Aliyense Amafuna Kukhala na Tsogolo Labwino
Kodi mumalakalaka kukhala na tsogolo lotani? Mosakayikila, mofanana na anthu ambili mumafuna kukhala na tsogolo labwino—tsogolo limene inu na banja lanu mudzakhala mwamtendele, mudzakhala acimwemwe, athanzi labwino, komanso simudzakhala na mavuto a zacuma.
Koma ambili amakayikila zakuti angakhale na tsogolo limene amafuna. Iwo aona zinthu zosayembekezeleka monga mlili wa COVID-19, zikusokoneza umoyo wa anthu, kubweletsa umphawi, na kutayitsa miyoyo yambili. Pa cifukwa cimeneci, iwo alibiletu ciyembekezo ca tsogolo labwino.
Cifukwa cakuti zinthu zimasintha mosayembekezeleka pa umoyo, anthu akuyesetsa kufuna-funa cimene cingawathandize kukhala na tsogolo labwino. Ena amakhulupilila kuti mphamvu zinazake zosaoneka ndizo zimayendetsa zocitika pa umoyo wawo. Ndipo ambili amayesetsa kuti apate maphunzilo apamwamba kapena cuma, poganiza kuti zinthu zimenezi ndizo zingawathandize kupeza zimene amafuna. Komanso pali ena amene amaganiza kuti kungokhala munthu wabwino n’kumene kungathandize kuti zinthu ziziwayendela bwino pa umoyo wawo.
Kodi zinthu zimenezi zingakuthandizenidi kukhala na tsogolo labwino limene mumafuna? Kuti mupeze yankho, muyenela kuganizila mafunso awa:
Kodi tsogolo lanu limadalila pa ciani maka-maka?
Kodi maphunzilo na ndalama zingakuthandizeni kukhala na tsogolo labwino?
Kodi kukhala munthu wabwino kungakuthandizeni kukhala na tsogolo labwino?
Mungapeze kuti malangizo odalilika amene angakuthandizeni kukhala na tsogolo labwino?
Kope ino ya Nsanja ya Mlonda ingakuthandizeni kupeza mayankho.