Citsimikizo Camphamvu Kucokela ku Kacilembo Kocepetsetsa Kaciheberi
Kodi tingatsimikiziledi kuti malonjezo onse a Mulungu adzakwanilitsidwa? Yesu anali kukhulupilila zimenezi, ndipo zimene anali kuphunzitsa zinathandiza anthu kukhala na cikhulupililo. Ganizilani zimene anakamba pa Ulaliki wake wa pa Phili wolembewa pa Mateyu 5:18. Iye anati: “Ndithu ndikukuuzani kuti kumwamba ndi dziko lapansi zingacoke mosavuta, kusiyana n’kuti kalemba kocepetsetsa kapena kacigawo kamodzi ka lemba kacoke m’Cilamulo zinthu zonse zisanacitike.”
Kacilembo kocepa kwambili mu alifabeti ya Ciheberi ni י (yod). Aka ni kacilembo koyambilila pa zilembo zinayi zoimila dzina la Mulungu lopatulika lakuti Yehova. * Kuwonjezela pa mau na zilembo zeni-zeni za m’Cilamulo ca Mulungu, alembi na Afarisi anali kuona kuti kacigawo ka cilembo ciliconse kanali kofunika maningi.
Yesu anali kukamba kuti kumwamba ndi dziko lapansi zingacoke kusiyana n’kuti mbali yocepa kwambili ya m’Cilamulo isakwanilitsike. Komabe, Malemba amatitsimikizila kuti kumwamba na dziko lapansi zidzakhala kwamuyaya. (Salimo 78:69) Conco, mfundo yocititsa cidwi imeneyi ionetsa kuti ngakhale mbali yocepa kwambili ya m’Cilamulo singapite pacabe osakwanilitsika.
Kodi Yehova Mulungu amaona kuti mbali zocepa kwambili n’zofunika? Inde. Ganizilani izi: Aisiraeli akale anauzidwa kuti safunika kuphwanya fupa lililonse la nkhosa ya mwambo wa Pasika. (Ekisodo 12:46) Zimenezi zingaoneke zazing’ono. Kodi iwo anamvetsa cifukwa cake sanafunike kuphwanya fupa lililonse? Mwina ayi. Komabe, Yehova Mulungu anadziŵa kuti mbali imeneyi inali ulosi woonetsa kuti Mesiya sadzaphwanyidwa fupa lililonse akadzaphedwa mwa kupacikidwa pamtengo wozunzikilapo.—Salimo 34:20; Yohane 19:31-33, 36.
Kodi mau a Yesu atiphunzitsa ciani? Na ise tingakhale na cidalilo conse kuti malonjezo onse a Yehova Mulungu adzakwanilitsidwa, ngakhale mbali iliyonse yaing’ono. Ha! N’citsimikizo camphamvu cotani nanga kucokela ku kacilembo kocepetsetsa kaciheberi!
^ par. 3 Mu alifabeti ya Cigiriki, kacilembo kocepetsetsa ni iota. Mwacionekele kacilembo aka kalinganako na kaciheberi י (yod). Popeza Cilamulo ca Mose cinalembedwa m’Ciheberi, Yesu ayenela kuti anali kukamba za kacilembo kaciheberi.