Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Tifunikila Dziko Labwino!

Tifunikila Dziko Labwino!

“Tikukhala m’dziko lodzala na mavuto,” anatelo António Guterres, kalembela wamkulu wa bungwe la United Nations. Kodi si zoona zimene anakamba?

Nthawi zambili pa nyuzi timamvela nkhani zodetsa nkhawa monga za:

  • Matenda na milili

  • Matsoka a zacilengedwe

  • Umphaŵi na njala

  • Kuwonongeka kwa cilengedwe na kutentha kwa padziko

  • Upandu, ciwawa, na katangale

  • Nkhondo

N’zosacita kufunsa kuti tifunikila dziko labwino. Dziko limene

  • Tidzakhalamo tili na thanzi labwino

  • Aliyense adzakhala wotetezeka

  • Mudzakhala cakudya coculuka

  • Lidzakhala lokongola

  • Aliyense adzacitilidwa zinthu mwacilungamo

  • Mudzakhala mtendele

Koma kodi titanthauza ciani tikanena kuti dziko labwino?

Kodi n’ciani cidzacitikila dziko limene tikukhalamoli?

Nanga tingacite ciani kuti tikakhalemo m’dziko labwino?

Magazini ino ya Nsanja ya Mlonda, ifotokoza mayankho a m’Baibo okhazika mtima pansi pa mafunso amenewa na ena.