Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YA PACIKUTO | BAIBULO—MMENE YAPULUMUKILA

Nkhani Yofunika Kwambili

Nkhani Yofunika Kwambili

Palibe buku ina yacipembedzo imene ingalingane ndi Baibulo. Anthu ambili akhala akuikhulupilila kwa nthawi yaitali kupambana mabuku ena. Komabe, palibe buku ina imene yafufuzidwa kwambili ndi kutsutsidwa kuposa Baibulo.

Mwacitsanzo, akatswili ena amakaikila ngati zimene zili m’Mabaibulo a masiku ano n’zimenenso zinali m’mipukutu yoyambilila ya Baibulo. Pulofesa wina wa maphunzilo a zacipembedzo anati: “Sitidziŵa ngati tamasulila Baibulo molondola mogwilizana ndi mipukutu yoyambilila. Makope amene tili nawo ali ndi zolakwika zambili, ndipo analembedwa zaka mahandiledi ambili mipukutu yoyambilila ya Baibulo italembedwa kale. Makope amenewa ni osiyana ndi mipukutu yoyambilila m’njila zambili.”

Anthu ena amakaikila ngati Baibulo ni yoona cifukwa ca cipembedzo cao. Mwacitsanzo, Faizal anaphunzitsidwa ndi makolo ake, amene sanali Akhiristu, kuti Baibulo ni buku yopatulika koma inasinthidwa. Iye anakamba kuti: “Anthu akafuna kuniphunzitsa Baibulo, n’nali kukana. N’nali kuona kuti io analibe Baibulo yoyambilila ndipo Baibulo imene anali nayo inasinthidwa.”

Kodi kudziŵa kuti Baibulo inasinthidwa kapena ayi kuli ndi phindu? Inde. Ganizilani mafunso awa: Kodi mungakhulupilile malonjezo otonthoza a m’Baibulo ngati simudziŵa kuti malonjezowo analimo m’mipukutu yoyambilila ya Baibulo? (Aroma 15:4) Kodi mukanatsatila mfundo za m’Baibulo popanga zosankha zofunika kwambili monga zokhudza nchito, banja, kapena kulambila, ngati Mabaibulo a masiku ano anali ndi zolakwika zokhazokha?

Ngakhale kuti mipukutu yoyambilila ya Baibulo palibe, tingatsimikizile kuti Mabaibulo amene tili nao ni olondola mwa kuwayelekezela ndi makope ndiponso mipukutu yakale ya Baibulo. Kodi mipukutu imeneyo inapulumuka bwanji kuti isawonongeke? Nanga inapulumuka bwanji kwa anthu otsutsa ndi ofuna kusintha uthenga wake? Kodi kudziŵa mmene inapulumukila kungakuthandizeni bwanji kukhulupilila kuti Baibulo imene tili nayo masiku ano ni yoona? Pezani mayankho a mafunso amenewa m’nkhani yotsatila yokamba za mmene Baibulo inapulumukila.