Musalole Kuti Cikondi Canu Cizilale
“Cifukwa ca kuwonjezeka kwa kusamvela malamulo, cikondi ca anthu ambili cidzazilala.”—MAT. 24:12.
1, 2. (a) Kodi mau a Yesu a pa Mateyu 24:12 anali kukamba za ndani poyamba? (b) Kodi buku la Macitidwe lionetsa bwanji kuti Akhristu ambili oyambilila anapitiliza kuonetsa cikondi? (Onani pikica pamwambapa.)
MBALI imodzi ya cizindikilo ca “mapeto a nthawi ino” cimene Yesu anakamba ni yakuti, “cikondi ca anthu ambili cidzazilala.” (Mat. 24:3, 12) M’zaka 100 zoyambilila, Ayuda amene anali kudzicha anthu a Mulungu, analola cikondi cawo pa Mulungu kuzilala.
2 Koma Akhristu ambili panthawiyo anali “kulengeza uthenga wabwino wonena za Khristu” mwacangu. Anali kucitanso zinthu zina zoonetsa kukonda Mulungu, kukonda Akhristu anzawo, ndi anthu osakhulupilila. (Mac. 2:44-47; 5:42) Ngakhale zinali conco, ena mwa otsatila a Yesu a m’zaka 100 zoyambilila analola cikondi cawo kuzilala.
3. N’ciani cimene ciyenela kuti cinacititsa cikondi ca Akhristu ena kuzilala?
3 Pokamba na Akhristu a ku Efeso a m’zaka 100 zoyambilila, Yesu Khristu anati: “Ndakupeza ndi mlandu wakuti wasiya cikondi cimene unali naco poyamba.” (Chiv. 2:4) N’cifukwa cimodzi citi cimene ciyenela kuti cinacititsa zimenezi? Ophunzila a Khristu oyambilila amenewa, ayenela kuti anasonkhezeledwa na nzelu za dzikoli. (Aef. 2:2, 3) Monga mmene zilili na mizinda yambili masiku ano, nawonso mzinda wa Efeso unali wodzala na makhalidwe oipa. Unali wolemela ngako, ndipo anthu a mu mzindawo anali na mtima wokonda zinthu zapamwamba, zosangulutsa, ndi umoyo wa wofu-wofu. Kukonda zinthu zosangalatsa kunawapangitsa kukhala odzikonda. Kuwonjezela apo, khalidwe lotayilila ndi laciwelewele zinali zofala mumzindawo.
4. (a) Kodi masiku ano cikondi cazilala m’njila ziti? (b) Kodi cikondi cathu cingayesedwa m’mbali zitatu ziti?
4 Ulosi wa Yesu wokamba za kuzilala kwa cikondi ukukwanilitsidwanso masiku ano. Masiku ano, cikondi ca anthu pa Mulungu cikucepela-cepela. Anthu mamiliyoni ambili aleka kudalila Mulungu. M’malomwake, aika cidalilo cawo pa mabungwe a anthu kuti ndi amene adzathetsa mavuto padziko. Zimenezi zapangitsa kuti cikondi cicepe kwambili pakati pa anthu osalambila Yehova Mulungu. Ngakhale Akhristu oona masiku ano, cikondi cawo cikhoza kuzilala monga mmene zinalili kwa Akhristu oyambilila a ku mpingo wa Efeso. Lomba tidzakambilana mbali zitatu za mmene cikondi cathu cingayesedwele. Mbali zimenezi ndi (1) kukonda Yehova, (2) kukonda coonadi ca m’Baibo, ndi (3) kukonda abale athu.
KUKONDA YEHOVA
5. N’cifukwa ciani tifunika kum’konda Mulungu?
5 Pa tsiku limene Yesu anapeleka cenjezo pa nkhani ya kutha kwa cikondi, anachulanso amene tiyenela kum’konda ngako. Iye anati: “‘Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.’ Limeneli ndilo lamulo lalikulu kwambili komanso loyamba.” (Mat. 22:37, 38) Ndithudi, kukonda kwambili Mulungu kumatithandiza kumvela malamulo ake, kupilila, ndi kudana n’zoipa. (Ŵelengani Salimo 97:10.) Komabe, Satana ndi dziko lake amafuna kutilepheletsa kukonda Mulungu.
6. Kodi kusakonda Mulungu kwakhala na zotulukapo zotani?
6 Anthu a m’dzikoli ali na maganizo olakwika pa nkhani ya cikondi. M’malo mokonda Mlengi wawo, ‘amadzikonda’ okha. (2 Tim. 3:2) Dzikoli, limene wolamulila wake ni Satana, limalimbikitsa anthu kukhala ndi “cilakolako ca thupi, cilakolako ca maso ndi kudzionetsela ndi zimene munthu ali nazo pa moyo wake.” (1 Yoh. 2:16) Mtumwi Paulo anacenjeza Akhristu anzake za kuopsa kokhutilitsa cilakolako ca thupi. Iye anati: “Kuika maganizo pa zinthu za thupi kumabweletsa imfa . . . cifukwa kuika maganizo pa zinthu za thupi ndiko udani ndi Mulungu.” (Aroma. 8:6, 7) Kunena zoona, anthu amene amakonda kufuna-funa zinthu zakuthupi kapena kukhutilitsa cilakolako cawo ca kugonana, amagwilitsidwa mwala, ndipo amadzibweletsela mavuto ambili.—1 Akor. 6:18; 1 Tim. 6:9, 10.
7. Ni ngozi yanji imene otsatila a Khristu angakumane nayo masiku ano?
7 Ku mayiko ena, anthu amene sakhulupilila kuti kuli Mulungu ndiponso amene amakhulupilila cisinthiko, amalimbikitsa mfundo zimene zacititsa kuti anthu asamakonde Mulungu ndi kum’khulupilila. Iwo acititsa anthu ambili kuona kuti kukhulupilila kuti kuli Mlengi ni umbuli ndiponso n’kupanda nzelu. Komanso, anthu amalemekeza kwambili asayansi, ndipo zimenezi zacititsa kuti asamalemekeze Mlengi. (Aroma 1:25) Ngati timvetsela zimene iwo amakamba, pang’ono ndi pang’ono tingacoke kwa Yehova, ndipo cikondi cathu pa iye cingayambe kuzilala.—Aheb. 3:12.
8. (a) Ni mavuto ati amene anthu ambili a Yehova amakumana nawo? (b) Kodi mu Salimo 136, muli mau olimbikitsa ati?
1 Yoh. 5:19) Mwina palipano tikuvutika ndi ukalamba, matenda, kapena mavuto a zacuma. N’kuthekanso kuti tikuvutika cifukwa codziona ngati wosafunika, kugwilitsidwa mwala, kapena cifukwa ca zinthu zina zimene timalephela kucita bwino. Olo kuti tikumane na mavuto aconco, sitiyenela kuganiza kuti Yehova watisiya. M’malomwake, tiziganizila mau a pa Salimo 136:23 amene aonetsa kuti Yehova amatikonda nthawi zonse. Lembali limati: “Iye amene anatikumbukila pamene adani anatinyazitsa. Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.” Zoonadi, Yehova sadzaleka kukonda atumiki ake. Conco, tingakhale otsimikiza kuti iye amamvela na kuyankha ‘madandaulo athu.’—Sal. 116:1; 136:24-26.
8 Zokhumudwitsa na mavuto zingafooketsenso cikhulupililo cathu ndi kucititsa cikondi cathu pa Mulungu kuzilala. Popeza tikukhala m’dziko loipa lolamulidwa na Satana, tonse timakumana ndi mavuto. (9. N’ciani cinathandiza Paulo kupitiliza kukonda Mulungu?
9 Mofanana ndi wamasalimo, Paulo nayenso anapeza mphamvu mwa kuganizila mmene Yehova anali kum’thandizila nthawi zonse. Iye anati: “Yehova ndiye mthandizi wanga. Sindidzaopa. Munthu angandicite ciani?” (Aheb. 13:6) Kudalila kwambili Yehova kunam’thandiza Paulo kupilila mavuto pa umoyo wake. Iye sanalole kuti mavuto amufooketse. Ndipo pamene anali m’ndende, Paulo analemba makalata ambili olimbikitsa. (Aef. 4:1; Afil. 1:7; Filim. 1) Inde, ngakhale pamene anakumana ndi mavuto aakulu, iye anapitiliza kukonda Mulungu. N’ciani cinam’thandiza kukhala wolimba conco? Anali kudalila “Mulungu amene amatitonthoza m’njila iliyonse, amenenso amatitonthoza m’masautso athu onse.” (2 Akor. 1:3, 4) Tingatengele bwanji citsanzo ca Paulo ndi kupitilizabe kum’konda kwambili Yehova?
10. Tingacite ciani kuti tilimbitse cikondi cathu pa Yehova?
10 Paulo anafotokoza cinthu cimodzi cofunika kwambili cimene tingacite kuti tilimbitse cikondi cathu pa Yehova. Iye analembela okhulupilila anzake kuti: “Muzipemphela mosalekeza.” Pambuyo pake, analembanso kuti: “Limbikilani kupemphela.” (1 Ates. 5:17; Aroma 12:12) Kukamba na Mulungu m’pemphelo n’kofunika kwambili kuti munthu akhale naye pa ubale wolimba. (Sal. 86:3) Ngati timakhala na nthawi yokwanila yomuuza Yehova za mumtima mwathu, timayandikila kwambili kwa Atate wathu wakumwamba, amene ni “Wakumva pemphelo.” (Sal. 65:2) Kuwonjezela apo, tikazindikila kuti Yehova amayankha mapemphelo athu, cikondi cathu pa iye cimakula. Komanso, timayamba kukhulupilila kwambili kuti “Yehova ali pafupi ndi onse oitanila pa iye.” (Sal. 145:18) Kukhulupilila Yehova mwa njila imeneyi kudzatithandiza kupilila mavuto oyesa cikhulupililo amene tingakumane nawo.
KUKONDA COONADI CA M’BAIBO
11, 12. N’ciani cimene tingacite kuti tizikonda kwambili coonadi ca m’Baibo?
11 Ise monga Akhristu, timakonda kwambili coonadi. Mau a Mulungu ndiye gwelo la coonadi. N’cifukwa cake Yesu popemphela kwa Atate wake anati: “Mau anu ndiwo coonadi.” (Yoh. 17:17) Conco, kuti tiyambe kukonda coonadi, tifunika kuphunzila kuti tikhale na cidziŵitso colongosoka ca Mau a Mulungu. (Akol. 1:10) Komabe, kukhala na cidziŵitso pakokha si kokwanila. Pali zambili zimene tifunika kucita. Zimene wamasalimo anauzilidwa kulemba pa Salimo 119, zimatithandiza kumvetsetsa tanthauzo la kukonda coonadi ca m’Baibo. (Ŵelengani Salimo 119:97-100.) Kodi tikaŵelenga Baibo, timayesetsa tsiku lonse kusinkhasinkha kapena kuti kuganizila pa zimene taŵelengazo? Tikamaganizila mmene tapindulila na coonadi ca m’Baibo pa umoyo wathu, timayamba kucikonda kwambili.
12 Wamasalimo anapitiliza kukamba kuti: “Mau anu amatsekemela m’kamwa mwanga, kuposa mmene uci umakomela!” (Sal. 119:103) Nafenso timadya cakudya cauzimu cokoma cozikidwa pa Baibo, cimene timalandila m’gulu la Mulungu. Conco, kuti timvele kukoma kwa cakudyaci, sitiyenela kucidya mothamanga. Tifunika kusinkha-sinkha zimene taŵelenga kuti tizitha kukumbukila “mau okoma”a coonadi ndi kuwaseŵenzetsa pothandiza ena.—Mlal. 12:10.
13. N’ciani cinathandiza Yeremiya kukonda coonadi ca m’Malemba? Nanga coonadico cinam’khudza bwanji?
13 Mneneli Yeremiya anali kukonda coonadi ca m’Malemba. Onani mmene Mau a Mulungu anam’khudzila. Iye anati: “Mau anu anandipeza ndipo ndinawadya. Mau anu amandikondweletsa ndi kusangalatsa mtima wanga, pakuti ine ndimachedwa ndi dzina lanu, inu Yehova Mulungu wa makamu.” (Yer. 15:16) Yeremiya anadya mau amtengo wapatali a Mulungu mophiphilitsila mwa kuwasinkhasinkha. Kucita zimenezi kunam’thandiza kuyamikila mwayi wochedwa na dzina la Mulungu. Kodi kukonda coonadi kwatithandiza kuzindikila mwayi wapadela umene tili nawo wodziŵika na dzina la Mulungu ndi kulengeza za Ufumu wake m’nthawi ya mapeto ino?
14. N’ciani cingatithandize kuti tizikonda kwambili coonadi?
14 Kuwonjezela pa kuŵelenga Baibo na mabuku athu ozikidwa pa Baibo, n’ciani cina cimene cingatithandize kuti tizikonda kwambili coonadi? Tifunika kumapezeka pa misonkhano yampingo nthawi zonse. Kuphunzila Baibo pogwilitsila nchito Nsanja ya Mlonda ndiyo njila yaikulu imene Mulungu amatiphunzitsila. Kuti timvetsetse mfundo za m’nkhani imene tidzaphunzila, tifunika kukonzekela bwino phunzilo lililonse la Nsanja ya Mlonda. Njila imodzi imene tingacitile zimenezi ndi kuŵelenga lemba lililonse limene sanaligwile mau. Masiku ano, munthu angacite daunilodi magazini ya Nsanja ya Mlonda pa webusaiti ya jw.org kapena angaiŵelenge pa JW Laibulale, imene ipezeka m’zitundu zambili. Magazini a pa webusaiti ndi pa JW Laibulale apezekanso mumpangidwe umene ungathandize munthu kupeza mwamsanga malemba osagwila mau pa nkhani iliyonse yophunzila. Koma mosasamala kanthu za njila imene tingaseŵenzetse pokonzekela, tifunika kuŵelenga malemba amenewa mosamala na kuwasinkhasinkha. Kucita zimenezi kudzatithandiza kukonda kwambili coonadi ca m’Baibo.—Ŵelengani Salimo 1:2.
KUKONDA ABALE ATHU
15, 16. (a) Kodi lemba la Yohane 13:34, 35, lionetsa kuti tili na udindo wanji? (b) Kodi kukonda abale athu kumagwilizana bwanji ndi kukonda Mulungu na Baibo?
15 Usiku wakuti mawa aphedwa, Yesu anauza ophunzila ake kuti: “Ndikukupatsani lamulo latsopano, kuti muzikondana. Mmene ine ndakukondelani, inunso muzikondana. Mwakutelo, onse adzadziŵa kuti ndinu ophunzila anga, ngati mukukondana.”—Yoh. 13:34, 35.
16 Kukonda abale na alongo athu n’kogwilizana ndi kukonda kwathu Yehova. Ndipo n’zosatheka kukonda Mulungu ngati sitikonda abale athu. N’cifukwa cake mtumwi Yohane analemba kuti: “Amene sakonda m’bale wake amene amamuona, sangakonde Mulungu amene sanamuonepo.” (1 Yoh. 4:20) Kuwonjezela apo, kukonda Yehova ndi abale athu, kumagwilizana ndi kukonda Baibo. Takamba conco cifukwa kukonda coonadi kumatilimbikitsa kumvela na mtima wonse malamulo a m’Baibo akuti tizikonda Mulungu ndi abale athu.—1 Pet. 1:22; 1 Yoh. 4:21.
17. Ni zinthu ziti zimene tingacite zoonetsa kuti timakonda abale na alongo athu?
17 Ŵelengani 1 Atesalonika 4:9, 10. Ni zinthu ziti zimene tingacite zoonetsa kuti timakonda abale athu mumpingo? Tingathandize m’bale kapena mlongo wacikulile amene amavutika kuyenda popita kumisonkhano. Tingathandizenso mkazi wamasiye mwa kum’konzela zinthu zowonongeka panyumba. (Yak. 1:27) Timafunikanso kulimbikitsa ndi kutonthoza abale na alongo acikulile ndi acicepele omwe, amene ali na zothetsa nzelu, opsinjika maganizo, kapena amene akumana ndi mavuto ena. (Miy. 12:25; Akol. 4:11) Tikacita zimenezi, timaonetsa mwa zokamba ndi zocita zathu kuti timakondadi “abale ndi alongo athu m’cikhulupililo.”—Agal. 6:10.
18. N’ciani cingatithandize kuthetsa kusamvana ndi okhulupilila anzathu?
18 Baibo inakambilatu kuti anthu ambili ‘m’masiku otsiliza’ a dongosolo loipa lino la zinthu, adzakhala odzikonda ndi aumbombo. (2 Tim. 3:1, 2) Conco, ise monga Akhristu tifunika kucita khama kuti tizikonda kwambili Mulungu, coonadi, ndi anthu anzathu. N’zoona kuti nthawi zina tingasiyane maganizo pankhani zing’ono-zing’ono ndi okhulupilila anzathu. Komabe, ngati tiyesetsa kuthetsa mikangano m’njila yacikondi, onse mumpingo amapindula. (Aef. 4:32; Akol. 3:14) Conco, tisalole kuti cikondi cathu cizilale. M’malomwake, tiyeni tipitilize kukonda kwambili Yehova, Mau ake, ndi abale athu.