Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MBILI YANGA

Poyamba N’nali Wosauka, Koma Lomba Nalemela

Poyamba N’nali Wosauka, Koma Lomba Nalemela

N’nabadwila m’nyumba yamitengo ya cipinda cimodzi m’tauni yaing’ono yochedwa Liberty, ku Indiana, m’dziko la United States. Pamene n’nabadwa, makolo anga anali kale ndi ana atatu, mkulu wanga mmodzi na azilongosi anga aŵili. M’kupita kwa nthawi, amayi anabeleka ang’ono anga aŵili na mlongosi wanga mmodzi.

Nyumba yamitengo imene n’nabadwilamo

PAMENE n’nali pa sukulu, zinthu zambili sizinasinthe. Anthu amene n’nayamba nawo giledi 1 na amenenso n’natsiliza nawo sukulu. Anthu ambili a m’tauniyo n’nali kuwadziŵa maina awo, ndipo nawonso anali kunidziŵa.

N’nali mmodzi wa ana 7, ndipo pamene n’nali mnyamata n’naphunzila nchito zambili zaulimi

Tauni ya Liberty inali yozungulilidwa na mafamu ang’ono-ang’ono, ndipo alimi ambili anali kulima milisi. Pamene n’nabadwa, atate anali kuseŵenza kwa mmodzi wa alimiwo. Nili mnyamata, n’naphunzila kuyendetsa thilakita na nchito zina zaulimi.

Atate anali acikulile kale pamene n’nabadwa. Panthawiyo, iwo anali na zaka 56, ndipo amayi anali na zaka 35. Atate anali munthu wocepa thupi, koma wathanzi ndi wamphamvu. Iwo anali kukonda kugwila nchito zovuta. Ndipo ise tonse anatiphunzitsa kukonda nchito. Atate sanali kupeza ndalama zambili, koma anali kuonetsetsa kuti tili na pogona, zovala, na cakudya. Anali kutisamalila nthawi zonse. Iwo anamwalila na zaka 93. Amayi anamwalila na zaka 86. Onse sanatumikilepo Yehova. Pa abale anga onse, pali mng’ono wanga mmodzi amene watumikila mokhulupilika monga mkulu kungocokela pamene makonzedwe okhala na akulu pa mpingo anayamba m’ma 1970.

UMOYO WANGA PAMENE N’NALI WACICEPELE

Amayi anali munthu wokonda kupemphela. Anali kupita nase ku chechi ya Baptist pa Sondo paliponse. Nthawi yoyamba pamene n’namvela za ciphunzitso ca Utatu, n’nali na zaka 12. Pofuna kudziŵa zambili, n’nafunsa amayi kuti: “Zingatheke bwanji Yesu kukhala Mwana komanso Atate pa nthawi imodzi?” Iwo anayankha kuti: “Mwana wanga, n’cisinsi. Sitingazimvetsetse.” Kwa ine, zinalidi zovuta kumvetsa. Olo zinali conco, n’tafika zaka 14, n’nabatizika mu kamtsinje kapafupi. Ananimiza katatu, monga cizindikilo ca Utatu.

Mu 1952 Pamene n’nali na zaka 17, nikalibe kungena usilikali

Nili ku sekondale, n’nali na mnzanga amene anali katswili wa nkhonya. Iye ananituntha kuti niyambe maseŵela a nkhonya. N’nayambadi kuphunzila, ndipo n’naloŵa m’gulu la nkhonya lochedwa Golden Gloves. Zinali kunivuta cakuti n’taphunzilako maulendo oŵelengeka, n’naleka. Patapita nthawi, n’naloŵa m’gulu la asilikali a United States, ndipo ananitumiza ku Germany. Akulu-akulu kumeneko anan’tumiza ku sukulu yapamwamba ya maphunzilo a usilikali cifukwa coona kuti n’nali na luso lokhala mtsogoleli wabwino. Iwo anali kufuna kuti nchito yanga ikhale ya usilikali. Koma ine sin’naikonde nchitoyi. Conco, n’tatsiliza zaka ziŵili, mu 1956 n’naileka. Koma posapita nthawi itali, n’naloŵa usilikali wa mtundu wina.

1954 mpaka 1956, N’natumikila m’gulu la asilikali a United States kwa zaka ziŵili

CIYAMBI CA UMOYO WATSOPANO

Nikalibe kuphunzila coonadi, n’nali na maganizo olakwika ponena za mmene mwamuna weni-weni afunika kukhalila. N’nali kutengela maganizo olakwika a anthu amene n’nali kuwaona m’mafilimu na anthu ena a m’dela lathu. N’nali kuona kuti anthu amene amalalikila si amuna eni-eni. Koma n’nayamba kuphunzila zinthu zina zimene zinasintha kwambili umoyo wanga. Tsiku lina, pamene n’nali kuyenda m’tauni pa motoka yanga yofiila, atsikana aŵili ananibaibitsa. Anali azimulamu anga, ndipo anali a Mboni za Yehova. M’mbuyomo, iwo ananipatsako magazini a Nsanja ya Mlonda na Galamukani! Koma Nsanja ya Mlonda sin’nali kuikonda cifukwa coona ngati yovuta kuimvetsetsa. Koma panthawiyi, ananiitanila ku Phunzilo la Buku la Mpingo, kumene anali kukambilana na kuphunzila zokhudza Baibo. Phunziloli linali kucitikila ku nyumba kwawo. N’nawauza kuti nidzaganizilapo. Iwo anamwetulila na kunifunsa kuti “Mudzabweladi?” N’nawauza kuti “Inde, nidzabwela.”

N’nadziimba mlandu cifukwa colonjeza kuti nidzapita, koma n’naona kuti nifunika kupitabe. Conco, m’madzulo tsiku limenelo n’nayendadi. Nili kumeneko, n’nacita cidwi ngako ndi ana. N’nadabwa poona kuculuka kwa zimene anali kudziŵa zokhudza Baibo. Olo kuti n’nali kuyenda ku chechi na amayi anga mobweleza-bweleza pa Sondo, n’nali kudziŵa zocepa cabe zokhudza Baibo. Kuyambila nthawiyi, n’nakhala na colinga cophunzila zambili zokhudza Baibo. N’navomela phunzilo la Baibo. N’tangoyamba, n’naphunzila kuti dzina leni-leni la Mulungu Wamphamvuyonse ni Yehova. Zaka zingapo m’mbuyomo, pamene n’nafunsa amayi za Mboni za Yehova, ananiuza kuti, “Amalambila munthu winawake wakale wochedwa Yehova.” Koma n’tayamba kuphunzila, n’naona kuti maso anga ayamba kutseguka.

N’napita patsogolo mwamsanga cifukwa n’nadziŵa kuti napeza coonadi. N’nabatizika mu March 1957. Apa n’kuti papita miyezi 9 cabe kucokela pamene n’napezeka pa phunzilo ya buku ija. Ndipo kaonedwe kanga ka zinthu mu umoyo kanasinthilatu. Nikaganizila za umoyo wanga wakale, nimakondwela cifukwa Baibo yanithandiza kudziŵa mmene mwamuna weni-weni afunika kukhalila. Mwacitsanzo, Yesu anali wangwilo komanso wamphamvu cakuti kulibe mwamuna wamphamvu amene angalingane naye. Ngakhale n’conco, iye sanali kucita ndewo, koma ‘analola kusautsidwa’ monga mmene Baibo inakambila. (Yes. 53:2, 7) N’naphunzila kuti wotsatila weni-weni wa Yesu, “ayenela kukhala wodekha kwa onse.”—2 Tim. 2:24.

Caka cotsatila ca 1958, n’nayamba upainiya. Koma posakhalitsa, n’naima upainiyawo kwa kanthawi. Cifukwa ciani? N’naganiza zokwatila Gloria, mmodzi wa atsikana aja amene ananiitanila ku phunzilo ya buku. Siniona kuti n’nalakwitsa kucita zimenezi. Gloria anali ciphadzuwa, ndipo na manje ni ciphadzuwa. Kwa ine, iye ni wamtengo wapatali kuposa mwala uliwonse wa dayamondi, ndipo ndine wokondwa ngako kuti tinakwatilana. Lekani akuuzeni yekha zina zokhudza umoyo wake:

“Ndine mmodzi mwa ana 17. Amayi anali Mboni yokhulupilika. Iwo anamwalila nili na zaka 14. Apa m’pamene atate anayamba kuphunzila Baibo. Amayi atamwalila, atate anapanga makonzedwe apadela na ahedi a pa sukulu pathu. Panthawiyo, mkulu wanga anali pafupi kutsiliza maphunzilo a ku sekondale, ndipo atate anapempha ahediwo kuti mkulu wangayo na ine tiziyenda ku sukulu pa masiku osiyana. Colinga cinali cakuti wina akapita ku sukulu, wina azitsala pa nyumba kusamalila ana na kukonza cakudya cam’madzulo, kuti atate pobwela ku nchito azipeza zonse zili m’malo. Tica wamkuluyo anavomela, ndipo izi n’zimene zinali kucitika mpaka mkulu wanga anatsiliza sukulu. Mabanja aŵili a Mboni na amene anali kutiphunzitsa Baibo anafe, cakuti 11 a ife tinakhala Mboni. Ulaliki n’nali kuukonda ngako, olo kuti mwacibadwa ndine wamanyazi. Amuna anga akhala akunithandiza kulimbana ndi vuto imeneyi.”

Ine na Gloria tinakwatilana mu February, 1959. Tinakondwela kucita upainiya pamodzi. Mu July caka cimeneco, tinafunsila utumiki wa pa Beteli, cifukwa tinali kulaka-laka kukatumikila ku likulu. M’bale wokondedwa, dzina lake Simon Kraker anatifunsa mafunso kuti aone ngati tinali oyenelela. Iye anatiuza kuti pa nthawiyo ku Beteli sanali kuitana anthu amene ali pabanja. Izi sizinathetse cikhumbo cathu cokatumikila pa Beteli, koma panatenga nthawi yaitali kuti tipeze mwayi wa utumiki umenewu.

Tinalembela kalata ku likulu, yopempha kuti atitumize ku dela losoŵa. Potiyankha, anangotiuza kuti tipite ku Pine Bluff, m’dela la Arkansas. M’masiku amenewo, ku Pine Bluff kunali mipingo iŵili, wina wa azungu na wina wa anthu akuda. Ise tinatumiziwa ku mpingo wa anthu akuda, umene unali na ofalitsa 14 cabe.

KUPILILA VUTO LA KUSANKHANA MITUNDU

Mwina mungadabwe kuti, ‘N’cifukwa ciani m’mipingo ya Mboni za Yehova munali tsankho?’ Kuyankha mwacidule, cifukwa cinali cakuti zinthu zinali zovuta ngako nthawi imeneyo. Panali malamulo oletsa anthu a mitundu yosiyana kucitila zinthu pamodzi, ndiponso anthu anali aciwawa kwambili. Conco, m’madela ambili, abale a mitundu yosiyana sanali kusonkhana pamodzi poyopa kuti Nyumba ya Ufumu idzawonongedwa. Zaconco zinali kucitika. Ngati Mboni zacikuda zilalikila ku nyumba ndi nyumba m’dela lokhala azungu, zinali kumangidwa komanso nthawi zambili zinali kumenyedwa. Conco, pofuna kuti nchito yolalikila isasokonezeke, tinali kutsatila malamulo, tili na cikhulupililo cakuti zinthu zidzasintha m’tsogolo.

Mu ulaliki, tinali kukumana na mavuto osiyana-siyana. Polalikila m’gawo la anthu acikuda, nthawi zina tinali kugogoda pa nyumba ya azungu mosadziŵa. Zikakhala conco, mwamsanga tinali kufunika kuganiza zocita, kaya kupepesa na kucokapo kapena kuwalalikila mwacidule. M’masiku amenewo, ni mmene zinthu zinalili m’madela ena.

Tinali kufunika kuseŵenza mwakhama kuti tizipeza zocilikizila umoyo wathu pocita upainiya. Tikagwila nchito, nthawi zambili anali kutilipila madola atatu pa tsiku. Mkazi wanga anali kugwila nchito pa nyumba zingapo. Ine n’naloledwa kumuthandiza kusamalila pa nyumba imodzi n’colinga cakuti azitsiliza mwamsanga nchitoyo. Tinali kupatsiwa cakudya ca masana, cimene ine na mkazi wanga tinali kudya tikalibe kubwelela ku nyumba. Wiki iliyonse, mkazi wanga anali kugwila nchito yochisa zovala za banja lina lake. Ine n’nali kugwila nchito za panja, kutsuka mawindo, na nchito zina. Pa nyumba ina ya mzungu, tinali kutsuka mawindo. Mkazi wanga Gloria anali kutsuka mkati, ine n’nali kutsuka kunja. Tinali kucomelela, conco anali kutipatsa cakudya ca masana. Gloria anali kudyela mkati koma payekha, ndipo ine n’nali kudyela panja m’galaji. Kwa ine, malo odyela analibe kanthu. Cakudya cimene anali kutipatsa cinali cabwino. Anthu a m’banja limenelo anali okoma mtima, koma anali kungotengela zocita za anthu ambili a pa nthawiyo. Nikumbukila zimene zinacitika nthawi ina pamene tinaima pa filing’i sitesheni. Pambuyo pothila mafuta m’motoka yathu, n’napempha kwa wanchito wa pamenepo kuti mkazi wanga aseŵenzetseko toileti ya pa malowo. Iye anangoniyang’anitsitsa mwaukali na kukamba kuti, “Ni yokhoma!”

ANATICITILA ZINTHU ZABWINO ZIMENE SITIDZAIŴALA

Mosiyana na zimenezi, tinali kukondwela ngako kukhala na abale, komanso ulaliki tinali kuukonda. Pamene tinafika ku Pine Bluff, tinayamba kukhala ku nyumba kwa m’bale amene anali mtumiki wa mpingo pa nthawiyo. Mkazi wake sanali Mboni, ndipo mkazi wanga anayamba kuphunzila naye Baibo. Inenso n’nayamba kuphunzila na mwana wawo wamkazi pamodzi na mwamuna wake. Mwanayo na amayi ake, onse anasankha kutumikila Yehova ndipo anabatizika.

Tinalinso na anzathu mumpingo wa azungu. Anali kutitenga kuti tikadye nawo cakudya camadzulo, koma anali kucita izi kukafipa. Pa nthawiyo, gulu lolimbikitsa tsankho na ciwawa, lochedwa Ku Klux Klan (KKK), linali lamphamvu maningi. Nikumbukila kuti usiku wina pa tsiku la mwambo wa Halloween, n’naona mwamuna wina ali pa khonde pa nyumba yake atavala malaya oyela na cisoti, monga mmene anthu a KKK anali kuvalila. Koma izi sizinalepheletse abale kuticitila zabwino. Mwacitsanzo, caka cina m’malanga, tinasoŵa ndalama zoyendela kupita ku msonkhano wacigawo. M’bale wina anavomela kugula motoka yathu kuti tipeze ndalama zoyendela. Tsiku lina, patapita mwezi umodzi, tinalema ngako pambuyo poyenda ku nyumba ndi nyumba kukacititsa maphunzilo a Baibo m’nyengo yotentha imeneyo. Koma tinadabwa kwambili titafika ku nyumba. Tinapeza motoka yathu ili pa nyumba. Pa gilasi ya patsogolo panali mau akuti “Tengani motoka yanu. Nakubwezelani monga mphatso. Ndine m’bale wanu.”

Palinso zinthu zina zabwino zimene munthu wina anan’citila zimene sinidzaiŵala. Mu 1962, ananiitana ku Sukulu ya Utumiki wa Ufumu ku South Lansing, mu New York. Inali sukulu ya mwezi wathunthu ya akulu, oyang’anila madela, na oyang’anila zigawo. Koma pa nthawiyo, sin’nali kuseŵenza cakuti zinali zonivuta kupeza ndalama zoyendela. Ngakhale n’conco, kampani ina ya zamafoni ku Pine Bluff inali itanifunsa mafunso kuti inilembe nchito. Nikanalembedwa nchitoyo, sembe n’nakhala munthu woyamba wakuda pa kampaniyo. Pambuyo pake, ananiuza kuti adzanilemba. Kodi n’nakacita ciani? N’nalibe ndalama zoyendela ku New York. N’taganizilapo mwakuya, n’naona kuti cili bwino nisapite ku sukulu koma niyambe nchito. Koma pamene n’nali kukonzekela kuti nilembe kalata yonena kuti sinidzabwela ku sukulu, panacitika cinthu cina cosaiŵalika.

Mlongo wina wa mumpingo wathu, amene mwamuna wake sanali Mboni, anabwela kunyumba kwathu m’mamaŵa na kunipatsa emvulupu. Munali ndalama zambili. Mlongoyo na ana ake anali kuuka kuseni-seni kukacita pisiweki yolima m’munda wa thonje kuti apeze ndalama zakuti nikayendele ku New York. Iye anati, “Yendani ku sukulu mukaphunzile zambili, kuti mukadzabwela mudzatiphunzitse!” Pambuyo pake, n’napempha ku kampani ya zamafoni ija kuti nikayambe kuseŵenza pambuyo pa mawiki 5. Koma iwo anakana kwamtu wagalu. Zimenezo sin’nade nazo nkhawa cifukwa n’nali n’tasankha kale zocita. Ndine wokondwa kuti sin’nayambe nchitoyo.

Lomba lekani Gloria afotokozeko mmene anali kumvelela pamene tinali kutumikila ku Pine Bluff: “Gawo la kumeneko n’nalikonda ngako! N’nali na maphunzilo okwana 15 kapena kuposelapo. Conco, tinali kucita ulaliki wa ku nyumba ndi nyumba m’maŵa, ndipo m’madzulo tinali kucititsa maphunzilo a Baibo. Nthawi zina tinali kukomboka 23:00hrs usiku. N’nali kukondwela maningi na ulaliki! Nikanakonda kukhalabe mu utumiki umenewo. Ndipo kukamba zoona, sin’nali kufuna kuti ticoke mu utumiki umenewo na kuyamba nchito yoyendela dela. Koma Yehova anali nase na colinga cinacake.” Mwakamba zoona.

KUTUMIKILA MONGA WOYANG’ANILA WOYENDELA

Pamene tinali kucita upainiya ku Pine Bluff, tinafunsila upainiya wapadela ku Beteli. Tinali kuyembekezela kuti adzatiyankha mwamsanga cifukwa woyang’anila cigawo wathu anali kufuna kuti tikacilikize mpingo wa ku Texas, tili monga apainiya apadela. Tinali kuona kuti utumiki umenewo udzakhala wokondweletsa. Conco, tinayembekezela kwa nthawi yaitali yankho yocoka ku Beteli, koma tinali kungopeza kuti m’bokosi ya makalata mulibe ciliconse. Patapita nthawi, kalata inabwela, ndipo anatipatsa utumiki woyendela dela. Izi zinacitika mu January, 1965. Pa nthawiyo, nayenso M’bale Leon Weaver, amene lomba ni mgwilizanitsi wa Komiti ya Nthambi ya ku United States anaikidwa kukhala woyang’anila dela.

N’nali kuyopa kukhala woyang’anila dela. Pafupi-fupi caka cimodzi m’mbuyomo, M’bale James A. Thompson, Jr., amene anali woyang’anila cigawo anapenda ziyenelezo zanga kuti aone ngati n’nali woyenelela kukhala wadela. Mokoma mtima, iye ananifotokozela mbali zimene n’nafunika kuwongolela, komanso maluso amene woyang’anila dela wabwino amafunika kukhala nawo. Pambuyo potumikila m’dela kwa nthawi yocepa cabe, n’naona kuti uphungu wake unali wofunikadi. N’taikidwa pa udindowo, M’bale Thompson ndiye anali woyang’anila wacigawo woyamba kutumikila naye. N’naphunzila zambili kwa m’bale wauzimu komanso wokhulupilika ameneyo.

Nimayamikila maningi thandizo limene n’nalandila kwa abale okhulupilika

M’masiku amenewo, woyang’anila dela sanali kuphunzitsidwa kwa nthawi itali. Ine n’natumikila kwa wiki imodzi na wadela n’kumaona mmene iye anali kucezetsela mpingo. Ndiyeno, wiki yokonkhapo, ine n’nacezetsa mpingo wina ndipo wadelayo anali kuniyang’anila. Iye ananipatsa malangizo na kunifotokozela mfundo zina zothandiza. Koma kucokela pa nthawiyi, tinayamba kuyenda tekha. Nikumbukila n’nauza mkazi wanga kuti, “Niona kuti acoka mwamsanga.” M’kupita kwa nthawi, n’nazindikila mfundo ina yofunika yakuti, nthawi zonse pamakhala abale ofikapo amene angakuthandize malinga ngati uwalola kutelo. Nimayamikilabe thandizo limene n’nalandila kwa abale okhwima mwauzimu monga J. R. Brown, amene anali woyang’anila dela, na Fred Rusk amene anali kutumikila pa Beteli.

Kusankhana mitundu kunali kofala pa nthawiyo. Tsiku lina, gulu la KKK linacita zionetselo m’tauni ya Tennessee, kumene tinali kucezetsa mpingo. Komanso, nthawi ina, ine na kagulu kathu ka ulaliki tinapita ku lesitilanti kukadya cakudya pa nthawi yopumula. Tili kumeneko, n’nanyamuka kupita ku toileti. Ndipo n’naona munthu wina woyofya m’maonekedwe akunikonkha, wokhala na zolemba-lemba pakhungu mofanana na anthu amene anali kudana ndi anthu akuda. Koma m’bale wina waciyela anatikonkha. Iye anali wamkulu ndi wamphamvu kuposa ine na munthu winayo. M’baleyo anafunsa kuti, “Kodi zonse zili bwino M’bale Herd?” Munthuyo anacoka mwamsanga popanda kuseŵenzetsa toiletiyo. Kwa zaka zambili, naona kuti ceni-ceni cimene cimacititsa anthu kusankhana si kusiyana kwa khungu ayi. Koma ucimo wocokela kwa Adamu, umene tonsefe tinatengela. Naonanso kuti m’bale ni m’bale ndithu, kaya akhale wakuda kapena mzungu, ndipo angathe kukufela pakakhala pofunikila.

LOMBA NALEMELA MWAUZIMU

Tinatumikila m’dela kwa zaka 12, ndipo pambuyo pake tinatumikila m’cigawo kwa zaka 21. M’zaka zimenezi, tinakondwela na utumiki, tinadalitsidwa, komanso tinali na zokumana nazo zolimbikitsa. Koma madalitso ena anali m’tsogolo. Mu August 1997, tinalandila mwayi wa utumiki umene tinali kuulakalaka kwa nthawi yaitali. Tinaitaniwa kuti tikatumikile pa ofesi ya nthambi mu United States. Apa n’kuti papita zaka 38 kucokela nthawi yoyamba pamene tinafunsila utumikiwu. M’mwezi wokonkhapo, tinayamba utumiki wathu wa pa Beteli. N’naganiza kuti abale oyang’anila pa Beteli anali kufuna kuti nithandizeko nchito kwa nthawi yocepa cabe, koma zinthu sizinakhale conco.

Mkazi wanga Gloria anali ciphadzuwa, ndipo na manje ni ciphadzuwa

Coyamba n’nauzidwa kuti nizitumikila ku Service Department. N’naphunzila zambili kumeneko. Abale kumeneko amayankha mafunso ambili pa nkhani zacisinsi na zovuta, zocokela ku mabungwe a akulu na oyang’anila madela a m’dziko lonse la United States. Niyamikila kuti abale analeza mtima poniphunzitsa nchitoyo. Ngakhale n’conco, nimaona kuti ngati ataniuza kuti nikatumikilenso kumeneko, ningafunikenso kuphunzitsidwa.

Ine na mkazi wanga timaukonda umoyo wa pa Beteli. Timakonda kuuka mwamsanga, ndipo cizoloŵezi cimeneci cimathandiza pa Beteli. Pambuyo pa caka cimodzi, n’nayamba kutumikila monga wothandizila m’Komiti ya Utumiki ya Bungwe Lolamulila la Mboni za Yehova. Ndiyeno, mu 1999, n’naikidwa kukhala mmodzi wa mamembala a m’Bungwe Lolamulila. Naphunzila zambili mu utumiki umenewu. Koma cacikulu n’cakuti nadzionela nekha kuti Yesu Khristu, osati munthu, ndiyedi mutu wa mpingo wacikhristu.

Kuyambila mu 1999, nakhala na mwayi wotumikila m’Bungwe Lolamulila

Nikaganizila kale langa, nthawi zina nimaona kuti umoyo wanga ulinganako na wa mneneli Amosi. Yehova anayang’ana m’busa wodzicepetsa ameneyo, amene anali kugwila nchito ya pansi yoboola nkhuyu, cakudya cimene cinali kuonedwa kukhala ca anthu osauka. Mulungu anaika Amosi kukhala mneneli wake. Ndithudi, uwu unali utumiki wapadela kwambili. (Amosi 7:14, 15) Mofanana ndi Amosi, Yehova ananiyang’ana ine, mwana wa mlimi wosauka wa m’tauni ya Liberty, ku Indiana, na kunikhuthulila madalitso ambili amene siningathe kuwachula onse. (Miy. 10:22) Olo kuti poyamba n’nali wosauka, lomba nalemela kwambili mwauzimu kuposa mmene n’nali kuyembekezela.