu mu ulaliki cayamba kuzilala, amatithandiza mwamsanga. Amatimvetsela, kutilimbikitsa, na kutipatsa uphungu woyenela wa m’Malemba. Kodi mumaona thandizo limeneli kukhala umboni wa cikondi ca Yehova pa imwe?

16 Nthawi zina, akulu angaone kuti n’zovuta kutifikila kuti atipatse uphungu umene tikufunikila. Mwacitsanzo, ganizilani mmene mneneli Natani anamvelela pamene anapita kukakamba na Mfumu Davide za chimo lake lalikulu limene anayesa kulibisa. (2 Sam. 12:1-14) Nayenso mtumwi Paulo anafunika kulimba mtima kuti apeleke uphungu kwa Petulo, mmodzi wa atumwi 12, pamene anaonetsa khalidwe lokondela abale ake Aciyuda. (Agal. 2:11-14) Nanga imwe mungawapeputsileko bwanji akulu udindo wawo wopeleka uphungu? Khalani odzicepetsa, ofikilika, na oyamikila. Muziona thandizo lawo monga umboni wa cikondi ca Mulungu pa imwe. Mukacita conco, mudzapindula komanso mudzacititsa kuti akulu azikondwela na utumiki wawo.

17. Kodi mlongo wina anapindula bwanji atathandiziwa mwacikondi na akulu?

17 Cifukwa ca zimene zinamucitikila m’mbuyomo, mlongo wina anali kuona kuti n’zovuta kukonda Yehova. Iye anati: “Nthawi ina, n’navutika ngako na nkhawa cifukwa coganizila zimene zinanicitikila kale komanso mavuto ena. Conco, n’naona kuti nifunika kuuzako akulu. Iwo sananikalipile kapena kunidzudzula, koma ananilimbikitsa. Ndipo nthawi zonse pambuyo pa misonkhano, akulu anali kunifunsako za umoyo wanga olo pamene anali otangwanika kwambili. Cifukwa ca zimene zinanicitikila m’mbuyomo, n’nali kuona kuti Mulungu sanganikonde. Komabe, nthawi na nthawi, Yehova anali kuseŵenzetsa mpingo na akulu ponitsimikizila kuti amanikonda. Nimapemphela kuti nisakamusiye.”

CIMENE CILI COŴAŴA NGAKO KUPOSA ULULU WA CILANGO

18, 19. N’ciani coŵaŵa ngako kuposa ululu uliwonse umene tingamve cifukwa colandila cilango kapena uphungu? Fotokozani citsanzo.

18 N’zoona kuti cilango cimakhala coŵaŵa. Koma coŵaŵa ngako ni mavuto amene tingakumane nawo cifukwa cokana cilango kapena uphungu. (Aheb. 12:11) Ganizilani zitsanzo ziŵili izi: Ca Kaini na ca Mfumu Zedekiya. Pamene Kaini anakwiya kwambili n’kufuna kupha Abele, Mulungu anam’patsa uphungu Kaini. Anati: “N’cifukwa ciani wapsa mtima conco, ndipo nkhope yako yagwelanji? Ukasintha n’kucita cabwino, sindikuyanja kodi? Koma ngati susintha kuti ucite cabwino, ucimo wamyata pakhomo kukudikilila, ndipo ukulakalaka kukudya. Kodi iweyo suugonjetsa?” (Gen. 4:6, 7) Koma Kaini sanamvele. Ndipo ucimo unamugonjetsa. Kaini anadzibweletsela mavuto aakulu amene akanatha kuwapewa. (Gen. 4:11, 12) Ha! Akanalandila cilango ca Mulungu, sembe sanakumane na mavuto amenewo.

19 Zedekiya, mfumu yofooka na yoipa ya Yuda, inalamulila m’nthawi ya mavuto aakulu ku Yerusalemu. Mobweleza-bweleza, mneneli Yeremiya analangiza mfumu Zedekiya kuti aleke zoipa zimene anali kucita, koma sanamvele. Mofanana ndi Kaini, nayenso anakumana na mavuto aakulu. (Yer. 52:8-11) Inde! Yehova amatipatsa malangizo pofuna kutiteteza ku mavuto ngati amenewa.—Ŵelengani Yesaya 48:17, 18.

20. Kodi anthu amene amalandila cilango ca Mulungu ndi amene amacikana ali na tsogolo lotani?

20 M’dzikoli anthu amanyozela cilango ca Mulungu, ndipo amaona kuti kudzilanga wekha n’kosafunika. Koma posacedwa, anthu oipa amenewa adzawongewa. (Miy. 1:24-31) Conco, tifunika ‘kumvela malangizo kuti tikhale anzelu.’ Miyambo 4:13 imati: “Gwila malangizo, usawataye. Uwasunge bwino cifukwa iwo ndiwo moyo wako.”