NSANJA YA MLONDA—YOPHUNZILA May 2018

Magazini ino ili na nkhani zophunzila wiki ya July 9-August 5, 2018.

MBILI YANGA

Poyamba N’nali Wosauka, Koma Lomba Nalemela

M’bale Samuel Herd anakulila m’banja losauka, koma lomba walemela kwambili mwauzimu kuposa mmene anali kuyembekezela.

Mtendele—Kodi Mungaupeze Bwanji?

Cifukwa cakuti tikukhala m’dziko loipa, tiyenela kucita khama kuti tikhale na mtendele. Mau a Mulungu angatithandize.

Yehova Amakonda Anthu Amene ‘Amabala Zipatso mwa Kupilila’

Tingafooke ngati tilalikila m’magawo amene anthu samvetsela uthenga wathu. Ngakhale n’conco, ise tonse tingathe kubala zipatso mu utumiki wathu.

Cifukwa Cake ‘Timapitiliza Kubala Zipatso’

Kukumbukila zifukwa zake timagwila nchito yolalikila n’kofunika kwambili.

M’dziŵeni Bwino Mdani Wanu

Ise timadziŵa bwino mphamvu zimene Satana ali nazo na njila zake za macenjela.

Acicepele—Cilimikani Polimbana ndi Mdyelekezi

Tonse tili pa nkhondo yauzimu. Maka-maka Akhristu acicepele angaoneke monga osatetezeka, koma ubwino wake ni wakuti avala zovala zonse zomenyela nkhondo.

Zokolola Zoculuka!

M’dela lina ku Ukraine, munthu mmodzi pa anthu 4 alionse ni wa Mboni za Yehova!