Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YA PACIKUTO | KODI MUDZALANDILA MPHATSO YA MULUNGU YOPAMBANA ZONSE?

Mudzacitapo Ciani pa Mphatso ya Mulungu Yopambana Zonse?

Mudzacitapo Ciani pa Mphatso ya Mulungu Yopambana Zonse?

“Cikondi cimene Khristu ali naco cimatikakamiza . . . Iye anafelanso onse kuti amene ali moyo asakhale moyo wongodzisangalatsa okha, koma akhale moyo wosangalatsa amene anawafela.”—2 Akorinto 5:14, 15.

MPHATSO yapadela imene tingalandile iyenela kutisonkhezela kuyamikila. Yesu anaonetsa kufunika kocita zimenezi atacilitsa amuna 10 odwala matenda ofooketsa opanda mankhwala. Mmodzi wa iwo “anabwelela, akutamanda Mulungu mokweza mau.” Ndiyeno Yesu anati: “Amene ayeletsedwa si anthu 10 kodi? Nanga ena 9 ali kuti?” (Luka 17:12-17) Tiphunzilapo ciani pamenepa? Ena akaticitila zabwino, timaiŵala mwamsanga.

Dipo imapambana mphatso zonse. Palibe mphatso ina yaikulu imene tinalandilapo kuposa imeneyi. Nanga mufunika kucitapo ciani pa zimene Mulungu wakucitilani?

  • Mudziŵeni bwino Wopeleka mphatso. Dipo lidzabweletsela anthu moyo wamuyaya. Koma kuti akapeze moyo umenewo, afunika kucitapo kanthu. Yesu anauza Mulungu m’pemphelo kuti: “Moyo wosatha adzaupeza akamaphunzila ndi kudziŵa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munamutuma.” (Yohane 17:3) Ngati wina wakuuzani kuti pamene munali mwana, munthu wina anapulumutsa moyo wanu, mudzakhala ndi cidwi cofuna kudziŵa zambili zokhudza munthuyo, komanso cifukwa cake anakupulumutsani, si conco? Yehova Mulungu, amene anapeleka mphatso ya dipo yopulumutsa moyo, afuna kuti mum’dziŵe bwino. Afunanso kuti mukhale naye paubale. Baibo imatilimbikitsa kuti: “Yandikilani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikilani.”—Yakobo 4:8.

  • Khulupililani dipo. Baibo imati: “Iye wokhulupilila mwa Mwanayo ali nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:36) Kodi kukhulupilila kumatanthauza ciani? Kumatanthauza kucitapo kanthu. Cikhulupililo cathu mu dipo cimaonekela mwa nchito zathu. (Yakobo 2:17) Ni nchito zabwanji zimenezo? Kuti mphatso ikhale yako, umangofunika kutambasula dzanja ndi kuilandila. N’cimodzi-modzi na dipo. Mufunika kutambasula dzanja na kuilandila. Mungacite bwanji zimenezi? Mwa kuphunzila ndi kucita zimene Mulungu amafuna kwa inu. * Pemphani Mulungu kuti akukhululukileni, ndi kuti mukhale na cikumbumtima coyela. Fikilani Mulungu m’pemphelo muli ndi cidalilo conse kuti dipo idzabweletsadi mtendele, citetezo, na madalitso osatha kwa onse amene amaikhulupilila.—Aheberi 11:1.

  • Muzipezeka pa Cikumbutso ca imfa ya Yesu. Yesu anayambitsa mwambo umene umacitika caka ciliconse pofuna kutikumbutsa za mphatso ya dipo. Pokamba za mwambo umenewu, Yesu anati: “Muzicita zimenezi pondikumbukila.” (Luka 22:19) Mboni za Yehova zidzakumbukila imfa ya Yesu pa Ciŵili, April 11, 2017, dzuŵa litaloŵa. Pulogilamu imeneyi, imene idzatenga ola limodzi, idzaphatikizapo nkhani ya m’Baibo imene idzafotokoza cifukwa cake imfa ya Yesu ni yofunika. Idzafotokozanso madalitso amene imabweletsa masiku ano, ndi amene tidzapeza kutsogolo. Caka catha, anthu pafupi-fupi 20 miliyoni zungulile dziko lonse anapezeka pa Cikumbutso. Tikupemphani kuti mukakhale nafe poyamikila mphatso yaikulu ya Mulungu imeneyi.

^ par. 7 Njila yabwino ngako yodziŵila Mulungu na kukhala naye pa ubwenzi, ni mwa kuphunzila Mau ake, Baibo. Kuti mudziŵe mmene mungacitile zimenezi, pemphani wa Mboni za Yehova kapena yendani pa webusaiti yathu ya www.pr418.com.