NSANJA YA MLONDA—YOPHUNZILA September 2017

Magazini ino ili na nkhani zophunzila wiki ya October 23-November 26, 2017.

Phunzilani Kukhala Wodziletsa

Kodi zitsanzo za m’Baibo zingatithandize bwanji kukhala odziletsa? N’cifukwa ciani Akhristu afunika kuphunzila kukhala odziletsa?

Tengelani Khalidwe la Yehova la Cifundo

Panthawi ina, Mulungu anadzidziŵikitsa kwa Mose mwa kuchula dzina lake ndi makhalidwe ake. Khalidwe loyamba limene Mulungu anachula ndi cifundo. Kodi cifundo n’ciani, nanga n’cifukwa ciani muyenela kuyesetsa kukhala na khalidwe limeneli?

MBILI YANGA

Nakhala na Mwayi Wotumikila Pamodzi ndi Amuna Auzimu

David Sinclair afotokoza zina zokhudza mautumiki amene wacita ndi cimwemwe cimene wapeza potumikila pamodzi ndi abale na alongo okhulupilika kwa zaka 61, pa Beteli ya ku Brooklyn.

“Mau a Mulungu Wathu Adzakhala Mpaka Kalekale”

Baibo inalembedwa kale-kale, koma ni buku imene imagulidwa na anthu ambili kuposa buku ina iliyonse mosasamala kanthu za kusintha kwa zinenelo, kusintha kwa zandale, ndi kuletsedwa kwa nchito yomasulila Baibo.

“Mau a Mulungu . . . Ndi Amphamvu”

Anthu ambili asintha kwambili umoyo wawo cifukwa cophunzila Mau a Mulungu. N’ciani cimene tifunika kucita kuti Mau a Mulungu athe kusintha umoyo wathu?

‘Limba Mtima, Ugwile Nchito Mwamphamvu’

N’cifukwa ciani tifunika kukhala olimba mtima? Nanga tingacite ciani kuti tikhale nalo khalidwe limeneli?