Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kukambilatu Zakutsogolo

Kukambilatu Zakutsogolo

Kodi munadzifunsapo kuti umoyo wanu na banja lanu udzakhala bwanji m’tsogolo? Kodi muona kuti mudzalemela kapena mudzasauka? Kodi m’banja mwanu mudzakhala cikondi kapena kusungulumwa? Kodi mudzakhala na moyo wautali, kapena mudzafa mwadzidzidzi? Anthu akhala akudzifunsa mafunso amenewa kwa zaka zambili.

Masiku ano, akatswili amafufuza zocitika za padziko lonse, na kufotokoza zimene zidzacitika m’tsogolo. Ngakhale kuti zambili zimene amakamba zimacitika, zina sizicitika, ndipo zina zalephela mocititsa manyazi. Mwacitsanzo, mu 1912, Guglielmo Marconi amene anali mmodzi mwa anthu oyamba kupanga telegalafu, analosela kuti: “Telegalafu imeneyi idzacititsa kuti nkhondo zithe.” Munthu wina woimila kampani yochedwa, Decca Record Company, amene anakana kujambula nyimbo za gulu loimba lochedwa Beatles mu 1962, anali kukhulupilila kuti magulu oimba magita adzatha m’tsogolo.

Ambili amafunsila kwa anthu amizimu kuti adziŵe zakutsogolo. Ena amafunsila malangizo kwa okhulupilila zakuthambo, ndipo kaŵili-kaŵili nkhani zawo zimapezeka m’magazini na m’manyuzipepa. Ena amafunsila kwa olosela zam’tsogolo kapena kwa owombeza, amene amati amalosela zimene zidzacitika kutsogolo poseŵenzetsa makhadi a njuga, manamba, kapena mizela ya padzanja.

Kale, anthu ena akafuna kudziŵa zakutsogolo anali kufunsila kwa ansembe ocita mayele amene anali kulosela zakutsogolo. Iwo anali kukamba kuti amauza anthu uthenga wocokela kwa mulungu amene anali kuimila. Mwacitsanzo, ena amakamba kuti Kolosase Mfumu ya ku Lydia, anatumiza mphatso zamtengo wapatali kwa wansembe wina wolosela zam’tsogolo ku Greece m’tauni ya Delphi, kuti adziŵe ngati adzapambana pa nkhondo yolimbana na Koresi wa ku Perisiya. Wansembeyo anauza Kolosase kuti adzagonjetsa “ufumu wamphamvu.” Poganiza kuti adzapambana, Kolosase anayenda kukacita nkhondo na Koresi, koma “ufumu wamphamvu” umene unagonjetsedwa unali wake!

Zimene wansembe wocita za mayele uja anakamba zinali zosoceletsa ndiponso zopanda phindu. Zikanaokabe kukhala zoona kaya Kolosase ndiye akanapambana nkhondo kapena ayi. Kolosase anataya zonse cifukwa ca kulosela kosoceletsa kumene kunam’bweletsela mavuto. Kodi aja amene amakonda kufunsila kwa olosela zam’tsogolo masiku ano, iwo zinthu zimawayendela bwino?