Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Mapeto a Dzikoli Ali Pafupi?

Kodi Mapeto a Dzikoli Ali Pafupi?

Anthu akhala akukamba kuti dzikoli lidzatha, koma likalipo, silinathe! Ndiye kodi nkhani ya kutha kwa dziko, ni yazoona kapena ni nkhambakamwa cabe?

KODI BAIBO IMATI CIANI?

  • Kodi dziko lidzatha bwanji?

  • Lidzatha liti?

  • Kodi n’zotheka kudzapulumuka?

  • Kodi zinthu zidzakhala bwanji dzikoli likadzatha?

Magazini ino yafotokoza mayankho a m’Baibo pa mafunso amenewa. Mayankhowo angakudabwitseni, koma adzakukhazikani mtima pansi.

Mboni za Yehova zingakonde kukuthandizani kudziŵa zambili za colinga ca Mulungu.