Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YA PACIKUTO | BAIBULO—MMENE YAPULUMUKILA

Cifukwa Cake Baibulo Yapulumuka

Cifukwa Cake Baibulo Yapulumuka

Baibulo yapulumuka zambili. Pa cifukwa cimeneci, masiku ano tili na mwai wokhala nayo ndi kuiŵelenga. Ngati mwasankha kuŵelenga Baibulo lomasulidwa bwino, mungatsimikizile kuti muŵelenga Malemba ogwilizana kwambili ndi zolemba zoyambilila. * Baibulo siinawole ngakhale kuti inalembedwa pa zinthu zosalimba, ndipo inatetezeka kwa anthu otsutsa ndi kwa omasulila amene anafuna kusintha uthenga wake. Kodi zimenezi zinatheka bwanji? Kodi buku limeneli lili ndi uthenga wabwanji kwenikweni?

“Tsopano nikhulupilila kuti Baibulo imene nili nayo ni mphatso yocokela kwa Mulungu”

Anthu ambili amene amaphunzila Baibulo afika pokamba mau amene mtumwi Paulo analemba akuti: “Malemba onse anauzilidwa ndi Mulungu.” (2 Timoteyo 3:16) Iwo akhulupilila kuti Baibulo lapulumuka cifukwa ni Mau a Mulungu, ndi kuti Iye ndiye waiteteza kufikila masiku ano. Faizal amene takamba m’nkhani yoyambilila, anaganiza zophunzila Baibulo n’colinga cakuti adzionele yekha ngati n’locokeladi kwa Mulungu. Zimene anapeza ataiphunzila, zinam’cititsa cidwi. Posapita nthawi, iye anazindikila kuti ziphunzitso zambili zimene zili m’machechi osiyanasiyana si zipezeka m’Baibulo. Kuwonjezela apo, iye anakhudzidwa kwambili atadziŵa colinga ca Mulungu ca dziko lapansi cimene Mau Ake amakamba.

Iye anakambanso kuti: “Tsopano nikhulupilila kuti Baibulo imene nili nayo ni mphatso yocokela kwa Mulungu. Ngati Mulungu anapanga cilengedwe conse, iye sangalephele kutipatsa Baibulo ndi kuiteteza. Ndipo ngati ningaganize kuti Mulungu sangateteze Baibulo, zingakhale monga nikamba kuti Mulungu alibe mphamvu. Kumeneku kungakhale kukaikila Mulungu Wamphamvuyonse. Koma ndine ndani kuti nicite zimenezo?”—Yesaya 40:8.

^ par. 3 Onani nkhani imene ili mu Nsanja ya Olonda ya May 1, 2008, ya mutu wakuti: “Kodi Mungadziŵe Bwanji Baibulo Lomasulilidwa Bwino?