Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mulungu Amasamala za Inu

Mulungu Amasamala za Inu

M’Baibo muli malangizo abwino kwambili cifukwa ni buku locokela kwa Mulungu. Baibo si buku la malangizo a zaumoyo. Komabe, ingatithandize kudziŵa zimene tingacite tikakumana na zinthu zosoŵetsa mtendele, tikamavutika maganizo, tikapwetekedwa mtima, kapena tikadwala matenda odetsa nkhawa.

Koposa zonse, Baibo imatitsimikizila kuti Mlengi wathu, Yehova Mulungu, a amamvetsa maganizo athu na mmene timamvela kuposa munthu wina aliyense. Iye ni wofunitsitsa kutithandiza pa mavuto aliwonse amene timakumana nawo. Mwacitsanzo, onani malemba aŵili awa olimbikitsa:

“Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka. Ndipo odzimvela cisoni mumtima mwawo amawapulumutsa.”—SALIMO 34:18.

“Pakuti ine, Yehova Mulungu wako, ­ndagwila dzanja lako lamanja. Ine amene ndikukuuza kuti, ‘Usacite mantha. Ineyo ndikuthandiza.’”—YESAYA 41:13.

Koma kodi Yehova amatithandiza bwanji ngati tikudwala matenda a maganizo? Monga muonele m’nkhani zotsatilazi, Yehova amatithandiza m’njila zambili poonetsa kuti amasamaladi za ife.

a Yehova ni dzina la Mulungu.—Salimo 83:18.