Muganiza Bwanji?
Kodi Baibo ingakuthandizeni kukhala bwenzi la Mulungu?
ANTHU ENA AMAKHULUPILILA KUTI . . .
sangakhale mabwenzi a Mulungu cifukwa amadziona kuti ni odetsedwa komanso ocimwa. Ena amakamba kuti Mulungu satidela nkhawa. Imwe muganiza bwanji?
ZIMENE BAIBO IMAKAMBA
Mulungu “amakonda anthu owongoka mtima.” (Miyambo 3:32) Ngati timvela Mulungu, tingakhale mabwenzi ake.
MFUNDO ZINA ZIMENE BAIBO IMAKAMBA
Mulungu afuna kuti tikhale mabwenzi ake. —Yakobo 4:8.
Monga Bwenzi lathu, Mulungu ni wokonzeka kutikhululukila na kutithandiza.—Salimo 86:5.
Mabwenzi a Mulungu amakonda zimene iye amakonda na kudana na zimene amadana nazo. —Aroma 12:9.