Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Musalole Ciliconse Kukumanitsani Mphoto

Musalole Ciliconse Kukumanitsani Mphoto

“Musalole kuti munthu aliyense . . . akumanitseni mphotoyo.” —AKOL. 2:18.

NYIMBO: 122, 139

1, 2. (a) Kodi atumiki a Mulungu ali na ciyembekezo canji? (b) N’ciani cimatithandiza kuyang’anabe pa mphoto? (Onani pikica pamwambapa.)

MOFANANA na mtumwi Paulo, Akhristu odzozedwa na mzimu masiku ano ali na ciyembekezo cokalandila “mphoto ya ciitano ca Mulungu copita kumwamba.” (Afil. 3:14) Iwo akuyembekezela mwacidwi nthawi pamene adzalamulila pamodzi na Yesu Khristu mu Ufumu wake wakumwamba. Adzakhalanso na mwayi wogwila naye nchito yobwezeletsa anthu ku ungwilo. (Chiv. 20:6) Mulungu wawapatsadi ciyembekezo cabwino kwambili. Koma a nkhosa zina ali na ciyembekezo cosiyanako. Iwo akuyembekezela kudzalandila mphoto ya moyo wosatha pano padziko lapansi. Cimeneci ni ciyembekezo cokondweletsa ngako!—2 Pet. 3:13.

2 Paulo analembela kalata Akhristu anzake odzozedwa pofuna kuwathandiza kukhalabe okhulupilika kuti akapeze mphoto. Iye anati: “Ikani maganizo anu pa zinthu zakumwamba.” (Akol. 3:2) Iwo anafunika kuikabe maganizo awo pa ciyembekezo cokalandila coloŵa cawo cakumwamba. (Akol. 1:4, 5) Ndithudi, kuganizila za madalitso amene Yehova watisungila monga atumiki ake, kumatithandiza tonse kuyang’anabe pa mphoto yathu, kaya ni yokakhala na moyo kumwamba kapena pano padziko.—1 Akor. 9:24.

3. Kodi Paulo anacenjeza Akhristu anzake pa zinthu ziti?

3 Komanso, mtumwi Paulo anacenjeza Akhristu anzake za zinthu zimene zikanawalepheletsa kukalandila mphoto. Mwacitsanzo, analembela mpingo wa ku Kolose za Akhristu onama amene anali kuyesa kukondweletsa Mulungu mwa kutsatila Cilamulo m’malo mokhulupilila Khristu. (Akol. 2:16-18) Paulo anafotokozanso zinthu zina zimene zingatimanitse mphoto zimene zilipo ngakhale masiku ano. Mwacitsanzo, anafotokoza mmene tingapewele zilakolako zoipa, zimene tingacite ngati tasemphana maganizo na okhulupilila anzathu, kapena ngati m’banja lathu muli mavuto. Malangizo amene anapeleka pa mbali zimenezi ni ofunika ngako kwa ise masiku ano. Conco, tiyeni tikambilane ena mwa malangizo acikondi a m’kalata imene Paulo analembela Akhristu a ku Kolose.

THETSANI ZILAKOLAKO ZOIPA

4. N’cifukwa ciani zilakolako zoipa zingatimanitse mphoto?

4 Paulo atakumbutsa Akhristu anzake za ciyembekezo cawo cokondweletsa, analemba kuti: “Conco cititsani ziwalo za thupi lanu padziko lapansi kukhala zakufa ku dama, zinthu zodetsa, cilakolako ca kugonana, cikhumbo coipa, ndi kusilila kwa nsanje.” (Akol. 3:5) Zilakolako zoipa zingakhale zamphamvu kwambili, ndipo zingasokoneza ubwenzi wathu na Yehova na kutitayitsa ciyembekezo cathu ca za m’tsogolo. Pambuyo pobwezeletsedwa mu mpingo, m’bale wina amene anatengeka na cilokolako coipa mpaka kucita ciwelewele, anakamba kuti: “N’nasoceletsedwa kwambili na zilakolako zoipa cakuti panatenga nthawi itali kuti nibwelele mu mpingo.”

5. Kodi tingadziteteze bwanji pa zocitika zimene zingatiike pa ciyeso?

5 Tiyenela kukhala osamala kwambili ngati takumana na zocitika zimene zingaticititse kuphwanya mfundo za Yehova za makhalidwe abwino. Mwacitsanzo, n’cinthu canzelu kuti mwamuna na mkazi akangoyamba cibwenzi adziikile malile oyenela pa nkhani yoonetsana cikondi. Angakambilane zokhudza kugwilana, kupsompsonana, kapena kukhala kwaokha. (Miy. 22:3) Mkhristu angakhalenso pa ciyeso ngati wacoka panyumba n’kupita kwinakwake kutali kukacita bizinesi, kapena ngati amaseŵenza na munthu amene si mwamuna kapena mkazi mnzake. (Miy. 2:10-12, 16) Zikakhala conco, dzifotokozeni kuti ndimwe wa Mboni za Yehova, muzicita zinthu mwaulemu, ndipo muzipewa kuceza mokopana cifukwa kumakhala na zotulukapo zoipa. Zingakhalenso zosavuta kugonja ku ciyeso ngati tili na nkhawa kapena ngati ndise osungulumwa. Panthawi ngati imeneyi, tikhoza kumalakalaka kukhala na munthu amene amaoneka kuti amasamala za ise. Maganizo aconco angakhale amphamvu kwambili cakuti tingakopeke na munthu aliyense amene angationetse cikondi. Ngati zaconco zakucitikilani, dalilani thandizo locokela kwa Yehova ndi kwa anthu ake n’colinga cakuti musakamaniwe mphoto.—Ŵelengani Salimo 34:18; Miyambo 13:20.

6. Pankhani yosankha zosangalatsa, kodi tiyenela kukumbukila mfundo ziti?

6 Kuti tithetse zilakolako zoipa, tifunika kupewa zosangalatsa zoipa. Zosangalatsa zambili masiku ano zimalimbikitsa makhalidwe oipa ngati amene anali mu Sodomu na Gomora. (Yuda 7) Ocita zosangalatsa amapangitsa anthu kuona khalidwe la ciwelewele monga labwino, lopanda zotulukapo zilizonse zoipa. Ise Akhristu tiyenela kudziteteza mwa kusankha zosangalatsa mosamala. Tifunika kupewa zosangalatsa zoipa zimene zingatilepheletse kuikabe maganizo athu pa mphoto ya moyo.—Miy. 4:23.

“VALANI” CIKONDI NA KUKOMA MTIMA

7. Ni mavuto anji amene tingakumane nawo mumpingo?

7 Tonse timaona kuti ni dalitso kukhala mu mpingo wacikhristu. Tikakhala pa misonkhano, timaphunzila Mau a Mulungu na kulimbikitsana. Izi zimatithandiza kuikabe maganizo athu pa mphoto. Komabe, nthawi zina tingasemphane maganizo na Akhristu anzathu mu mpingo, ndipo zimenezi zingacititse kuti tiyambe kukwesana. Ngati sitingacitepo kanthu kuti tithetse vutolo, tingayambe kukhala wokhumudwa.—Ŵelengani 1 Petulo 3:8, 9.

8, 9. (a) Ni makhalidwe ati amene tiyenela kukhala nawo kuti tikalandile mphoto? (b) N’ciani cimene cingatithandize kuti tikhalebe pa mtendele na Mkhristu mnzathu amene watilakwila?

8 Tingacite ciani kuti mkwiyo usakatimanitse mphoto? Paulo analimbikitsa Akhristu a ku Kolose kuti: “Monga ocita kusankhidwa ndi Mulungu, oyela ndi okondedwa, valani cifundo cacikulu, kukoma mtima, kudzicepetsa, kufatsa, ndi kuleza mtima. Pitilizani kulolelana ndi kukhululukilana ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi cifukwa codandaulila za mnzake. Monga Yehova anakukhululukilani ndi mtima wonse, inunso teloni. Koma kuwonjezela pa zonsezi, valani cikondi, pakuti cimagwilizanitsa anthu mwamphamvu kwambili kuposa cinthu cina ciliconse.”—Akol. 3:12-14.

9 Cikondi na kukoma mtima zingatilimbikitse kukhululukila ena. Mwacitsanzo, ngati takhumudwa na zokamba kapena zocita za Mkhristu mnzathu, tingacite bwino kukumbukila nthawi pamene ise tinakamba kapena kucita zinthu zimene zinakhumudwitsa ena. Kodi sitinayamikile cikondi na kukoma mtima kumene abale na alongo anationetsa mwa kutikhululukila? (Ŵelengani Mlaliki 7:21, 22.) Komanso, ndise oyamikila ngako kuti Khristu anatibweletsa m’gulu la olambila oona amene ni ogwilizana. (Akol. 3:15) Tonse timakonda Mulungu mmodzi, timalalikila uthenga wofanana, ndipo mavuto ambili amene timakumana nawo ni olingana. Kukhululukila ena kumaonetsa kuti ndise acikondi ndi okoma mtima, ndipo kumalimbikitsa mgwilizano mu mpingo. Cinanso, kumatithandiza kuti tipitilize kuika maganizo athu pa mphoto ya moyo.

10, 11. (a) N’cifukwa ciani nsanje ni yoopsa? (b) Tingacite ciani kuti nsanje isakatimanitse mphoto?

10 M’Baibo muli zitsanzo zoticenjeza zimene zionetsa kuti nsanje ingatilepheletse kukalandila mphoto. Mwacitsanzo, Kaini anapha m’bale wake Abele cifukwa ca nsanje. Kora, Datani, na Abiramu anayamba kutsutsana na Mose cifukwa ca nsanje. Komanso, Mfumu Sauli ataona kuti Davide zinthu zikumuyendela bwino, anacita nsanje cakuti anafuna kumupha. N’cifukwa cake Mau a Mulungu amati: “Pamene pali nsanje ndi mtima wokonda mikangano, palinso cisokonezo ndi zoipa zamtundu uliwonse.”—Yak. 3:16.

11 Kukhala acikondi na okoma mtima kudzatithandiza kupewa kucitila nsanje anthu ena. Mau a Mulungu amati: “Cikondi n’coleza mtima ndiponso n’cokoma mtima. Cikondi sicicita nsanje.” (1 Akor. 13:4) Kuti nsanje isazike mizu mu mtima mwathu, tifunika kuyesetsa kuona zinthu mmene Mulungu amazionela. Tiyenela kukumbukila kuti ise na Akhristu anzathu ndise ziwalo za thupi limodzi. Kucita izi kudzatilimbikitsa kutsatila malangizo ouzilidwa akuti: “Ciwalo cimodzi cikalemekezedwa, ziwalo zina zonse zimasangalalila naco limodzi.” (1 Akor. 12:16-18, 26) Conco, sitiyenela kucitila nsanje m’bale wathu ngati zinthu zamuyendela bwino, koma tiyenela kukondwela naye. Ganizilani za Yonatani, mwana wa Mfumu Sauli. Iye sanacite nsanje pamene Davide anadzozedwa kuti adzakhale mfumu ya Isiraeli yotsatila. Koma anam’limbikitsa. (1 Sam. 23:16-18) Na ise tiyenela kukhala okoma mtima ndi acikondi ngati Yonatani.

ZIMENE MUNGACITE KUTI NONSE M’BANJA MUKALANDILE MPHOTO

12. Ni malangizo ati a m’Malemba amene anthu onse m’banja ayenela kuseŵenzetsa kuti akalandile mphoto?

12 Kuseŵenzetsa mfundo za m’Baibo kungathandize banja kukhala lamtendele ndi lacimwemwe, ndipo kungathandizenso kuti banjalo likalandile mphoto. Kwa Akhristu a ku Kolose, kodi Paulo anapeleka malangizo ati a m’Malemba othandiza mabanja? Iye anati: “Inu akazi, muzigonjela amuna anu, pakuti zimenezi ndiye zoyenela kwa anthu otsatila Ambuye. Inu amuna, musaleke kukonda akazi anu ndipo musamawapsele mtima kwambili. Ananu, muzimvela makolo anu pa zinthu zonse, pakuti kucita zimenezi kumakondweletsa Ambuye. Inu abambo, musamakwiyitse ana anu, kuti angakhale okhumudwa.” (Akol. 3:18-21) Mosakayikila, na imwe mungavomeleze kuti kuseŵenzetsa malangizo ouzilidwa a Paulo amenewa kungapindulitse mwamuna, mkazi, ndi ana.

13. Kodi mkazi wacikhristu angakope bwanji mwamuna wake amene si Mboni kuti ayambe kulambila koona?

13 Bwanji ngati mwamuna wanu si Mboni, ndipo muona kuti sakucitilani zinthu mokoma mtima? Kodi kukangana naye kungakonze zinthu? Mwina iye angagonjele n’kucita zimene imwe mufuna, koma kodi kucita zimenezi kungam’thandize kukopeka naco coonadi? N’zokayikitsa. Koma ngati mulemekeza mwamuna wanu monga mutu wa banja, m’banja mwanu mudzakhala mtendele, Yehova adzatamandika, ndipo mwamuna wanu angakopeke n’kuyamba kulambila koona. Ndiyeno, nonse aŵili mungakhale na mwayi wokapeza mphoto.—Ŵelengani 1 Petulo 3:1, 2.

14. Kodi mwamuna wacikhristu ayenela kucita ciani ngati mkazi wake amene si Mboni samulemekeza?

14 Bwanji ngati mkazi wanu si Mboni, ndipo muona kuti sakulemekezani? Kodi kumukalipila kungacititse kuti ayambe kukulemekezani monga mutu wa banja? Kutalitali! Mulungu amafuna kuti muzicita umutu wanu mwacikondi, monga mmene Yesu amacitila. (Aef. 5:23) Yesu amacita umutu wake mwacikondi ndi moleza mtima pa mpingo. (Luka 9:46-48) Ngati mwamuna atengela citsanzo ca Yesu, angakope mkazi wake kuti ayambe kutumikila Yehova.

15. Kodi mwamuna wacikhristu angaonetse bwanji kuti amakonda mkazi wake?

15 Malemba amalangiza amuna kuti: “Musaleke kukonda akazi anu ndipo musamawapsele mtima kwambili.” (Akol. 3:19) Mwamuna wacikondi angaonetse kuti amalemekeza mkazi wake mwa kumumvetsela pamene akamba maganizo ake, na kumuyamikila pa zimene wakambazo. (1 Pet. 3:7) N’zoona kuti si nthawi zonse pamene mwamuna angatsatile malingalilo a mkazi wake. Koma kufunsako malingalilo a mkazi kungathandize mwamunayo kupanga cosankha coyenela. (Miy. 15:22) Mwamuna wacikondi sakakamiza mkazi wake kuti azimulemekeza, koma amayesetsa kucita zinthu zimene zingacititse mkaziyo kuyamba kum’lemekeza. Ngati mwamuna amakonda mkazi wake ndi ana, banja lake limatumikila Yehova mwacimwemwe, ndipo limakhala na mwayi wokalandila mphoto ya moyo.

Tingacite ciani kuti mavuto a m’banja asakatimanitse mphoto? (Onani palagilafu 13-15)

ACICEPELE—MUSALOLE CILICONSE KUKUMANITSANI MPHOTO

16, 17. Acicepele, mungapewe bwanji kukwiyila makolo anu?

16 Nanga bwanji ngati ndinu wacicepele, ndipo muona kuti makolo anu acikhristu sakumvetsetsani kapena sakupatsani ufulu wokwanila? Mwina mungakhumudwe n’kuyamba kuona ngati kutumikila Yehova n’kosakondweletsa. Koma mukaleka kutumikila Yehova cifukwa cokhumudwa, posakhalitsa mudzadzionela mwekha kuti palibe wina aliyense amene amakukondani zeni-zeni, mofanana na makolo anu acikhristu kapena abale na alongo mu mpingo.

17 Mwacionekele, na imwe mudziŵa kuti ngati makolo anu amakupatsani malangizo, ndiye kuti amakukondani. (Aheb. 12:8) Koma mwina simukondwela na mmene amakupatsilani malangizowo. M’malo mokhumudwa na kapelekedwe ka malangizo, yesetsani kuganizila cifukwa cimene amapelekela malangizo mwanjila imeneyo. Conco, muzikhala wodekha ndi kupewa kukhumudwa akakupatsani uphungu. Mau a Mulungu amati: “Aliyense wosalankhulapo mau ake ndi wodziŵa zinthu, ndipo munthu wozindikila amakhala wofatsa.” (Miy. 17:27) Phunzilani kucita zinthu mwaucikulile. Muzilandila uphungu moleza mtima, na kuuseŵenzetsa popanda kudandaula na mmene wapelekedwela. (Miy. 1:8) Kukhala na makolo amene amakonda Yehova na mtima wonse ni dalitso. Iwo amafuna kukuthandizani kuti mukalandile mphoto ya moyo.

18. Kodi mwatsimikiza mtima kuyang’anabe pa mphoto? Cifukwa ciani?

18 Kuganizila mphoto imene tikuyembekezela n’kofunika ngako, kaya tili na ciyembekezo cokalandila moyo wosafa kumwamba kapena codzakhala na moyo wosatha pano padziko lapansi. Ciyembekezo cimeneci n’codalilika cifukwa Mlengi wathu ndiye anatilonjeza. Pokamba za dziko la Paradaiso, Mulungu anati: “Dziko lapansi lidzadzaza ndi anthu odziŵa Yehova.” (Yes. 11:9) Aliyense amene adzakhala mmenemo azikaphunzitsiwa na Mulungu. Ndithudi, iyi ni mphoto yabwino ngako imene tonse tiyenela kucita khama kuti tikaipeze. Conco, sumikani maganizo anu pa zimene Yehova walonjeza, ndipo musalole ciliconse kukumanitsani mphoto!