Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

“Mau a Mulungu Wathu Adzakhala Mpaka Kalekale”

“Mau a Mulungu Wathu Adzakhala Mpaka Kalekale”

“Udzu wobiliwilawo wauma. Maluwawo afota. Koma mau a Mulungu wathu adzakhala mpaka kalekale.”—YES. 40:8.

NYIMBO: 95, 97

1, 2. (a) Kodi umoyo ukanakhala bwanji kukanakhala kuti kulibe Baibo? (b) Kodi cofunika n’ciani kuti kuŵelenga Baibo kukhale kopindulitsa?

KODI muganiza kuti umoyo ukanakhala bwanji kukanakhala kuti kulibe Baibo? Sembe palibe malangizo odalilika otithandiza pa umoyo wathu. Ndipo sitikanapeza mayankho okhutilitsa a mafunso okhudza Mulungu, moyo, na tsogolo la anthu. Komanso, sitikanadziŵa zimene Yehova anacitila anthu m’mbuyomu.

2 Komabe, cosangalatsa n’cakuti zinthu sizili conco. Yehova watipatsa Mau ake, Baibo. Ndipo watitsimikizila kuti Mau akewo adzakhalapo mpaka kale-kale. Mtumwi Petulo anagwila mau a pa Yesaya 40:8. Vesi imeneyi siikamba mwacindunji za Baibo monga mmene tiidziŵila masiku ano. Ngakhale n’conco, mfundo yake ingagwilenso nchito ponena za uthenga wa m’Baibo. (Ŵelengani 1 Petulo 1:24, 25.) Tingapindule na uthenga wa m’Baibo maka-maka ngati imapezeka m’citundu cimene timamvetsetsa. Kuyambila kale-kale, anthu okonda Mau a Mulungu akhala akuidziŵa mfundo imeneyi. Ndipo kwa zaka zambili, anthu oona mtima anagwila nchito yomasulila ndi kufalitsa Mabaibo mwakhama, ngakhale kuti anakumana ndi mavuto. Colinga cawo cinali cogwilizana kwambili na cifunilo ca Mulungu cakuti “anthu, kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke ndi kukhala odziwa coonadi molondola.”—1 Tim. 2:3, 4.

3. N’ciani cimene tidzakambilana m’nkhani ino? (Onani pikica kuciyambi.)

3 M’nkhani ino, tidzakambilana mmene Mau a Mulungu apitilizila kukhalapo mosasamala kanthu za (1) kusintha-sintha kwa zinenelo, (2) kusintha kwa zandale kumene kunakhudza zinenelo, ndi (3) kuletsedwa kwa nchito yomasulila Baibo. Kodi kukambilana zimenezi kudzatithandiza bwanji? Kudzatithandiza kuti tizikonda kwambili Mau a Mulungu. Kudzatithandizanso kuti tizikonda kwambili Yehova, Mlembi wa Baibo amene anatipatsa Mau ake kuti tipindule nawo.—Mika 4:2; Aroma 15:4.

KUSINTHA KWA ZINENELO

4. (a) Kodi zinenelo zimasintha bwanji m’kupita kwa nthawi? (b) N’ciani cionetsa kuti Mulungu wathu amakonda anthu a zinenelo zonse? Nanga zimenezi zimakupangitsani kumva bwanji?

4 M’kupita kwa nthawi, zinenelo zimasintha, moti mau amene poyamba anali kutanthauza zinthu zina angasinthe kwambili n’kuyamba kutanthauza zinthu zinanso. Mwina mwakumbukila mau ena a m’citundu canu amene muona kuti asintha kwambili tanthauzo. Izi n’zimenenso zinacitika na Ciheberi komanso Cigiriki, zinenelo zimene zinagwilitsidwa nchito polemba Baibo. Ciheberi na Cigiriki camakono n’cosiyana ngako na cimene cinaliko panthawi imene Baibo inali kulembedwa. Conco, pafupi-fupi munthu aliyense, kuphatikizapo aja amene amadziŵa Ciheberi na Cigiriki camakono, amafunika kuŵelenga Baibo yomasulilidwa kuti amvetsetse Mau a Mulungu. Ena amaganiza kuti afunika kuphunzila Ciheberi ndi Cigiriki kuti azitha kuŵelenga Baibo m’cinenelo cakale. Komabe, kucita izi sikungakhale kothandiza kweni-kweni. * N’zokondweletsa kuti lomba Baibo kapena mbali yake, yamasulilidwa m’zinenelo pafupi-fupi 3,000. N’zoonekelatu kuti Yehova afuna kuti anthu ocokela ‘kudziko lililonse, fuko lililonse, ndi cinenelo ciliconse’ apindule na Mau ake. (Ŵelengani Chivumbulutso 14:6.) Kodi izi sizikupangitsani kumuyandikila kwambili Mulungu wathu wacikondi ndi wopanda tsankho?—Mac. 10:34.

5. N’ciani cinacititsa Baibo ya King James Version kukhala yochuka?

5 Baibo yamasulilidwa m’zinenelo zosiyana-siyana, koma m’kupita kwa nthawi, zinenelo zimenezo nazonso zimasintha. Baibo imene poyamba inali yosavuta kumva, m’kupita kwa zaka imakhala yovuta kumva. Mwacitsanzo, ganizilani za Baibo yomasulidwa m’Cizungu ya King James Version. Baibo imeneyi inafalitsidwa koyamba mu 1611. Baibo ya King James Version inakhala imodzi mwa mabaibo a Cizungu ofala ngako, ndipo inakhudza kwambili cinenelo ca Cizungu. * Komabe, m’Baibo imeneyi, dzina la Mulungu limapezeka m’malo ocepa kwambili. Dzina lakuti “Yehova” limapezeka m’mavesi oŵelengeka, ndipo m’mavesi ena a Malemba Aciheberi muli dzina lakuti “AMBUYE,” lolembedwa m’zilembo zazikulu. M’mabaibo amene anapulintiwa pambuyo pake, dzina lakuti “AMBUYE,” lolembedwa m’zilembo zazikulu, limapezekanso m’mavesi ena a Malemba Acigiriki Acikhristu. Mwanjila imeneyi, omasulila Baibo ya King James Version anaonetsa kuti anali kudziŵa kuti dzina la Mulungu lifunika kupezekanso m’malemba ochedwa Cipangano Catsopano.

6. N’cifukwa ciani timayamikila kuti tili na Baibulo la Dziko Latsopano?

6 Ngakhale n’conco, m’kupita kwa zaka, mau ambili m’Baibo ya King James Version anakhala acikale. Umu ni mmenenso zilili na Mabaibo akale amene anamasulidwa m’zinenelo zina. Ndithudi, ndise oyamikila ngako kuti tili na Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika limene lili na mau osavuta kumva. Baibulo la Dziko Latsopano, lathunthu kapena mbali yake, lipezeka m’zinenelo zoposa 150. Mwa ici, anthu ambili akhoza kuŵelenga Baibo imeneyi. Cifukwa cakuti ili na mau osavuta kumva, Mau a Mulungu amatifika pamtima. (Sal. 119:97) Cinthu cina capadela kwambili na Baibulo la Dziko Latsopano n’cakuti linabwezeletsa dzina la Mulungu m’Malemba.

CINENELO COFALA

7, 8. (a) N’cifukwa ciani Ayuda ambili m’zaka za m’ma 200 B.C.E sanali kumvetsetsa Malemba Aciheberi? (b) Kodi Septuagint ya Cigiriki n’ciani?

7 Cifukwa ca kusintha-sintha kwa zandale, nazonso zinenelo zimene anthu ambili amakamba zimasintha. Kodi Mulungu wathandiza bwanji anthu kuti amve Mau ake olo kuti zinenelo zakhala zikusintha? Kuti tipeze yankho, tiyeni tikambilane zimene zinacitika zaka zambili m’mbuyomo. Mabuku 39 oyambilila a m’Baibo analembedwa ndi Aisiraeli, kapena kuti Ayuda. Iwo ndiwo anali oyamba kupatsidwa “mau opatulika a Mulungu.” (Aroma 3:1, 2) Komabe, pofika m’zaka za m’ma 200 B.C.E, Ayuda ambili sanali kumvetsetsa Ciheberi. Cifukwa ciani? Cifukwa cakuti Alexander Wamkulu anafutukula ufumu wa Girisi mwa kugonjetsa madela ambili. (Dan. 8:5-7, 20, 21) Pamene ufumu wa Girisi unakula, anthu ambili a mu ufumuwo, kuphatikizapo Ayuda amene anali m’madela osiyana-siyana, anayamba kukamba Cigiriki. Popeza kuti Ayuda ambili anayamba kukamba Cigiriki, cinakhala covuta kwambili kuti azimvetsetsa Malemba Aciheberi. Kodi vutoli linathetsedwa bwanji?

8 Capakati pa zaka za m’ma 200 B.C.E., mabuku asanu oyambilila a m’Baibo anamasulilidwa kucoka m’Ciheberi kupita m’Cigiriki. Kumasulila mabuku onse a Malemba a Ciheberi kupita m’Cigiriki kunatha m’zaka za m’ma 100 B.C.E. Mabuku a Cigiriki amenewo anayamba kuchedwa kuti Septuagint ya Cigiriki. Imeneyi inali Baibo yoyamba ya Cigiriki yokhala na mabuku onse a malemba amene ena amati Cipangano Cakale.

9. (a) Kodi Baibo ya Septuagint na ena akale anakhudza bwanji anthu amene anali kuŵelenga Mau a Mulungu? (b) Kodi inu mumakonda kwambili vesi iti m’Malemba a Ciheberi?

9 Baibo ya Septuagint inathandiza kwambili Ayuda ndi anthu ena amene anali kukamba Cigiriki kuti azitha kuŵelenga Malemba amene poyamba anali m’Ciheberi. Tangoganizilani mmene iwo anasangalalila kumvetsela kapena kuŵelenga Mau a Mulungu m’citundu cimene anali kucimvetsetsa! M’kupita kwa nthawi, mabuku ena a m’Baibo anamasulidwa m’zinenelo zina zofala, monga Cisiriya, Cigotiki, ndi Cilatini. Mwacionekele, ambili amene anali kuŵelenga Malemba Oyela m’citundu cimene anali kumvetsetsa, anapeza mavesi ena amene anawakonda kwambili. Nafenso tili na mavesi ena a m’Baibo amene timakonda. (Ŵelengani Salimo 119:162-165.) Ndithudi, Mau a Mulungu apitiliza kukhalapo ngakhale kuti zinenelo zakhala zikusintha-sintha.

KULETSA NCHITO YOMASULILA BAIBO

10. N’cifukwa ciani zinali zovuta kwa anthu ambili kukhala na Baibo m’nthawi ya John Wycliffe?

10 Panthawi ina, atsogoleli osiyana-siyana amphamvu anayesetsa kuletsa nchito yomasulila Baibo kuti anthu wamba asakhale na mwayi woiŵelenga. Komabe, anthu ena oona mtima anayesetsa molimba mtima kumasulila Baibo. Mwacitsanzo, ganizilani za katswili wina wa zacipembedzo wa m’zaka za m’ma 1300 C.E., dzina lake John Wycliffe. Iye anali kufunitsitsa kuti munthu aliyense akhale na mwayi wopindula na Mau a Mulungu. Koma panthawiyo, zinali zovuta kwambili kuti anthu wamba a ku England akhale na Baibo. Cifukwa ciani? Cifukwa cimodzi cinali cakuti Mabaibo anali odula. Zinali conco cifukwa Mabaibo anali kucita kuwakopa pa manja, ndipo panali kuloŵa ndalama zambili kuti alembe Baibo. Kuwonjezela apo, anthu ambili sanali kudziŵa kuŵelenga. N’zoona kuti anthu anali kumvetsela Baibo ikuŵelengedwa akapita ku chechi. Koma n’zokayikitsa kuti anali kumvetsetsa zimene zinali kuŵelengedwa. Takamba conco cifukwa cakuti Baibo imene inali kugwilitsidwa nchito m’machechi panthawiyo (yochedwa Vulgate) inali ya Cilatini. Koma m’zaka zimenezo, anthu wamba ambili sanali kumva Cilatini. Kodi anthuwo akanacipeza bwanji cuma camtengo wapatali ca m’Baibo?—Miy. 2:1-5.

John Wycliffe ndi anthu ena anali ofunitsitsa kuti Mau a Mulungu afikile munthu aliyense. Kodi nanunso n’zimene mumafuna? (Onani palagilafu 11)

11. Kodi Baibo ya Wycliffe inawakhudza bwanji anthu?

11 Mu 1382, Baibo ya Cizungu ya Wycliffe inayamba kufalitsidwa. Posapita nthawi, anthu ambili otsatila Wycliffe anayamba kuikonda kwambili Baibo imeneyi. Otsatila a Wycliffe ochedwa kuti a Loladi anali ofunitsitsa kuthandiza anthu wamba kuti Mau a Mulungu awafike pamtima. Iwo anali kuyenda m’midzi yosiyana-siyana m’dziko lonse la England kukalalikila. Kaŵili-kaŵili, a Loladi akapeza anthu anali kuwaŵelengela mavesi ena a m’Baibo ya Wycliffe, ndi kuwasiyila Mabaibo olembedwa pa manja. Zimene anacitazi zinapangitsa kuti zinthu zisinthe kwambili. Zinathandiza anthu ambili kukhalanso ndi cidwi na Mau a Mulungu.

12. Kodi atsogoleli a cipembedzo anacita ciani ndi Wycliffe, Baibo yake, ndi otsatila ake?

12 Kodi atsogoleli acipembedzo anacita ciani? Anayamba kuzonda Wycliffe, otsatila ake, ndi Baibo yake. Iwo anayambanso kuzunza a Loladi. Atsogoleli amenewo anayesetsa kufuna-funa Mabaibo a Wycliffe, ndipo akawapeza anali kuwaononga. Olo kuti Wycliffe anali atafa kale, iwo anamuweluzabe kuti anali wampatuko. Popeza kuti anali atafa kale, zinali zosatheka kumulanga. Ngakhale n’conco, iwo analamula kuti mafupa ake afukulidwe. Mafupawo anawatentha, ndipo phulusa lake anakalitaya mumtsinje wochedwa Swift. Komabe, atsogoleli acipembedzo analephela kuletsa Mau a Mulungu kufalikila kwa anthu, amene anali na cifuno coŵelenga Baibo na kuimvetsetsa. Kuyambila nthawi imeneyo, anthu ambili a ku Europe ndi a m’maiko ena anayamba kumasulila ndi kufalitsa Mabaibo kuti ngakhale anthu wamba apindule na Mau a Mulungu.

“AMENE NDIMAKUPHUNZITSANI KUTI ZINTHU ZIKUYENDELENI BWINO”

13. Kodi ndise otsimikiza za ciani? Nanga zimenezi zimalimbitsa bwanji cikhulupililo cathu?

13 Baibo inauzilidwa ndi Mulungu. Koma sikuti nchito yomasulila Mabaibo monga Septuagint, Wycliffe, King James Version, ndi Mabaibo ena ocita kumasulidwa, inauzilidwa mwacindunji ndi Mulungu. Komabe, tikaona mbili ya Mabaibo amenewa na ena amene afalitsidwa, timapeza umboni wakuti lonjezo la Yehova lakwanilitsidwa, lakuti Mau ake adzakhala mpaka kale-kale. Kodi umenewu si umboni wamphamvu wotsimikizila kuti malonjezo ena onse a Yehova adzakwanilitsidwa?—Yos. 23:14.

14. Kodi Mau a Mulungu amatithandiza bwanji kukulitsa cikondi cathu pa iye?

14 Kuwonjezela pa kulimbitsa cikhulupililo cathu, kukambilana mmene Baibo yatetezekela m’zaka zonsezi, kumalimbitsa cikondi cathu pa Yehova. * Ndiye cifukwa cake iye anatipatsa Mau ake, si conco kodi? Nanga n’cifukwa ciani waiteteza kuti ikhalepobe mpaka lelo? Cifukwa cakuti amatikonda, ndipo afuna kutiphunzitsa kuti zinthu zizitiyendela bwino. (Ŵelengani Yesaya 48:17, 18.) Conco, tiyenela kusonyeza kuti timayamikila cikondi cimene Yehova wationetsa mwa kumukonda na kumvela malamulo ake.—1 Yoh. 4:19; 5:3.

15. Kodi m’nkhani yotsatila tidzakambilana ciani?

15 Popeza kuti timakonda Mau a Mulungu, timafuna kupindula nawo mokwanila. Kodi tingacite ciani kuti tipindule kwambili na zimene timaŵelenga m’Baibo pa phunzilo laumwini? Tingacite ciani kuti tithandize anthu kulemekeza Baibo pamene tilalikila? Nanga anthu amene amakhala na mbali yophunzitsa ena mumpingo, angaonetse bwanji kuti Malemba ndiwo maziko a zimene amaphunzitsa? M’nkhani yotsatila, tidzakambilana mafunso amenewa.

^ par. 4 Onani nkhani yakuti “Kodi Muyenera Kuphunzira Chiheberi ndi Chigiriki?” mu Nsanja ya Olonda ya November 1, 2009.

^ par. 5 Mau ena okuluŵika amene anthu amakamba m’Cizungu anacokela m’Baibo ya King James Version.

^ par. 14 Onani kabokosi kakuti “ Kadzioneleni Mwekha!”