2 Thandizo pa Kuthetsa Mavuto
Mavuto ena mu umoyo, amakhala mwina kwa zaka zambili. Angayambe pang’ono-pang’ono ife osazindikila. Kodi Baibo ingatithandize kupeza nzelu zothetsela mavuto aconco okhalitsa ndi othetsa nzelu? Ganizilani zitsanzo zotsatila.
KUKHALA NA NKHAWA MOPAMBANITSA
Rosie anakamba kuti, “N’nali kuvutika maganizo kwambili cifukwa coganizila mavuto oopsa amene ningakumane nawo m’tsogolo.” Ni malemba ati a m’Baibo amene anam’thandiza? Imodzi mwa iwo ni Mateyu 6:34 imene imati: “Musamade nkhawa za tsiku lotsatila, cifukwa tsiku lotsatila lidzakhala ndi zodetsa nkhawa zakenso. Zoipa za tsiku lililonse n’zokwanila pa tsikulo.” Rosie anakamba kuti, mau awa a Yesu anam’thandiza kusadela nkhawa zimene zingacitike mailo. Anawonjezela kuti, “Popeza n’nali kale na nkhawa zambili, sin’nafune kuonjezela nkhawa zina cifukwa ca zinthu zimene sizingacitike, ndipo mwina sizikanacitika n’komwe.”
Yasmine nayenso anaona kuti nkhawa zinam’kulila kwambili. Anati: “N’nali kulila masiku ena mu wiki, tulo osatuona. N’nali kumvela monga nkhawa zikunimeza wamoyo.” Ni lemba liti linam’thandiza? Anati ni 1 Petulo 5:7 imene imati: ‘Mutulileni nkhawa zanu zonse [Mulungu], pakuti amakudelani nkhawa.’ Yasmine anakamba kuti: “N’napitiliza kupemphela kwa Yehova, ndipo anayankha mapemphelo anga. N’namvela monga kuti mtolo wolema wacoka pa mapewa anga. Nthawi na nthawi malingalilo oipa amabwelabe, koma lomba nimadziŵa mocitila nawo.”
KUZENGELEZA KUCITA ZINTHU
Mzimayi wacitsikana, Isabella, anakamba kuti: “Niganiza kuti kuzengeleza ise n’cakubanja, cifukwa 2 Timoteyo 2:15 imene imati: “Cita ciliconse cotheka kuti usonyeze kuti ndiwe wovomelezeka pamaso pa Mulungu, wanchito wopanda cifukwa cocitila manyazi.” Isabella anakamba kuti: “Sin’nali kufuna kuti Yehova azicita manyazi na nchito yanga, cabe cifukwa cakuti nimazengeleza.” Iye anasintha kwambili.
atate nawo niwozengeleza kucita zinthu. Nimaleka kugwila nchito yofunikila kuti ningokhala cabe, kapena kuti nitambe TV. Ni khalidwe loipa cifukwa nkhawa imawonjezeka, ndipo zimacititsa munthu kusacita bwino nchito.” Mfundo imene inam’thandiza ipezeka paNayenso Kelsey anati: “Nikakhala na nchito yakuti nicite, n’nali kuzengeleza mpaka nthawi yocita nchitoyo itatsala pang’ono kutha. Zikakhala conco, n’nali kudandaula, kusoŵa tulo, na kukhala na nkhawa. Zinthu sizinali bwino kwa ine.” Kelsey anapeza thandizo pa Miyambo 13:16, imene imati: “Aliyense wocenjela amacita zinthu mozindikila, koma wopusa amafalitsa ucitsilu.” Iye anafotokoza mfundo imene anaphunzilapo pa lembali. Anati: “Ni cinthu canzelu kucita zinthu mozindikila na kulinganiza bwino zinthu. Lomba pa thebulo yanga nimakhala na ndandanda ya nchito zimene nifunika kucita. Izi ziman’thandiza kucita zinthu pa nthawi yake, osati kuyembekezela mpaka nthawi itatha.”
KUSUNGULUMWA
Kirsten anati: “Mwamuna wanga ananithaŵa, n’kunisiya ndi ana anayi aang’ono.” Ni mfundo iti ya m’Malemba imene inam’thandiza? Ni mfundo ya pa Miyambo 17:17, yakuti: “Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse, ndipo ilo ndi m’bale amene anabadwila kuti akuthandize pakagwa mavuto.” Kirsten anapempha thandizo kwa ena mu mpingo, amene nawonso amatumikila Yehova. Kodi iwo anam’thandiza bwanji? Iye anati: “Anzanga a mumpingo ananithandiza m’njila zambili! Ena anali kunibweletsela mphatso, monga sopo, mafuta na zinthu zina, kuphatikizapo maluŵa ndipo anali kuzisiya pakhomo. Komanso, anzanga ena ananithandiza pamene ine ndi ana anga tinali kukukila ku nyumba ina. Izi zinacitika katatu konse. Mnzanga wina ananithandiza kupeza nchito. Nthawi zonse Akhristu anzanga anali kunithandiza.”
Delphine amene tam’chula kuciyambi, nayenso anali kusungulumwa. Pambuyo potaikilidwa zonse anati: “N’nali kuona kuti onse acitila pamodzi zinthu koma ine nili nekha. N’nali kusungulumwa kwambili.” Lemba limodzi limene linam’thandiza ni Salimo 68:6, limene limati: ‘Mulungu akucititsa osungulumwa kukhala ndi nyumba.’ Anafotokoza kuti: “N’nadziŵa kuti masiku ano, lembali silitanthauza cabe kukhala na nyumba yeni-yeni. N’namvetsa kuti Mulungu amatipatsanso nyumba yauzimu, malo a citetezo ceni-ceni kumene tingapeze mabwenzi eni-eni okonda Yehova, amene angatilimbikitse. Komanso, n’nadziŵa kuti siningakhale pa ubwenzi na ena ngati ine sindili pa ubwenzi na Yehova. Lemba la Salimo 37:4 linanithandiza kucita zimenezi. Lembali limati: ‘Komanso sangalala mwa Yehova, ndipo adzakupatsa zokhumba za mtima wako.’”
Potsiliza anakamba kuti: “N’nazindikila kuti niyenela kukhala pa ubwenzi wolimba na Yehova. Iye ndiye bwenzi labwino koposa onse. Conco, kuti nikhale pa ubwenzi na anthu amene amakonda Mulungu, n’nakonza ndandanda ya zocita zauzimu zimene ningacitile nawo pamodzi. N’naphunzila kuona zabwino zimene amacita, na kunyalanyaza zofooka zawo.”
N’zoona kuti mabwenzi amene amatumikila Mulungu nawonso ni opanda ungwilo. Ndipo mofanana ndi anthu ena onse, Mboni za Yehova zimakumana na mavuto. Koma zimene anthu amaphunzila m’Baibo zimawalimbikitsa kuthandiza ena mmene angathele. Ni cinthu canzelu kupanga ubwenzi na anthu aconco. Komabe, kodi mfundo za m’Baibo zingakuthandizeni kupilila mavuto amene sangathe masiku ano, monga matenda osacilitsika kapena cisoni cimene timakhala naco tikafedwa?
Ngati museŵenzetsa malangizo a m’Baibo mudzapeza mabwenzi abwino amene angakuthandizeni