Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Muziimba Mosangalala!

Muziimba Mosangalala!

“Kuimbila Mulungu wathu nyimbo zomutamanda n’kwabwino.”—SAL. 147:1.

NYIMBO: 10, 2

1. Kodi kuimba kumatipatsa mwayi wanji?

WOPEKA nyimbo wina anati: “Mau okambidwa amacititsa munthu kuganiza. Malimba a m’nyimbo amakondweletsa. Koma mau a m’nyimbo zoimba pakamwa amacititsa munthu kumvela bwino.” Ndithudi, palibe mau ena amene angaticititse “kumvela bwino” kuposa mau oimbidwa pofuna kutamanda Atate wathu wakumwamba Yehova, na kuonetsa cikondi cathu pa iye. Ndiye cifukwa cake kuimba, kaya patekha kapena pamodzi na anthu a Mulungu, ni mbali yofunika ngako pa kulambila koona.

2, 3. (a) Kodi ena amakuona bwanji kuimba mokweza pamisonkhano? (b) Ni mafunso ati amene tidzakambilana?

2 Kodi kuimba mokweza pamisonkhano mumakuona bwanji? Kodi mumakuona kuti n’kocititsa manyazi? M’madela ena, amuna sakhala omasuka kuimba pagulu. Izi zingakhudze mpingo wonse, maka-maka ngati akulu sakonda kuimbako nyimbo, kapena ngati ali na cizoloŵezi cocita zinthu zina pamene mpingo ukuimba.—Sal. 30:12.

3 Ngati timaonadi kuti kuimba nyimbo ni mbali ya kulambila, tidzapewa kuyenda-yenda kapena kuphonya mbali imeneyi ya misonkhano. Conco, aliyense wa ise ayenela kudzifunsa kuti: ‘Kodi kuimba pa misonkhano nimakuona bwanji? N’ciani cinganithandize kuthetsa mantha kuti niziimba mokweza na mokondwela? Nanga ningacite ciani kuti niziimba na mtima wonse?’

KUIMBA NI MBALI YOFUNIKA PA KULAMBILA KOONA

4, 5. Ni makonzedwe anji amene Aisiraeli anapanga okhudza kuimba polambila?

4 Kuyambila kale, atumiki okhulupilika a Yehova akhala akuimba nyimbo monga njila yotamandila Yehova. N’zocititsa cidwi kuti pamene Aisiraeli anali kutumikila Yehova mokhulupilika, kuimba nyimbo inali mbali yofunika ngako pa kulambila kwawo. Mwacitsanzo, Mfumu Davide anasankha Alevi 4,000 kuti aziimba nyimbo zotamanda Mulungu pa zocitika za pa kacisi zokhudza kulambila. Pakati pa Aleviwo, panali ena okwana 288, ‘ophunzitsidwa kuimbila Yehova, ndipo onse anali akatswili.’—1 Mbiri 23:5; 25:7.

5 Popatulila kacisi, kuimba nyimbo kunali mbali yofunika kwambili. Baibo imakamba kuti: “Tsopano anthu oimba malipenga ndi oimba pakamwa anayamba kuimba mogwilizana n’kumamveka ngati mau amodzi otamanda ndi kuthokoza Yehova. Komanso anayamba kuimba ndi malipenga, zinganga, ndi zoimbila zina potamanda Yehova, . . . Kenako . . . ulemelelo wa Yehova unadzaza nyumba ya Mulungu woona.” Cocitika cimeneci cinali colimbitsa cikhulupililo ngako!—2 Mbiri 5:13, 14; 7:6.

6. Fotokozani makonzedwe apadela okhudza kuimba amene Nehemiya anakonza pamene anali bwanamkubwa ku Yerusalemu.

6 Pamene Nehemiya anali kutsogolela Aisiraeli okhulupilika pa nchito yomanganso mpanda wa Yerusalemu, anakhazikitsa magulu a Alevi oimba na zida zoimbila. Pamene mpandawo unali kupelekedwa kwa Mulungu, nyimbo zoimbiwa mwapadela zinacititsa kuti pa mwambowo pakhale cisangalalo cacikulu. Panthawiyo, panali ‘magulu aŵili oimba nyimbo zoyamika’ Mulungu. Maguluwo anayenda kuloŵela mbali ziŵili zosiyana, ndipo anakumana pafupi na kacisi. Oimbawo anali kuimba mokweza kwambili cakuti mau awo anamveka kutali. (Neh. 12:27, 28, 31, 38, 40, 43) Mosakayikila, Yehova anakondwela ngako kumvela olambila ake akuimba nyimbo zom’tamanda mocokela pansi pa mtima.

7. Kodi Yesu anaonetsa bwanji kuti kuimba nyimbo n’kofunika pa kulambila kwacikhristu?

7 Mpingo wacikhristu utakhazikitsidwa, kuimba nyimbo kunakhalabe mbali yofunika pa kulambila koona. Ganizilani zimene zinacitika pa tsiku lapadela ngako m’mbili ya anthu. Pambuyo pakuti Yesu wakhazikitsa mwambo wa Mgonelo wa Ambuye, iye na atumwi ake anaimba nyimbo zotamanda Mulungu.—Ŵelengani Mateyu 26:30.

8. Kodi Akhristu a m’nthawi ya atumwi anapeleka citsanzo canji pankhani yoimba nyimbo polambila?

8 Akhristu a m’nthawi ya atumwi, anali citsanzo cabwino pankhani yoimba nyimbo zotamanda Mulungu. Ngakhale kuti nthawi zambili iwo anali kukumana m’nyumba za Akhristu anzawo kuti alambile Mulungu, sanaleke kuimba nyimbo zotamanda Yehova. Mouzilidwa na Mulungu, mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu anzake kuti: “Pitilizani kuphunzitsana ndi kulangizana mwa masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu, ndi nyimbo zauzimu zogwila mtima. Pitilizani kuimbila Yehova m’mitima yanu.” (Akol. 3:16) Nyimbo za m’buku lathu, ni “nyimbo zauzimu” zimene tiyenela kuziimba na mtima wonse. Nyimbozi ni mbali ya cakudya cauzimu cokonzewa na “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu.”—Mat. 24:45.

MMENE MUNGATHETSELE MANYAZI POIMBA

9. (a) N’ciani cingalepheletse ena kuimba mokweza na mokondwela pamisonkhano ya mpingo ndiponso ikulu-ikulu? (b) Kodi tiyenela kuimba bwanji nyimbo zotamanda Yehova? Nanga n’ndani ayenela kupeleka citsanzo cabwino pankhani yoimba? (Onani pikica kuciyambi.)

9 N’zinthu ziti zimene zingapangitse kuti muzicita manyazi poimba? Mwina simunajaile kuimba cifukwa ca mmene munakulila kapena cifukwa ca cibadwa canu. Komanso, popeza kuti zipangizo zamakono n’zofala, mwina mumakonda kumvetsela nyimbo zabwino zoimbiwa na akatswili. Ndipo mukadziyelekezela na mmene iwo amaimbila, mumaona kuti mau anu si abwino kweni-kweni cakuti simungakwanitse kuimba bwino. Koma musalole maganizo aconco kukulepheletsani kukwanilitsa udindo wanu woimba nyimbo zotamanda Yehova. Poimba, muzikwezako m’mwamba buku lanu la nyimbo, kuwelamutsa mutu, na kuimba mocokela pansi pa mtima. (Ezara 3:11; ŵelengani Salimo 147:1.) Masiku ano, m’Nyumba za Ufumu zambili muli masikilini amene amaonetselapo mau a m’nyimbo. Izi zimatithandiza kuimba mokweza. N’zocititsanso cidwi kuti gulu linakonza zakuti pa Sukulu ya Utumiki wa Ufumu imene akulu amacita, paziimbiwa Nyimbo za Ufumu. Izi zionetsa kuti pankhani yoimba pa misonkhano, akulu ayenela kukhala citsanzo cabwino.

10. Tiyenela kukumbukila ciani ngati mantha amatilepheletsa kuimba mokweza?

10 Cimodzi mwa zinthu zimene zimalepheletsa anthu ambili kuimba mokweza ni mantha. Mwina amaopa kuti mau awo angamveke kwambili kuposa a ena onse. Ena amaona kuti mau awo amamveka a cileya ndipo amaganiza kuti akamaimba, ena angaipidwe. Komabe, kumbukilani kuti ngati tikamba, “tonsefe timapunthwa nthawi zambili.” (Yak. 3:2) Koma kodi timaleka kukamba cifukwa ca zimenezi? Iyai. Conco, tisamaope kuimba nyimbo zotamanda Yehova cifukwa coganiza kuti mau athu samveka bwino.

11, 12. Ni mfundo zina ziti zimene zingatithandize kukulitsa luso lathu loimba?

11 N’kutheka kuti timacita manyazi kuimba nyimbo cifukwa sitidziŵa bwino mmene tingaimbile. Koma pali mfundo zina zimene zingatithandize kuwongolela kaimbidwe kathu. *

12 Mungakwanitse kuimba mwamphamvu ndi mokweza mwa kukoka mpweya wokwanila. Kukoka mpweya tingakuyelekezele na magetsi. Magetsi amathandiza kuti laiti iyake. N’cimodzi-modzi na kukoka mpweya. Kumatithandiza kuti pokamba kapena poimba, mau azituluka mwamphamvu. Muyenela kuimba mokweza monga mmene mumakambila kapena kuposa pamenepo. (Onani mfundo zina zothandiza m’buku la Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, mapeji 181 mpaka 184, kuyambila pa kamutu kakuti “Kapumidwe Koyenera.”) Ndipo pa nkhani yoimba imeneyi, Malemba amalangiza anthu a Yehova kuti nthawi zina ayenela “kufuula mosangalala.”—Sal. 33:1-3.

13. Fotokozani zimene tingacite kuti tiziimba mwamphamvu na mokweza.

13 Pocita kulambila kwa pabanja kapena phunzilo la umwini, mungayese kucita izi: Tengani buku lanu la nyimbo na kusankha imodzi mwa nyimbo zimene mumakonda kwambili. Ŵelengani mau a m’nyimboyo mokweza ndi mwamphamvu. Kenako, pambuyo pokoka mpweya kamodzi kokha, kambani mau a m’kaciganizo kamodzi na mphamvu ya mau yofananayo. Pambuyo pake, imbani mau a m’kaciganizoko na mphamvu ya mau imodzi-modziyo. (Yes. 24:14) Mukatsatila malangizo amenewa, mudzayamba kuimba mokweza, mwamphamvu, na momasuka. Zimenezi ndiye zofunika, ndipo musacite mantha kapena manyazi na mmene mau anu akutulukila.

14. (a) N’ciani cina cimene tingacite kuti tiziimba mwamphamvu na mokweza? (Onani bokosi yakuti “ Mmene Mungakulitsile Luso Loimba.”) (b) Ni mfundo ziti zimene muona kuti zingakuthandizeni ngati mau anu samveka bwino?

14 Sizingatheke kuimba mwamphamvu na mokweza ngati simutsegula pakamwa mokwanila. Conco, cina cimene cingakuthandizeni poimba ni kutsegula pakamwa kuposa mmene mumacitila pokamba. Nanga mungacite ciani ngati mau anu amamveka ofooka kapena okwela kwambili? M’buku la Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, pa peji 184, pa bokosi yakuti “Kuthana Ndi Mavuto Ena,” muli mfundo zimene zingakuthandizeni kuthetsa vuto limeneli.

MUZIIMBA NYIMBO ZOTAMANDA MULUNGU NA MTIMA WONSE

15. (a) Kodi pamsonkhano wa pacaka wa mu 2016 panalengezedwa ciani? (b) Kodi zina mwa zifukwa zimene anakonzela buku la nyimbo latsopano n’ziti?

15 Pa msonkhano wa pacaka wa mu 2016 wa Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, abale na alongo anasangalala ngako pamene M’bale Stephen Lett wa m’Bungwe lolamulila, analengeza kuti pamisonkhano tidzayamba kuseŵenzetsa buku la nyimbo latsopano lakuti, ‘Imbani Mokweza ndi Mosangalala’ kwa Yehova. M’bale Lett, anafotokoza kuti cimodzi mwa zifukwa zimene anakonzelanso bukuli n’cakuti mau ake agwilizane ndi a mu Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lokonzedwanso. Conco, mau ena a m’buku la nyimbo anasinthiwa kapena kucotsewa kuti agwilizane na mau amene ali mu Baibulo la Dziko Latsopano limene linakonzedwanso mu 2013. Kuwonjezela apo, m’bukuli anaikamo nyimbo zatsopano zokamba za nchito yathu yolalikila, ndiponso zoyamikila dipo la Yesu. Cinanso, popeza kuimba ni mbali yofunika pa kulambila kwathu, Bungwe Lolamulila linaona kuti buku la nyimbo lifunika kukhala lokongola, lacikuto colingana ndi ca Baibulo la Dziko Latsopano lokonzedwanso.

16, 17. Ni zinthu ziti zimene zinasinthiwa m’buku la nyimbo latsopano?

16 Nyimbo za m’buku lakuti ‘Imbani Mokweza ndi Mosangalala’ kwa Yehova,’ zinaikiwa mogwilizana na nkhani zake kuti tisamavutike kuliseŵenzetsa. Mwacitsanzo, nyimbo 12 zoyambilila zimakamba za Yehova, nyimbo 8 zokonkhapo zimakamba za Yesu na dipo, ndipo nyimbo zina zonse zinasanjidwa motsatila dongosolo limeneli. Kuciyambi, kuli mlongoza nkhani amene angatithandize m’njila zosiyana-siyana. Mwacitsanzo, angatithandize posankha nyimbo yoimba pa nkhani ya anthu onse.

17 Pofunanso kuthandiza aliyense kuti aziimba na mtima wonse, mau ena a m’nyimbozo anasinthiwa kuti akhale osavuta kumva, ndipo ena amene anali kumveka acikale anawacotsamo. Komanso, mutu wa nyimbo wakuti “Tetezani Mtima Wanu,” unasinthiwa n’kukhala, “Titeteze Mitima Yathu.” Cifukwa ciani? Pocita misonkhano yampingo ndi ikulu-ikulu, m’gulu mumakhala anthu osiyana-siyana monga acatsopano, okondwelela, acicepele, na alongo. Anthu amenewa akamaimba nyimboyi, zinali kukhala ngati kuti akuuza ena zofunika kucita. N’cifukwa cake mutu na mau ena m’nyimboyi zinasinthiwa.

Nyimbo zimenezi muziziphunzila pa kulambila kwanu kwa pabanja (Onani palagilafu 18)

18. N’cifukwa ciani tifunika kuzidziŵa bwino nyimbo za m’buku latsopano? (Onani mau amunsi.)

18 Zambili mwa nyimbo za m’buku lakuti ‘Imbani Mokweza ndi Mosangalala’ kwa Yehova,’ zili monga mapemphelo. Pamene tiimba nyimbozi, zimakhala ngati tikuuza Yehova za mumtima mwathu. Nyimbo zina ‘zimatilimbikitsa pa cikondi ndi nchito zabwino.’ (Aheb. 10:24) Conco, tifunika kudziŵa bwino macuni na mau a m’nyimbo zathu. Cimene cingatithandize kucita zimenezi ni kumvetsela nyimbo za mau zopezeka pa webusaiti yathu ya jw.org. Tiyenelanso kumapatula nthawi yophunzila nyimbozi kunyumba kwathu. Kucita izi kudzatithandiza kuti tiziimba na mtima wonse pamisonkhano. *

19. Kodi tonse mumpingo tili na mwayi wolambila Yehova m’njila iti?

19 Kumbukilani kuti kuimba nyimbo ni mbali yofunika pa kulambila kwathu. Ni njila yabwino kwambili yoonetsela kuti timakonda Yehova na kumuyamikila. (Ŵelengani Yesaya 12:5.) Ngati muimba mokweza na mokondwela, mudzalimbikitsanso ena kucita cimodzi-modzi. Kukamba zoona, tonse mumpingo, kaya ndise acicepele, acikulile, kapena okondwelela, tingathe kulambila Yehova mwa kuimba nyimbo za Ufumu. Conco, tisamacite mantha kapena kucita manyazi kuimba. M’malomwake, tizimvela malangizo ouzilidwa a wamasalimo akuti: “Imbilani Yehova.” Inde, tiyeni tiziimba mosangalala!—Sal. 96:1.

^ par. 11 Kuti mudziŵe zina zimene mungacite kuti mukulitse luso loimba, tambani pulogilamu ya Cizungu ya JW Broadcasting ya December 2014 (pitani pa mbali yakuti video, kenako pa FROM OUR STUDIO).

^ par. 18 Pofuna kutikonzekeletsa kuimba, cigawo ciliconse pa msonkhano wacigawo kapena wadela cimayamba na mbali ya mamineti 10 ya nyimbo. Nyimbo zimenezi zimakonzewa m’njila yakuti zitithandize kukonzekeletsa mitima na maganizo athu kaamba ka pulogilamu ya msonkhano. Conco, tikulimbikitsidwa kuti nthawi ikakwana, tizikhala pansi na kumvetsela mwachelu nyimbozi.