Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Ubatizo Ni Wofunika kwa Mkhristu Aliyense

Ubatizo Ni Wofunika kwa Mkhristu Aliyense

“Cofanana ndi cingalawaco cikupulumutsanso inuyo tsopano. Cimeneci ndico ubatizo.”—1 PET. 3:21.

NYIMBO: 52, 41

1, 2. (a) Kodi makolo ena acikhristu amamvela bwanji mwana wawo akawauza kuti afuna kubatizika? (b) N’cifukwa ciani anthu opita ku ubatizo amafunsidwa ngati anadzipeleka kwa Yehova? (Onani pikica pamwambapa.)

MAKOLO acikhristu akuyang’ana mwana wawo wamkazi wacicepele, amene tam’patsa dzina lakuti Maria. Iye waimilila pamodzi ndi anthu ena opita ku ubatizo. Ndiyeno, mokweza ndi momvekela bwino, Maria akuyankha mafunso aŵili amene mkambi wafunsa. Posapita nthawi, mtsikanayu akubatizika.

2 Makolo a Maria anasangalala kwambili pamene mwana wawo anasankha kudzipeleka kwa Yehova na kubatizika. Koma poyamba amayi ake anali kumudela nkhawa. Iwo anali kudzifunsa kuti: ‘Kodi Maria ni wamkulu mokwanila cakuti n’kubatizika? Kodi akumvetsetsa kuti zimene afuna kucita ni nkhani yaikulu? Kodi sizingakhale bwino kuti ayembekezeko pang’ono kuti adzabatizike m’tsogolo?’ Awa ni mafunso amene makolo ambili amadzifunsa mwana wawo akawauza kuti afuna kubatizika. (Mlal. 5:5) Izi n’zosadabwitsa cifukwa kudzipeleka na kubatizika ni nkhani yaikulu, komanso ni mbali yofunika kwambili mu umoyo wa Mkhristu.—Onani bokosi yakuti “ Kodi Munadzipeleka kwa Yehova?

3, 4. (a) Kodi mtumwi Petulo anaonetsa bwanji kuti ubatizo ni wofunika kwambili? (b) N’cifukwa ciani ubatizo ukuyelekezeledwa na nchito yomanga cingalawa imene Nowa anacita?

3 Mtumwi Petulo anayelekezela ubatizo na cingalawa cimene Nowa anamanga. Anati: “Cofanana ndi cingalawaco cikupulumutsanso inuyo tsopano. Cimeneci ndico ubatizo.” (Ŵelengani 1 Petulo 3:20, 21.) Cingalawa cinali umboni wosatsutsika wakuti Nowa anali munthu wodzipeleka pocita cifunilo ca Mulungu. Mokhulupilika, Nowa anagwila nchito yonse imene Yehova anam’patsa. Ndithudi, nchito za Nowa zoonetsa cikhulupililo zinacititsa kuti iye na banja lake apulumuke Cigumula. Kodi zimene Petulo anakamba zakuti ubatizo ufanana ndi cingalawa zitiphunzitsa ciani?

4 Cingalawa cinali umboni wakuti Nowa anali na cikhulupililo. Nawonso ubatizo wocitidwa pamaso pa anthu umacitila umboni za wobatizikayo. Umboni wotani? Wakuti iye anadzipeleka kwa Yehova cifukwa cokhala na cikhulupililo mwa Khristu, amene anaukitsidwa. Mofanana ndi Nowa, Akhristu odzipeleka amamvela Mulungu mwa kugwila nchito imene wawapatsa. Monga mmene Nowa anapulumukila Cigumula, Akhristu okhulupilika obatizika adzapulumuka pamene dziko loipali lidzawonongedwa. (Maliko 13:10; Chiv. 7:9, 10) Cotelo, kudzipeleka na kubatizika n’zofunika ngako. Munthu amene amawayawaya kubatizika, akhoza kutaya mwayi wokalandila moyo wosatha.

5. Kodi tidzakambilana ciani m’nkhani ino?

5 Popeza taona kuti ubatizo ni wofunika kwambili, tiyeni tikambilane mafunso atatu awa: Kodi Baibo imakamba ciani za ubatizo? Kodi munthu afunika kucita ciani kuti ayenelele ubatizo? N’cifukwa ciani mphunzitsi wa Mau a Mulungu ayenela kumaganizila za kufunika kwa ubatizo pamene akuphunzitsa Baibo mwana wake kapena munthu wina?

ZIMENE BAIBO IMAKAMBA PONENA ZA UBATIZO

6, 7. (a) Fotokozani colinga ca ubatizo wa Yohane. (b) Ni ubatizo wapadela uti umene Yohane anacita?

6 Ubatizo woyamba umene timaŵelenga m’Baibo ni uja umene unacitidwa na Yohane M’batizi. (Mat. 3:1-6) Anthu amene anali kubwela kwa Yohane kudzabatizika anali kucita izi poonetsa kuti alapa macimo amene anacita posamvela Cilamulo ca Mose. Yohane analinso na mwayi wapadela wobatiza Yesu, Mwana wa Mulungu wangwilo. Komabe, kubatizika kwa Yesu sikunali cizindikilo ca kulapa. (Mat. 3:13-17) Yesu sanacitepo chimo, conco sanafunikile kulapa. (1 Pet. 2:22) Ubatizo wake unali umboni wakuti wadzipeleka kuti acite cifunilo ca Mulungu.—Aheb. 10:7.

7 Pamene Yesu anali kucita utumiki wake pano padziko lapansi, ophunzila ake analinso kubatiza anthu. (Yoh. 3:22; 4:1, 2) Mofanana ndi ubatizo wa Yohane, nawonso ubatizo wocitidwa na ophunzila a Yesu unali cizindikilo cakuti munthu walapa macimo amene anacita posamvela Cilamulo ca Mose. Komabe, pambuyo pakuti Yesu waphedwa na kuukitsidwa, ubatizo unakhala na colinga cina capadela kwa otsatila ake.

8. (a) Pambuyo poukitsidwa, kodi Yesu anapeleka lamulo lanji kwa otsatila ake? (b) N’cifukwa ciani ubatizo wacikhristu ni wofunika kwambili?

8 Mu 33 C.E., Yesu ataukitsidwa anaonekela ku gulu la anthu oposa 500, amene anaphatikizapo amuna, akazi, mwinanso ngakhale ana. N’kutheka kuti inali nthawi imeneyi pamene iye anapeleka lamulo lakuti: “Conco pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzila anga. Muziwabatiza m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyela, ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulilani.” (Mat. 28:19, 20; 1 Akor. 15:6) Inde, cioneka kuti ophunzila ambili-mbili a Yesu analipo pamene iye anapeleka lamulo lakuti tiyenela kupanga ophunzila. Pamenepa, Yesu anaonetsa kuti munthu aliyense amene wasankha kukhala wotsatila wake, afunika kubatizika. (Mat. 11:29, 30) Aliyense wofuna kulambila Mulungu m’njila yoyenela afunika kuzindikila na kuvomeleza udindo wa Yesu pokwanilitsa colinga ca Yehova. Akatelo, m’pamene munthuyo amakhala woyenelela kubatizika. Ubatizo waconco ndiwo wokha wovomelezeka pamaso pa Mulungu. M’Baibo muli malemba ambili oonetsa kuti m’nthawi ya atumwi, ophunzila atsopano a Khristu anali kudziŵa bwino kufunika kwa ubatizo. Ndipo iwo sanazengeleze kubatizika.—Mac. 2:41; 9:18; 16:14, 15, 32, 33.

MUSAZENGELEZE

9, 10. Kodi zimene Mwiitiyopiya wotembenukila ku Ciyuda ndi mtumwi Paulo anacita zitiphunzitsa ciani ponena za ubatizo?

9 Ŵelengani Machitidwe 8:35, 36. Ganizilani za Mwiitiyopiya wotembenukila ku Ciyuda amene anali pa ulendo wobwelela kwawo kucokela ku Yerusalemu, kumene anapita kukalambila. Filipo atalamulidwa na mngelo wa Yehova, anapita kukakumana ndi Mwiitiyopiyayo ndipo anamulalikila “uthenga wabwino wonena za Yesu.” Kodi Mwiitiyopiyayo anacita ciani atamva uthengawo? Anacita zinthu zoonetsa kuti coonadi cimene anaphunzila cinam’fika pa mtima. Iye anali na mtima wofunitsitsa kucita zinthu mogwilizana ndi cifunilo ca Yehova, moti anabatizika mosazengeleza.

10 Ganizilaninso za mwamuna wina waciyuda amene anali kuzunza Akhristu. Iye anali wobadwila mu mtundu waciyuda umene unali wodzipeleka kwa Mulungu. Komabe panthawiyo, Ayuda sanalinso pa ubwenzi wapadela na Yehova. Mwamuna ameneyo anali wodzipeleka kwambili ku miyambo ya Ciyuda. Koma pambuyo pake, anaphunzila coonadi. Iye analalikidwa mwacindunji na Yesu Khristu, amene anali ataukitsidwa ndi kupatsidwa ulemelelo. Kodi mwamunayo anacita ciani pambuyo pake? Anavomeleza kuthandizidwa na Hananiya, wophunzila wa Khristu. Pokamba za mwamunayo, Baibo imati: “Kenako anapita kukabatizidwa.” (Mac. 9:17, 18; Agal. 1:14) Mosakayikila, mwadziŵa kuti mwamuna waciyuda amene tikukamba, ni uja amene anayamba kudziŵika kuti mtumwi Paulo. Koma onani kuti Paulo atamvetsetsa coonadi cokhudza udindo wa Yesu pokwanilitsa colinga ca Mulungu, anacitapo kanthu. Iye anabatizika mosazengeleza.—Ŵelengani Machitidwe 22:12-16.

11. (a) N’ciani cimasonkhezela ophunzila Baibo masiku ano kuti abatizike? (b) Kodi timamvela bwanji tikaona anthu amene anadzipeleka akubatizika?

11 N’cimodzi-modzinso na ophunzila Baibo masiku ano, kaya ni acicepele kapena acikulile. Awo amene ali na cikhulupililo ndipo amayamikila na mtima wonse coonadi ca m’Baibo cimene aphunzila, sawayawaya kudzipeleka na kubatizika. Nkhani ya ubatizo, imene imakonzedwela maka-maka opita ku ubatizo, ni mbali yofunika kwambili pa msonkhano uliwonse wadela ndi wacigawo. Mboni za Yehova zimasangalala wophunzila Baibo akamvetsetsa coonadi ndi kupita patsogolo mpaka kubatizika. Makolo acikhristu amakondwela kwambili kuona ana awo akubatizika pamodzi ndi ophunzila ena atsopano a Khristu. M’caka ca utumiki ca 2017, anthu a “maganizo abwino” oposa 284,000 anabatizika poonetsa kudzipeleka kwawo kwa Yehova. (Mac. 13:48) Mwacionekele, iwo anadziŵa kuti ubatizo ni wofunika ngako kwa Mkhristu aliyense. Kodi n’zinthu ziti zimene anacita kuti afike pobatizika?

12. N’zinthu ziti zimene wophunzila Baibo afunika kucita kuti ayenelele ubatizo?

12 Wophunzila asanabatizike, afunika kukhala na cikhulupililo. Amakhala na cikhulupililo pambuyo podziŵa Mulungu molondola, kudziŵa cifunilo cake, na njila imene wakonza yopulumutsila anthu. (1 Tim. 2:3-6) Cikhulupililo cimeneci cimam’thandiza kupewa makhalidwe amene Mulungu amawazonda, ndi kuyamba kutsatila miyezo yolungama ya Yehova. (Mac. 3:19) Kukamba zoona, ngati munthu wadzipeleka kwa Mulungu pamene akucitanso macimo aakulu amene angamulepheletse kukaloŵa mu Ufumu, ndiye kuti kudzipeleka kwake n’kosayenela. (1 Akor. 6:9, 10) Komabe, kungotsatila miyezo ya Yehova ya makhalidwe abwino si kokwanila. Munthu amene akutsatila cilungamo afunikanso kumapezeka pa misonkhano ya mpingo ndi kutengako mbali mokwanila m’nchito yopulumutsa moyo, yolalikila na kupanga ophunzila. Yesu anakamba kuti ophunzila ake oona ndi amene adzagwila nchito imeneyi. (Mac. 1:8) Wophunzila akamacita zimenezi, m’pamene angadzipeleke zeni-zeni kwa Yehova m’pemphelo, ndipo pambuyo pake angalengeze poyela kudzipeleka kwakeko mwa kubatizika.

COLINGA CIMENE OPHUNZILA BAIBO AYENELA KUKHALA NACO

Pamene muphunzitsa wophunzila wanu, kodi mumakumbukila kufunika kwa ubatizo na kukambilana naye za nkhaniyi? (Onani palagilafu 13)

13. N’cifukwa ciani mphunzitsi wa Mau a Mulungu afunika kuzindikila kuti ubatizo ni ofunika kwambili kwa wophunzila aliyense?

13 Pamene tikuthandiza ana athu na ophunzila Baibo kupita patsogolo, tifunika kukumbukila kuti ngati munthu sabatizika, sangakhale wotsatila weni-weni wa Khristu. Ngati nthawi zonse tikumbukila mfundo imeneyi, tidzawathandiza bwino ophunzila athu. Tidzayamba kukamba nawo pa nthawi yoyenela za kufunika kodzipeleka na kubatizika. Inde, timafuna kuti ana athu komanso ophunzila Baibo apite patsogolo mpaka akabatizike.

14. N’cifukwa ciani sitifunika kukakamiza aliyense kuti abatizike?

14 Palibe afunika kukakamiza munthu kuti abatizike, kaya ni kholo, wophunzitsa Baibo, kapena wina aliyense mu mpingo. Kucita conco, n’kosagwilizana ndi mmene Yehova amacitila zinthu. (1 Yoh. 4:8) M’malomwake, pamene tiphunzitsa ena, tiyenela kugogomeza kufunika kokhala pa ubwenzi wolimba na Mulungu. Cimene ciyenela kusonkhezela munthu kuti abatizike ni kuyamikila kwake coonadi na mtima wonse, na kufunitsitsa kwake kusenza udindo wokhala wophunzila wa Khristu.—2 Akor. 5:14, 15.

15, 16. (a) Kodi pali msinkhu woikika umene munthu afunika kufikapo kuti abatizike? Fotokozani. (b) N’cifukwa ciani wophunzila Baibo afunika kubatizika kuti akhale Mboni ya Yehova, olo kuti pamene anali ku cipembedzo cina anabatizikapo?

15 Palibe msinkhu woikika umene munthu afunika kufikapo kuti abatizike. Anthu amakula mosiyana-siyana. Ambili amabatizika ali acicepele, ndipo amakula ndi kukhalabe okhulupilika kwa Yehova. Anthu ena amaphunzila coonadi ca m’Baibo ndi kuona kufunika kobatizika ali acikulile, ndipo ena anabatizikapo ali na zaka zopitilila 100.

16 Mwacitsanzo, mzimayi wina wacikulile anafunsa mphunzitsi wake wa Baibo ngati kunalidi kofunika kuti abatizikenso. M’mbuyomo, iye anali atabatizikapo kale m’zipembedzo zosiyana-siyana. Mphunzitsi wake anakambilana naye malemba okhudza nkhaniyi. Mzimayiyo atamvetsetsa zimene Baibo imakamba pankhaniyi, posapita nthawi anabatizika. Olo kuti anali na zaka pafupi-fupi 80, iye anaonabe kuti afunika kubatizika. Zoonadi, kuti ubatizo ukhale woyenelela, coyamba munthu afunika kudziŵa cifunilo ca Yehova molondola. Conco, munthu afunika kubatizika kuti akhale Mboni, olo kuti m’mbuyomo anabatizikapo ku cipembedzo cina.—Ŵelengani Machitidwe 19:3-5.

17. N’zinthu ziti zimene munthu ayenela kusinkha-sinkha pa tsiku la ubatizo wake?

17 Tsiku limene munthu wabatizika, limakhala nthawi yokondweletsa kwambili. Imakhalanso nthawi imene munthu amaganizila mozama tanthauzo la kudzipeleka na ubatizo. Pamafunika khama kuti munthu apitilize kucita zinthu mogwilizana ndi kudzipeleka kwake. Ndiye cifukwa cake Yesu anayelekezela kukhala wotsatila wake ndi kunyamula goli. Ophunzila a Yesu safunika ‘kukhala ndi moyo wongodzisangalatsa okha, koma wosangalatsa amene anawafela n’kuukitsidwa.’—2 Akor. 5:15; Mat. 16:24.

18. Tidzakambilana mafunso ati m’nkhani yotsatila?

18 Izi n’zimene amayi ake a Maria anali kuganizila pamene anadzifunsa mafunso amene tawachula m’ndime yaciŵili. Ngati ndimwe kholo, mwina munadzifunsapo kuti: ‘Kodi mwana wanga ni wokonzekadi kubatizika? Kodi ali na cidziŵitso cofikapo moti angadzipeleke moyenela? Nanga bwanji zolinga zake zokhudza maphunzilo na nchito? Komanso bwanji ngati iye angabatizike, kenako n’kugwela m’chimo?’ M’nkhani yotsatila, tidzakambilana mafunso amenewa na mmene makolo acikhristu angakhalile ndi kaonedwe koyenela ka ubatizo.