Kuti Munthu Akhale Mtumiki Wacikhristu, Kodi Afunika Kukhala Wosakwatila?
PA DZIKO lonse, zipembedzo monga Chechi ya Roma Katolika, machechi osiyana-siyana a Orthodox, Cibuda, ndi zipembedzo zina, zimafuna kuti azibusa ndi atsogoleli awo azikhala osakwatila. Komabe, anthu ambili amaona kuti cimene cinayambitsa umbeta wacipembedzo ni ciwelewele cimene cafala pakati pa abusa a zipembedzo zosiyana-siyana.
Conco, ni bwino kufunsa kuti, Kodi umbeta wacipembedzo ni ciyenelezo ca m’Malemba ca atumiki acikhristu? Kuti tiyankhe funso limeneli, tiyeni tikambilane mmene mwambo umenewu unayambila na kufalikila, ndi mmene Mulungu amauonela.
MMENE UMBETA UNAYAMBILA M’CIPEMBEDZO
Buku yakuti Encyclopædia Britannica imafotokoza kuti umbeta ni “kukhala wosakwatila kapena wosakwatiwa komanso kupewa kugonana, nthawi zambili cifukwa ca udindo umene m’busa wacipembedzo ali nao, kapena pa cifukwa cakuti munthu ni wokangalika pa zacipembedzo.” Mu 2006, pokambilana ndi mabungwe a zipembedzo za Roma Katolika, Papa Benedict wa namba 16 anaonetsa kuti umbeta ni “mwambo umene unayamba kale kwambili, cifupi-fupi nthawi ya Atumwi.”
Komabe, Akhristu a m’zaka 100 zoyambilila sanali kucita mwambo wacipembedzo umenewu wa kukhala wosakwatila. Ndipo mtumwi Paulo, amene anakhalako m’zaka 100 zoyambilila, anacenjeza Akhristu za amuna amene anali kudzakamba “mau ouzilidwa omwe ndi osoceletsa,” ndi ‘kuletsa anthu kukwatila.’—1 Timoteyo 4:1-3.
M’zaka za m’ma 200 zoyambilila, mwambo wa kusakwatila m’pamene unayamba kutenga malo m’machechi “Acikhristu” m’maiko a azungu. Buku yakuti Celibacy and Religious Traditions, inakamba kuti mwambo umenewu “wopewa za kugonana unali m’citidwe watsopano umene unayambika mu Ufumu wa Roma.”
Zaka mahandiledi zotsatila, pa misonkhano ya chechi komanso anthu ochedwa Azimbo a Chechi, analimbikitsa kusakwatila. Anali kuona kuti kugonana kunali kudetsa munthu, ndipo sikunali kugwilizana ndi nchito za m’busa. Komabe, buku yakuti Encyclopædia Britannica inakamba kuti podzafika “ca kumapeto kwa zaka za m’ma 900, azibusa ambili ngakhale mabishopu ena anali ndi akazi.”
Pa Misonkhano ya Lateran ya m’caka ca 1123 ndi 1139 imene inali kucitikila ku Roma, anakhwimitsa lamulo lakuti azibusa sayenela kukwatila. Kuyambila nthawi imeneyo, lamulo limeneli likali kugwila nchito m’Chechi ca Roma Katolika. Poika lamulo limeneli, chechi cinateteza udindo na cuma, zimene zinawonongeka pamene abusa amene anali pabanja analemba wilo kuti ana awo adzatenge katundu wa chechi.
MMENE MULUNGU AMAONELA ANTHU OSAKWATILA
Mau a Mulungu Baibo, amaonetsa bwino mmene Iye amaonela umbeta. Mmenemo, timaŵelengamo mau a Yesu okamba za anthu amene anakhalabe mbeta, monga iye, “cifukwa ca Ufumu wakumwamba.” (Mateyu 19:12) Nayenso mtumwi Paulo anakamba za Akhristu amene anasankha kutengela citsanzo cake cokhala wosakwatila “cifukwa ca uthenga wabwino.”—1 Akorinto 7:37, 38; 9:23.
Koma sikuti Yesu na Paulo anali kulamula atumiki kuti azikhala osakwatila iyai. Yesu anakamba kuti kukhala wosakwatila inali “mphatso” imene si otsatila ake onse anali nayo. Pamene Paulo analemba za “amene sali pabanja,” moona mtima anavomeleza kuti: “Ndilibe lamulo lililonse la Ambuye, koma ndikupeleka maganizo anga.”—Mateyu 19:11; 1 Akorinto 7:25.
Kuwonjezela apo, Baibo ionetsa kuti atumiki acikhristu ambili a m’zaka 100 zoyambilila, kuphatikizapo mtumwi Petulo, anali okwatila. (Mateyu 8:14; Maliko 1:29-31; 1 Akorinto 9:5) Cifukwa ca makhalidwe a ciwele-wele amene anawanda m’dziko la Roma, Paulo analemba kuti ngati woyang’anila wacikhristu anali wokwatila, anafunika kukhala “mwamuna wa mkazi mmodzi,” ndiponso wa ana omumvela.—1 Timoteyo 3:2, 4.
Awa sanali maukwati akuti kugonana kunali koletsedwa iyai. Paja Baibo imakamba momveka bwino kuti ‘mwamuna adzafunika kupeleka kwa mkazi wake mangawa ake.’ Imakambanso kuti anthu okwatilana sayenela kukanizana pankhani yogonana. (1 Akorinto 7:3-5) Conco, kukhala mtumiki wa Mulungu sikudalila kuti munthu acite kukhala wosakwatila, ndipo siciyeneletso ca atumiki acikhristu.
CIFUKWA CA UTHENGA WABWINO
Ngati kukhala wosakwatila si lamulo, n’cifukwa ciani Yesu ndi Paulo anakambapo za ubwino wokhala mbeta? Cifukwa cakuti munthu amene sali pabanja amakhala ndi mipata yambili youzako ena uthenga wabwino. Anthu amene sali pabanja angacite zambili mu utumiki, cifukwa sakhala ndi nkhawa zimene anthu ali m’cikwati amakhala nazo.—1 Akorinto 7:32-35.
Ganizilani citsanzo ca David. Iye anasiya nchito yake ya malipilo apamwamba m’dziko la Mexico, ndi kuyenda kumudzi m’dziko la Costa Rica kukaphunzitsa ena Baibo. Kodi David amaona kuti kukhala wosakwatila kunam’thandiza kucita zimenezi? Iye anati: “Kunanithandizadi. Cinali covuta kuzoloŵela cikhalidwe ndi umoyo watsopano. Koma cifukwa cakuti n’nali wosakwatila, sizinanivute kuzoloŵela.”
Nayenso Claudia, Mkhristu amene ni mbeta, anasamukila kumadela kumene alengezi ni ocepa. Iye anati: “Nimakondwela kutumikila Mulungu. Cikhulupililo canga na ubale wanga ndi Mulungu zimalimbilako nikaona mmene iye amanisamalila.”
Umbeta suyenela kucita kukhala mtolo iyai. Claudia anakambanso kuti: “Zilibe kanthu kaya uli pabanja kapena ayi, ukhoza kukhala wosangalala ngati upatsa Yehova Mulungu zinthu zabwino koposa.”—Salimo 119:1, 2.
“Zilibe kanthu kaya uli pabanja kapena ayi, ukhoza kukhala wosangalala ngati upatsa Yehova Mulungu zinthu zabwino koposa.”—Claudia