Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Phunzilani Kukhala Wodziletsa

Phunzilani Kukhala Wodziletsa

“Makhalidwe amene mzimu woyela umatulutsa ndiwo . . . kudziletsa.”—AGAL. 5:22, 23.

NYIMBO: 83, 52

1, 2. (a) Ni mavuto ati amene amabwela cifukwa ca kusadziletsa? (b) N’cifukwa ciani kukambilana za kudziletsa n’kofunika kwambili?

KUDZILETSA ni khalidwe locokela kwa Mulungu. (Agal. 5:22, 23) Yehova amacita zinthu modziletsa nthawi zonse. Koma ise anthu opanda ungwilo, nthawi zina timalephela kukhala odziletsa. Ndipo mavuto ambili amene anthu akukumana nawo masiku ano amabwela cifukwa ca kusadziletsa. Mwacitsanzo, cifukwa ca kusadziletsa, anthu ena amanyalanyaza kucita zinthu, ena sacita bwino kusukulu ndipo enanso sagwila nchito mwakhama. Kusadziletsa kungabweletsenso mavuto monga ucidakwa, kukamba mau oipa, ciwawa, kusila kwa vikwati, nkhongole zosafunikila, zizoloŵezi zoipa, kumangidwa, kuvutika maganizo, matenda opatsilana mwa kugonana, mimba zapathengo, ndi mavuto ena ambili-mbili.—Sal. 34:11-14.

2 Ndithudi, anthu osadziletsa adzibweletsela mavuto ndi kubweletsanso mavuto kwa ena. Ndipo vuto la kusadziletsa likukulila-kulila. M’zaka za m’ma 1940, anthu anacita kafuku-fuku pa nkhani ya kudziletsa, koma kafuku-fuku waposacedwa waonetsa kuti masiku ano, vuto la kusadziletsa kwa anthu lafika poipa kwambili. Izi n’zosadabwitsa kwa anthu amene amaphunzila Mau a Mulungu, cifukwa Baibo inakambilatu kuti cimodzi mwa zizindikilo za “masiku otsiliza” n’cakuti anthu adzakhala “osadziletsa.”—2 Tim. 3:1-3.

3. N’cifukwa ciani Akhiristu afunika kuyesetsa kukhala odziletsa?

3 N’cifukwa ciani tifunika kuyesetsa kukhala odziletsa? Ganizilani zifukwa ziŵili izi zofunika kwambili. Coyamba, anthu odziletsa sakhala na mavuto ambili. Amakhala na mtendele wa m’maganizo, amatha kukhala na mabwenzi abwino, ndipo sakhala aukali, ankhawa kwambili, kapena ovutika maganizo ngati mmene amakhalila anthu osadziletsa. Caciŵili, kukaniza ziyeso na kudziletsa n’kofunika kwambili kuti munthu akhalebe pa ubwenzi wabwino na Mulungu. Umboni wa zimenezi ni mavuto amene anabwela cifukwa ca kusadziletsa kwa Adamu na Hava. (Gen. 3:6) Komanso, ganizilani za mavuto ambili-mbili amene anthu akumana nawo kucokela nthawi ya Adamu cifukwa colephela kukhala odziletsa.

4. N’cifukwa ciani anthu amene amalephela kudziletsa pa zinthu zina sayenela kutaya mtima?

4 Popeza ndise opanda ungwilo, nthawi zina zimativuta kukhala odziletsa. Yehova amadziŵa zimenezi, ndipo amafuna kutithandiza kugonjetsa zizoloŵezi zoipa zimene tingakhale nazo. (1 Maf. 8:46-50) Yehova pokhala Bwenzi lathu lacikondi, amalimbikitsa anthu oona mtima amene amafuna kum’tumikila koma amalephela kudziletsa pa zinthu zina. Tsopano tiyeni tikambilane za citsanzo cangwilo ca Yehova pa nkhaniyi. Kenako, tidzakambilana zimene tingaphunzilepo pa zitsanzo za anthu ochulidwa m’Baibo amene anali odziletsa ndi amene anali osadziletsa. Pamapeto pake, tidzakambilana zinthu zina zimene tingacite kuti tikulitse khalidwe lodziletsa.

YEHOVA WATIPATSA CITSANZO CA KUDZILETSA

5, 6. Kodi Yehova wapeleka citsanzo canji pa nkhani ya kudziletsa?

5 Yehova amacita zinthu modziletsa nthawi zonse cifukwa nchito zake zonse n’zangwilo. (Deut. 32:4) Koma ife ndife opanda ungwilo. Ngakhale n’conco, tingathe kulidziŵa bwino khalidwe la kudziletsa ndi kutengela citsanzo ca Yehova mwa kupenda mmene iye waonetsela khalidweli. Ni pa zocitika zina ziti pamene Yehova waonetsa kudziletsa?

6 Ganizilani mmene Yehova anaonetsela kudziletsa pamene Satana anam’pandukila mwamwano. Izi zitacitika, Mulungu anafunika kucitapo kanthu ndithu. Angelo okhulupilika a Mulungu ayenela kuti anakhumudwa, kukwiya, na kunyansidwa naye kwambili Mdyelekezi. Mwina inunso mumamvela cimodzi-modzi mukaganizila mavuto ambili-mbili amene Satana wacititsa. Koma Yehova sanacite zinthu mopupuluma pankhaniyi. Iye anacita zinthu modekha ndiponso mwanzelu. Komanso waonetsa khalidwe la kuleza mtima na cilungamo pocita zinthu ndi Satana wopandukayo. (Eks. 34:6; Yobu 2:2-6) Motani? Yehova walola kuti papite nthawi yaitali cifukwa safuna kuti aliyense adzawonongedwe, koma “amafuna kuti anthu onse alape.”—2 Pet. 3:9.

7. Kodi tiphunzilapo ciani pa citsanzo ca Yehova?

7 Citsanzo ca Yehova ca kudziletsa catiphunzitsa kuti nafenso tifunika kuganizila mosamala tisanakambe kapena kucita zinthu. Sitifunika kucita zinthu mopupuluma. Ngati takumana ndi vuto lalikulu, tifunika kudekha kuti ticite zinthu mwanzelu. Tiyenelanso kupempha nzelu kwa Mulungu kuti tikambe na kucita zinthu mwanzelu. (Sal. 141:3) Kumbukilani kuti ngati munthu acita zinthu ali wokwiya, n’zosavuta kulakwitsa. Ambili a ife tinakambapo mau oipa kapena kucita zinthu zosayenela cifukwa copupuluma, ndipo pambuyo pake tinadziimba mlandu.—Miy. 14:29; 15:28; 19:2.

ZITSANZO ZABWINO NA ZOIPA ZA ATUMIKI A MULUNGU

8. (a) N’kuti kumene tingapeze zitsanzo za anthu odziletsa? (b) N’ciani cinathandiza Yosefe kusangonja pamene mkazi wa Potifara anali kumunyengelela? (Onani pikica kuciyambi.)

8 N’zitsanzo ziti za m’Baibo zimene zionetsa kuti kudziletsa n’kofunika? Mosakayikila, mukumbukila anthu ena ochulidwa m’Baibo amene anadziletsa atakumana ndi ziyeso. Mmodzi wa iwo ni Yosefe, mwana wa Yakobo. Iye anaonetsa khalidwe la kudziletsa pamene anali kutumikila m’nyumba ya Potifara, mkulu wa asilikali olondela mfumu Farao. Mkazi wa Potifara anayamba kukhumbila Yosefe, amene anali “wokongola m’maonekedwe ndi wa thupi loumbika bwino,” mwakuti anamunyengelela mobweleza-bweleza kuti agone naye. N’ciani cinathandiza Yosefe kuti asagonje? Mwacionekele, anaganizila mavuto amene akanakumana nawo akanapanda kudziletsa. Ndipo zinthu zitafika poipa, iye anam’thaŵa mkaziyo. Yosefe anati: “Ndingacitilenji coipa cacikulu conci n’kucimwila Mulungu?”—Gen. 39:6, 9; ŵelengani Miyambo 1:10.

9. Mungakonzekele bwanji kukaniza ziyeso?

9 Kodi tiphunzilapo ciani pa citsanzo ca Yosefe? Coyamba n’cakuti nthawi zina tingafunike kuthaŵa ngati tayesedwa kuti ticite chimo. Anthu ena asanakhale Mboni anali na zizoloŵezi zoipa monga kudya kwambili, kumwa kwambili, kupepa fwaka, kuseŵenzetsa mankhwala osokoneza ubongo, ciwelewele, ndi zina. Ngakhale kuti anabatizika, ena nthawi zina amayesedwabe kuti ayambenso makhalidwe oipawa. Koma ngati mwayesedwa kuti muphwanye lamulo linalake la Yehova, ganizilani mavuto auzimu amene mungakumane nawo cifukwa colephela kudziletsa ku zilakolako zoipa. Cinanso, muyenela kuganizila nthawi na malo kumene mungakumane na ziyeso ndi kuonelatu zimene mungacite kuti muzipewe. (Sal. 26:4, 5; Miy. 22:3) Ngati mwakumana naco ciyeso, pemphani Yehova kuti akupatseni nzelu ndi kukuthandizani kukhala odziletsa.

10, 11. (a) Kodi acicepele ambili amakumana na vuto lanji kusukulu? (b) N’ciani cingathandize Akhristu acicepele kukana ngati ayesedwa kucita khalidwe loipa?

10 Acicepele ambili acikhristu akukumana ndi ciyeso ngati cimene Yosefe anakumana naco. Mwacitsanzo, ganizilani za mtsikana wina, dzina lake Kim. Ambili m’kilasi mwake anali na khalidwe laciwelewele cakuti akabwela kusukulu pa Mande, anali kucita kukamba monyadila za anthu amene anagona nawo kumapeto kwa wiki. Kim sanali kukambako nkhani zimenezi cifukwa sanali kucitako khalidwe loipalo. Iye anakamba kuti nthawi zina anali kudziona monga munthu “wotayika ndi wosoŵa anzake.” Anakambanso kuti anzake anali kumuona monga wopusa cifukwa analibe cisumbali. Koma Kim anacita bwino kusakhala na cisumbali. Anadziŵa kuti cilakolako ca kugonana cimakhala camphamvu ngako kwa acicepele. (2 Tim. 2:22) Anzake a kusukulu nthawi zambili anali kumufunsa ngati akali namwali. Zimenezi zinam’patsa mwayi wofotokoza cifukwa cake sanali kucitako zaciwelewele. Inu Akhristu acicepele amene mumakana kucita zaciwelewele, timakunyadilani kwambili. Ndipo Yehova nayenso amakunyadilani!

11 M’Baibo mulinso zitsanzo zoticenjeza za anthu amene anacita ciwelewele cifukwa ca kusadziletsa. Imafotokozanso mavuto amene amatulukapo cifukwa ca kusadziletsa. Ngati mukukumana na ciyeso monga cimene Kim anakumana naco, mungacite bwino kuganizila mozama nkhani ya mnyamata wopanda nzelu wochulidwa pa Miyambo caputa 7. Mufunikanso kuganizila zimene Aminoni anacita, ndi mavuto amene anakumana nawo cifukwa ca khalidwe lake loipa. (2 Sam. 13:1, 2, 10-15, 28-32) Makolo angathandize ana awo kucita zinthu mwanzelu ndi kukhala odziletsa pa nkhani ya cikondi ca pakati pa mwamuna ndi mkazi. Angacite zimenezi mwa kukambilana nawo pa kulambila kwa pabanja nkhani za m’Baibo zimene tachulazi.

12. (a) Kodi Yosefe anaonetsa bwanji kudziletsa pocita zinthu na abale ake? (b) Ni pa zocitika ziti pamene tiyenela kukhala odziletsa?

12 Pa cocitika cina, Yosefe anapelekanso citsanzo cabwino ca kudziletsa. Iye pofuna kudziŵa zimene zinali mumtima mwa abale ake, sanadziulule kwa iwo pamene anabwela ku Iguputo kudzagula cakudya. Atagwidwa ndi cifundo cacikulu, Yosefe anacoka n’kupita kwayekha kukalila. (Gen. 43:30, 31; 45:1) Ngati Mkhristu mnzanu kapena munthu wina amene mumakonda wakulakwilani, mungacite bwino kutengela citsanzo ca Yosefe. Kucita zimenezi kudzakuthandizani kupewa kucita zinthu mopupuluma. (Miy. 16:32; 17:27) Komanso, ngati muli na wacibale wocotsedwa, mufunika kukhala wodziletsa kuti musamakambe naye mosafunikila. N’zoona kuti kukhala wodziletsa pa zocitika ngati zimenezi si kopepuka. Koma cimene cingatithandize ndi kukumbukila kuti zimene tikucita n’zogwilizana ndi citsanzo cimene Mulungu watipatsa komanso malangizo ake.

13. Tiphunzilapo ciani pa nkhani ya Mfumu Davide?

13 Citsanzo cina ca m’Baibo pa nkhani ya kudziletsa ni ca Mfumu Davide. Iye anali na ulamulilo waukulu, koma anapewa kuugwilitsila nchito molakwika pamene anali kuvutitsidwa na Sauli ndi pamene ananyozedwa na Simeyi. (1 Sam. 26:9-11; 2 Sam. 16:5-10) Komabe, sikuti nthawi zonse Davide anali kudziletsa. Kumbukilani kuti iye anacita cigololo na Bati-seba, komanso anafuna kupha munthu waumbombo Nabala ndi banja lake. (1 Sam. 25:10-13; 2 Sam. 11:2-4) Ngakhale n’conco, tingaphunzile mfundo zofunika kwa Davide. Mfundo yoyamba ni yakuti, oyang’anila pakati pa anthu a Mulungu, afunika kusamala kwambili kuti apewe kuseŵenzetsa mphamvu zawo molakwika. Yaciŵili, sitifunika kudzidalila n’kumaganiza kuti sitingagonje ku ciyeso.—1 Akor. 10:12.

ZIMENE MUNGACITE KUTI MUKHALEBE ODZILETSA

14. N’ciani cinacitikila m’bale wina? Nanga n’cifukwa ciani na ise tifunika kukhala odekha pa zocitika zaconco?

14 Kodi mungacite ciani kuti mukulitse khalidwe la kudziletsa? Ganizilani zimene zinacitikila Luigi. Tsiku lina, motoka ya munthu wina inagunda kumbuyo kwa motoka yake. Ngakhale kuti dilaiva winayo ndiye anali wolakwa, anayamba kunyoza Luigi na kufuna kumumenya. Luigi anapemphela kwa Yehova kuti amuthandize kukhala wodekha. Kenako, anayesa kumukhazika mtima pansi dilaivayo, koma sizinathandize. Luigi anangolemba dzina la kampani ya inshuwalansi ya motoka ya munthuyo, n’kumusiya akali kukalipa. Patapita wiki imodzi, Luigi anapita kukacita ulendo wobwelelako kwa mayi wina. Iye anadabwa kuona kuti mwamuna wa mayiyo ni dilaiva uja amene anamunyoza. Munthuyo anacita manyazi, ndipo anam’pepesa Luigi cifukwa comulalatila. Iye analonjeza kuti adzapita kukakamba na kampani ya inshuwalansi ya Luigi kuti imukonzele mwamsanga motoka. Munthuyo anakhalapo pamene Luigi anali kulalikila mkazi wake ndipo anayamikila ngako zimene anamvelazo. Pamenepa, m’baleyu anazindikila kuti anacita bwino kwambili kukhala wodekha panthawi imene munthuyo anali kumunyoza. Anazindikilanso vuto limene likanakhalapo akanalephela kuugwila mtima.—Ŵelengani 2 Akorinto 6:3, 4.

Zimene timacita ngati ena atikhumudwitsa zingakhudze ulaliki wathu (Onani palagilafu 14)

15, 16. Kodi kuphunzila Baibo kungakuthandizeni bwanji inu na banja lanu kukulitsa khalidwe la kudziletsa?

15 Kuphunzila Baibo mwakhama ndi mosamala kungathandize Akhristu kukulitsa khalidwe la kudziletsa. Kumbukilani kuti Mulungu anauza Yoswa kuti: “Buku la malamulo ili lisacoke pakamwa pako, uziliwelenga ndi kusinkhasinkha usana ndi usiku, kuti uonetsetse kuti ukutsatila zonse zolembedwamo. Pakuti ukatelo, udzakhala ndi moyo wopambana, ndipo udzacita zinthu mwanzelu.” (Yos. 1:8) Kodi kuphunzila Baibo kungakuthandizeni bwanji kukulitsa khalidwe la kudziletsa?

16 Monga mmene taonela, m’Baibo muli nkhani zambili zoonetsa mapindu amene tingapeze tikakhala odziletsa ndi mavuto amene tingakumane nawo cifukwa ca kusadziletsa. Yehova anali na colinga pouzila anthu kulemba nkhani zimenezi. (Aroma 15:4) Conco, ni cinthu canzelu kuŵelenga nkhanizi, kuziphunzila, na kuzisinkha-sinkha. Yesetsani kuona zimene mungaphunzilepo inu panokha ndi banja lanu. Pemphani Yehova kuti akuthandizeni kuseŵenzetsa zimene mwaphunzila m’Mau ake. Yesetsani kuzindikila mbali imene mumalephela kudziletsa. Ndiyeno, ipempheleleni nkhaniyo ndi kuona zimene mungacite kuti muwongolele. (Yak. 1:5) Komanso, ngati mufufuza mosamala m’zofalitsa zathu, mudzapeza mfundo zina zabwino zimene zingakuthandizeni pa vuto lanulo.

17. Kodi makolo angathandize bwanji ana awo kukhala odziletsa?

17 Kodi mungathandize bwanji ana anu kukhala odziletsa? Makolo, kumbukilani kuti ana anu sanabadwe na khalidwe la kudziletsa. Kuti ana aphunzile makhalidwe abwino, kuphatikizapo khalidwe la kudziletsa, makolo mufunika kupeleka citsanzo cabwino. (Aef. 6:4) Conco, ngati ana anu amalephela kudziletsa, dzipendeni ndi kuona ngati mukupeleka citsanzo cabwino pankhaniyi. Ana anu adzapindula kwambili ngati aona kuti nthawi zonse inu mumalalikila, kupezeka pa misonkhano, ndi kucititsa kulambila kwa pabanja. Komanso, musamangololela zilizonse zimene anawo apempha. Akanileni ngati apempha zinthu zosayenela. Mwacitsanzo, Yehova anaikila Adamu na Hava malile kapena kuti malamulo. Colinga cake cinali cakuti awaphunzitse kulemekeza ulamulilo wake. Nanunso makolo mufunika kulangiza ana anu ndi kuwapatsa citsanzo cabwino kuti muwaphunzitse kukhala odziletsa. Kukonda ulamulilo wa Mulungu na kulemekeza mfundo zake zabwino, n’zinthu zofunika kwambili zimene inu makolo muyenela kuphunzitsa ana anu.—Ŵelengani Miyambo 1:5, 7, 8.

18. N’cifukwa ciani tifunika kusankha mabwenzi athu mwanzelu?

18 Kaya ndimwe kholo kapena ayi, mufunika kusankha mabwenzi anu mwanzelu. Sankhani mabwenzi amene adzakulimbikitsani kukhala na zolinga zauzimu ndi kupewa mavuto. (Miy. 13:20) Mabwenzi auzimu adzakulimbikitsani kucita zabwino ndipo mudzatengela citsanzo cawo ca kudziletsa. Mosakayikila, nawonso adzapindula na citsanzo canu cabwino. Kudziletsa kumene mudzakhala nako kudzakuthandizani kukhala na umoyo wabwino, kukhala pa ubwenzi wabwino na Mulungu, ndi kukhala bwino ndi anthu amene mumawakonda.