Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Pewani Kutengela Maganizo a Dziko

Pewani Kutengela Maganizo a Dziko

“Samalani: mwina wina angakugwileni ngati nyama, mwa nzelu za anthu ndi cinyengo copanda pake, . . . [ca] m’dzikoli.” —AKOL. 2:8.

NYIMBO: 38, 31

1. Ni malangizo anji amene mtumwi Paulo analembela Akhristu anzake? (Onani pikica pamwambapa.)

MTUMWI Paulo ayenela kuti analemba kalata yake yopita kwa Akhristu a ku Kolose ca pakati pa 60 C.E. na 61 C.E. Pa nthawiyo, anali atatsala pang’ono kumasulidwa m’ndende ku Roma. Iye anafotokozela Akhristuwo za kufunika ‘komvetsetsa zinthu zauzimu.’ (Akol. 1:9) Paulo anakambanso kuti: “Ndikunena zimenezi kuti munthu aliyense asakunyengeni ndi mfundo zokopa. Samalani: mwina wina angakugwileni ngati nyama, mwa nzelu za anthu ndi cinyengo copanda pake, malinga ndi miyambo ya anthu, malinganso ndi mfundo zimene zili maziko a moyo wa m’dzikoli, osati malinga ndi Khristu.” (Akol. 2:4, 8) Ndiyeno, iye anafotokoza cifukwa cake maganizo ena amene anali ofala pa nthawiyo anali olakwika. Anafotokozanso cifukwa cake maganizo a dziko angakhale okopa kwa anthu opanda ungwilo. Mwacitsanzo, angapangitse munthu kudziona ngati wanzelu na wapamwamba kuposa anzake. Paulo analemba kalatayi pofuna kuthandiza abale kupewa maganizo a dziko na zinthu zina zoipa.—Akol. 2:16, 17, 23.

2. N’cifukwa ciani tidzakambilana ena mwa maganizo amene anthu ali nawo m’dzikoli?

2 Maganizo a dziko amapangitsa munthu kunyalanyaza kapena kupeputsa malangizo a Yehova. Kutengela maganizo aconco, m’kupita kwa nthawi kungafooketse cikhulupililo cathu. Masiku ano, tonse tingakopeke mosavuta na maganizo a anthu a m’dzikoli cifukwa amafalitsidwa pa ma TV, pa Intaneti, ku nchito, kapena kusukulu. M’nkhani ino, tidzakambilana zimene tingacite kuti tipewe kutengela maganizo a anthu a m’dzikoli. Pokambilana, tidzaona zitsanzo zisanu za maganizo a dziko na mmene tingawapewele.

KODI TIFUNIKADI KUKHULUPILILA KUTI KULI MULUNGU?

3. Ni maganizo anji amene amakopa anthu ambili? Nanga n’cifukwa ciani?

3 “Ningakhalebe munthu wabwino popanda kukhulupilila Mulungu.” M’maiko ambili, n’zosadabwitsa kumvela anthu akukamba kuti sakhulupilila kuti kuli Mulungu. Amadziona kuti ni anthu osapembedza. Ena a iwo sanafufuze mosamala kuti adziŵe ngati Mulungu alikodi. Koma amasankha kusakhulupilila Mulungu cifukwa coganiza kuti adzakhala na ufulu wocita zilizonse zimene afuna. (Ŵelengani Salimo 10:4.) Ena m’dzikoli amadziona kuti ni anzelu, ndipo amakamba kuti, “Ningakhale na mfundo zabwino zoyendetsela umoyo wanga popanda kukhulupilila Mulungu.”

4. Mungamuyankhe bwanji munthu amene amakamba kuti kulibe Mlengi?

4 Kodi zimene anthu ena amakamba zakuti kulibe Mlengi n’zoona? Anthu amene amadalila sayansi kuti iwathandize kudziŵa ngati zamoyo zinacita kulengedwa, amasoceletsedwa na mfundo zosamvetsetseka za asayansi. Koma n’zosavuta munthu kudziŵa zoona pankhaniyi. Ngati nyumba iliyonse inacita kumangiwa na winawake, kuli bwanji zamoyo? Ndiye kuti nazonso zinacita kulengedwa na winawake. Ganizilani za maselo. Maselo onse amoyo ni opangiwa mwapamwamba kwambili kuposa nyumba iliyonse, cifukwa amatha kudziculukitsa. Iwo ali na njila yosungila malangizo owathandiza kugaŵikana na kupanga maselo ena. Kodi n’ndani anapanga maselo amenewa? Baibo imayankha kuti: “Nyumba iliyonse inamangidwa ndi winawake, koma amene anapanga zinthu zonse ndi Mulungu.”—Aheb. 3:4.

5. Kodi n’zoona kuti munthu akhoza kudziŵa zabwino na zoipa popanda kukhulupilila Mulungu? Fotokozani.

5 Tingawathandize bwanji anthu amene ali na maganizo akuti munthu akhoza kudziŵa zabwino na zoipa popanda kukhulupilila Mulungu? Mau a Mulungu amakamba kuti anthu osadziŵa Mulungu angakhale na makhalidwe ena abwino. (Aroma 2:14, 15) Mwacitsanzo, ena amalemekeza na kukonda makolo awo. Koma kodi munthu amene amakana kuti Mlengi wathu wacikondi ndiye ayenela kukhazikitsa miyezo ya cabwino na coipa, angakhaledi na mfundo zodalilika za makhalidwe abwino? (Yes. 33:22) Masiku ano, anthu ambili anzelu atsimikiza kuti mavuto amene ali pa dziko lapansi ni umboni wakuti anthu afunika thandizo la Mulungu. (Ŵelengani Yeremiya 10:23.) Conco, sitiyenela kukhala na maganizo akuti munthu payekha angadziŵe zabwino na zoipa popanda kukhulupilila Mulungu na kutsatila mfundo zake.—Sal. 146:3.

KODI KUKHALA M’CIPEMBEDZO N’KOFUNIKADI?

6. Kodi anthu ambili amaciona bwanji cipembedzo?

6 “Munthu angakhale wacimwemwe olo kuti sali m’cipembedzo.” Anthu ambili amakopeka na maganizo a dziko amenewa cifukwa amaona kuti kukhala m’cipembedzo n’kosakondweletsa ndipo n’kopanda phindu. Komanso, zipembedzo zambili zimapangitsa anthu kuona ngati Mulungu ni woipa mwa kuphunzitsa za moto wa helo, kukakamiza anthu kupeleka cakhumi, kapena kucilikiza zandale. Conco, n’zosadabwitsa kuti masiku ano, ambili amaona kuti angakhale acimwemwe ngati sali m’cipembedzo. Iwo angakambe kuti: “Zinthu zauzimu nimazikonda, koma sinifuna kuloŵa cipembedzo ciliconse.”

7. Kodi kulambila koona kumatithandiza bwanji kukhala acimwemwe?

7 Kodi n’zoona kuti munthu angakhale wacimwemwe ngati sali m’cipembedzo? Munthu angakhale na cimwemwe ngati sali m’cipembedzo conama. Koma kuti akhale na cimwemwe ceni-ceni afunika kukhala pa ubwenzi na Yehova, amene amachedwa “Mulungu wacimwemwe.” (1 Tim. 1:11) Zilizonse zimene Mulungu amacita zimapindulitsa ena. Atumiki ake amakhala acimwemwe cifukwa amakonda kuthandiza ena. (Mac. 20:35) Mwacitsanzo, ganizilani mmene cipembedzo coona cimathandizila atumiki a Mulungu kukhala na mabanja acimwemwe. Cipembedzo coona cimatiphunzitsa kulemekeza mnzathu wa m’cikwati, kuona malumbilo a cikwati kukhala opatulika, kupewa ciwelewele, kuphunzitsa ana kukhala aulemu, ndi kukhala na cikondi ceni-ceni. Mwa ici, kulambila koona kwathandiza anthu a Mulungu kukhala ogwilizana m’mipingo na kukhala paubale wa padziko lonse.—Ŵelengani Yesaya 65:13, 14.

8. Mungaseŵenzetse bwanji Mateyu 5:3 pokambilana na anthu za cimene cimapangitsa munthu kukhala wacimwemwe?

8 Kodi tiyenela kuiona bwanji mfundo yakuti munthu angakhale na cimwemwe olo kuti satumikila Mulungu? Ganizilani funso ili, N’ciani cimacititsa munthu kukhala wacimwemwe? Ena amakondwela na nchito imene amagwila, maseŵela, kapena zosangalatsa. Kwa ena, cimene cimawapatsa cimwemwe ni kusamalila banja kapena anzawo. N’zoona kuti kucita zimenezi kumakondweletsa. Koma moyo wathu uli na colinga capadela, cimene munthu akacidziŵa, amakhala na cimwemwe cokhalitsa. Mosiyana na nyama, ise anthu tikhoza kuphunzila za Mlengi wathu na kum’tumikila mokhulupilika, ndipo kucita izi kumatipatsa cimwemwe. Umu ni mmene Mulungu anatilengela. (Ŵelengani Mateyu 5:3.) Mwacitsanzo, olambila oona amasangalala ndiponso amalimbikitsana akasonkhana kuti alambile Yehova. (Sal. 133:1) Amasangalalanso kukhala m’gulu la abale a padziko lonse, amakhala na umoyo wabwino, komanso amakhala na ciyembekezo cabwino ca m’tsogolo.

KODI TIFUNIKADI KUTSATILA MFUNDO ZA MAKHALIDWE ABWINO?

9. (a) Kodi anthu ambili m’dzikoli ali na maganizo anji pa nkhani ya kugonana? (b) N’cifukwa ciani Mau a Mulungu amaletsa kugonana na munthu amene suli naye m’cikwati?

9 Anthu ena amati: “Kugonana na munthu amene suli naye m’cikwati kulibe vuto.” Iwo angakambe kuti: “N’cifukwa ciani mumalimbitsa zinthu kwambili? Munthu umafunika kusangalala na umoyo.” Koma si zoona kuti kucita ciŵeleŵele kulibe vuto. N’cifukwa ciani takamba conco? Cifukwa Mau a Mulungu amaletsa ciwelewele. * (Ŵelengani 1 Atesalonika 4:3-8) Yehova ali na ufulu wotipatsa malamulo cifukwa ndiye anatilenga. Lamulo la Mulungu n’lakuti mwamuna na mkazi okwatilana ndiwo okha ayenela kugonana. Kwa Mulungu, limenelo ndilo banja. Iye amatipatsa malamulo cifukwa amatikonda. Malamulo ake amatipindulitsa. Ngati mwamuna na mkazi amamvela malamulo a Mulungu amakhala okondana, olemekezana, ndi acimwemwe. Mulungu sadzalekelela anthu amene amaphwanya lamulo lake limeneli mwadala.—Aheb. 13:4.

10. Kodi Mkhristu angacite ciani kuti apewe ciwelewele?

10 Mau a Mulungu amatiuza mmene tingapewele ciwelewele. Njila yabwino kwambili yopewela ciwelewele ni mwa kusamala na zimene timaona. Yesu anati: “Aliyense woyang’anitsitsa mkazi mpaka kumulakalaka, wacita naye kale cigololo mumtima mwake. Tsopano ngati diso lako lakumanja limakucimwitsa, ulikolowole ndi kulitaya.” (Mat. 5:28, 29) Conco, Mkhristu afunika kupewa kutamba zamalisece kapena kumvetsela nyimbo zolimbikitsa ciwelewele. Mtumwi Paulo analembela Akhristu anzake kuti: “Cititsani ziwalo za thupi lanu padziko lapansi kukhala zakufa ku dama.” (Akol. 3:5) Cinanso, tifunika kuyesetsa kulamulila maganizo athu, ndi kupewa kukamba zinthu zosayenela.—Aef. 5:3-5.

KODI COFUNIKA KWAMBILI N’KUKHALA PA NCHITO YAPAMWAMBA?

11. N’cifukwa ciani n’zosavuta Mkhristu kukhala na colinga cofuna-funa nchito yapamwamba?

11 Anthu ena amati: “Kukhala pa nchito yapamwamba n’kumene kumapangitsa munthu kukhala wacimwemwe.” Ambili angatilimbikitse kukhala na colinga copeza nchito yapamwamba, imene ingaticititse kukhala na mphamvu zolamulila ena, kukhala wochuka, ndi wolemela. Popeza anthu ambili amaona kuti kugwila nchito yapamwamba ndiye cinthu cofunika ngako, n’zosavuta Mkhristu kutengela maganizo aconco.

12. Kodi kukhala pa nchito yapamwamba n’kumene kumapangitsa munthu kukhala wacimwemwe?

12 Kodi n’zoona kuti kukhala pa nchito yapamwamba kungatibweletsele cimwemwe cokhalitsa? Iyai. Kumbukilani kuti cifukwa ca mtima wofuna kuchuka na kulamulila ena, Satana anapandukila Mulungu. Koma kodi palipano iye ali na cimwemwe? Kutalitali! Ali na mkwiyo. (Mat. 4:8, 9; Chiv. 12:12) Cimwemwe cimene munthu angapeze cifukwa cogwila nchito yakuthupi n’cosakhalitsa tikaciyelekezela na cimene munthu amapeza ngati aphunzitsa anthu za Mulungu kuti akapeze moyo wosatha. Komanso, anthu pofuna kupeza nchito yapamwamba, amacita zinthu mwampikisano, amakhala ansanje, ndipo pothela pake amangokhala ngati ‘akuthamangitsa mphepo.’—Mlal. 4:4.

13. (a) Kodi nchito yakuthupi tiyenela kuiona bwanji? (b) Kodi kalata imene Paulo analembela Akhristu a ku Tesalonika ionetsa kuti ni nchito yanji imene inamupatsa cimwemwe ceni-ceni?

13 N’zoona kuti tifunika kupeza ndalama zogulila zinthu zofunika mu umoyo, ndipo palibe vuto lililonse ngati munthu wasankha nchito imene amakonda. Koma sitiyenela kuona kuti nchito yathu yakuthupi ndiye cinthu cofunika kwambili mu umoyo wathu. Paja Yesu anati: “Kapolo sangatumikile ambuye aŵili, pakuti adzadana ndi mmodzi ndi kukonda winayo, kapena adzakhulupilika kwa mmodzi ndi kunyoza winayo. Simungathe kutumikila Mulungu ndi Cuma nthawi imodzi.” (Mat. 6:24) Ngati tiika patsogolo nchito yotumikila Yehova na kuphunzitsa ena Mau ake, tidzakhala na cimwemwe coculuka. Citsanzo pankhani imeneyi ni mtumwi Paulo. Pamene anali wamng’ono, iye anali kufuna kudzakhala pa nchito yapamwamba. Koma atayamba kugwila nchito yopanga ophunzila, anapeza cimwemwe ceni-ceni cifukwa anaona mmene anthu anali kusinthila miyoyo yawo atamva Mau a Mulungu. (Ŵelengani 1 Atesalonika 2:13, 19, 20.) Palibe nchito ina imene ingatipatse cimwemwe ceni-ceni kuposa imeneyi.

Munthu amapeza cimwemwe cokhalitsa ngati aphunzitsa ena za Mulungu (Onani palagilafu 12, 13)

KODI ANTHU ANGAKWANITSE KUTHETSA MAVUTO AWO?

14. N’cifukwa ciani maganizo akuti anthu angakwanitse kuthetsa mavuto awo angakhale okopa?

14 “Anthu angakwanitse kuthetsa mavuto awo.” Ambili angakopeke na maganizo a dziko amenewa. Cifukwa ciani? Cifukwa amaona kuti ngati zimenezi zingatheke, ndiye kuti anthu sangafunikile kutsogoleledwa na Mulungu, ndipo angakhale na ufulu wocita zilizonse zimene afuna. Cinanso, mfundo yakuti anthu angakwanitse kuthetsa mavuto awo ingaoneke ya zoona kwa ena, cifukwa kafuku-fuku waonetsa kuti nkhondo, upandu, matenda, ndi umphawi, lomba zikucepekela. Lipoti ina inati: “Cimene capangitsa kuti mavuto acepekele n’cakuti anthu agwilizana zakuti akonze zinthu padziko.” Kodi mfundo imeneyi ionetsa kuti anthu atsala pang’ono kuthetsa mavuto amene awasautsa kwa nthawi yaitali? Kuti tiyankhe funsoli, tiyeni tikambilane za mavutowo.

15. N’zinthu ziti zimene zionetsa kuti mavuto a anthu akuculukila-culukila?

15 Nkhondo: Nkhondo ziŵili za pa dziko lonse zimene zinacitika, zinapha anthu pafupi-fupi 60 miliyoni kapena kuposelapo. Kucokela pamene Nkhondo Yaciŵili ya Padziko Lonse inasila, anthu apitiliza kumenya nkhondo padziko. Pofika mu 2015, ciŵelengelo ca anthu othaŵa kwawo cifukwa ca nkhondo na cizunzo cinakwela kwambili kufika pa 65 miliyoni. Ndipo mu 2015 cabe, anthu amene anathaŵa kwawo anali pafupi-fupi 12.4 miliyoni. Upandu: N’zoona kuti mitundu ina ya upandu yacepako m’maiko ena. Koma mitundu inanso monga upandu wa pa intaneti, nkhanza za m’banja, na ucigaŵenga, zaculuka kwambili. Kuwonjezela apo, anthu ambili amaona kuti ziphuphu zaculuka ngako padziko. Kukamba zoona, anthu alephela kuthetsa upandu. Matenda: N’zoona kuti matenda ena, anthu akwanitsa kuwapezela mankhwala. Koma lipoti ya mu 2013, inaonetsa kuti caka ciliconse anthu 9 miliyoni a zaka zosakwana 60, amafa na matenda a mtima, sitroko, khansa, matenda a m’cifuwa, ndi a shuga. Umphawi: Malinga ni lipoti ya World Bank, ciŵelengelo ca anthu osauka kwambili mu Africa mokha cinawonjezeka kucoka pa 280 miliyoni mu 1990, kufika pa 330 miliyoni mu 2012.

16. (a) N’cifukwa ciani Ufumu wa Mulungu wokha ndiwo ungacotsepo mavuto a anthu? (b) Ni madalitso a Ufumu ati amene Yesaya na wamasalimo anakambilatu kuti Mulungu adzabweletsa?

16 Masiku ano, mabungwe a zamalonda na maboma, akulamulidwa na anthu adyela. Anthu amenewa sangakwanitse kucotsapo nkhondo, upandu, matenda, na umphawi. Ufumu wa Mulungu wokha ndiwo ungacotse mavuto amenewa. Onani zimene Yehova adzaticitila. Nkhondo: Ufumu wa Mulungu udzacotsapo zinthu zonse zimene zimayambitsa nkhondo, monga kudzikonda, ziphuphu, mzimu wokonda dziko lako, na cipembedzo conama. Nayenso Satana adzacotsedwa. (Sal. 46:8, 9) Upandu: Ufumu wa Mulungu unayamba kale kuphunzitsa anthu mamiliyoni kuti azikondana na kukhulupililana. Palibe boma ina ililonse imene ingakwanitse kucita zimenezi. (Yes. 11:9) Matenda: Yehova adzadalitsa anthu ake mwa kuwapatsa thanzi labwino. (Yes. 35:5, 6) Umphawi: Yehova adzauthetsa. Anthu ake adzakhala na umoyo wacimwemwe ndipo adzakhala naye paubwenzi wolimba, umene n’cinthu camtengo wapatali kuposa cuma cakuthupi.—Sal. 72:12, 13.

‘DZIŴANI MMENE MUNGAYANKHILE’

17. Mungacite ciani kuti mupewe kutengela maganizo a dziko?

17 Ngati mwamvela mfundo inayake imene muona kuti ingafooketse cikhulupililo canu, muzifufuza m’Mau a Mulungu kuti mudziŵe zimene amakamba pa nkhaniyo. Komanso, muzifunsilako kwa Mkhristu wokhwima kuuzimu. Ganizilani cimene cipangitsa mfundoyo kukhala yokopa, cifukwa cake ni yabodza, ndi zimene mungacite kuti mupewe kutengela maganizo aconco. Ndithudi, tonse tingakwanitse kupewa kutengela maganizo a dziko mwa kumvela mau amene Paulo analembela Akhristu a ku Kolose. Iye anati: “Pitilizani kuyenda mwanzelu pocita zinthu ndi anthu akunja . . . kuti mudziŵe mmene mungayankhile wina aliyense.”—Akol. 4:5, 6.

^ par. 9 Anthu ambili sadziŵa kuti mau opezeka m’ma Baibo ena pa Yohane 7:53–8:11 ni owonjezela cabe, ndipo sali mbali ya Mau a Mulungu ouzilidwa. Cifukwa ca mau a pa lembali, anthu ena amakamba kuti popeza tonse ndise ocimwa, sitiyenela kumuimba mlandu munthu akacita cigololo. Koma Mulungu anapatsa mtundu wa Aisiraeli lamulo lakuti: “Mwamuna akapezeka akugona ndi mkazi wa mwiniwake, mwamuna ndi mkaziyo, onsewo azifela pamodzi.”—Deut. 22:22.