Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MBILI YANGA

Yehova Sananigwilitse Mwala

Yehova Sananigwilitse Mwala

N’nali mmodzi wa twatsikana 4 tumene tunasankhidwa kuti tukapeleke maluŵa kwa Adolf Hitler atatsiliza kukamba ku gulu la anthu. N’cifukwa ciani n’nasankhidwa? Atate anga anali membala wacangu wa cipani ca Nazi, ndipo anali dilaiva wa mtsogoleli wa cipani ca Nazi m’dela lathu. Amayi anali Mkatolika wokangalika, ndipo anali kufuna kuti ine nikakhale sisitele. Olo kuti n’nakulila m’banja laconco, sin’nakhale wa cipani ca Nazi kapena sisitele. Lekani n’kuuzeni cifukwa cake.

INE n’nakulila ku Graz, m’dziko la Austria. Nili na zaka 7, n’natumizidwa ku sukulu yophunzitsa za cipembedzo. Koma, kumeneko n’nakhumudwa na khalidwe lonyansa la ciwelewele limene linali kucitika pakati pa ansembe na masisitele. Conco, caka cisanathe amayi anavomela kuti nicoke pa sukulupo.

Banja lathu, ndipo Atate avala yunifomu ya usilikali

Pambuyo pake, n’napita ku sukulu ya boding’i. Tsiku lina usiku, atate anabwela kudzanitenga kuti tithaŵe ku Graz cifukwa asilikali a adani anali kuponya mabomba oopsa mu mzindawo. Tinathaŵila ku tauni ya Schladming. Titangofika na kuwoloka pa buliji, bulijiyo inaphulitsidwa. Pa nthawi ina, ndeke za nkhondo zouluka ca munsi zinaombela pa nyumba yathu pamene panali ine na ambuye anga aakazi. Pamene nkhondo inali kutha, n’naona kuti boma na cipembedzo zinalephela kutithandiza.

N’NAPHUNZILA ZA YEHOVA, GWELO LA THANDIZO LODALILIKA

Mu 1950, munthu wina wa Mboni za Yehova anayamba kuphunzitsa Baibo amayi. N’nali kumvetselako zimene anali kukambilana, ndipo nthawi zina n’nali kupita ku misonkhano ya mpingo pamodzi na amayi. Amayi atakhutila kuti Mboni za Yehova zimaphunzitsa coonadi, anabatizika mu 1952.

Pa nthawiyo, mpingo wa kwathu wa Mboni za Yehova n’nali kuuona monga kilabu ya nkhalamba. Patapita nthawi, tinapita kukasonkhana ku mpingo wina umene sunali monga kilabu ya nkhalamba, koma unali na acicepele ambili. Titabwelela ku Graz, n’nayamba kupezeka pa misonkhano yonse. Posakhalitsa, na ine n’nakhutila kuti zimene n’nali kuphunzila ni coonadi. Komanso n’nazindikila kuti Yehova ni Mulungu amene amapeleka thandizo lodalilika kwa atumiki ake. Iye amatithandiza olo pamene takumana na mavuto aakulu kwambili.—Sal. 3:5, 6.

N’nayamba kufuna kuphunzitsako ena coonadi. N’nayambila kuphunzitsako abale anga. Pa nthawiyo, azikulu anga 4 anali atacoka kale pa nyumba n’kukayamba nchito ya uphunzitsi. Koma n’nali kupita ku midzi imene anali kukhala, kukawalimbikitsa kuphunzila Baibo. M’kupita kwa nthawi, abale anga onse anaphunzila Baibo na kukhala Mboni za Yehova.

Mu wiki yaciŵili kucokela pamene n’nayamba ulaliki wa ku nyumba na nyumba, n’nakumana na mzimayi wina wa zaka za m’ma 30. N’nayamba kuphunzila naye Baibo, ndipo anapita patsogolo mpaka kubatizika. Pambuyo pake, amuna ake ndi ana awo aamuna aŵili, nawonso anakhala Mboni. Kuphunzila Baibo na mzimayi ameneyu kunalimbitsa kwambili cikhulupililo canga. Zili conco cifukwa cakuti sin’naphunzitsidweko Baibo mokhazikika na munthu wina aliyense. Nthawi iliyonse pokacititsa phunzilo, n’nali kuyesetsa kukonzekela bwino. Kukamba kwina tingati n’nali kudziphunzitsa nekha coyamba n’colinga cakuti nikaphunzitse wophunzila wanga. Izi zinanithandiza kumvetsetsa coonadi. Mu April 1954, n’nadzipeleka kwa Yehova na kubatizika.

‘TINAZUNZIDWA, KOMA OSATI MOCITA KUSOWA KOLOWELA’

Mu 1955, n’napezeka pa misonkhano ya maiko imene inacitikila ku Germany, France, na England. Pamene n’nali ku London, n’nakumana na M’bale Albert Schroeder. Iye anali mlangizi wa Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibo, ndipo pambuyo pake anatumikila mu Bungwe Lolamulila. Tsiku lina pamene tinayenda kukaona malo osungila zinthu zakale ochedwa British Museum, M’bale Schroeder anatilatila mipukutu yakale ya Baibo. Mipukutuyo inali na dzina la Mulungu m’zilembo za Ciheberi, ndipo M’baleyo anatifotokozela kufunika kwa mipukutuyo. Izi zinalimbitsa kwambili cikhulupililo canga, na kunicititsa kukhala wofunitsitsa kufalitsa coonadi ca m’Mau a Mulungu.

Nili na mnzanga (ku lamanja), pamene tinali kutumikila monga apainiya apadela ku Mistelbach, m’dziko la Austria

Pa January 1, 1956, n’nayamba kutumikila monga mpainiya wanthawi zonse. Pambuyo pa miyezi inayi, n’napemphedwa kuti nikatumikile monga mpainiya wapadela mu Austria. Pa nthawiyo, m’tauni ya Mistelbach imene ananitumizako munalibe Mboni. Koma panali vuto linalake. Ine na mnzanga wocita naye upainiya, tinali osiyana ngako. Ine n’nali mtsikana wa zaka pafupi-fupi 19 wocokela ku tauni, koma iye anali na zaka 25 ndipo anali wocokela ku mudzi. Ine n’nali kukonda kuuka mocedwa, koma iye anali kukonda kuuka mwamsanga. Komanso, ine n’nali kugona mocedwa, koma iye anali kugona mwamsanga. Olo zinali conco, cifukwa cokonkha malangizo a m’Baibo, tinakwanitsa kuthetsa kusamvana na kuyamba kutumikila pamodzi mokondwela.

Koma tinakumananso na mavuto ena aakulu kwambili. Nthawi zina tinali kuzunzidwa, koma ‘sitinasoŵe koloŵela.’ (2 Akor. 4:7-9) Mwacitsanzo, tsiku lina pamene tinali kulalikila m’mudzi wina, anthu ena anamasula agalu awo. Posapita nthawi, vaagalu vinatizungulila ndipo vinali kutiuwa. Tinagwilana manja na kupemphela kuti, “Yehova, conde, agaluwa akayamba kutiluma, tife mwamsanga cabe!” Agaluwo atafika pafupi, anaima na kuyamba kukweteza micila, ndipo kenako anacoka. Pamenepa, tinaona kuti Yehova anatiteteza. Pambuyo pake, tinalalikila m’mudzi wonsewo, ndipo tinakondwela kuona kuti anthu a kumeneko anali acidwi ngako. Mwina anacita cidwi poona kuti agaluwo sanatilume kapenanso cifukwa cakuti tinalimba mtima pamene tinawopsezedwa na agaluwo. M’kupita kwa nthawi, ena mwa anthu amenewo anakhala Mboni.

Tsiku lina, tinakumananso na zoopsa zina. Eni nyumba imene tinali kukhalamo anabwela atakolewa, ndipo anayamba kuopseza kuti atipha. Iwo anali kukamba kuti tinali kusokoneza anthu amene tinali kukhala nawo pafupi. Akazi awo anayesa kuwakhazika mtima pansi, koma sizinaphule kanthu. Ise tinali kumva zonsezi tili m’cipinda cathu capamwamba. Mofulumila, tinaika mipando ku citseko na kuyamba kulongedza zovala. Pamene tinatsegula citseko, tinawaona eni nyumbayo ataimilila pa pakhomo ali na cimpeni m’manja. Conco, tinanyamula katundu wathu yense na kuthaŵa potulukila ku khomo la kumbuyo kwa nyumbayo, ndipo sitinabwelelenso.

Tinapita kukakhala ku hotela. Tinakhala kumeneko pafupi-fupi kwa caka cathunthu, ndipo izi zinatipatsa mwayi wowonjezela zocita pa nchito yathu yolalikila. Motani? Popeza kuti hotelayo inali pakati pa tauni, ena mwa ophunzila Baibo athu anali kufuna kuti tiziphunzilila nawo Baibo ku hotelako. Posakhalitsa, tinayamba kucita phunzilo la buku ndi la Nsanja ya Mlonda wiki iliyonse m’cipinda cathu ca pa hotelayo, ndipo panali kupezeka anthu pafupi-fupi 15.

Tinakhala mu mzinda wa Mistelbach kwa caka na miyezi. Ndiyeno n’napemphedwa kuti nikatumikile mu tauni ya Feldbach, kumpoto cakum’mawa kwa mzinda wa Graz. Kumeneko, n’nali na mnzanga watsopano wocita naye upainiya, koma kunalibenso mpingo. Tinali kukhala m’kacipinda kakang’ono kapamwamba m’nyumba ya matabwa ya nsanjika. Mphepo inali kuloŵa kwambili m’mipata ya matabwa, conco tinacita kutsekamo na manyuzipepa. Komanso, madzi tinali kutapa pacitsime. Olo zinali conco, kupilila kwathu kunabala zipatso. M’miyezi yocepa cabe, panakhazikitsiwa kagulu ka mpingo. M’kupita kwa nthawi, anthu 30 a m’banja lina limene tinaphunzila nalo Baibo anakhala Mboni.

Zocitikazi zinanilikimbitsa kuti nizimuyamikila kwambili Yehova cifukwa ca thandizo lodalilika limene amapeleka kwa atumiki ake amene amaika zinthu za Ufumu patsogolo. Olo anthu alephele kutithandiza, Yehova salephela.—Sal. 121:1-3.

N’NATHANDIZIDWA NA ‘DZANJA LAMANJA LACILUNGAMO’ LA MULUNGU

Mu 1958, panapangiwa makonzedwe akuti ku New York City kucitike msonkhano wa maiko. Msonkhanowo unali kudzacitikila mu Yankee Stadium na mu Polo Grounds. N’napempha kuti nikapezekeko, ndipo ofesi ya nthambi ya mu Austria inanifunsa ngati n’nali kufunanso kukaloŵa nawo kilasi ya namba 32 ya Sukulu ya Giliyadi. Ndani angakane mwayi ngati umenewu? Conco, mofulumila n’nayankha kuti “Nifuna!”

M’kilasi ku Sukulu ya Giliyadi, n’nali kukhala pafupi na M’bale Martin Poetzinger. M’baleyu anapilila mavuto aakulu m’ndende zozunzilako anthu za Nazi. M’kupita kwa nthawi, nayenso anatumikilapo m’Bungwe Lolamulila. Tili m’kilasi, M’bale Poetzinger nthawi zina anali kunifunsa coŵeleŵesa kuti, “Mlongo Erika, kodi mau amenewa amatanthauza ciani m’Cijelemani?”

Tili ca pakati-kati pa sukuluyo, M’bale Nathan Knorr anatiuza kumene tinagaŵilidwa kuti tikatumikile tikatsiliza sukulu. Ine n’nauzidwa kuti nikatumikila ku Paraguay. Popeza n’nali wacicepele, panali kufunika cilolezo ca atate kuti niloledwe kuloŵa m’dzikolo. N’talandila cilolezo, n’nafika ku Paraguay mu March 1959. N’nali kukhala m’nyumba ya amishonale ku Asunción, pamodzi na mnzanga wina wake.

Posakhalitsa, n’nakumana na m’bale Walter Bright, amene analoŵa kilasi ya namba 30 ya Giliyadi. Patapita nthawi, tinakwatilana ndipo tinayamba kupilila limodzi mavuto amene tinali kukumana nawo. Tikakumana na vuto, tinali kuŵelenga pa Yesaya 41:10, pamene Yehova anati: “Usacite mantha, pakuti ndili nawe. Usayang’ane uku ndi uku mwamantha, pakuti ine ndine Mulungu wako. Ndikulimbitsa.” Izi zinatithandiza kukhulupilila kuti malinga ngati tikhalabe okhulupilika kwa Mulungu na kuika Ufumu wake patsogolo, iye sadzatisiya.

M’kupita kwa nthawi, tinatumizidwa kuti tikatumikile m’dela lina la kufupi na dziko la Brazil. Kumeneko, atsogoleli a cipembedzo anatuntha acicepele kuti ayambe kuponya miyala pa nyumba ya amishonale imene tinali kukhala, imenenso inali yowonongeka kale. Pa nthawiyo, m’bale Bright anayamba kuphunzila Baibo na mkulu wa apolisi. Kwa wiki yathunthu, wapolisiyo anaonetsetsa kuti pafupi na nyumba yathu pakukhala apolisi, moti anthu oukilawo sanapitilize kutivutitsa. Patapita nthawi yocepa, tinakukila m’dela lina labwino kumalile na dziko la Brazil. Izi zinathandiza kuti tizikwanitsa kucita misonkhano ku Paraguay komanso ku Brazil. Pamene tinali kucoka, m’delali munali mutakhazikitsidwa mipingo iŵili ing’ono-ing’ono.

Nili na amuna anga, a Bright, pamene tinali kutumikila monga amishonale ku Asunción, m’dziko la Paraguay

YEHOVA AKALI KUNITHANDIZA

M’mbuyomo, madokota ananiuza kuti sinidzabeleka. Koma mu 1962 tinadabwa pamene n’nauzidwa kuti ndine woyembekezela. Patapita nthawi, tinakukila ku Hollywood, mu mzinda wa Florida, kufupi na acibululu a amuna anga. Kwa zaka, ine na amuna anga tinayamba taima kucita upainiya. Tinali kusamalila banja lathu. Komabe, tinapitiliza kuika zinthu za Ufumu patsogolo.—Mat. 6:33.

Titafika ku Florida mu November 1962, tinadabwa pamene tinamva kuti kumeneko abale aciyela na acikuda sanali kufuna kusonkhana pamodzi kapena kulalikila m’dela limodzi. Koma Yehova alibe tsankho, ndipo posapita nthawi itali abale a mitundu yosiyana anayamba kucitila zinthu pamodzi mogwilizana m’mipingo. Madalitso a Yehova anacita kuonekelatu cakuti lomba m’delali muli mipingo yambili.

N’zomvetsa cisoni kuti mu 2015 amuna anga anamwalila na khansa ya mu ubongo. N’nakhala nawo m’banja kwa zaka 55. Iwo anali mwamuna wabwino kwambili. Anali kukonda Yehova na kuthandiza abale ambili. Niyembekezela mwacidwi kudzawaonanso ali na thanzi labwino akadzaukitsidwa.—Mac. 24:15.

Nimaona kuti ni mwayi waukulu kukhala mu utumiki wa nthawi zonse kwa zaka zoposa 40. Nakumana na zambili zokondwetsa na kulandila madalitso oculuka. Mwacitsanzo, ine na amuna anga tinali na mwayi woonelela maubatizo a ophunzila Baibo athu okwana 136. N’zoona kuti panali zovuta zina. Komabe, sitinaleke kutumikila Mulungu wathu wokhulupilika. M’malomwake, tinamuyandikila kwambili, pokhulupilila kuti adzakonza zinthu m’njila yoyenela komanso pa nthawi yake yoyenela. Ndipo izi n’zimenedi amacita.—2 Tim. 4:16, 17.

Nimawayewa ngako amuna anga, koma kucita upainiya kumanithandiza kupilila. Nimalimbikitsiwa ngako ngati niphunzitsa ena, maka-maka za ciyembekezo cathu ca ciukililo. Ndithudi, Yehova wanithandiza m’njila zambili. Sananigwilitsepo mwala. Mogwilizana na lonjezo lake, wanipatsa mphamvu, kunilimbikitsa, ndi kunigwila na ‘dzanja lake lamanja lacilungamo.’—Yes. 41:10.