Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

M’dziŵeni Bwino Mdani Wanu

M’dziŵeni Bwino Mdani Wanu

“Tikudziŵa bwino ziwembu [za Satana].”—2 AKOR. 2:11.

NYIMBO: 150, 32

1. Mu Edeni, kodi Yehova anavumbula zinthu ziti zokhudza mdani wathu?

N’ZOONEKELATU kuti Adamu anali kudziŵa kuti njoka siingakambe. Conco, ayenela kuti anadziŵa kuti colengedwa camzimu n’cimene cinakamba na Hava kupitila mwa njoka. (Gen. 3:1-6) Adamu na Hava sanali kudziŵa zilizonse zokhudza colengedwa cimeneci. Olo zinali conco, mwadala Adamu anasankha kukana Atate wake wacikondi wakumwamba na kugwilizana ndi mngelo wosamudziŵayo potsutsa cifunilo ca Mulungu. (1 Tim. 2:14) Izi zitangocitika, Yehova anayamba kuvumbula zinthu zina zokhudza mdani ameneyu, amene anasoceletsa Adamu na Hava. Ndipo analonjeza kuti pamapeto pake, mngelo woipayu adzawonongedwa. Koma Yehova anacenjezanso kuti, kwa kanthawi, colengedwa cauzimu cimene cinakamba na Hava kupitila mwa njoka, cidzalimbana ndi anthu okonda Mulungu.—Gen. 3:15.

2, 3. Kodi zioneka kuti n’cifukwa ciani Mulungu sanavumbule zambili zokhudza Satana, Mesiya asanabwele?

2 Mwa nzelu zake, Yehova sanatiuze dzina leni-leni la mngelo amene anam’pandukila. * Komanso Mulungu sanaulule ngakhale dzina lolongosola zocita za mdani ameneyu, mpaka patapita zaka 2,500 kucokela pamene iye anapanduka mu Edeni. (Yobu 1:6) Ndipo ni mabuku atatu cabe a m’Malemba Aciheberi amene amachulako dzina lakuti Satana, limene limatanthauza “Wotsutsa.” Mabuku amenewa ni 1 Mbiri, Yobu, na Zekariya. N’cifukwa ciani Mulungu sanavumbule zambili zokhudza mdani ameneyu Mesiya asanabwele?

3 Mwacionekele, Yehova sanafune kuchukitsa Satana mwa kuuzila atumiki ake kulemba zambili zokhudza iye na zocita zake m’Malemba Aciheberi. Colinga cacikulu cimene Yehova anauzila anthu kulemba cigawo cimeneci ca Baibo, cinali cakuti adziŵikitse Mesiya na kutsogolela anthu ake kwa iye. (Luka 24:44; Agal. 3:24) Colinga cake citakwanilitsidwa komanso Mesiya atabwela, Yehova anamuseŵenzetsa pamodzi na ophunzila ake povumbula zambili zokhudza Satana na angelo amene anakhala ku mbali yake. * Kucita izi kunali koyenela, cifukwa Yesu na odzozedwa amene adzalamulila nawo pamodzi, ni amene Yehova adzawaseŵenzetsa pophwanya Satana na otsatila ake.—Aroma 16:20; Chiv. 17:14; 20:10.

4. N’cifukwa ciani sitiyenela kumuyopa maningi Mdyelekezi?

4 Mtumwi Petulo anachula Satana Mdyelekezi kuti “mkango wobangula,” ndipo Yohane anamuchula kuti “njoka,” komanso “cinjoka.” (1 Pet. 5:8; Chiv. 12:9) Koma sitiyenela kumuyopa maningi Mdyelekezi, cifukwa mphamvu zake zili na pothela. (Ŵelengani Yakobo 4:7.) Ku mbali yathu tili na Yehova, Yesu, na angelo okhulupilika. Mwa thandizo lawo, tingakwanitse kumutsutsa Satana. Ngakhale n’conco, tifunika kudziŵa mayankho pa mafunso atatu ofunika kwambili aya: Kodi mphamvu za Satana n’zazikulu bwanji? Kodi iye amaseŵenzetsa ciani pofuna kusoceletsa anthu? Nanga n’zinthu ziti zimene Satana sangakwanitse kucita? Pamene tikambilana mafunso amenewa, tidzaonanso zimene tingaphunzilepo.

KODI MPHAMVU ZA SATANA N’ZAZIKULU BWANJI?

5, 6. N’cifukwa ciani maboma a anthu sangakwanitse kutsiliza mavuto aakulu amene ise anthu timakumana nawo?

5 Gulu lalikulu ndithu la angelo linakhala ku mbali ya Satana popandukila Mulungu. Cigumula cisanacitike, Satana anasonkhezela ena mwa angelo amenewa kubwela pa dziko lapansi na kuyamba kugonana ndi akazi. Baibo imafotokoza zimenezi mophiphilitsa mwa kunena kuti cinjoka cinakokolola gawo limodzi mwa magawo atatu a nyenyezi zakumwamba. (Gen. 6:1-4; Yuda 6; Chiv. 12:3, 4) Pamene angelowo anacoka m’banja la Mulungu, anayamba kulamulidwa na Satana. Koma angelo opanduka amenewa sali gulu laciwawa lopanda dongosolo. Satana anakhazikitsa ufumu wake mokopelako Ufumu wa Mulungu, ndipo anadziika mfumu. Kumene aliliko, Satana analinganiza magulu a ziŵanda n’kupanga maboma osaoneka, ndipo anapatsa ziŵandazo mphamvu, na kuziika kukhala olamulila dziko.—Aef. 6:12.

6 Kupitila m’gulu lake la ziŵanda, Satana ali na mphamvu pa maboma onse a anthu. Mfundo imeneyi inaonekela bwino pamene iye anaonetsa Yesu “maufumu onse a padziko lapansi,” na kumuuza kuti: “Ndikupatsani ulamulilo pa maufumu onsewa ndi ulemelelo wawo wonse, cifukwa unapelekedwa kwa ine. Ndikhoza kuupeleka kwa aliyense amene ndakonda kum’patsa.” (Luka 4:5, 6) Olo kuti pali cisonkhezelo coipa ca Satana, maboma ambili amayesako kucitila nzika zawo zinthu zabwino. Ndipo olamulila ena amakhala na zolinga zabwino. Komabe, palibe boma la anthu kapena wolamulila aliyense waumunthu amene angakwanitse kutsiliza mavuto aakulu amene ise anthu timakumana nawo.—Sal. 146:3, 4; Chiv. 12:12.

7. Kodi Satana amaseŵenzetsa bwanji maboma, cipembedzo conama, na magulu a zamalonda posoceletsa anthu? (Onani pikica kuciyambi.)

7 Satana na ziŵanda amaseŵenzetsa maboma, cipembedzo conama, komanso anthu oyendetsa zamalonda ‘posoceletsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu.’ (Chiv. 12:9) Poseŵenzetsa cipembedzo conama, iye amafalitsa mabodza ponena za Yehova. Kuwonjezela apo, Mdyelekezi amacita ciliconse cotheka kuti aiwalitse anthu ambili dzina la Mulungu. (Yer. 23:26, 27) Zotulukapo zake n’zakuti anthu oona mtima asoceletsedwa, ndipo mosadziŵa amalambila ziŵanda m’malo molambila Mulungu. (1 Akor. 10:20; 2 Akor. 11:13-15) Cinanso, Satana amafalitsa mabodza poseŵenzetsa anthu oyendetsa zamalonda. Mwacitsanzo, iwo amalimbikitsa mfundo yakuti cuma na ndalama zambili ndiye zimapatsa munthu cimwemwe ceni-ceni. (Miy. 18:11) Anthu amene amakhulupilila bodza limeneli amaseŵenzetsa moyo wawo wonse kutumikila “Cuma” m’malo motumikila Mulungu. (Mat. 6:24) M’kupita kwa nthawi, kukonda kwawo Cuma kumatsiliza cikondi cimene anali naco pa Mulungu.—Mat. 13:22; 1 Yoh. 2:15, 16.

8, 9. (a) Ni mfundo ziŵili ziti zimene taphunzilapo pa citsanzo ca Adamu, Hava, na angelo opanduka? (b) Kodi kudziŵa mphamvu za Satana kuli na ubwino wanji?

8 Pa zitsanzo zimene takambilana, ca Adamu, Hava, na angelo opanduka, tiphunzilapo mfundo ziŵili zofunika kwambili. Yoyamba ni yakuti, pali mbali ziŵili cabe ndipo tifunika kusankhapo mbali imodzi. Kaya kukhalabe wokhulupilika kwa Yehova kapena kukhala ku mbali ya Satana. (Mat. 7:13) Yaciŵili, anthu amene amasankha kukhala ku mbali ya Satana sapindula kweni-kweni. Mwacitsanzo, Adamu na Hava atapandukila Mulungu, anakhala na ufulu wodziikila okha miyezo ya cabwino na coipa. Nazonso ziŵanda zinakhala na mphamvu yolamulila maboma a anthu. (Gen. 3:22) Koma zimene munthu amataya akasankha kukhala ku mbali ya Satana, nthawi zonse zimakhala zambili kuposa zimene angapeze kwa Satana.—Yobu 21:7-17; Agal. 6:7, 8.

9 Kodi kudziŵa mphamvu za Satana kuli na ubwino wanji? Kumatithandiza kukhala na kaonedwe koyenela ka maboma a anthu. Komanso kumatilimbikitsa kugwila nchito yolalikila. Tidziŵa kuti Yehova amafuna kuti tizilemekeza maboma. (1 Pet. 2:17) Ndiponso amafuna kuti tizimvela malamulo a boma malinga ngati sawombana na malamulo ake. (Aroma 13:1-4) Ngakhale n’conco, timadziŵa kuti sitifunika kuloŵelela m’zandale mwa kukondela cipani kapena wolamulila winawake. (Yoh. 17:15, 16; 18:36) Cinanso, tidziŵa kuti Satana amafuna kuipitsa mbili ya Yehova na kuiŵalitsa anthu dzina lake. Kudziŵa izi, kumatisonkhezela kuphunzitsa ena mwakhama coonadi ponena za Mulungu wathu. Timanyadila kudziŵika na dzina lake komanso kuliseŵenzetsa, podziŵa kuti kukonda Mulungu kumabweletsa madalitso oculuka kuposa kukonda ndalama na zinthu zina.—Yes. 43:10; 1 Tim. 6:6-10.

KODI SATANA AMASEŴENZETSA CIANI POFUNA KUSOCELETSA ANTHU?

10-12. (a) N’kuthenga kuti Satana anacita ciani poseŵenzetsa nyambo imene anakopa nayo anzake? (b) Kodi tiphunzilapo ciani pa zimene zinacitikila angelo ena ambili?

10 Satana amaseŵenzetsa njila zamacenjela pofuna kusoceletsa anthu. Mwacitsanzo, amaseŵenzetsa nyambo pokopa anthu kuti azicita zofuna zake. Komanso, amaopseza anthu kuti amugonjele.

11 Ganizilani mmene Satana anaseŵenzetsela nyambo yake pokopa gulu la angelo anzake. Iye ayenela kuti anaphunzila kacitidwe kawo ka zinthu kwa nthawi yaitali akalibe kuwakopa kuti akhale ku mbali yake. Pamene ena mwa angelowo anakopeka na kubwela pa dziko lapansi kudzacita ciwelewele na akazi, akaziwo anabala vimphona vimene vinayamba kupondeleza mtundu wa anthu. (Gen. 6:1-4) Kuwonjezela pa kukopa angelowo na khalidwe la ciwelewele, mwina Satana anawakopanso mwa kuwalonjeza kuti adzakhala na mphamvu yolamulila anthu onse. Mwina colinga cake cinali cakuti alepheletse kubwela kwa ‘mbewu ya mkazi,’ imene Mulungu analonjeza. (Gen. 3:15) Mulimonsemo, pa nthawiyo Yehova analepheletsa zolinga na zoyesa-yesa za Satana ndi angelo opandukawo mwa kubweletsa Cigumula.

Satana Amafuna Kutikopa (Onani palagilafu 12, 13) khalidwe la ciwelewele, kunyada, na zamizimu

12 Kodi tiphunzilapo ciani pa zimene zinacitikila angelo amenewa? Sitifunika kudelela msampha wa ciwelewele kapena kuopsa kwa khalidwe la kunyada. Kumbukilani kuti kwa zaka zambili-mbili, angelo amene anakhala ku mbali ya Satana anali kutumikila pamaso pa Mulungu. Ngakhale kuti anali kutumikila m’malo otetezeka mwauzimu, analola zilakolako zoipa kuzika mizu m’mitima yawo na kukula. Mofananamo, mwina tatumikila Mulungu m’gulu lake kwa zaka zambili. Koma ngakhale tili m’malo otetezeka mwauzimu, zilakolako zoipa zikhoza kuzika mizu m’mitima yathu. (1 Akor. 10:12) Conco, n’kofunika kwambili kuti nthawi zonse tizisanthula mtima wathu, kukaniza maganizo oipa, na kupewa mzimu wonyada.—Agal. 5:26; ŵelengani Akolose 3:5.

13. Kodi nyambo ina imene Satana amaseŵenzetsa ni iti? Nanga tingaipewe bwanji?

13 Nyambo ina yokopa kwambili imene Satana amaseŵenzetsa ni zamizimu. Masiku ano, iye amalimbikitsa anthu kucita cidwi na ziŵanda poseŵenzetsa zipembedzo zonama na zosangalatsa zosiyana-siyana. Zinthu monga mafilimu, maseŵela a pa kompyuta, na zosangalatsa zina, zimalengetsa anthu kuona ngati zamizimu n’zokondweletsa. Kodi tingapewe bwanji kukodwa mu msampha umenewu? Sitiyenela kuyembekezela kuti gulu la Mulungu lidzacita kutindandalikila zosangalatsa zoyenela na zosayenela. Aliyense payekha afunika kuphunzitsa cikumbumtima cake kuti cizimutsogolela mogwilizana na miyezo ya Mulungu. (Aheb. 5:14) Komanso, tidzakwanitsa kupanga zosankha mwanzelu ngati titsatila malangizo a mtumwi Paulo akuti cikondi cathu pa Mulungu siciyenela ‘kukhala caciphamaso.’ (Aroma 12:9) Tingadzifunse kuti: ‘Kodi kucita zosangalatsa zimenezi kudzaonetsa kuti ndine wacinyengo? Ngati anthu amene nimaphunzila nawo Baibo kapena amene nimacitako maulendo obwelelako aonako zosangalatsa zanga, kodi angaone kuti nimacitadi zimene nimawaphunzitsa?’ Ngati tiyesetsa kucita zinthu mogwilizana na zimene timaphunzitsa, tidzakhala otetezeka ku misampha ya Satana.—1 Yoh. 3:18.

Satana amatiyofya (Onani palagilafu 14) Ciletso ca boma, Kutunthiwa na anzathu a kusukulu, Kutsutsidwa ndi a m’banja lathu

14. Kodi Satana angayese bwanji kutiopseza? Nanga n’ciani cingatithandize kupilila?

14 Kuwonjezela pa kuseŵenzetsa nyambo, Satana amatiyofya kuti ticite zinthu zosakhulupilika pamaso pa Yehova. Mwacitsanzo, angasonkhezele maboma kuti aletse nchito yathu yolalikila. Kapena angasonkhezele anzathu kunchito kapena kusukulu kuti azitiseka cifukwa cotsatila makhalidwe abwino a m’Baibo. (1 Pet. 4:4) Angasonkhezelenso abululu athu amene amatikonda kuti azitiletsa kupita ku misonkhano. (Mat. 10:36) N’ciani cingatithandize kupilila? Coyamba, sitiyenela kudabwa na mavuto aconco, cifukwa Satana ali pa nkhondo na ise. (Chiv. 2:10; 12:17) Cina, tifunika kukumbukila nkhani yaikulu imene imalengetsa kuti tizikumana na mavuto amenewa. Paja Satana amakamba kuti timatumikila Yehova kokha ngati zinthu zili bwino. Amakambanso kuti ngati tingakumane na mavuto, tingamusiye Mulungu. (Yobu 1:9-11; 2:4, 5) Koposa zonse, tifunika kudalila Yehova kuti atipatse mphamvu kuti tipilile. Kumbukilani kuti iye analonjeza kuti sadzatisiya.—Aheb. 13:5.

N’ZINTHU ZITI ZIMENE SATANA SANGAKWANITSE KUCITA?

15. Kodi Satana angatikakamize kucita zinthu zimene sitifuna? Fotokozani.

15 Satana sangakwanitse kukakamiza anthu kucita zimene iwo safuna. (Yak. 1:14) Mosadziŵa, anthu ambili amacita zinthu mogwilizana ndi colinga cake. Koma akaphunzila coonadi, aliyense payekha amakhala na ufulu wodzisankhila amene afuna kum’tumikila. (Mac. 3:17; 17:30) Ngati tatsimikiza mtima kucita cifunilo ca Mulungu, Satana sangakwanitse kutitaitsa cikhulupililo cathu.—Yobu 2:3; 27:5.

16, 17. (a) N’zinthu zina ziti zimene Satana na ziŵanda zake sangakwanitse kucita? (b) N’cifukwa ciani sitiyenela kuyopa kupemphela mokweza mau kwa Yehova?

16 Palinso zina zimene Satana na ziŵanda zake sangakwanitse kucita. Mwacitsanzo, palibe paliponse m’Malemba pamene paonetsa kuti iwo angakwanitse kudziŵa zimene zili m’maganizo kapena mumtima wa munthu. Ni Yehova na Yesu cabe amene amakwanitsa kucita zimenezi. (1 Sam. 16:7; Maliko 2:8) Nanga bwanji tikamalankhula kapena kupemphela mokweza mau? Kodi tiyenela kuyopa kuti Mdyelekezi na ziŵanda zake adzamvetsela zimene tikamba m’pemphelo na kuzigwilitsila nchito polimbana nase? Iyai. Sitiyopa kucita nchito zabwino mu utumiki wa Yehova poganiza kuti Satana adzationa. Conco, sitifunikanso kuyopa kupemphela mokweza poganiza kuti iye akhoza kutimvela. Ndipo m’Baibo muli zitsanzo zambili za atumiki a Mulungu amene anapemphela mokweza mau, koma palibe ciliconse coonetsa kuti iwo anayopa kuti Mdyelekezi akhoza kuwamvela. (1 Maf. 8:22, 23; Yoh. 11:41, 42; Mac. 4:23, 24) Ngati tiyesetsa kukamba na kucita zinthu mogwilizana na cifunilo ca Mulungu, Yehova sadzalola Mdyelekezi kutiwononga kothelatu.—Ŵelengani Salimo 34:7.

17 Tifunika kum’dziŵa bwino mdani wathu, koma sitifunika kumuyopa. Mwa thandizo la Yehova, ngakhale ise anthu opanda ungwilo tikhoza kum’gonjetsa Satana. (1 Yoh. 2:14) Ngati timutsutsa, iye adzatithaŵa. (Yak. 4:7; 1 Pet. 5:9) Koma Satana amakondanso kuukila anthu acicepele. N’ciani maka-maka cimene acicepele angacite kuti asagonje polimbana na Mdyelekezi? M’nkhani yotsatila, tidzakambilana funso imeneyi.

^ par. 2 Baibo imaonetsa kuti angelo ali na maina awo. (Ower. 13:18; Dan. 8:16; Luka 1:19; Chiv. 12:7) Popeza kuti Yehova anapatsa dzina nyenyezi iliyonse (Sal. 147:4), n’zosakayikitsa kuti angelo onse ali na maina, kuphatikizapo mngelo amene anakhala Satana.

^ par. 3 Dzina lakuti Satana limachulidwa maulendo 18 cabe m’Malemba Aciheberi. Koma m’Malemba Acigiriki Acikhristu limachulidwa koposa ka 30.