NKHANI YA PACIKUTO | KODI TINGAPEZE KUTI CITONTHOZO?
Kupeza Citonthozo pa Nthawi Yovuta
Mavuto amene timakumana nawo amakhala osiyana-siyana. M’nkhani ino sitingakambe za mavuto onse, koma tidzakambilana za mavuto anayi amene tawachula poyamba paja. Onani mmene anthu amene akumanapo na mavuto osiyana-siyana apezela citonthozo ceni-ceni kwa Mulungu.
KUTHA KWA NCHITO
Seth * anakamba kuti: “Nchito yanga ndi ya mkazi wanga inatha pa nthawi imodzi. Kwa zaka ziŵili tinali kudalila cabe thandizo la acibale ndi mapisiweki. Zotsatilapo zake zinali zakuti mkazi wanga anayamba kuvutika maganizo, ndipo ine n’nali kudziwona ngati wacabe-cabe.
“N’ciani cinatithandiza kupilila? Priscilla nthawi zambili anali kukumbukila mau a Yesu a pa Mateyu 6:34. Yesu anakamba kuti sitiyenela kudela nkhawa za tsiku lotsatila, cifukwa tsiku lililonse lili ndi zodetsa nkhawa zake. Ndiponso pemphelo locokela pansi pa mtima linamuthandiza kupilila. Koma ine, lemba limene linanilimbikitsa kwambili ni Salimo 55:22. Mofanana ni wamasalimo, n’natulila Yehova nkhawa zanga ndipo iye ananicilikiza. Ngakhale kuti tsopano n’nayamba kuseŵenza, nimayesetsa kukhala na umoyo wosafuna zambili mogwilizana na malangizo a Yesu a pa Mateyu 6:20-22. Kuwonjezela apo, ubwenzi wathu ndi Mulungu walimba kwambili, ndipo ndife ogwilizana kwambili pabanja pathu.”
Jonathan anakamba kuti, “Pamene Bizinesi yathu inatha, n’nali na nkhawa kwambili. Cifukwa ca mavuto a zacuma, nchito imene tinagwila mwamphamvu kwa zaka 20, inapita pacabe. Tinayamba kukangana ndi mkazi wanga cifukwa cosoŵa ndalama. Tinali kuopa kugula zinthu pa nkhongole cifukwa coganiza kuti makampani satilola kugula pa nkhongole.
“Koma Mau a Mulungu ndi mzimu wake woyela zinatithandiza kusankha zocita mwanzelu. N’nali wokonzeka kugwila nchito iliyonse imene yapezeka, ndipo tinayamba kupewa kugula zinthu zosafunika kweni-kweni. Popeza ndife Mboni za Yehova, Akhiristu anzathu analinso kutithandiza. Anali kutilimbikitsa ndi kutithandiza panthawi imene zinthu zinali zovuta kwambili.”
KUTHA KWA CIKWATI
Raquel anati: “Pamene mwamuna wanga ananisiya, cinaniŵaŵa kwambili, ndipo n’nakhumudwa. N’nayamba kudzimvela cisoni kwambili. Koma n’napemphela kwa Mulungu, ndipo ananitonthoza. Mtendele wa Mulungu unali kuteteza mtima wanga nikapemphela kwa iye tsiku lililonse. Zinali ngati kuti iye wacilitsa mtima wanga.
“Cifukwa ca Mau ake, Baibulo, n’naleka kukhala wokhumudwa. N’nali kukumbukila mau a mtumwi Paulo a pa Aroma 12:21, akuti: ‘Musalole kuti coipa cikugonjetseni, koma pitilizani kugonjetsa coipa mwa kucita cabwino.’
“Pofuna kunithandiza, mnzanga wina ananiuza kuti niiŵaleko cabe zimene zinacitikazo. Iye ananiwonetsa mau a pa Mlaliki 3:6 n’kuniuza kuti pali nthawi “yovomeleza kuti cinthu catayika.” Malangizo amenewa anali oŵaŵa, koma ndi amene ananithandiza. Lomba nili na zolinga zatsopano pa umoyo.”
Elizabeth anakamba kuti, “Cikwati cikatha, munthu amafuna thandizo. Ine n’nali na mnzanga amene anali kunithandiza tsiku lililonse. Anali kulila nane pamodzi, kunitonthoza, ndi kunipangitsa kudzimva kuti ndine wofunika. Nikhulupilila kuti Yehova anaseŵenzetsa mnzanga ameneyu kuti anitonthoze.”
MATENDA NA UKALAMBA
Luis, amene tamuchula m’nkhani yoyamba, ali na vuto lalikulu la mtima, ndipo maulendo aŵili anatsala pang’ono kufa. Iye amafunika kukhala ku oksijini kwa maola 16 pa tsiku. Luis anati: “Nimapemphela kwa Yehova kaŵili-kaŵili. Nikapemphela, mzimu wake umanipatsa mphamvu. Pemphelo limanithandiza kupilila cifukwa Mulungu nimam’khulupilila komanso nimadziŵa kuti amanikonda.”
Petra, amene ali na zaka za m’ma 80, anati: “Nimafuna kucita zinthu zambili, koma siningakwanitse. Cimaniŵaŵa kuona kuti mphamvu zanga ziyenda zisila. Nimakhala otopa, ndipo moyo wanga umadalila cabe mankhwala. Kaŵili-kaŵili nimamvela ngati mmene Yesu anamvelela pamene anapempha Atate wake kuti, ngati n’kotheka alole mavuto kumupitilila. Koma Yehova anamupatsa mphamvu, ndipo inenso amanilimbikitsa. Pemphelo lakhala ngati mankhwala amene nimamwa tsiku lililonse. Nimamvelako bwino nikapemphela kwa Mulungu.”—Mateyu 26:39.
Afilipi 4:13.
Nayenso, Julian amene wakhala akudwala matenda opha ziwalo kwa zaka 30, amamvela cimodzimodzi. Iye anati: “M’malo mokhala pa mpando wa mkulu wa pakampani, tsopano nimakhala pa njinga ya olemala. Koma moyo wanga uliko bwino tsopano cifukwa nimadzipeleka kwambili kutumikila ena. Kukhala opatsa kumabweletsa cimwemwe ngakhale tikumana ndi mavuto, ndipo Yehova amasunga lonjezo lake lakuti adzatilimbikitsa pamene tifunikila kulimbikitsidwa. Mofanana ndi Paulo, ningakambe motsimikiza kuti: ‘Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kucokela kwa iye amene amandipatsa mphamvu.’”—WACIBALE AKAMWALILA
Antonio anati: “Atate atamwalila pa ngozi ya pamsewu, poyamba zinanivuta kukhulupilila. N’nali kuona kuti zimene zinacitika zinali zopanda cilungamo cifukwa atate anali munthu wosalakwa. Koma palibe cimene nikanacita. Anakhala wokomoka kwa masiku asanu, pambuyo pake anamwalila. N’nayesetsa kupewa kulila pamaso pa amayi, koma nikakhala kwanekha n’nali kulila kwambili. N’nali kudzifunsa kuti, ‘N’cifukwa ciani? N’cifukwa ciani zimenezi zacitika?’
“M’masiku ovuta amenewo, n’nali kupempha Yehova kuti anithandize kupilila ndi kukhala na mtendele wa m’maganizo. Ndipo pang’ono ndi pang’ono, mtima unakhala m’malo. N’nakumbukila kuti Baibulo imakamba kuti “zinthu zosayembekezeleka” zingathe kugwela aliyense wa ife. Popeza kuti Mulungu sanganame, nikhulupilila kuti atate nidzawaonanso pa nthawi ya kuuka kwa akufa.”—Mlaliki 9:11; Yohane 11:25; Tito 1:2.
Robert, amene tamuchula m’nkhani yoyamba, ali na maganizo ofanana ndi amenewa. Iye anati: “Ine na mkazi wanga tinali na mtendele wa m’maganizo umene lemba la Afilipi 4:6, 7 limakamba. Tinapeza mtendele umenewo cifukwa copemphela kwa Yehova. Mtendele wa mumtima unatithandiza kukhala na mphamvu zofotokozela atolankhani za ciyembekezo cathu ca ciukililo. Ngakhale kuti mwana wathu anafa pa ngozi ya ndeke, timakumbukilabe nthawi imene tinali kusangalalila pamodzi. Timayesetsa kuganizila zimenezo.
“Pamene Akhiristu anzathu anatiuza kuti anationa pa TV tikufotokoza molimba mtima za cikhulupililo cathu, tinawauza kuti zimenezo zinatheka cifukwa ca mapemphelo awo ambili-mbili amene anali kutipelekela. Sitikayikila kuti Yehova anali kutilimbikitsa kupitila m’mauthenga ambili olimbikitsa amene Akhiristu anzathu anali kutitumila.”
Monga taonela m’zitsanzo zapitazi, Mulungu angathe kutonthoza anthu amene akumana na mavuto osiyana-siyana. Kodi inunso angakutonthozeni? Kaya mukumana na mavuto abwanji, mungathe kupeza citonthozo. * Conco, muyenela kupempha Yehova kuti akuthandizeni. Iye ndi “Mulungu amene amatitonthoza m’njila iliyonse.”—2 Akorinto 1:3.
^ par. 5 Maina ena m’nkhani ino asinthidwa.
^ par. 23 Ngati mufuna thandizo kuti mukhale pafupi na Mulungu kapena kuti mupeze citonthozo, pemphani a Mboni za Yehova m’dela lanu kapena lembelani kalata ku ofesi ya nthambi ya kufupi na kwanu.