Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Maphunzilo na Ndalama Zingakuthandizeni Kukhala na Tsogolo Labwino?

Kodi Maphunzilo na Ndalama Zingakuthandizeni Kukhala na Tsogolo Labwino?

Ambili amaganiza kuti anthu ophunzila kwambili komanso olemela ali na tsogolo labwino. Iwo amakhulupilila kuti maphunzilo a ku yunivesite angathandize munthu kukhala wanchito wabwino, wothandiza kwambili m’banja, ndiponso nzika yabwino. Iwo angaganizenso kuti maphunzilo apamwamba amathandiza munthu kupeza nchito ya malipilo abwino, komanso kuti anthu amene ali na ndalama zambili amakhala acimwemwe.

CISANKHO CA ANTHU AMBILI

Ganizilani zimene Zhang Chen wa ku China anakamba. Iye anati: “N’nali kukhulupilila kuti niyenela kutenga digili ku yunivesite kuti umphawi wanga uthe. N’nali kukhulupililanso kuti nchito ya malipilo abwino idzanithandiza kukhala na umoyo wacimwemwe komanso wokhutilitsa.”

Pofuna kudzikonzela tsogolo labwino, ambili amacita zonse zotheka kuti akaphunzile ku mayunivesite ochuka, ngakhale a ku maiko ena. Zimenezi zinali kucitika kwambili mpaka pamene mlili wa COVID-19 unapangitsa kuti zikhale zovuta anthu kupita ku maiko ena. Lipoti la 2012 la bungwe lina loona pa zacuma na umoyo wa anthu linati: “52% pelesenti ya anthu amene anali kucita maphunzilo ku maiko ena anali ocokela ku Asia.”

Nthawi zambili makolo amagwila nchito molimbika kuti ana awo akacite maphunzilo a ku yunivesite ku maiko ena. Qixiang, wa ku Taiwan anati: “Makolo athu sanali olemela. Koma ana tonse anayi anatipeleka ku koleji ya ku America.” Kuti apeze ndalama zolipilila maphunzilo amenewo, banja lake linacita kutenga nkhongole yaikulu. Izi n’zimenenso mabanja ena ambili amacita.

KODI ZOTULUKAPO ZAKE ZAKHALA ZOTANI?

Ambili amene amayesetsa kuzama nawo maphunzilo ndiponso kufunafuna cuma amagwilitsidwa mwala

N’zoona kuti maphunzilo angathandize munthu kukhalako na umoyo wabwino. Koma si nthawi zonse pamene amathandiza ophunzila kupeza zimene anali kuyembekezela. Mwacitsanzo, ambili amagwila nchito molimbika kwa zaka zambili na kukongola ndalama zoculuka kuti alipilile maphunzilo apamwamba. Koma akatsiliza maphunzilowo sapeza nchito imene anali kufuna. Mu lipoti yake ya m’nyuzipepala ya ku Singapore yochedwa Business Times, Rachel Mui anati: “Vuto la kusoŵa nchito kwa anthu amene anacita maphunzilo a ku yunivesite likukulilakulila.” Munthu wina wophunzila kwambili wa ku Taiwan dzina lake Jianjie, anati, “Ambili amasoŵa cocita moti amangolola kugwila nchito yosagwilizana na maphunzilo a ku yunivesite amene anacita.”

Ngakhale anthu amene amapeza nchito yogwilizana na maphunzilo amene anacita, angaonebe kuti umoyo wawo sunakhale mmene anali kuyembekezela. Niran, wa ku Thailand anapita ku United Kingdom kukacita maphunzilo a ku yunivesite. Atabwelela kwawo, anapeza nchito yogwilizana na maphunzilo amene anacita. Iye anati: “Monga mmene n’nali kuyembekezela, digili imene n’natenga inanithandiza kupeza nchito ya ndalama zambili. Koma kuti nilandile malipilo amenewo, n’nafunika kugwila nchito molimbika komanso kwa maola ambili. M’kupita kwa nthawi, kampani imene n’nali kugwilako nchito inacotsa anchito ambili kuphatikizapo ine. N’nazindikila kuti kulibe nchito imene ingathandize munthu kukhala na tsogolo labwino.”

Ngakhale anthu olemela amene amaoneka kuti ali na umoyo wabwino, amakumanabe na mavuto a m’banja, amadwala, komanso amakhalabe na nkhawa pa nkhani ya zacuma. Katsutoshi wa ku Japan anakamba kuti, “N’nali na ndalama zambili, koma n’nalibe cimwemwe cifukwa anthu anali kunicitila nsanje, ndipo sanali kucita nane zinthu mwacikondi.” Mayi wina wa ku Vietnam dzina lake Lam anati: “Nimaona anthu ambili akufunafuna nchito ya malipilo apamwamba kuti apeze ndalama zambili. Koma zotulukapo zake n’zakuti amakhala na nkhawa kwambili, komanso amapsinjika maganizo ngakhale kudwala kumene.”

Mofanana na Franklin, anthu ambili azindikila kuti pali zinthu zambili zofunika ngako pa umoyo kuposa kucita maphunzilo apamwamba kapena kukhala na cuma. M’malo moika maganizo onse pa kufuna-funa cuma, ena mwa anthu amenewa amayesa kudzikonzela tsogolo labwino mwa kuyesetsa kukhala anthu abwino na kucitila ena zabwino. Koma kodi kucita zimenezi kungathandize munthu kukhala na tsogolo labwino? Nkhani yotsatila idzayankha funso limeneli.