Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

BAIBULO LIMASINTHA ANTHU

Ndinaphunzila Kulemekeza Akazi Ndiponso Kudziona Moyenela

Ndinaphunzila Kulemekeza Akazi Ndiponso Kudziona Moyenela
  • CAKA COBADWA: 1960

  • DZIKO: FRANCE

  • MBILI YANGA: NDINALI KUKONDA MANKHWALA OSOKONEZA UBONGO NDIPO SINDINALI KULEMEKEZA AKAZI

KUKULA KWANGA:

Ndinabadwila m’dziko la France, kum’maŵa koma cakumpoto kwa dzikoli mum’zinda wa Mulhouse, umene unali kudziŵika cifukwa ca ciwawa. Ndipo anthu a kumeneko anali osauka. Ndimakumbukila ciwawa komanso mikangano imene inalipo m’mabanja ambili m’delalo. M’banja lathu tinali kuona kuti akazi ndi otsika ndipo nthawi zambili anali kunyalanyazidwa ndi amuna. Ndinaphunzitsidwa kuti mkazi afunika kugwila nchito ku khichini, kusamalila mwamuna, ndi ana.

Zinthu paumwana wanga zinali zovuta kwambili. Nditafika zaka 10, atate anamwalila cifukwa ca kumwa moŵa kwambili. Patapita zaka 5, mkulu wanga anadzipha. Ndipo m’caka cimodzimodzico, ndinadzipenyela ndekha wina akuphedwa cifukwa ca mikangano ya pabanja. Zimenezi zinandisoŵetsa cocita. Anthu a m’banja langa anandiphunzitsa mmene ndingagwilitsile nchito mipeni ndi mfuti pa cocitika ciliconse cimene cinafuna kuti ndigwilitsile nchito zinthu zimenezi. Ndili wosokonezeka maganizo conco, ndinayamba kudzidinda zizindikilo pa khungu, ndipo ndinayamba kumwa moŵa.

Nditafika zaka 16, tsiku lililonse ndinali kumwa mabotolo 10 kapena 15 a moŵa. Posapita nthawi ndinayamba kuseŵenzetsa mankhwala osokoneza bongo. Conco, ndinayamba kuba zinthu ndi kugulitsa nsimbi zakale kuti ndipeze ndalama zolipilila milandu yanga. Pamene ndinali kukwanitsa zaka 17, ndinali nditaloŵako kale m’ndende. Cifukwa ca kuba ndi ciwawa, ndinaloŵa m’ndende nthawi zokwanila 18.

Zinthu zinafika poipa kwambili nditafika zaka 20. Patsiku ndinali kukoka ndudu 20 za camba, ndinalinso kuseŵenzetsa mankhwala a mtundu wa heroin ndi mitundu ina yoletsedwa. Nthawi zambili ndinali kutsala pang’ono kufa cifukwa ca kuledzela. Ndinayamba kugulitsa mankhwala osokoneza bongo ndipo sindinali kusiya mipeni ndi mfuti kulikonse kumene ndinali kupita. Tsiku lina ndinafuna kulasa munthu ndi mfuti, koma mpholopolo inagunda kansimbi ka palamba wake ndi kugwa pansi. Nditakwanitsa zaka 24, amai anamwalila ndipo mkwiyo wanga unaonjezeka. Anthu akandiona ndikubwela, anali kuthaŵa. Ndipo cifukwa ca ndeu, pafupifupi wikendi iliyonse ndinali kukhomeledwa ku polisi kapena kugonekedwa m’cipatala cacikulu kuti andisoke mabala a zilonda.

Nditakwanitsa zaka 28, ndinakwatila. Malinga ndi zimene ndafotokoza kale, mkazi wanga sindinali kum’patsa ulemu. Ndinali kumutukwana ndi kumumenya. Sitinali kucitila zinthu limodzi monga banja. Ndinali kuganiza kuti kum’patsa zinthu zakuba monga ndolo (masikiyo), mphete, ndi zibangili kunali kokwanila. Koma mwadzidzidzi zinthu zinasintha. Mkazi wanga anayamba kuphunzila Baibulo ndi Mboni za Yehova. Atangophunzilako kamodzi, mkazi wanga analeka kukoka fodya, anayamba kukana kutenga ndalama zakuba, ndipo anandibwezela ndolo (masikiyo), mphete, ndi zibangili. Zimenezi zinandikwiitsa kwambili. Ndinali kutsutsa zakuti iye aziphunzila Baibulo ndipo ndinali kukoka fodya pamaso pake. Ndinamupanga kukhala coseketsa kwa onse a m’dela lathu.

Tsiku lina usiku ndili woledzela kwambili, mwangozi ndinatentha nyumba yathu. Mkazi wanga anandipulumutsa, ndipo anapulumutsanso mwana wathu wamkazi wa zaka 5 kumoto umene unali kuyaka kwambili. Moŵa utatha m’mutu, ndinayamba kudziimba mlandu. Mumtima, ndimangoti Mulungu sangandikhululukile. Ndinakumbukila kuti nthawi ina abusa anakamba kuti wocita zoipa adzapita ku helo. Ngakhalenso dokotala wanga wa zamaganizo anandiuza kuti: “Iwe kwatha, sungapulumuke.”

MMENE BAIBULO LINASINTHILA UMOYO WANGA:

Nyumba yathu itapsa, tinasamukila kwa makolo a mkazi wanga. A Mboni atabwela kudzaceza ndi mkazi wanga, ndinawafunsa kuti: “Kodi Mulungu angandikhululukile macimo anga onse?” Iwo anandiŵelengela 1 Akorinto 6:9-11 m’Baibulo. Mavesi amenewa amakamba za makhalidwe amene Mulungu sakondwela nao. Koma amakambanso kuti: “Ena mwa inu munali otelo.” Mau amenewa ananditsimikizila kuti n’zotheka kusintha. Ndipo a Mboniwo anandiuza kuti Mulungu amandikonda, ndipo ananditsimikizila mwa kundiŵelengela mau a pa 1 Yohane 4:8. Atandilimbikitsa conco, ndinawapempha kuti azindiphunzitsa Baibulo kaŵili pa mlungu, ndipo ndinayamba kupezeka pa misonkhano yao yacikristu. Nthawi zonse ndinali kupemphela kwa Yehova.

Mwezi usanathe, ndinaganiza zoleka kuseŵenzetsa mankhwala osokoneza bongo ndi kumwa moŵa. Posakhalitsa, ndinamva monga cinacake caphulika m’thupi mwanga. Kucokela panthawiyo, ndinayamba kukumana ndi mavuto monga kuona zideludelu, mutu kuŵaŵa, kumva kupweteka m’thupi, ndi mavuto ena obwela cifukwa coleka kukoka ndi kumwa moŵa. Ngakhale zinali conco, ndinaona kuti Yehova akundigwila dzanja ndipo akundilimbikitsa. Ndinamva ngati mmene mtumwi Paulo anamvelela. Ponena za thandizo limene Mulungu anam’patsa, Paulo anati: “Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kucokela kwa iye amene amandipatsa mphamvu.” (Afilipi 4:13) Patapita nthawi, ndinaleka kukoka fodya.—2 Akorinto 7:1.

Kuonjezela pa kundithandiza kuti ndikhale ndi umoyo wabwino, Baibulo linatithandizanso kukhala ndi banja labwino. Ndinayamba kuona mkazi wanga moyenelela. Ndinayamba kumulemekeza kwambili ndi kumuuza mau kuti “pepani” ndi akuti “zikomo.” Ndinakhalanso tate wabwino kwa mwana wathu. Nditaphunzila Baibulo kwa caka cimodzi, ndinadzipeleka kwa Yehova ndi kubatizidwa, potengela citsanzo ca mkazi wanga.

MAPINDU AMENE NDAPEZA:

Ndine wotsimikiza kuti Baibulo linandipulumutsa. Ngakhale anthu a m’banja langa amene si Mboni amakamba kuti ndikanafa kale cifukwa coseŵenzetsa mankhwala osokoneza bongo kapena pomenyana ndi anthu.

Umoyo wa banja lathu unasintha kwambili cifukwa ca mfundo za m’Baibulo, zimene zimafotokoza udindo wanga monga mwamuna ndi tate. (Aefeso 5:25; 6:4) Tinayamba kucitila zinthu pamodzi monga banja. Tsopano, sindilekelela mkazi wanga kugwila nchito yekhayekha kukhichini. M’malomwake, ndimamuthandiza kuti acite bwino nchito yake youza anthu mau a Mulungu. Iyenso amandicilikiza mosangalala popeza kuti ndine mkulu pampingo.

Cikondi ndi cifundo ca Yehova Mulungu zakhudza kwambili umoyo wanga. Ndine wofunitsitsa kuuzako ena amene amadziona kuti sangasinthe, za makhalidwe a Yehova amenewa, popeza kuti inenso ndi mmene ndinalili. Ndidziŵa kuti Baibulo lili ndi mphamvu zothandiza aliyense kuti akhale ndi moyo wabwino ndi waphindu. Baibulo landiphunzitsa kulemekeza anthu onse, amuna ndi akazi omwe. Landiphunzitsanso kudziona moyenela.