Kodi Mulungu Amamva Mapemphelo Anu?
Mukamapemphela, kodi muganiza kuti Mulungu amamvadi mapemphelo anu?
ZIMENE BAIBO IMAKAMBA
Mulungu amamvetsela. Baibo imatitsimikizila kuti “Yehova ali pafupi ndi onse oitanila pa iye. Iye ali pafupi ndi onse amene amamuitana m’coonadi. . . . Adzamva kufuula kwawo kopempha thandizo.”—Salimo 145:18, 19.
Mulungu amafuna kuti muzipemphela kwa iye. Baibo imati: “Pa ciliconse, mwa pemphelo ndi pembedzelo, pamodzi ndi ciyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu.” —Afilipi 4:6.
Mulungu amasamala kwambili za imwe. Mulungu amadziŵa bwino kwambili mavuto athu na nkhawa zathu, ndipo amafuna kutithandiza. Baibo imati: “Citani zimenezi pamene mukumutulila nkhawa zanu zonse, pakuti amakudelani nkhawa.”—1 Petulo 5:7.