NSANJA YA MLONDA—YOPHUNZILA November 2017

Magazini ino ili na nkhani zophunzila wiki ya December 25, 2017-January 28, 2018.

Muziimba Mosangalala!

Ngati mumacita manyazi kuimba na mpingo, kodi mungathetse bwanji vutoli kuti muzikwanitsa kutamanda Yehova na mau anu?

Kodi Mumathaŵila kwa Yehova?

Makonzedwe a mizinda yothaŵilako m’nthawi ya Aisiraeli amatiphunzitsa za kukhululuka kwa Mulungu.

Tengelani Cilungamo ca Yehova na Cifundo Cake

Kodi makonzedwe a mizinda yothaŵilako aonetsa bwanji cifundo ca Yehova? Kodi amatiphunzitsa ciani za mmene iye amaonela moyo? Nanga aonetsa bwanji kuti iye ni wacilungamo kwambili?

“Munthu Wopatsa Mowolowa Manja Adzalandila Mphoto”

Tingaseŵenzetse nthawi yathu, mphamvu, na zinthu zina popititsa patsogolo nchito yolalikila Ufumu.

Pewani Kutengela Maganizo a Dziko

Tonse timafunika kupewa kutengela maganizo ofala a m’dzikoli amene akhoza kutisokoneza. Onani zitsanzo zisanu za maganizo a dziko.

Musalole Ciliconse Kukumanitsani Mphoto

Paulo atakumbutsa Akhristu anzake za ciyembekezo cawo cokondweletsa, anawacenjeza pa zinthu zina cifukwa cowakonda.

Mungacite Ciani Kuti Mujaile mu Mpingo Wanu Watsopano?

Ngati mufuna kukukila mumpingo wina, mukhoza kukhala na nkhawa. N’ciani cingakuthandizeni kujaila mumpingo wanu watsopano?