Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Tengelani Cilungamo ca Yehova na Cifundo Cake

Tengelani Cilungamo ca Yehova na Cifundo Cake

“Muzicita cilungamo ceni-ceni poweluza milandu. Muzisonyezana kukoma mtima kosatha ndi cifundo.”—ZEK. 7:9.

NYIMBO: 125, 88

1, 2. (a) Kodi Yesu anali kuciona bwanji Cilamulo ca Mulungu? (b) Kodi alembi na Afarisi anapotoza bwanji Cilamulo ca Mulungu?

YESU anali kucikonda Cilamulo ca Mose. Ndipo m’pomveka, cifukwa cinacokela kwa Atate ake, Yehova, amene ni wofunika ngako mu umoyo wake. Lemba la Salimo 40:8 linaonetselatu kuti Yesu adzakhala munthu wokonda cilamulo ca Mulungu. Pa lembali pamati: “Ndimakondwela ndi kucita cifunilo canu, inu Mulungu wanga, ndipo cilamulo canu cili mumtima mwanga.” Mwa mau na zocita zake, Yesu anaonetsa kuti Cilamulo ca Mulungu ni cangwilo, copindulitsa, ndiponso kuti zonse zolembedwa m’cilamuloco sizingalephele kukwanilitsidwa.—Mat. 5:17-19.

2 Conco, Yesu ayenela kuti anakhumudwa kwambili kuona alembi na Afarisi akupotoza Cilamulo ca Atate wake. Iwo anali kutsatila mosamalitsa mfundo zina zing’ono-zing’ono za m’Cilamulo. Yesu anati: “Mumapeleka cakhumi ca timbewu ta minti, dilili, ndi citowe.” Koma kodi vuto lawo linali ciani? Yesu anakambanso kuti: “Koma mumanyalanyaza zinthu zofunika za m’Cilamulo, monga cilungamo, cifundo ndi kukhulupilika.” (Mat. 23:23) Mosiyana na Afarisi, amene anali odzilungamitsa, Yesu anali kudziŵa bwino colinga ca Cilamulo, komanso makhalidwe a Mulungu amene anali kuonekela pa lamulo lililonse la m’cilamuloco.

3. Kodi m’nkhani ino tidzakambilana ciani?

3 Ise Akhristu sitili pansi pa Cilamulo ca Mose. (Aroma 7:6) Koma Yehova anaonetsetsa kuti Cilamulo casungiwa m’Mau ake Baibo, kuti citithandize. Sikuti amafuna kuti tizitsatila ciliconse colembewa m’Cilamulo, koma amafuna kuti tidziŵe na kutsatila “zinthu zofunika” kwambili, kapena kuti mfundo zimene panazikiwa malamulowo. Mwa ici, tingafunse kuti, ni mfundo ziti zimene tiphunzilapo pa makonzedwe okhala na mizinda yothaŵilako? M’nkhani yapita, tinakambilana zimene tiphunzilapo pa zimene munthu wothaŵa anali kucita. Koma makonzedwe amenewa atiphunzitsanso za makhalidwe a Yehova, na zimene tingacite kuti titengele citsanzo cake. Conco, m’nkhani ino tidzakambilana mafunso atatu awa: Kodi makonzedwe a mizinda yothaŵilako aonetsa bwanji cifundo ca Yehova? Kodi amatiphunzitsa ciani za mmene iye amaonela moyo? Nanga aonetsa bwanji kuti ni wacilungamo kwambili? Pokambilana funso lililonse, ganizilani zimene mungacite potengela citsanzo ca Atate wathu wakumwamba.—Ŵelengani Aefeso 5:1.

MAKONZEDWE OSANKHA “MIZINDA YOYENELELA” ANAONETSA CIFUNDO CA MULUNGU

4, 5. (a) Kodi Aisiraeli anacita ciani kuti mizinda yothaŵilako isakhale yovuta kufikako? (b) Kodi zimenezi zitiphunzitsa ciani za Yehova?

4 Mizinda 6 yothaŵilako inali yosavuta kufikako. Yehova analamula Aisiraeli kuti asankhe mizinda itatu kum’maŵa kwa Mtsinje wa Yorodano, na ina itatu kum’madzulo kwake. N’cifukwa ciani anacita zimenezi? Colinga cinali cakuti munthu wothaŵa azifika mwamsanga ndi mosavuta mumzinda wothaŵilako. (Num. 35:11-14) Miseu yopita ku mizinda yothaŵilako anali kuilambula na kuikonza bwino. (Deut. 19:3) Malinga ni mbili ya Ayuda, Aisiraeli anali kuika zikwangwani zothandiza munthu wothaŵa kudziŵa kumene kuli mizinda yothaŵilako. Popeza mizinda yothaŵilako inalipo, munthu amene wapha mnzake mwangozi sanali kuthaŵila kudziko lina, kumene akanayamba kulambila mafano.

5 Ganizilani cabe: Yehova analamula kuti munthu wopha mnzake mwadala, aziphedwa. Koma iye analamulanso kuti ngati munthu wapha mnzake mwangozi, azicitilidwa cifundo na kutetezedwa. Katswili wina wa Baibo anati: “Malangizo amene anapelekedwa anali omveka bwino na osavuta kuwatsatila. Pamenepa, Mulungu anaonetsa cisomo cake.” Yehova si woweluza wouma mtima amene amangofuna kulanga atumiki ake. Koma ni “wacifundo coculuka.”—Aef. 2:4.

6. Kodi khalidwe la Afarisi linali losiyana bwanji na cifundo ca Mulungu?

6 Koma Afarisi anali opanda cifundo. Mwacitsanzo, malinga ni olemba mbili ya Ayuda, Afarisi sanali kulola kukhululukila munthu ngati wacita colakwa cimodzi-modzi katatu. Yesu anapeleka fanizo limene lionetsa kuti Afarisi sanali kucitila cifundo anthu olakwa. Iye anakamba za Mfarisi wina amene popemphela anati: “Mulungu wanga, ndikukuyamikani cifukwa ine sindili ngati anthu enawa ayi. Iwo ndi olanda, osalungama ndi acigololo. Sindilinso ngati wokhometsa msonkho uyu.” Koma panthawi imodzi-modziyo, wokhometsa msonkhoyo anali kupemphela modzicepetsa kwa Mulungu kuti amukhululukile. N’cifukwa ciani Afarisi anali ouma mtima conco? Baibo imakamba kuti anali ‘kuona ena onse ngati opanda pake.’—Luka 18:9-14.

Ngati mukhala wofikilika, mumakhala ngati mwatsegula “njila” na kuilambula kuti anthu akhale omasuka kupempha cikhululukilo kwa inu (Onani palagilafu 4-8)

7, 8. (a) Kodi mungatengele bwanji citsanzo ca Yehova ngati munthu wina wakulakwilani? (b) N’cifukwa ciani kudzicepetsa n’kofunika kuti munthu athe kukhululukila ena?

7 Ise Akhristu tiyenela kutengela Yehova, osati Afarisi. Tifunika kukhala acifundo. (Ŵelengani Akolose 3:13.) Njila imodzi imene tingaonetsele kuti ndise acifundo ni mwa kukhala wokonzeka kukhululukila ena. (Luka 17:3, 4) Dzifunseni kuti, ‘Kodi nimaonetsa kuti ndine wokonzeka kukhululukila anthu amene anilakwila, ngakhale amene amanilakwila mobweleza-bweleza? Ngati wina wanilakwila, kodi nimakhala wofunitsitsa kukambilana naye kuti nibwezeletse mtendele?’

8 Kukhala wodzicepetsa n’kofunika kuti munthu akwanitse kukhululukila ena. Afarisi sanali kukhululukila ena cifukwa anali kuwaona ngati acabe-cabe. Koma ise Akhristu tifunika kukhululukila ena. Kucita zimenezi kudzaonetsa kuti ndise odzicepetsa ndipo ‘timaona ena kukhala otiposa.’ (Afil. 2:3) Kodi inu mudzatengela citsanzo ca Yehova mwa kukhala odzicepetsa? Ngati ndimwe wodzicepetsa, mumakhala ngati mwatsegula “njila” na kuilambulila kuti anthu akhale omasuka kupempha cikhululukilo kwa inu. Muzikhala wokonzeka kucitila cifundo ena, ndipo musamafulumile kukwiya.—Mlal. 7:8, 9.

MUZILEMEKEZA MOYO, NDIPO ‘SIMUDZAKHALA NA MLANDU WAMAGAZI’

9. Kodi Yehova anawathandiza bwanji Aisiraeli kuona kuti moyo wa munthu ni wopatulika?

9 Colinga cacikulu ca mizinda yothaŵilako cinali cofuna kuteteza Aisiraeli kuti asakhale na mlandu wa magazi. (Deut. 19:10) Yehova amaona kuti moyo ni wamtengo wapatali, ndipo amadana ndi “manja okhetsa magazi a anthu osalakwa.” (Miy. 6:16, 17) Popeza kuti Mulungu ni wacilungamo ndiponso woyela, sanalekelele anthu opha anzawo, olo kuti acita zimenezo mwangozi. N’zoona kuti munthu akapha mnzake mwangozi anali kumucitila cifundo. Komabe, iye anali kufunika kufotokozela akulu nkhaniyo. Ndipo akuluwo akapeza kuti sanaphe mnzake mwadala, munthuyo anali kufunika kukhala mumzinda wothaŵilako mpaka mkulu wa ansembe atamwalila. Nthawi zina, anali kukhala kumeneko kwa moyo wake wonse. Kuganizila zovuta zimene munthu wopha mnzake anali kukumana nazo, kunathandiza Aisiraeli onse kuona kuti moyo wa munthu ni wopatulika. Kuti Aisiraeli aonetse kuti anali kulemekeza wopatsa moyo, anali kufunika kupewa kucita zinthu zimene zikanaika moyo wa mnzawo paciopsezo.

10. Malinga ni mau a Yesu, kodi alembi na Afarisi anaonetsa bwanji kuti sanali kulemekeza moyo?

10 Mosiyana na Yehova, alembi na Afarisi sanali kulemekeza moyo. Motani? Yesu anawauza kuti: “Munalanda anthu kiyi yowathandiza kudziŵa zinthu. Inuyo simunaloŵemo, ndipo ofuna kuloŵamo munawatsekeleza!” (Luka 11:52) Alembi na Afarisi anali kufunika kuphunzitsa anthu tanthauzo la Mau a Mulungu na kuwathandiza kuyenda pa njila ya ku moyo wosatha. Koma iwo anali kucotsa anthu kwa Yesu, “Mtumiki Wamkulu wa moyo,” na kuwatsogolela m’njila yopita ku ciwonongeko camuyaya. (Mac. 3:15) Alembi na Afarisi anali onyada ndi odzikonda, ndipo sanali kulemekeza moyo kapena kuona ena kukhala ofunika. Anali ankhanza na opanda cifundo.

11. (a) Kodi mtumwi Paulo anaonetsa bwanji kuti anali kuona moyo mmene Mulungu amauonela? (b) N’ciani cingatithandize kuona nchito yolalikila ngati mmene Paulo anali kuionela?

11 Tingapewe bwanji khalidwe la alembi na Afarisi na kutengela Yehova? Tiyenela kulemekeza moyo na kuuona kukhala wamtengo wapatali. Mtumwi Paulo anaonetsa kuti anali kulemekeza moyo mwa kucitila umboni mokwanila. N’cifukwa cake anakamba kuti: “Ndine woyela pa mlandu wa magazi a anthu onse.” (Ŵelengani Machitidwe 20:26, 27.) Koma sikuti Paulo anali kulalikila cifukwa coopa mlandu wa magazi kapena cifukwa congofuna kukwanilitsa udindo wake ayi. Iye anali kukonda anthu, ndipo anali kuona miyoyo yawo kukhala yamtengo wapatali. (1 Akor. 9:19-23) Na ise tiyenela kuyesetsa kuona moyo mmene Mulungu amauonela. Yehova “amafuna kuti anthu onse alape.” (2 Pet. 3:9) Kodi n’zimene inunso mumafuna? Kukhala wacifundo kudzakulimbikitsani kugwila nchito yolalikila mwakhama, ndipo mwa kucita izi, mudzakhala na cimwemwe coculuka.

12. N’cifukwa ciani anthu a Mulungu afunika kupewa ngozi?

12 Njila ina imene tingasonyezele kuti timaona moyo mmene Yehova amauonela ni mwa kupewa ngozi. Tifunika kuyendetsa motoka mosamala, olo kuti tiyenda ku misonkhano. Tizipewanso ngozi poseŵenza, ngakhale pamene timanga kapena kukonzanso malo olambilila. Komanso, tizipewa kuika moyo wa ena paciwopsezo cifukwa cofuna kugwila nchito yoculuka, kupeza ndalama zambili, kapena kutsiliza msanga nchito. Mulungu wathu wacilungamo nthawi zonse amacita zinthu zoyenela, ndipo ise timafuna kutengela citsanzo cake. Maka-maka akulu ayenela kuyesetsa kupewa ngozi, ndiponso ayenela kuthandiza amene amaseŵenza nawo kukhala osamala. (Miy. 22:3) Conco, ngati mkulu wakukumbutsani malangizo opewela ngozi, muzilabadila. (Agal. 6:1) Muziona moyo mmene Yehova amauonela. Mukacita conco, ‘simudzakhala na mlandu wa magazi.’

MUZIWELUZA “MALINGA NDI MALAMULO AMENEWA”

13, 14. N’ciani cimene akulu ku Isiraeli anali kucita pofuna kuonetsa cilungamo ca Yehova?

13 Yehova analamula akulu a mu Isiraeli kuti aziweluza milandu mogwilizana na cilungamo cake. Coyamba, akuluwo anafunika kumvetsetsa zimene zinacitikazo. Ndiyeno, pofuna kudziŵa ngati wopha munthu ni woyenela kum’citila cifundo kapena ayi, anafunika kupenda mosamala colinga cake, maganizo, na khalidwe lake la m’mbuyomo. Kuti aweluze mogwilizana na cilungamo ca Mulungu, anafunika kudziŵa ngati munthuyo anapha mnzake “atamubisalila” ndiponso “cifukwa codana naye.” (Ŵelengani Numeri 35:20-24.) Cinanso, ngati mlandu unali na mboni, zinali kufunika kukhala zosacepela ziŵili kuti atsimikizile kuti munthu anaphadi mnzake mwadala.—Num. 35:30.

14 Conco, pambuyo pomvetsetsa nkhani yonse, akulu anali kuganizilanso za munthuyo, osati za colakwa cake cabe. Anafunika kukhala na luso la kuzindikila, kapena kuti luso loganizila nkhani mwakuya kuti aone cimene cinapangitsa vutolo. Koposa zonse, anafunika mzimu woyela wa Yehova, umene ukanawathandiza kucita zinthu mogwilizana na nzelu, cifundo, na cilungamo cake.—Eks. 34:6, 7.

15. Kodi Yesu na Afarisi anali kusiyana bwanji pa nkhani ya mmene anali kuonela ocimwa?

15 Afarisi anali kungoganizila colakwa cimene munthu wacita osati mtima wake. Mwacitsanzo, pamene Afarisi anaona Yesu akudya cakudya kunyumba kwa Mateyu, anafunsa ophunzila ake kuti: “N’cifukwa ciani mphunzitsi wanu amadya limodzi ndi okhometsa msonkho ndi anthu ocimwa?” Yesu anawayankha kuti: “Anthu abwinobwino safuna dokotala, koma odwala ndi amene amamufuna. Conco pitani mukaphunzile tanthauzo la mau akuti, ‘Ndikufuna cifundo, osati nsembe.’ Cifukwa ine sindinabwele kudzaitana anthu olungama, koma ocimwa.” (Mat. 9:9-13) Kodi pamenepa tingakambe kuti Yesu anali kulekelela macimo? Kutalitali! Kumbukilani kuti imodzi mwa mfundo zikulu-zikulu mu ulaliki wa Yesu inali yolimbikitsa anthu kulapa macimo awo. (Mat. 4:17) Koma panthawiyi, Yesu anazindikila kuti ena mwa ‘okhometsa msonkho na anthu ocimwa’ anali kufuna kusintha. Iwo sanabwele kunyumba kwa Mateyu kudzadya cakudya cabe. Koma ‘ambili mwa iwo anali kutsatila [Yesu].’ (Maliko 2:15) N’zomvetsa cisoni kuti Afarisi sanaone zabwino zimene Yesu anaona mwa anthuwo. Mosiyana na Mulungu wacilungamo ndi wacifundo, Afarisi anali kuweluza anzawo kuti ni ocimwa ndi kuti sangasinthe.

16. Kodi komiti ya ciweluzo iyenela kuyesetsa kuzindikila ciani?

16 Akulu masiku ano afunika kuyesetsa kutengela Yehova, Mulungu amene “amakonda cilungamo.” (Sal. 37:28) Coyamba, afunika ‘kufufuza na kufunsa’ mafunso mosamala kuti atsimikizile ngati munthuyo anacitadi chimo. Akapeza kuti munthuyo anacitadi chimo, ayenela kuweluza mlanduwo mogwilizana ndi Malemba. (Deut. 13:12-14) Akulu amene ali m’komiti ya ciweluzo afunika kupenda mosamala kuti atsimikizile ngati Mkhristu amene anacita chimo lalikulu ni wolapa. Nthawi zina, zimavuta kudziŵa ngati munthu ni wolapadi kapena ayi. Kuti akulu adziŵe ngati munthu ni wolapadi, afunika kupenda kaonedwe kake ka zinthu, kaimidwe ka maganizo ake, na mmene mtima wake ulili. (Chiv. 3:3) Munthu wolapa ndiye ayenela kucitilidwa cifundo. *

17, 18. N’ciani cimene akulu ayenela kucita kuti adziŵe ngati munthu ni wolapadi? (Onani pikica kuciyambi.)

17 Mosiyana na Yehova na Yesu, akulu sangaone za mumtima mwa munthu. Ngati ndinu mkulu, kodi mungacite ciani kuti mudziŵe ngati munthu ni wolapadi na mtima wonse? Coyamba, pemphani Mulungu kuti akupatseni nzelu na luso la kuzindikila. (1 Maf. 3:9) Caciŵili, pendani Mau a Mulungu na kufufuza malangizo m’zofalitsa za kapolo wokhulupilika kuti mukwanitse kusiyanitsa pakati pa “cisoni ca dziko,” na “cisoni cogwilizana ndi cifunilo ca Mulungu,” kapena kuti kulapa kweni-kweni. (2 Akor. 7:10, 11) Ganizilani zimene Malemba amakamba ponena za anthu amene anali olapa na amene anali osalapa. Kodi Baibo imakambanji ponena za kaimidwe kawo ka maganizo, mmene anali kumvelela, komanso kacitidwe kawo ka zinthu?

18 Cotsiliza, yesetsani kuganizila za munthuyo. Ganizilani za umoyo wake, zolinga zake, na zofooka zake. Ponena za Yesu mutu wa mpingo, Baibo inakambilatu kuti: “Sadzaweluza potengela zimene wangoona ndi maso ake, kapena kudzudzula potengela zimene wangomva ndi makutu ake. Adzaweluza mwacilungamo anthu onyozeka ndipo adzadzudzula anthu mowongoka mtima, pothandiza ofatsa a padziko lapansi.” (Yes. 11:3, 4) Imwe akulu ndimwe abusa aang’ono a Yesu. Conco, Yesuyo adzakuthandizani kuweluza ngati mmene iye amaweluzila. (Mat. 18:18-20) Kodi si ndise oyamikila kukhala na akulu acikondi amene amayesetsa kuweluza mwacilungamo? Timayamikila ngako zimene iwo amacita potithandiza kuonetsa cifundo na cilungamo kwa wina na mnzake mumpingo.

19. Pa zimene taphunzila zokhudza mizinda yothaŵilako, ni mfundo ziti zimene mufuna kuseŵenzetsa mu umoyo wanu?

19 M’Cilamulo ca Mose, muli “zinthu zofunika kuzidziŵa ndi coonadi” cokhudza Yehova na mfundo zake zolungama. (Aroma 2:20) Mwacitsanzo, pa makonzedwe okhala na mizinda yothaŵilako, akulu aphunzilapo mmene angaweluzile milandu mogwilizana na “cilungamo ceni-ceni.” Komanso, ife tonse taphunzilapo mmene tingaonetsele “kukoma mtima kosatha ndi cifundo” kwa abale athu. (Zek. 7:9) Masiku ano, sitili pansi pa Cilamulo ca Mose. Koma Yehova sasintha, ndipo amaonabe kuti cilungamo na cifundo n’zofunika kwambili. Ni mwayi waukulu ngako kulambila Mulungu, amene anatilenga m’cifanizilo cake. Conco, tiyenela kutengela makhalidwe ake, ndi kuthaŵila kwa iye.

^ par. 16 Onani “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” mu Nsanja ya Olonda ya September 15, 2006, peji 30.