Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

ZA M’NKHOKWE YATHU

“Cangu na Cikondi Cathu Zinawonjezeka Kwambili”

“Cangu na Cikondi Cathu Zinawonjezeka Kwambili”

PACISANU m’maŵa, mu September 1922, anthu okwana 8,000 anakhamukila m’ciholo cacikulu. Panthawiyo kunja kunali kutayamba kale kutentha. Cheyamani analengeza kuti m’cigaŵo cimeneci, aliyense ni wololedwa kutuluka m’holoyo, koma palibe amene adzaloledwa kungenanso.

M’sonkhanowo unayamba na nyimbo zotamanda Mulungu. Pambuyo pake, M’bale Joseph F. Rutherford anapita kukaimilila pa pulatifomu. Ambili pamsonkhanowo anali na cidwi ngako cofuna kumvetsela. Ena ocepa anali kuyenda-yenda cifukwa kunali kotentha. Mkambi anawapempha kuti akhale pansi kuti amvetsele nkhani. Nkhaniyo itayamba, palibe amene anadziŵa kuti m’mwamba kutsogolo kwa pulatifomu kunali cinsalu copindidwa bwino.

M’bale Rutherford anakamba nkhani ya mutu wakuti, “Ufumu wa kumwamba wayandikila.” Iye anakamba nkhaniyi pafupi-fupi ola limodzi na hafu. Mau ake amphamvu anali kumveka m’holo yonseyo pamene anali kufotokoza mmene aneneli akale analengezela mopanda mantha za Ufumu umene ukubwelawo. Pamene nkhaniyi inafika pacimake, M’bale Rutherford anafunsa kuti, “Kodi mukhulupilila kuti Mfumu yaulemelelo yayamba kulamulila?” Anthu onse pamsonkhanowo anayankha mokweza kuti: “Inde!”

Ndiyeno M’bale Rutherford anafuula kuti: “Ndiye pitani mukalalikile, inu ana a Mulungu wam’mwamba-mwamba! Onani, Mfumu yayamba kale kulamulila ndipo inu ndinu atumiki ake olengeza ufumuwo. Conco lengezani, lengezani, lengezani Mfumu ndi ufumu wake.”

Panthawi imeneyo, cinsalu copinda cimene cinali ku pulatifomu cinatambasuliwa, ndipo panali mau akuti: “Lengezani Mfumu ndi ufumu wake.”

Ray Bopp anati: “Anthu pamsonkhanowo anakondwela ngako.” Komanso mlongo Anna Gardner anakamba kuti “mtenje unanjenjemela mwamphamvu cifukwa abale na alongo anaomba m’manja kwambili na cisangalalo.” Nayenso M’bale Fred Twarosh anati: “Onse pamsonkhanowo anaimilila panthawi imodzi.” M’bale winanso, dzina lake Evangelos Scouffas, anati: “Zinali monga kuti cinthu cina cake camphamvu catinyamula tonse pamipando yathu. Tinaimilila ndipo m’maso mwathu munadzala misozi yacisangalalo.”

Ambili pamsonkhanowo anali atayamba kale kulalikila uthenga wabwino wa Ufumu. Koma panthawiyo analimbikitsidwa kuwonjezela cangu cawo. Ethel Bennecoff anakamba kuti pamene Ophunzila Baibulo anabwelela kumanyumba kwawo, ‘cangu na cikondi [cawo] zinawonjezeka kwambili.’ Odessa Tuck, amene panthawiyo anali na zaka 18, atacoka pamsonkhanowo anatsimikiza mtima kukhala wodzipeleka monga Yesaya. Iye anati: “Sin’nali kudziŵa kumene nidzapita kukatumikila, utumiki umene nidzacita, kapena mmene nidzaucitila. Koma n’nali wofunitsitsa kukhala monga Yesaya, amene anati: ‘Ine ndilipo! Nditumizeni.’” (Yes. 6:8) M’bale Ralph Leffler anakamba kuti “Tsiku limenelo linali ciyambi ceni-ceni ca nchito yolengeza Ufumu imene yafalikila padziko lonse lapansi.”

N’zosadabwitsa kuti msonkhano wacigawo umenewu, umene unacitika mu 1922 ku Cedar Point, Ohio, wakhala wosaiŵalika m’mbili ya atumiki a Mulungu. M’bale George Gangas anati, “Msonkhanowu unanicititsa kukhala na colinga cakuti nisadzaphonye msonkhano uliwonse.” Ndipo kuyambila nthawiyo, iye sanaphonyekodi msonkhano uliwonse. Komanso mlongo Julia Wilcox analemba kuti: “Siningakwanitse kufotokoza cimwemwe cimene nimakhala naco nthawi iliyonse ngati m’mabuku athu akambamo za msonkhano umene unacitika ku Cedar Point mu 1922. Nthawi zonse nimayamikila Yehova cifukwa conipatsa mwayi wopezekapo.’”

Ambili a ise timakumbukila msonkhano wacigawo umene unatisangalatsa ndi kutilimbikitsa kukhala wacangu, ndiponso kukonda kwambili Mulungu wathu wamkulu ndi Mfumu yake. Tikakumbukila nthawi yokondweletsa imeneyo, naise timalimbikitsidwa kukamba kuti, “Zikomo kwambili Yehova cifukwa conipatsa mwayi wopezekapo.”