Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Mumathaŵila kwa Yehova?

Kodi Mumathaŵila kwa Yehova?

“Yehova amawombola moyo wa atumiki ake. Ndipo palibe aliyense wothaŵila kwa iye amene adzapezeka wolakwa.”—SAL. 34:22.

NYIMBO: 8, 54

1. Cifukwa ca ucimo, kodi atumiki ambili a Mulungu amamvela bwanji?

“MUNTHU wovutika ine!” (Aroma 7:24) Mau amenewa anakamba ni mtumwi Paulo. Atumiki ambili okhulupilika a Mulungu amamvela cimodzi-modzi. Tonse tili na ucimo wobadwa nawo, koma timafuna kucita zinthu zokondweletsa Yehova. Conco, tikacita chimo, timavutika mumtima. Akhristu ena amene anacita chimo lalikulu afika poona ngati kuti Mulungu sangawakhululukile.

2. (a) Kodi Salimo 34:22 imaonetsa bwanji kuti atumiki a Mulungu safunika kumangodziimba mlandu? (b) Kodi m’nkhani ino tidzakambilana ciani? (Onani bokosi yakuti “ Zimene Tiphunzilapo, Osati Zimene Inali Kuimila.”)

2 Malemba amakamba kuti anthu ocimwa amene amathaŵila kwa Yehova, safunika kumangodziimba mlandu. (Ŵelengani Salimo 34:22.) Kodi kuthaŵila kwa Yehova kutanthauza ciani? Nanga tingacite ciani kuti Yehova aticitile cifundo na kutikhululukila? Tidzapeza mayankho pa mafunso amenewa mwa kukambilana za makonzedwe a mizinda yothaŵilako m’nthawi ya Aisiraeli. N’zoona kuti makonzedwe amenewa anali mbali ya pangano la Cilamulo, limene linaloŵedwa m’malo na pangano latsopano pa Pentekosite wa mu 33 C.E. Koma kumbukilani kuti Cilamulo cimeneco cinacokela kwa Yehova. Conco, kukambilana za makonzedwe a mizinda yothaŵilako, kudzatithandiza kudziŵa mmene Yehova amaonela ucimo, anthu ocimwa, na kulapa. Coyamba, tiyeni tikambilane za colinga ca mizinda imeneyi.

“SANKHANI MIZINDA YOTHAŴILAKO”

3. Kodi Aisiraeli anali kuweluza bwanji mlandu wa kupha munthu mwadala?

3 M’nthawi ya Aisiraeli, Yehova anali kuona mlandu uliwonse wa kupha munthu kukhala nkhani yaikulu kwambili. Munthu wopha mnzake mwadala nayenso anali kuphedwa na m’bululu wa munthu wophedwayo, amene anali kuchedwa “wobwezela magazi.” (Num. 35:19) Mwanjila imeneyi, wakuphayo anali kulipila moyo wake cifukwa ca kupha munthu wosalakwa. Izi zinathandiza kuti Dziko Lolonjezedwa lisadetsedwe, cifukwa Yehova analamula kuti: ‘Musadetse dziko limene mukukhalamo, cifukwa [kukhetsa] magazi [a munthu] ndiko kumadetsa dziko.’—Num. 35:33, 34.

4. Kodi milandu ya kupha munthu mwangozi anali kuiweluza bwanji m’nthawi ya Aisiraeli?

4 Nanga bwanji za milandu ya kupha munthu mwangozi? Kodi Aisiraeli anali kuiweluza bwanji? Munthu akapha mnzake mwangozi, anali kukhalabe na mlandu wa magazi cifukwa ca kupha munthu wosalakwa. (Gen. 9:5) Komabe, mwacifundo ca Mulungu, munthuyo anali kuloledwa kuthaŵila ku umodzi mwa mizinda 6 yothaŵilako kuti wobwezela magazi asamuphe. Kumeneko, iye anali kukhala wotetezeka. Munthu wakupha mnzake mwangozi anali kufunika kukhalabe mumzinda wothaŵilako mpaka mkulu wa ansembe akamwalile.—Num. 35:15, 28.

5. Kodi makonzedwe okhala na mizinda yothaŵilako angatithandize bwanji kum’dziŵa bwino Yehova?

5 Si anthu amene anapanga makonzedwe akuti pakhale mizinda yothaŵilako. Yehova ndiye analamula. Iye anauza Yoswa kuti: “Uza ana a Isiraeli kuti, ‘Sankhani mizinda yothaŵilako.’” Mizindayo itasankhiwa, inakhala “yopatulika.” (Yos. 20:1, 2, 7, 8) Popeza kuti Yehova ndiye analamula kuti pakhale mizinda yothaŵilako, tingafunse kuti: Kodi makonzedwe amenewa atiphunzitsa ciani za cifundo cake? Nanga atithandiza bwanji kudziŵa zimene tingacite kuti tithaŵile kwa Yehova masiku ano?

“AZIFOTOKOZA NKHANI YAKE KWA AKULU”

6, 7. (a) Fotokozani udindo umene akulu anali nawo poweluza munthu wopha mnzake mwangozi. (Onani pikica kuciyambi.) (b) N’cifukwa ciani wopha munthu mwangozi anali kufunika kukaonana na akulu?

6 Munthu amene wapha mnzake mwangozi akafika pacipata coloŵela mumzinda wothaŵilako, coyamba anali kufunika ‘kufotokoza nkhani yake kwa akulu.’ Iwo anali kufunika kumulandila bwino. (Yos. 20:4) Pakapita nthawi, wolakwayo anali kum’tumiza kwa akulu a mumzinda umene anaphela munthu, ndipo akulu a kumeneko ndiwo anali kuweluza mlandu wake. (Ŵelengani Numeri 35:24, 25.) Munthuyo anali kum’bwezela ku mzinda wothaŵilako kokha ngati apeza kuti sanaphe mnzake mwadala.

7 N’cifukwa ciani mlanduwo unali kuweluzidwa na akulu? Cifukwa cakuti iwo anali na udindo wothandiza kuti mtundu wa Aisiraeli ukhale woyela. Zinali kuthandizanso munthu wakupha mnzake mwangozi kupindula na cifundo ca Yehova. Katswili wina wa Baibo analemba kuti ngati wakupha munthu sanaonane na akulu, “anali kuika moyo wake paciwopsezo.” Anakambanso kuti: “Magazi ake anali kukhala pamutu pake, cifukwa sanagwilitsile nchito makonzedwe a Mulungu omuteteza.” Ngati munthu wapha mnzake mwangozi, thandizo linalipo. Koma munthuyo anali kufunika kucitapo kanthu kuti athandizidwe. Anali kufunika kuthaŵila ku umodzi mwa mizinda yothaŵilako imene Yehova anakhazikitsa. Ngati sanatelo, m’bululu wa wophedwayo anali kuloledwa kumupha.

8, 9. N’cifukwa ciani Mkhristu amene wacita chimo lalikulu ayenela kupempha thandizo kwa akulu?

8 Masiku ano, Mkhristu akacita chimo lalikulu afunika kuonana na akulu mumpingo kuti amuthandize. N’cifukwa ciani kucita izi n’kofunika ngako? Coyamba, malinga n’zimene Mau a Mulungu amakamba, Yehova ndiye anapanga makonzedwe akuti akulu azisamalila nkhani zokhudza macimo aakulu. (Yak. 5:14-16) Caciŵili, makonzedwe amenewa amathandiza wolakwa amene walapa kuti akonzenso ubwenzi wake na Mulungu, ndi kupewa kukhala na cizoloŵezi cocita machimo. (Agal. 6:1; Aheb. 12:11) Cacitatu, akulu anapatsiwa udindo wolimbikitsa wolakwa amene walapa, ndipo anaphunzitsidwa mocitila zimenezi. Kulimbikitsa wolakwa kumam’thandiza kuti asamangodzimvela cisoni kapena kudziimba mlandu. Yehova anakamba kuti akulu ni “malo ousapo mvula yamkuntho.” (Yes. 32:1, 2) Kukamba zoona, makonzedwe amenewa amaonetsa cifundo ca Mulungu.

9 Atumiki ambili a Mulungu adzionela okha kuti ukacimwa umapeza mpumulo ngati wapempha na kulandila thandizo kwa akulu. Mwacitsanzo, m’bale wina dzina lake Daniel anacita chimo lalikulu, koma kwa miyezi yambili anali kuopa kuulula chimolo kwa akulu. Iye anati: “Patapita nthawi yaitali conco, n’nayamba kuganiza kuti akulu sanganipatsenso thandizo lina, koma kunicotsa cabe mu mpingo. Komabe, nthawi zonse n’nali kukhala mwamantha, cifukwa n’nadziŵa kuti sinidzapewa zotulukapo za chimo langa. Ndipo popemphela kwa Yehova, n’nali kuyamba mwa kupepesa pa zimene n’nacita.” Koma m’kupita kwa nthawi, Daniel anakapemphabe thandizo kwa akulu. Pokumbukila zimene zinacitikazo, iye anati: “Kukamba zoona, n’nali kucita mantha kuulula chimo langa kwa akulu. Koma n’taulula, n’namvela ngati kuti winawake wacotsa cikatundu colema pamutu panga. Lomba nimaona kuti nili na ufulu wopemphela kwa Yehova popanda cododometsa ciliconse.” Tsopano, Daniel ali na cikumbumtima coyela, ndipo posacedwa anaikiwa kukhala mtumiki wothandiza.

“AZITHAŴILA KUMZINDA UMODZI MWA MIZINDAYI”

10. Kodi munthu wopha mnzake mwangozi anali kufunika kucita ciani kuti acitilidwe cifundo?

10 Munthu wakupha mnzake mwangozi anayenela kucitapo kanthu kuti acitilidwe cifundo. Anafunika kuthaŵila ku mzinda wothaŵilako wapafupi na kwawo. (Ŵelengani Yoswa 20:4.) Iye sanafunike kuwaya-waya. Anafunika kuthaŵila ku mzindawo mwamsanga na kukhala kumeneko kuti ateteze moyo wake. Kuti acite izi anali kufunika kulolela kusiya nchito na nyumba yake, ndiponso analibe ufulu wotuluka mu mzindawo mpaka pamene mkulu wa ansembe akafe. * (Num. 35:25) Koma panali poyenela kwa iye kupilila zimenezi. Ngati wothaŵayo wacoka mumzindawo, anali kuonetsa kuti sanali kudela nkhawa za moyo wa munthu amene anamuphayo, ndipo zimenezo zinali kuika moyo wake paciopsezo.

11. Kodi Mkhristu wolapa afunika kucita ciani kuti aonetse kuti amayamikila cifundo ca Mulungu?

11 Masiku anonso, wocimwa amene walapa afunika kucitapo kanthu kuti acitilidwe cifundo na Mulungu. Afunika kulekelatu kucita macimo, osati mwa kupewa cabe macimo aakulu, komanso ngakhale zolakwa zina zazing’ono zimene kaŵili-kaŵili zimatsogolela ku chimo lalikulu. Mouzilidwa, mtumwi Paulo anafotokoza zimene Akhristu a ku Korinto anacita atalapa. Iye analemba kuti: “Taonani zimene cisoni cogwilizana ndi cifunilo ca Mulungu cimeneci cakucitilani. Cakucititsani kukhala akhama kwambili, cakucititsani kudziyeletsa, kuipidwa, mantha, kufunitsitsa kulapa, kudzipeleka, ndiponso kukonza colakwaco.” (2 Akor. 7:10, 11) Inde, ngati munthu acita khama kuti aleke kucita macimo, zimaonetsa kuti anaipidwadi na chimo lake, ndi kuti amayamikila cifundo ca Yehova.

12. Kodi Mkhristu angafunike kuleka ciani kuti Mulungu apitilize kumucitila cifundo?

12 N’zinthu ziti zimene Mkhristu angafunike kuleka kuti Mulungu apitilize kumucitila cifundo? Afunika kuleka zilizonse zimene zingamugwetsele m’chimo, ngakhale zimene amazikonda ngako. (Mat. 18:8, 9) Mwacitsanzo, ngati anzanu ena amakutunthani kucita zinthu zokhumudwitsa Yehova, muyenela kuleka kugwilizana nawo. Ngati mumalephela kudziletsa pa kamwedwe ka mowa, muyenela kupewa zocitika zimene zingakuikeni pa ciyeso cakuti mumwe kwambili. Komanso ngati mumalimbana na zilakolako zoipa zakugonana, mufunika kupewa mavidiyo na mawebusaiti osayenela. Muyenelanso kupewa kucita zinthu zosonkhezela maganizo aciwelewele. Musaiŵale kuti ciliconse cimene timacita kuti tikhalebe okhulupilika kwa Yehova cili na phindu lake. Palibe cinthu coŵaŵa kuposa kusiyidwa na Mulungu. Ndipo palibe cinthu cina cokondweletsa kuposa kusonyezedwa ‘kukoma mtima kwake kosatha.’—Yes. 54:7, 8.

“MIZINDAYO . . . IKHALE YOTI WOPHA MUNTHU MWANGOZI AZITHAŴILAKO”

13. Fotokozani cifukwa cake wothaŵa anali kukhala wotetezeka ndi wacimwemwe mumzinda wothaŵilako.

13 Akakhala mumzinda wothaŵilako, munthu wopha mnzake mwangozi anali kukhala wotetezeka. Pokamba za mizindayo, Yehova anati: “Mizindayo nchito yake ikhale yoti wopha munthu mwangozi azithaŵilako.” (Yos. 20:2, 3) Yehova sanalole kuti wopha mnzakeyo adzapatsiwenso cilango mtsogolo cifukwa ca chimo lakelo. Komanso, munthu wobwezela magazi sanali kuloledwa kuloŵa mumzinda wothaŵilako kuti akaphe wothaŵayo. Conco, wothaŵayo sanali kukhala mwamantha poopa kuti mwina adzaphedwa na wobwezela magazi. Akakhala mumzindawo, anali kutetezedwa na Yehova. Kumeneko, iye sanali kukhala ngati ali ku jele. Anali na ufulu woseŵenza, kuthandiza anthu ena, na kutumikila Yehova mwamtendele. Inde, anali na mwayi wokhala na umoyo wacimwemwe ndi wokhutilitsa.

Musamakayikile kuti Yehova anakukhululukilani (Onani palagilafu 14-16)

14. Kodi Mkhristu amene walapa safunika kukayikila za ciani?

14 Atumiki ena a Mulungu amene anacita chimo lalikulu pambuyo pake n’kulapa, amadziimbabe mlandu mpaka kufika poganiza kuti Yehova sadzaiŵala chimo lawo. Ngati umu ni mmene inunso mumamvelela, dziŵani kuti pamene Yehova anakukhululukilani, anaiŵalako za chimo lanu. Conco, simuyenelanso kudziimba mlandu. Daniel, amene tamuchula poyamba paja anamvetsa mfundo imeneyi. Akulu atam’patsa uphungu na kumuthandiza kukhalanso na cikumbumtima coyela, iye anati: “N’napeza mpumulo. Nkhani yanga itasamalidwa, n’naleka kudziimba mlandu. Ngati Mulungu wakukhululukila chimo, ndiye kuti latha. Monga mmene Yehova anakambila, amacotsa zolakwa zathu na kuziika kutali kwambili na ise cakuti sitingakwanitse kuzionanso.” Kumbukilani kuti wopha mnzake mwangozi akakhala mumzinda wothaŵilako, sanali kukhalanso mwamantha poopa wobwezela magazi. Mofananamo, Yehova akatikhululukila, sitifunika kukhala mwamantha poganiza kuti akusakila cifukwa cokumbutsila chimo lakale kuti atipatse cilango.—Ŵelengani Salimo 103:8-12.

15, 16. Kodi kuganizila udindo wa Yesu monga Wotiombola na Mkulu wa Ansembe kungatithandize bwanji kukhulupilila kuti Mulungu angaticitile cifundo?

15 Mosiyana na Aisiraeli, ise tili na cifukwa cacikulu cokhulupilila kuti Yehova angaticitile cifundo. Kumbukilani kuti Paulo anadzimvela cisoni cifukwa colephela kumvela Yehova pa zinthu zina. Komabe, pambuyo pake iye anati: “Mulungu [adzandipulumutsa] kudzela mwa Yesu Khristu Ambuye wathu.” (Aroma 7:25) N’zoona kuti Paulo anali kulimbana na ucimo, ndipo analakwitsapo zinthu zina. Koma atalapa, sanakayikile kuti Mulungu anamukhululukila kupitila mu nsembe ya dipo la Yesu. Monga Wotiwombola, Yesu amayeletsa cikumbumtima cathu na kutipatsa mtendele wa mumtima. (Aheb. 9:13, 14) Komanso monga Mkulu wa Ansembe, “iye akhoza kupulumutsa kwathunthu anthu amene akufika kwa Mulungu kudzela mwa iye, cifukwa adzakhalabe ndi moyo nthawi zonse ndipo aziwacondelela kwa Mulungu.” (Aheb. 7:24, 25) M’nthawi yakale, zimene mkulu wa ansembe anali kucita zinali kuthandiza Aisiraeli kutsimikizila kuti macimo awo akhululukidwa. Nanga kuli bwanji ise amene Mkulu wa Ansembe wathu ni Yesu? Sitiyenela kukayikila ngakhale pang’ono kuti Mulungu ‘adzaticitila cifundo ndi kutisonyeza kukoma mtima kwakukulu pa nthawi imene tikufunika thandizo.’—Aheb. 4:15, 16.

16 Conco, kuti tithaŵile kwa Yehova, tiyenela kukhulupilila nsembe ya Yesu. Musamaone kuti nsembe ya dipo la Yesu imapindulitsa cabe anthu monga gulu. Koma muziionanso monga nsembe yokupindulitsani inu panokha. (Agal. 2:20, 21) Muzikhulupilila kuti kupyolela m’dipo limeneli, macimo anu angakhululukidwe. Muzikhulupililanso kuti cifukwa ca dipoli, inu muli na ciyembekezo ca moyo wosatha. Dipo la Yesu ni mphatso imene Yehova anapeleka kwa inu.

17. N’cifukwa ciani muyenela kuthaŵila kwa Yehova?

17 Makonzedwe okhala na mizinda yothaŵilako amaonetsa kuti Yehova ni wacifundo. Kupitila m’makonzedwe amenewa, Mulungu anaonetsa kuti moyo ni wopatulika. Komanso, anaonetsa mmene akulu amatithandizila, na zimene kulapa kweni-kweni kumatanthauza. Cinanso, makonzedwe amenewa amatiphunzitsa kuti iye akatikhululukila, amaiŵalako za chimo limene tinacita. Kodi inu mumathaŵila kwa Yehova? Kulibenso malo ena otetezeka kumene munthu angathaŵile kuposa kwa Yehova. (Sal. 91:1, 2) M’nkhani yotsatila, tidzakambilana mmene makonzedwe a mizinda yothaŵilako angatithandizile kutengela citsanzo cabwino ca Yehova pankhani yoonetsa cilungamo na cifundo.

^ par. 10 Malinga ni buku lina lokamba za Ayuda, cioneka kuti banja la munthu wopha mnzake mwangozi linali kupita kukakhala naye ku mzinda wothaŵilako.